ZAKUMAPETO
Mawu kwa Makolo Achikhristu:
Monga makolo, mumafunitsitsa kuthandiza ana anu kuti ayambe kukonda Yehova komanso kuti adzipereke kwa iye. Kodi mungatani kuti muthandize ana anu kuti afike pobatizidwa? Kodi ndi nthawi iti imene angayenerere kubatizidwa?
Yesu analamula otsatira ake kuti: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.” (Mat. 28:19) Mawu amenewa akusonyeza kuti chofunika kwambiri kuti munthu abatizidwe ndi kukhala wophunzira wa Yesu. Apa tikutanthauza kuti munthuyo ayenera kumvetsa zimene Yesu anaphunzitsa, kuzikhulupirira komanso kuzitsatira mosamala. Ndipo zimenezi n’zoti ngakhale ana aang’ono angakwanitse.
Makolo muzipereka chitsanzo chabwino kwa ana anu ndipo muzikhomereza mawu a Yehova m’mitima yawo. (Deut. 6:6-9) Mungagwiritse ntchito mabuku monga la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndi lakuti Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani? pophunzitsa ana anu mfundo zoyambirira za choonadi ndi kuwathandiza kuti azichita zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Muzithandiza ana anu kuti azitha kufotokoza m’mawu awoawo zimene amakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Zinthu zimene mungawaphunzitse, zimene mungachite powalimbikitsa, kuphunzira Baibulo paokha, kulambira kwa pabanja, misonkhano ya mpingo ndiponso anthu abwino ocheza nawo, zingawathandize kuti apite patsogolo mpaka abatizidwe komanso zidzawathandiza mpaka kalekale. Muziwathandizanso kuti akhale ndi zolinga zauzimu.
Lemba la Miyambo 20:11 limati: “Ngakhale mnyamata amadziwika ndi ntchito zake, ngati zochita zake zili zoyera ndiponso zowongoka.” Kodi ndi zinthu ziti zimene mwana ayenera kuchita posonyeza kuti tsopano ndi wophunzira wa Yesu Khristu ndipo ndi woyenerera kubatizidwa?
Mwana amene akufuna kubatizidwa, ayenera kukhala womvera makolo ake. (Mac. 5:29; Akol. 3:20) Pofotokoza za Yesu ali ndi zaka 12, Baibulo limati: “Anapitiriza kuwamvera [makolo ake].” (Luka 2:51) N’zoona kuti simungayembekezere kuti mwana wanu azichita zonse osalakwitsa chilichonse. Komabe monga munthu woti akufuna kubatizidwa, ayenera kuyesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu ndipo azidziwika kuti ndi mwana womvera makolo.
Ayeneranso kusonyeza kuti amakonda kuphunzira Mawu a Mulungu. (Luka 2:46) Kodi mwana wanu amakonda kusonkhana ndiponso kuyankha pa misonkhano? (Sal. 122:1) Kodi amakonda kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kuphunzira Baibulo payekha?—Mat. 4:4.
Mwana amene akufuna kubatizidwa ayenera kuyesetsa kuti aziika zinthu za Ufumu patsogolo. (Mat. 6:33) Amadziwa kuti ali ndi udindo wouza ena zimene amakhulupirira. Amatha kulalikira pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira ndipo sachita manyazi kuuza aphunzitsi ake ndi anzake akusukulu kuti ndi wa Mboni za Yehova. Ndiponso amakonzekera ndi kukamba nkhani zimene wapatsidwa mu Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu.
Amayesetsanso kukhala ndi makhalidwe abwino ndipo amapewa kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33) Zimenezi zimaonekera m’zinthu zimene amakonda monga nyimbo, mafilimu, mapologalamu apa TV, masewera apakompyuta ndi mmene amagwiritsirira ntchito intaneti.
Pali ana ambiri amene apindula chifukwa cha khama la makolo awo, ndipo anatenga choonadi kukhala chawochawo moti anabatizidwa ali aang’ono. Yehova apitirize kukudalitsani pamene mukuyesetsa kuthandiza ana anu kuti asankhe kuchita zimenezi chifukwa n’zofunika kwambiri pa ubwenzi wawo ndi Yehova.
Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizidwa:
Kutumikira mumpingo ngati wofalitsa wosabatizidwa ndi mwayi waukulu kwambiri. Tikukuyamikirani chifukwa cha kupita kwanu patsogolo mwauzimu. Kuphunzira Baibulo kwakuthandizani kudziwa Mulungu ndiponso kukhulupirira malonjezo ake.—Yoh. 17:3; Aheb. 11:6.
N’kutheka kuti musanayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, munali m’chipembedzo chinachake kapenanso mwina simunali m’chipembedzo chilichonse. Kapena munkachita zinthu zina zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Koma tsopano mwasonyeza chikhulupiriro ndipo mwalapa, kutanthauza kuti mukumva chisoni kwambiri chifukwa cha zoipa zimene munkachita komanso mwatembenuka, kutanthauza kuti mwasiya zoipa zimene munkachita ndipo mwatsimikiza kuti muzichita zabwino zimene Mulungu amafuna.—Mac. 3:19.
Komanso mwina ‘kuyambira muli akhanda’ mwadziwa malemba oyera, ndipo zimenezi zakuthandizani kuti musachite nawo zinthu zoipa zosiyanasiyana. (2 Tim. 3:15) Munaphunzira mmene mungapewere kuti musamangotengera zochita za anzanu komanso zomwe mungachite ngati ena akukukakamizani kuchita zinthu zimene Yehova amati n’zoipa. Munasonyeza chikhulupiriro polowa m’gulu la Mulungu ndi kumauza ena zimene mumakhulupirira. Munaphunzitsidwanso mmene mungachitire utumiki wachikhristu. Tsopano munasankha kutumikira Yehova ngati wofalitsa wosabatizidwa.
Ndiye kaya munaphunzira za Yehova muli aang’ono kapena mutakula kale, panopo muyenera kuganizira zochita zinthu ziwiri zimene zingakuthandizeni kupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu. Zinthu zake ndi kudzipereka ndiponso kubatizidwa. Munthu amadzipereka kwa Yehova pomufotokozera m’pemphero zimene wasankha zoti akufuna kumutumikira mpaka kalekale. (Mat. 16:24) Kenako amabatizidwa m’madzi kusonyeza kudzipereka kwakeko. (Mat. 28:19, 20) Mukadzipereka ndi kubatizidwa, mumakhala ndi mwayi waukulu kwambiri woikidwa kukhala mtumiki wa Yehova Mulungu.
Monga mmene mwaonera pophunzira Baibulo, muzikumana ndi mayesero osiyanasiyana. Kumbukirani kuti Yesu atangobatizidwa kumene, ‘mzimu unamutsogolera kuchipululu kuti akayesedwe ndi Mdyerekezi.’ (Mat. 4:1) Nanunso mukabatizidwa n’kukhala wophunzira wa Khristu, muzikumana ndi mayesero. (Yoh. 15:20) Mayeserowo angakhale osiyanasiyana. Mwina mungamatsutsidwe ndi anthu a m’banja lanu. (Mat. 10:36) Kapena munganyozedwe ndi anzanu akusukulu, akuntchito kapenanso omwe munkacheza nawo poyamba. Nthawi zonse muzikumbukira mawu a Yesu opezeka pa Maliko 10:29, 30, akuti: “Ndithu ndikukuuzani amuna inu, palibe amene anasiya nyumba, abale, alongo, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100 m’nthawi ino. Iye adzapeza nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, limodzi ndi mazunzo, ndipo m’nthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.” Choncho yesetsani kupitirizabe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi kutsatira mfundo zake zolungama.
Ngati mukufuna kubatizidwa, uzani wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu. Akulu adzakambirana nanu mafunso amene ali m’bukuli kuti aone ngati muli woyenerera kubatizidwa. Mukhoza kuyamba kumawerenga mafunso amenewa pa nthawi yanu yophunzira Baibulo panokha.
Pokonzekera kukambirana ndi akulu mafunsowa, mungachite bwino kuwerenga ndi kusinkhasinkha malemba amene aikidwa pamenepo. Ngati mungafune, mukhoza kulemba notsi zanu m’bukuli kapena pena paliponse. Pokambirana ndi akulu, mungadzagwiritse ntchito notsi zanuzo, komanso bukuli litha kudzakhala lotsegula. Ngati simukumvetsa mafunso ena, funsani amene akukuphunzitsani Baibulo kapena akulu kuti akuthandizeni.
Mukamakambirana ndi akulu mafunsowa, musaganize kuti mukufunika kupereka mayankho aatali. Mayankho aafupi komanso ofotokoza zinthu m’mawu anuanu ndiye abwino. Poyankha mafunso ambiri, mungachite bwino kutchula lemba limodzi kapena awiri omwe akusonyeza mfundo ya m’Malemba pa yankho lanulo.
Ngati zikuoneka kuti simunadziwebe mokwanira ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo, akulu adzakonza zoti mupitirize kuphunzira n’cholinga choti mufike potha kufotokoza m’mawu anuanu mfundo zimene mukuphunzira m’Malemba, ndipo mutha kudzabatizidwa nthawi ina.
[Mawu kwa akulu: Malangizo opendera ofuna kubatizidwa ali patsamba 208-212.]