Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hf gawo 9 mbali 1-2
  • Muzilambira Yehova Mogwirizana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilambira Yehova Mogwirizana
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA
  • 2 KULAMBIRA KWA PABANJA N’KOFUNIKA
  • Mphatso Yothandiza kwa Mabanja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kulambira kwa Pabanja Kuzikhala Kosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • “Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf gawo 9 mbali 1-2
Mwamuna ndi mkazi wake akuphunzira Baibulo limodzi

MUTU 9

Muzilambira Yehova Mogwirizana

‘Lambirani amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.’—Chivumbulutso 14:7

M’kabukuka taona kuti Baibulo lili ndi mfundo zambiri zimene zingathandize banja lanu. Yehova amafuna kuti mukhale osangalala. Iye amalonjeza kuti mukamaika zofuna zake pamalo oyamba, “zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Amafunitsitsa mutakhala naye pa ubwenzi wabwino. Choncho muziyesetsa kulimbitsa ubwenziwu. Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri.—Mateyu 22:37, 38.

1 MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

Mwamuna ndi mkazi wake akulalikira limodzi

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Yehova anati: “Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.” (2 Akorinto 6:18) Mulungu amafuna kuti mukhale mnzake wapamtima. Pemphero lingakuthandizeni kuchita zimenezi. Yehova amatiuza kuti ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Atesalonika 5:17) Iye amafunitsitsa kumva zakukhosi kwanu. (Afilipi 4:6) Mukamapemphera limodzi, banja lanu lidzaona kuti Mulungu ndi mnzanu weniweni.

Koma sikuti muzingolankhula ndi Mulungu. Muyeneranso kumvetsera akamakulankhulani. Mungachite zimenezi pophunzira Mawu ake ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo. (Salimo 1:1, 2) Muziganiziranso kwambiri zimene mwaphunzira. (Salimo 77:11, 12) Kuti mumvetsere Mulungu muyeneranso kufika pa misonkhano yachikhristu nthawi zonse.—Salimo 122:1-4.

Kuuza anthu ena za Yehova kungakuthandizeninso kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Choncho muzigwira ntchitoyi mwakhama.—Mateyu 28:19, 20.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikhala ndi nthawi yowerenga Baibulo ndiponso yopemphera tsiku lililonse

  • Muziona kuti zinthu zokhudza kulambira n’zofunika kuposa zosangalatsa

2 KULAMBIRA KWA PABANJA N’KOFUNIKA

Bambo akukonzekera kuphunzira ndi banja lake kenako akupanga kulambira kwa pa banja

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Banja lanu liyenera kukhala ndi pulogalamu yolambira Yehova limodzi ndipo muziyesetsa kuti musamaphonye. (Genesis 18:19) Koma si zokhazi. Muyeneranso kuganizira za Mulungu nthawi zonse. Muzithandiza banja lanu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu polankhula za iye ‘mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Tsanzirani Yoswa amene ananena kuti: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Pokonza pulogalamu yophunzitsa banja lanu, muziganizira zimene zingathandize aliyense

Mayi akuwerengera mwana wake; banja likuchita sewero la m’Baibulo; bambo akuphunzira ndi mwana wake

MUZITUMIKIRA YEHOVA MOSANGALALA

Kunena zoona, kulambira Yehova Mulungu n’kosangalatsa kwambiri kuposa chinthu china chilichonse. Iye amasangalala kwambiri akaona kuti mukumutumikira mokhulupirika limodzi ndi banja lanu. Mukamatero, mudzayamba kukonda kwambiri Yehova ndiponso kumutsanzira. (Maliko 12:30; Aefeso 5:1) Kulola Mulungu kuti azitsogolera banja lanu kumathandiza kuti banjalo likhale logwirizana. (Mlaliki 4:12; Yesaya 48:17) Zonsezi zingathandize kuti banja lanu likhale losangalala mpaka kalekale ndipo mudzaona kuti “Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.”—Deuteronomo 12:7.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndi liti pamene ndinapemphera limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wanga?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene ndingaphunzire ndi banja langa kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu?

MALANGIZO KWA MUTU WA BANJA

  • Musalole chilichonse kusokoneza pulogalamu yanu yophunzira Baibulo ndi banja lanu

  • Muzigwirizana zimene mudzaphunzire n’cholinga choti aliyense azikonzekera, tsikulo lisanafike

  • Muzionetsetsa kuti aliyense alipo

  • Muzithandiza aliyense kuti azimasuka komanso kusangalala pa nthawi yolambira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena