Kodi Mphamvu Zoipa Zapambana?
MALINGALIRO akuti pali nkhondo yachilengedwe chonse pakati pa mphamvu zabwino ndi zoipa, apangitsa anthu olemba nkhani ndiponso anzeru zadziko m’mbiri yonse kukhala ndi maganizo ambirimbiri. Komabe, pali buku limene lili ndi nkhani yolondola ya nkhondo ya Mulungu ndi Mdyerekezi. Bukulo ndi Baibulo. Limalongosola nkhani zimene zikukhudza nkhondo imeneyi ndipo limathandiza kudziŵa amene wapambanadi pankhondoyi.
Patangotha nthaŵi pang’ono mwamuna ndi mkazi woyamba atalengedwa, cholengedwa chauzimu chosaoneka, Satana Mdyerekezi, chinakayikira ulamuliro wa Mulungu. Motani? Mwakunena mosaonekera kuti Mulungu anali kumana zolengedwa zake zinthu zina zabwino ndiponso kuti zinthu zingawayendere bwino anthu popanda kumudalira.—Genesis 3:1-5; Chivumbulutso 12:9.
Kenako, Satana m’masiku a kholo lakale Yobu, anadzutsa nkhani ina. Pofuna kulepheretsa Yobu kukhala wokhulupirika kwa Mulungu, Satana anati: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Kunali kukayikira kwakukulutu kumeneku! Satana pogwiritsa ntchito mawu amene angaimire aliyense akuti “munthu” m’malo mwa dzina la Yobu, anakayikira kukhulupirika kwa anthu onse. Iye kwenikweni anali kunena kuti: ‘Munthu adzachita zonse zotheka kuti apulumutse moyo wake. Ndipatseni mpata, nditha kupatutsa anthu onse kwa Mulungu.’
Tingapeze amene wapambana pankhondo ya Mulungu ndi Mdyerekezi mwa kuyankha mafunso aŵiri aŵa: Kodi anthu angadzilamulire okha bwinobwino? Kodi Mdyerekezi wapatutsa anthu onse kwa Mulungu woona?
Kodi Anthu Angadzilamulire Okha Bwinobwino?
Kwa zaka zambiri, anthu ayesa mitundu yosiyanasiyana ya maulamuliro. M’mbuyomo anthu ayesa maboma monga ulamuliro wa mafumu, wa anthu apamwamba, wa demokalase, wa chipani chimodzi, wa Chifasizimu ndiponso wa Chikomunizimu. Kodi mfundo yokha yakuti nthaŵi zonse amafuna kuyesera mtundu wina wa boma siikusonyeza kuti njira zosiyanasiyana zolamulirira zimenezi n’zoperewera?
“Aroma mosadziŵa anayesera mitundu yosiyanasiyana ya maulamuliro,” anatero H. G. Wells mu buku lakuti A History of the World, lofalitsidwa mu 1922. Iye anatinso: “Nthaŵi zonse anthu anali kusintha ulamuliro, sunkakhazikika. Kumbali ina kuyesera ulamuliro kumeneku kunakanika. Kumbali ina kuyeseraku sikunathe, ndipo masiku ano ku Ulaya ndi ku America akuyesa kuthetsa mavuto aakulu ameneŵa a ulamuliro wa mayiko padziko lonse amene Aroma anali oyamba kukumana nawo.”
Kuyesera ulamuliro kunapitirira mu zaka za m’ma 1900. Pamene zaka zimenezi zinkatha ulamuliro wa demokalase ndi umene unatenga malo kwambiri kuposa kale. Tinganene kuti demokalase imalola aliyense kulamulira. Koma kodi demokalase yasonyeza kuti anthu angadzilamulire okha bwinobwino popanda kudalira Mulungu? Jawaharlal Nehru, yemwe anali nduna yaikulu ku India, ananena kuti demokalase ndi yabwino, koma anatinso: “Ndikunena zimenezi chifukwa maulamuliro ena anyanya kuipa powayerekezera ndi umenewu.” Pulezidenti wakale wachifalansa Valéry Giscard d’Estaing anati: “Tikupeza mavuto aakulu ndi ulamuliro umene anthu amasankha okha okawaimira ku nyumba ya malamulo.”
Ngakhale m’zaka za m’ma 400 B.C.E., munthu wina wophunzira kwambiri wa ku Greece dzina lake Plato anaona vuto la ulamuliro wa demokalase. Malinga ndi buku lakuti A History of Political Theory iye anadzudzula “umbuli ndi kusadziŵa ntchito kwa anthu andale, lomwe ndi vuto lalikulu la ulamuliro wa demokalase.” Anthu andale ambiri masiku ano amadandaula kuti zimawavuta kupeza anthu odziŵa ntchito amene akuyenera kulamulira. Anthu “amakwiya ndi atsogoleri amene amaoneka kuti sangakwanitse kuthandiza pamene anthuwo akumana ndi mavuto aakulu,” inatero nyuzipepala ya The Wall Street Journal. Inanenanso kuti: “Anthuwo amaipidwa akaona kuti atsogoleri awo akusoŵa chochita ndiponso kuti akuchita chinyengo pamene iwo akufuna malangizo.”
Tsopano onani ulamuliro wa Mfumu Solomo mu Israyeli wakale. Yehova Mulungu anam’patsa Solomo nzeru zambiri. (1 Mafumu 4:29-34) Kodi mtundu wa Israyeli zinthu zinawuyendera bwanji mu ulamuliro wa Solomo wa zaka 40? Baibulo limayankha kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.” Nkhaniyo imanenanso kuti: “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.” (1 Mafumu 4:20, 25) Mtunduwo unali wokhazikika, wotukuka ndiponso wosangalala kwambiri mu ulamuliro wa mfumu yanzeru yooneka imene inali kuimira Wolamulira Wamkulu wosaoneka, Yehova Mulungu.
Koma ndiye palitu kusiyana pakati pa ulamuliro wa munthu ndi wa Mulungu! Kodi alipo anganenedi kuti Satana wapambana pankhani ya ulamuliro? Ayi, popeza mneneri Yeremiya ananena zoonadi kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
Kodi Satana Angapatutse Anthu Onse kwa Mulungu?
Kodi Satana wapambana pa zimene ananena kuti akhoza kupatutsa anthu onse kwa Mulungu? Mu chaputala 11 cha kalata ya Ahebri, mtumwi Paulo anatchula anthu okhulupirika angapo amene anakhalako chikristu chisanayambe. Ndiyeno anati: “Idzandiperewera nthaŵi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita; za Davide, ndi Samueli ndi aneneri.” (Ahebri 11:32) Paulo anati atumiki a Mulungu okhulupirika ameneŵa ali ngati ‘mtambo waukulu wa mboni.’ (Ahebri 12:1) Mawu a Chigiriki amene agwiritsidwa ntchito pano kutanthauza “mtambo” sikuti amatanthauza mtambo wapadera wooneka bwinobwino kukula kwake ndi malire ake, koma mtambo waukulu wosadziŵika malire ake. Izi n’zoyenera chifukwa atumiki a Mulungu okhulupirika akale ndi ambiri zedi moti ali ngati mtambo waukulu wosadziŵika malire ake. Inde, kwa zaka zambiri, anthu osaŵerengeka asonyeza zofuna zawo ndipo asankha kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu.—Yoswa 24:15.
Kodi masiku ano timaona chiyani? Mboni za Yehova padziko lonse zawonjezeka mpaka zapitirira sikisi miliyoni ngakhale kuti m’zaka za m’ma 1900 zazunzidwa ndiponso zatsutsidwa kwambiri. Pafupifupi anthu okwana nayini miliyoni amasonkhana ndi anthu ameneŵa, ndipo ambiri mwa iwo akuchita zofunika kuti akhale paunansi wathithithi ndi Mulungu.
Yankho labwino kwambiri pa zimene Satana ananena zoti akhoza kupatutsa anthu kwa Yehova, linachokera kwa Mwana weniweni wa Mulungu, Yesu Kristu. Ngakhale ululu wosaneneka umene anamva ali pamtengo wozunzirapo sunamusiyitse kukhala wokhulupirika. Yesu akumwalira, anafuula kuti: “Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga.”—Luka 23:46.
Satana amagwiritsa ntchito chilichonse chimene angathe kungoyambira zokopa mpakana chizunzo chenicheni kuti azilamulira anthu. Pogwiritsa ntchito “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo” poyesa anthu, amafuna kuwapatutsa kapena kuwanyengerera kuti achoke kwa Yehova. (1 Yohane 2:16) Satana ‘wachititsanso khungu maganizo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, chisawawalire.’ (2 Akorinto 4:4) Ndipo Satana sachedwa kugwiritsa ntchito kuwopseza ndiponso kuopa anthu pokwaniritsa cholinga chake.—Machitidwe 5:40.
Komabe amene ali ku mbali ya Mulungu, sagonjera Mdyerekezi. Adziŵa Yehova Mulungu ndi ‘kumukonda ndi mtima wawo wonse, ndi moyo wawo wonse, ndi nzeru zawo zonse.’ (Mateyu 22:37) Inde, kukhulupirika kolimba kwa Yesu Kristu ndi kwa anthu osaŵerengeka zikutsimikizira kuti Satana Mdyerekezi walephereratu.
Kodi M’tsogolo Muli Zotani?
Kodi anthu adzapitiriza kuyesera mitundu yosiyanasiyana ya maulamuliro mpaka kalekale? Mneneri Danieli analosera kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ufumu umene Mulungu wakumwamba anakhazikitsa ndi boma lakumwamba limene wolamulira wake ndi Yesu Kristu. Ndi Ufumu umenewu umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziupempherera. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewo udzawononga maboma onse a anthu pa “nkhondo [imene ikudza] ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” ndipo idzakhudza dziko lonse.—Chivumbulutso 16:14, 16.
Kodi n’chiyani chidzachitikire Satana? Baibulo limafotokoza zimene zidzamuchitikire motere: “[Mngelo wa Yehova] anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nam’manga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi.” (Chivumbulutso 20:1-3) Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Kristu udzayamba Satana akadzaponyedwa kuphompho kumene sadzatha kuchita kalikonse.
Nthaŵi imeneyo si mmene dziko lino lidzasangalatsire! Kuipa ndiponso amene amakuchititsa kudzakhala kulibe. Baibulo limalonjeza kuti: “Pakuti ochita zoipa adzadulidwa . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:9-11) Palibe chidzasokoneze mtendere wawo, kaya anthu kapena zinyama. (Yesaya 11:6-9) Ngakhale anthu ambiri amene m’mbuyomo anali ku mbali ya Mdyerekezi chifukwa chosadziŵa ndiponso chifukwa choti sanapeze mpata wodziŵa Yehova, adzaukitsidwa ndipo adzaphunzitsidwa za Mulungu.—Machitidwe 24:15.
Pamene Ulamuliro wa Zaka 1,000 uzidzafika kumapeto, dziko lidzakhala lili paradaiso, ndipo anthu okhala mmenemo adzakhala ali angwiro. Ndiyeno Satana adzamasulidwa kwa “kanthaŵi,” mapeto ake adzawonongedweratu pamodzi ndi otsutsa ulamuliro wa Mulungu.—Chivumbulutso 20:3, 7-10.
Kodi Mudzakhala Kumbali ya Ndani?
M’zaka za m’ma 1900 inali nthaŵi imene Satana wasakaza kwambiri dziko. Komabe, mmene zinthu zilili padziko lapansi zikungosonyeza kuti tili m’masiku otsiriza a dziko loipa lino, osati kuti Satana wapambana. (Mateyu 24:3-14; Chivumbulutso 6:1-8) Kuchuluka kwa mavuto padziko lapansi kapena zimene anthu ambiri amaganiza si zimene zingasonyeze amene wapambana. Koma tingaone amene wapambana mwa kuona kuti ndi ulamuliro uti umene uli wabwino ndiponso ngati pali amene atumikira Mulungu chifukwa choti amamukonda. Tikaona mbali ziŵiri zimenezi, wapambana ndi Yehova.
Ngati nthaŵi imene Satana waloledwa kukhalapo yasonyeza kale kuti walephera, n’chifukwa chiyani Mulungu akulola zoipa kupitirirabe? Yehova akuleza mtima chifukwa ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Tikukhulupirira kuti nthaŵi imene yatsalayi muigwiritsa ntchito kuphunzira Baibulo ndi ‘kudziŵa Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene anam’tuma.’ (Yohane 17:3) Mboni za Yehova zidzasangalala kukuthandizani kudziŵa zimenezi kuti inunso mukhale m’gulu la anthu ambiri amene aima zolimba kumbali imene yapambana.
[Zithunzi patsamba 5]
Mwa kukhala okhulupirika, Mboni za Yehova zaperekanso umboni wakuti Satana walephera
[Chithunzi patsamba 7]
Yehova ali ndi anthu ambiri okhulupirika kumbali yake