Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 3/15 tsamba 3-6
  • Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1. MUNGAKHALE PA UBWENZI NDI MULUNGU
  • 2. ANGAKUTHANDIZENI KUTI MUZIKHALA NDI MTENDERE WAMUMTIMA
  • 3. ANGAKUTHANDIZENI KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO
  • 4. ANGAKUTHANDIZENI MUKAFUNA KUSANKHA ZOCHITA KOMANSO MUKAKHALA NDI MAVUTO
  • PHUNZIRANI BAIBULO KUTI MUDZIWE ZAMBIRI ZOKHUDZA MULUNGU
  • Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • N’chiyani Chimapangitsa Moyo Kukhala ndi Cholinga Chenicheni?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika
    Galamukani!—2021
  • Chifuno Chenicheni cha Moyo
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 3/15 tsamba 3-6
Munthu wakhala pansi ndipo akuyang’ana mapiri ndi kumwamba kokongola

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Kukhulupirira Zoti Kuli Mulungu N’kothandiza Bwanji?

Anthu ambiri sadziwa ngati Mulungu alipo kapena ayi ndipo ena saona n’komwe kuti imeneyi ndi nkhani yofunika. Mwachitsanzo, Hervé yemwe anakulira ku France, anati: “Sindinganene kuti kuli Mulungu kapena kulibe, koma ineyo sindikhulupirira Mulungu. Ndimaona kuti ukhoza kumangogwiritsa ntchito nzeru zachibadwa n’kumachita zinthu bwinobwino popanda kukhulupirira zoti kuli Mulungu.”

Nayenso John, yemwe amakhala ku United States, anati: “Makolo anga sankakhulupirira zoti kuli Mulungu koma ineyo ndinalibe mbali. Komabe nthawi zina ndinkafuna kudziwa ngati kulidi Mulungu kapena ayi.”

Kodi nanunso munayamba mwaganizapo ngati Mulungu alipo kapena ayi? Komanso kuti ngati alipo, kodi n’kutheka kuti anali ndi cholinga polenga anthufe? Mwina mumaona kuti pali zinthu zina zomwe popanda kukhulupirira kuti kuli Mulungu, n’zovuta kuzimvetsa. Zinthu zake ndi monga umboni woti zamoyo sizinachokere ku zinthu zopanda moyo komanso woti dzikoli lili ndi zonse zofunika ku zinthu zamoyo.—Onani bokosi lakuti, “Umboni Woti Kuli Mulungu.”

Kudziwa zoona pa nkhani zimenezi kungakuthandizeni kwambiri. Ndipotu mutapeza umboni wosatsutsika woti Mulungu alipo n’kudziwa zambiri za Mulunguyo, mungapindule kwambiri. Taonani mfundo 4 zotsatirazi.

1. MUNGAKHALE PA UBWENZI NDI MULUNGU

Munthu akuwerenga buku lalikulu

Ngati Mulungu anali ndi cholinga polenga anthufe, aliyense angafune atachidziwa n’kudziwanso zoyenera kuchita. Choncho munthu amene sakudziwa kuti Mulungu alipo, sangathenso kudziwa chifukwa chake Mulungu analenga anthufe ndipo sangakhale naye pa ubwenzi.

Baibulo limati Mulungu ndi amene analenga zamoyo zonse. (Chivumbulutso 4:11) Kodi kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji? Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

Pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga, anthu ndi apadera kwambiri. Baibulo limati anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu kuti tizisonyeza makhalidwe ake. (Genesis 1:27) Limaphunzitsanso kuti anthufe tingathe kukhala mabwenzi a Mulungu. (Yakobo 2:23) Palibe chinthu chaphindu kuposa kukhala bwenzi la Mulungu.

Kodi munthu angapindule bwanji ngati atakhala bwenzi la Mulungu? Anthu amene ali pa ubwenzi ndi Mulungu amatha kulankhula naye momasuka m’pemphero, n’kumuuza chilichonse. Ndipo Mulungu amamvetsera mapemphero awo komanso amawathandiza. (Salimo 91:15) Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kungatithandizenso kuti tizidziwa maganizo ake pa nkhani zosiyanasiyana ndipo tingapeze mayankho a mafunso ovuta amene timakhala nawo.

Munthu amene sakudziwa kuti Mulungu alipo, sangathenso kudziwa chifukwa chake Mulungu analenga anthufe ndipo sangakhale naye pa ubwenzi

2. ANGAKUTHANDIZENI KUTI MUZIKHALA NDI MTENDERE WAMUMTIMA

Munthu akuoneka kuti ali ndi mtendere wamumtima

Anthu ena zimawavuta kukhulupirira Mulungu akaona mavuto amene akuchitika padzikoli. Amafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wamphamvuyonse, amalola kuti zoipa zizichitika?’

Baibulo limanena kuti cholinga cha Mulungu sichinali choti anthufe tizivutika. Adamu atalengedwa, sankakumana ndi mavuto alionse. Komanso Mulungu sanalenge anthu kuti m’kupita kwa nthawi adzafe. (Genesis 2:7-9, 15-17) Kodi mukuganiza kuti zimenezi ndi zoona kapena ndi nkhambakamwa chabe? Mulungu ndi wamphamvuyonse komanso khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Choncho n’zosakayikitsa kuti polenga anthufe, ankafuna kuti tizikhala mosangalala.

Koma kodi mavuto onsewa anayamba bwanji? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga anthu ndi ufulu wosankha zochita. Iye sanatilenge ngati maloboti kuti tizingochita chilichonse chomwe akufuna. Makolo athu oyambirira anagwiritsa ntchito ufulu wosankhawu molakwika ndipo anasankha kuti asamatsogoleredwe ndi Mulungu. (Genesis 3:1-6, 22-24) Ndiye chifukwa choti ndife ana awo, tonse timakumana ndi mavuto chifukwa cha kusamvera kwawo.

Kudziwa kuti mavuto amene timakumana nawowa sichinali cholinga cha Mulungu polenga anthu, kungakuthandizeni kuti muzikhala ndi mtendere wamumtima. Komabe tonsefe tikakumana ndi mavuto timafuna kulimbikitsidwa. Timafunanso kukhala ndi chiyembekezo cham’tsogolo.

3. ANGAKUTHANDIZENI KUKHALA NDI CHIYEMBEKEZO

Dziko Lapansi

Adamu ndi Hava atangochimwa, Mulungu analonjeza kuti cholinga chake polenga anthu chidzakwaniritsidwa. Popeza iye ndi wamphamvuyonse, palibe chimene chingalepheretse cholinga chakechi. (Yesaya 55:11) Posachedwapa, Mulungu athetsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kusamvera kwa makolo athu. Kenako anthu adzayamba kukhala ndi moyo wosangalala komanso dzikoli lidzakhala paradaiso.

Kodi ndi zinthu ziti zosangalatsa zomwe zidzachitike padzikoli? Taonani malonjezo awiri opezeka m’Baibulo awa.

  • PADZIKO LONSE PADZAKHALA MTENDERE NDIPO OIPA ADZAWONONGEDWA. “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.

  • SIPADZAKHALANSO MATENDA NDI IMFA. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”—Yesaya 25:8.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malonjezo amenewa? N’chifukwa choti pali maulosi ambirimbiri omwe analembedwa m’Baibulo ndipo anakwaniritsidwa ndendende. Koma mwina mungaganize kuti ngakhale kuti tili ndi chiyembekezo choti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, panopa timakumanabe ndi mavuto. Ndiye kodi Mulungu amatithandiza bwanji panopa?

4. ANGAKUTHANDIZENI MUKAFUNA KUSANKHA ZOCHITA KOMANSO MUKAKHALA NDI MAVUTO

Munthu akufuna amugwire mnzake dzanja

Mulungu amatipatsa malangizo amene angatithandize tikakumana ndi mavuto komanso kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Zosankha zina zimakhala zing’onozing’ono. Koma nthawi zina timafunika kusankha zinthu zomwe zingakhudze moyo wathu wonse. Palibe munthu amene angatipatse malangizo anzeru kuposa Mlengi wathu. Izi zili choncho chifukwa ndi amene anatilenga komanso amadziwa mavuto amene tingakumane nawo ngati titasankha molakwika. Choncho tinganene kuti Mulungu amadziwa zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino.

Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo ndipo anthuwa analemba maganizo ake mothandizidwa ndi mzimu woyera. Choncho tingadziwe maganizo a Mulungu ngati titamawerenga Baibulo. N’chifukwa chake limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”—Yesaya 48:17, 18.

Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire ndipo ndi wokonzeka kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo potithandiza. Baibulo limanena kuti Mulungu ali ngati bambo wachikondi amene amafunitsitsa kutithandiza. Limati: “Atate wakumwamba . . . adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Choncho Yehova angagwiritse ntchito mzimu wake potitsogolera ndi kutithandiza.

Ndiye kodi mungatani kuti Mulungu akuthandizeni ndi mzimu wake woyera? Baibulo limati: “Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Kuti munthu asamakayikire zoti kuli Mulungu ayenera kufufuza umboni wosonyeza kuti Mulungu alipodi.

PHUNZIRANI BAIBULO KUTI MUDZIWE ZAMBIRI ZOKHUDZA MULUNGU

Pamatenga nthawi kuti munthu adziwe zoona zokhudza Mulungu. Koma kuchita zimenezi kungakuthandizeni kwambiri. Xiujin Xiao anabadwira ku China koma panopa amakhala ku United States. Iye ananena kuti: “Ndinkakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Komabe ndinkafuna nditadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Choncho ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Nditafika chaka chomaliza kukoleji ndinasiya kuphunzira Baibulo chifukwa ndinkatanganidwa kwambiri. Koma nditasiya kuphunzirako, sindinkasangalala kwenikweni. Patapita nthawi ndinayambiranso kuphunzira Baibulo ndipo ndinayambanso kukhala wosangalala.”

Kodi mungakonde kudziwa zambiri zokhudza Yehova Mulungu yemwe anatilenga? Tikukulimbikitsani kuti muphunzire Baibulo kuti mudziwe zambiri zokhudza Mulungu ameneyu.

Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Mulungu

Zimene Baibulo limafotokoza zokhudza Mulungu si zovuta kumvetsa. Komabe ambiri akawerenga Baibulo amadabwa ndi zomwe limanena komanso amaona kuti muli mfundo zambiri zofunika kuziganizira.

  • Mulungu ndi weniweni osati mphamvu chabe. Ali ndi makhalidwe abwino ambiri ndipo dzina lake ndi Yehova.a—Yesaya 42:8.

  • Yehova Mulungu alibe chiyambi komanso mapeto.—Salimo 93:2; Yesaya 40:28.

  • Khalidwe lalikulu la Mulungu ndi chikondi, choncho sikuti iye amangofuna kulanga anthu akalakwitsa, ngati mmene zipembedzo zina zimaphunzitsira.—1 Yohane 4:8.

  • Mulungu amatikonda ndipo watiuza zimene amafuna kuti tizichita.—Mlaliki 12:13; Mika 6:8.

Kodi Baibulo limanena zonse zokhudza Mulungu? Ayi. Ndipotu limanena kuti zimene timadziwa zangokhala “kambali kakang’ono chabe.”—Yobu 26:14.

a M’Mabaibulo ambiri munalembedwa mawu akuti “AMBUYE” pamalo pomwe panali zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu, zomwe anazimasulira kuti YHWH. M’Chichewa zilembozi anazimasulira kuti “Yehova” kapena “Yahwe.”

Umboni Woti Kuli Mulungu

  • Chikuto cha kabuku kakuti, The Origin of Life—Five Questions Worth Asking

    The Origin of Life​—Five Questions Worth Asking

    Kabuku kameneka kakupezeka m’zinenero 47

    Patsamba 12 pali mawu akuti: “Anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina amayesetsa kufotokoza mmene moyo unayambira. Koma akafufuza zambiri zokhudza mmene moyo unayambira amaonabe kuti payenera pali winawake amene analenga zinthu zonse.”

  • Chikuto cha kabuku kakuti, Was Life Created?

    Was Life Created?

    Kabuku kameneka kakupezeka m’zinenero 80

    Patsamba 24 pali mawu akuti: “Anthu ambiri amanena kuti asayansi amatsutsa mfundo ya m’Baibulo pa nkhani ya kutalika kwa nthawi yomwe chilengedwe chakhalapo. Koma sikuti zimene asayansi amanena komanso zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi zimatsutsana. Koma chifukwa choti Akhristu ena amaphunzitsa ziphunzitso zabodza zokhudza chilengedwe, zimapangitsa anthu kuganiza kuti zimene asayansi amanena ndi zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi, zimatsutsana.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena