Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/06 tsamba 7
  • Kodi Mwana Wanu Angathe Kusankha Zinthu Mwanzeru?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwana Wanu Angathe Kusankha Zinthu Mwanzeru?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kupulumutsa Moyo ndi Mwazi—Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mafunso Ophunzirira Brosha ya Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 1/06 tsamba 7

Kodi Mwana Wanu Angathe Kusankha Zinthu Mwanzeru?

1. Kodi achinyamata a Mboni asankha zotani pankhani ya magazi? Perekani chitsanzo.

1 Kodi tikunena kusankha zinthu mwanzeru pa nkhani yotani? Pa nkhani yoikidwa magazi. Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1991, ya mutu wakuti “Yendani Monga Momwe Mwalangizidwira ndi Yehova,” inasonyeza kuti ana ambiri a Mboni za Yehova aonetsa kulimba mtima posankha okha kumvera lamulo la Mulungu losala magazi. Zimenezi zikutsimikizira kuti anawa, mofanana ndi makolo awo, akuona kufunika komvera lamulo losala magazi. Kodi mwana wanu angafunikire kusankha yekha zimene akufuna pankhaniyi?

2. Kodi ndi mfundo iti imene khoti lina linagwiritsa ntchito poweruza mlandu wa mwana amene anakana kuikidwa magazi, ndipo kodi makolo achikristu ndi ana awo angaphunzirepo chiyani pamenepa?

2 Kodi Malamulo Amati Chiyani? Ku United States, pa makhoti onse aakulu, khoti lalikulu ku Illinois ndilo linalamulapo kuti ana nawonso ali ndi ufulu wokana kuikidwa magazi. Poweruza mlandu wa mlongo wina wa zaka 17, khotilo linati: “Ngati pali umboni woona ndiponso wosatsutsika wakuti mwanayo akuzindikira zotsatirapo za zimene wasankha ndi kuti nkhaniyi waiganizira monga mmene angachitire munthu wamkulu, ndiye kuti mwanayo ali ndi ufulu wolola kapena wokana chithandizo chinachake kuchipatala mogwirizana ndi mfundo ya zamalamulo yakuti ana ena amakhwima maganizo ali aang’ono.” Choncho, pofuna kudziwa ngati mwana ali wokhwima maganizo moti atha kusankha yekha zimene akufuna, madokotala kapena akuluakulu a boma angam’funse mwana wodwalayo kuti amve okha mwanayo akukana kuikidwa magazi. Panthawiyi mwanayo amafunikira kumvetsa bwino za kuopsa kwa matenda amene akudwalawo ndiponso amafunikira kumvetsa zotsatirapo za zimene wasankha komanso amafunikira kufotokoza bwinobwino chikhulupiriro chake pa zimene malamulo a Mulungu amanena pa nkhani ya magazi.

3. Kodi ndi mafunso otani amene makolo ayenera kuwaganizira mofatsa, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kutero?

3 Kodi Mwana Wanu Anganene Chiyani? Kodi ana anu ndi okonzeka kunena okha maganizo awo pankhani imeneyi? Kodi amakhulupirira ndi mtima wawo wonse kuti lamulo la Mulungu limati, ‘tisale mwazi’? (Mac. 15:29; 21:25) Kodi angathe kufotokoza zimene iwowo amakhulupirira pa nkhaniyi pogwiritsa ntchito Malemba? Kodi madokotala atawauza kuti amwalira akakana magazi, anawo angalimbe mtima n’kukanabe magaziwo, ngakhale makolo awo kulibe? Popeza kuti zinthu zimatha kutigwera mwadzidzidzi, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti akhale okonzeka kuthana ndi mavuto osayembekezeka amene angayese chikhulupiriro chawo?—Mlal. 9:11, Aef. 6:4.

4, 5. (a) Kodi ndi udindo wotani umene makolo ali nawo, ndipo angaukwaniritse motani? (b) Kodi pali mabuku otani amene angathandize makolo?

4 Kodi Makolo Mungachite Chiyani? Makolo, muli ndi udindo wophunzitsa ana anu kuona magazi monga mmene Yehova amawaonera. (2 Tim. 3:14, 15) Nkhaniyi yafotokozedwa bwino m’buku la Kukambitsirana, tsamba 313 mpaka 317. Werengani nkhaniyi mosamala pamodzi ndi banja lanu. Pogwiritsa ntchito gawo lakuti “Ngati Wina Anena Kuti—” pa tsamba 317 mpaka 319, chitani zitsanzo ndi ana anu kuti muwathandize kudziwa mmene angafotokozere zimene amakhulupirira ndi kufotokoza zifukwa zake. (1 Pet. 3:15) Zinthu zinanso zomwe tingagwiritse ntchito kuti tidziwe zambiri za nkhani ya magazi ndi kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? ndi Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, kuyambira tsamba 14 mpaka 24. Kodi banja lanu lawerenga kale ndi kukambirana zimenezi posachedwapa? Ngati simunatero bwanji osawerenga ndi kukambirana zimenezi panopa?

5 Thandizani ana anu kuti ‘azindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro’ pankhani ya magazi. Potero ana anu angathe kusankha zinthu mwanzeru ndipo Yehova angawadalitse.—Aroma 12:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena