Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/14 tsamba 6
  • Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?
  • Galamukani!—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Lapadziko Lonse
    Galamukani!—2001
  • Kudzipha—Mliri Umene Ukuwononga Achinyamata
    Galamukani!—1998
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amatopa Nawo Moyo?
    Galamukani!—2001
  • Kudzipha—Mliri Wobisika
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 4/14 tsamba 6
Munthu wasowa mtengo wogwira ndipo akuganiza zongodzipha

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto?

DIANAa amaoneka kuti ndi mtsikana wanzeru, wansangala komanso wokonda kucheza ndi anthu. Koma ngakhale amaoneka chonchi, ali ndi mavuto aakulu amene amam’chititsa kuti nthawi zambiri azivutika maganizo. Iye anati: “Tsiku silidutsa ndisanaganize zoti kuli bwino nditangofa. Ndimaona kuti ngakhale nditamwalira, palibe amene angandisowe chifukwa ndine wosafunika.”

Nyuzipepala ina ya ku Canada inanena kuti: “Kafukufuku wina anasonyeza kuti pa anthu 200 amene amafuna kudzipha, mmodzi amadziphadi ndipo pa anthu 400 amene amaganiza zoti adzadzipha, m’modzi amadzadziphadi.”—THE GAZETTE, MONTREAL, CANADA.

Diana amanena kuti sangayerekeze n’komwe kudzipha. Komabe, nthawi zina amaona kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo. Iye ananena kuti: “Ndimalakalaka patachitika ngozi inayake ine n’kufa. Kwa ine imfa si mdani, ndipo sindiiopa.”

Anthu ambiri amaganiza zofanana ndi zimene Diana amaganizazi, ndipo ena amaganiza zodzipha pamene ena anayesapo kudzipha. Koma akatswiri amanena kuti anthu ambiri amene amafuna kudzipha sikuti kwenikweni amafunadi kufa, koma amangoona kuti kudzipha ndi njira imene angathetsere mavuto awo. Mwachidule tingati, anthu amenewa amaona kuti pali zifukwa zokwanira zoti kuli bwino angofa, choncho amafunika kuwatsimikira kuti palinso zifukwa zomveka zokhalira ndi moyo.

Kodi zifukwa zimenezi ndi ziti? Taonani mfundo zitatu zimene zatchulidwa m’nkhani yotsatirayi.

ZIMENE ANTHU AMANENA: Kukambirana nkhani yodzipha kapena kungonena chabe mawuwa, kungachititse kuti anthu ena adziphedi.

ZOONA ZAKE: Nthawi zambiri kukambirana nkhaniyi momasuka, kumathandiza munthu amene ali ndi maganizo ofuna kudzipha kuti asadziphe.

a Si dzina lake lenileni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena