Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/1 tsamba 8-13
  • Yehova, “Woweruza Wa Dziko Lonse” Wopanda Tsankhu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova, “Woweruza Wa Dziko Lonse” Wopanda Tsankhu
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira ya Yehova Yoweruzira
  • Oweruza Aumunthu m’Nthaŵi za Makolo Akale
  • Dongosolo Lachiweruzo la Israyeli
  • Oweruza m’Israyeli
  • Kupereka Chiweruzo Cholungama
  • Akulu, Weruzani Mwachilungamo
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Malamulo Amene Mulungu Anapatsa Aisiraeli Anali Achilungamo?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Chilungamo Kaamba ka Onse ndi Woweruza Woikidwa ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Mkazi wa Kaini Anali Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/1 tsamba 8-13

Yehova, “Woweruza Wa Dziko Lonse” Wopanda Tsankhu

“Atate . . . aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankhu.”​—1 PETRO 1:17.

1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ponse paŵiri amantha ndi otonthozedwa ndi lingaliro lakuti Yehova ndiye Woweruza wamkulu? (b) M’nkhani yachiweruzo ya Yehova motsutsana ndi mitundu, kodi ndimbali yotani imene atumiki ake apadziko lapansi amakhala nayo?

YEHOVA ndiye “woweruza [wamkulu] wa dziko lonse.” (Genesis 18:25) Monga Mulungu Wamkulukulu koposa m’chilengedwe chonse, iye ali ndi kuyenera kotheratu kwa kuweruza zolengedwa zake. Limeneli ndilingaliro lowopsa ndipo panthaŵi imodzimodziyo nlotonthoza. Mose mosonkhezeredwa anafotokoza mawu owonekera kukhala akulankhula mosiyana akumati: “Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi wowopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu. Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.”​—Deuteronomo 10:17, 18.

2 Ha ndiuchikatikati wotheratu chotani nanga! Mulungu wamkulu, wamphamvu, wowopsa, komabe wopanda tsankhu ndipo mwachikondi akumatetezera zokomera ana amasiye ndi akazi amasiye, ndi alendo ogonera. Kodi ndani amene akanafuna Woweruza wachikondi kwambiri koposa Yehova? Akumadzisonyeza monga wokhala ndi mlandu motsutsana ndi mitundu ya dziko la Satana, Yehova akuitanira atumiki ake padziko lapansi kuti akhale mboni zake. (Yesaya 34:8; 43:9-12) Iye samadalira pa umboni wawo kutsimikizira umulungu wake ndi ulamuliro wake woyenerera. Koma iye amapatsa mboni zake mwaŵi waukulu kopambana wa kuchitira umboni pamaso pa anthu onse kuti izo zimavomereza ukulu wake. Mboni zake zimadzigonjetsera kuulamuliro wake wolungama, ndipo mwa uminisitala wawo wapoyera, zimasonkhezera ena kuti adziike pansi pa ulamuliro wa Woweruza Wamkulukulu Kopambana.

Njira ya Yehova Yoweruzira

3. Kodi ndimotani mmene njira ya Yehova yoweruzira ingafotokozedwere mwachidule, ndipo kodi zimenezi zinasonyezedwa motani m’nkhani ya Adamu ndi Hava?

3 Mkati mwa mbiri yoyambirira ya anthu, Yehova iyemwini anaweruza opalamula ena. Zitsanzo za njira yake yosamalilira nkhani zachiweruzo zinakhazikitsa chitsanzo kwa awo a atumiki ake amene pambuyo pake akakhala ndi thayo la kusamalira nkhani zachiweruzo pakati pa anthu ake. (Salmo 77:11, 12) Njira yake yoweruzira ingafotokozedwe mwachidule motere: kusagwedezeka pamene kuli kofunikira, chifundo pamene kuli kotheka. Ponena za Adamu ndi Hava, zolengedwa zaumunthu zangwiro zimene zinapanduka modzifunira, sanafunikire chifundo. Chotero, Yehova anawaweruzira kuimfa. Koma chifundo chake chinagwira ntchito kumbadwa zawo. Yehova anasiya kaye chiweruzo cha imfa, mwakutero akumalola Adamu ndi Hava kubala ana. Iye mwachikondi anapatsa mbadwa zawo chiyembekezo cha kulanditsidwa kuukapolo wa uchimo ndi imfa.​—Genesis 3:15; Aroma 8:20, 21.

4. Kodi Yehova anachita motani ndi Kaini, ndipo kodi nchifukwa ninji nkhani imeneyi iri yokondweretsa mwapadera?

4 Njira imene Yehova anachitira ndi Kaini njokondweretsa mwapadera chifukwa chakuti ndiwo mlandu woyamba wolembedwa wophatikizapo mmodzi wa mbadwa zopanda ungwiro za Adamu ndi Hava, ‘zogulitsidwa kapolo wa uchimo.’ (Aroma 7:14) Kodi Yehova analingalira zimenezi ndi kuchita ndi Kaini mosiyana ndi mmene Iye anachitira ndi makolo ake? Ndipo kodi mlandu umenewu ungapereke phunziro kwa oyang’anira Achikristu lerolino? Tiyeni tiwone. Akumazindikira kachitidwe kolakwa ka Kaini pamene nsembe yake sinalandiridwe mwachiyanjo, Yehova mwachikondi anamchenjeza za ngozi imene analimo. Mwambi wakale umati: ‘Muvi wopenyerera umagwera mmaso.’ Yehova anachita zonse zimene akanatha mwa kuchenjeza Kaini ponena za kulola chikhoterero chake chauchimo kumgonjetsa. Iye anayesa kumthandiza ‘kuchita zabwino.’ (Genesis 4:5-7) Imeneyi ndinthaŵi yoyamba pamene Mulungu anauza munthu wochimwa kuti alape. Kaini atasonyeza mkhalidwe wosalapa nachita tchimo lake lowopsa, Yehova anamuweruzira kukukhala wothawathawa, akumafewetsa chiweruzochi mwa kupereka lamulo loletsa anthu ena kumupha.​—Genesis 4:8-15.

5, 6. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anachitira ndi mbadwo wa Chigumula chisanakhale? (b) Kodi Yehova anachitanji asanapereke chiweruzo motsutsana ndi nzika za Sodomu ndi Gomora?

5 Chigumula chisanadze, pamene ‘anawona Yehova kuti kuipa kwa munthu kunali kwakukulu padziko lapansi, iye anavutika mumtima.’ (Genesis 6:5, 6) Iye “anamva chisoni” kwambiri chifukwa chakuti unyinji wa mbadwo wa Chigumula chisanachitikewo unagwiritsira ntchito molakwa ufulu wawo ndi kuti iye anayenera kupereka chiweruzo pa iwo. Komabe, anawapatsa chenjezo lokwanira, akumagwiritsira ntchito Nowa kwazaka zambiri monga “mlaliki wa chilungamo.” Pambuyo pake, Yehova analibe chifukwa ‘cholekelera dziko lakale la osapembedza limenelo.’​—2 Petro 2:5.

6 Mofananamo Yehova anakakamizika kusamalira nkhani yachiweruzo motsutsana ndi nzika zoluluzika za Sodomu ndi Gomora. Koma tawonani mmene iye anachitira. Anali atamva ‘mfuwu yadandaulo’ ponena za kudzisungira koluluzika kwa anthu amenewa, mwina kokha mwamapemphero a Loti wolungamayo. (Genesis 18:20; 2 Petro 2:7, 8) Koma asanachitepo kanthu, iye ‘anatsika’ kukatsimikizira maumboni mwanjira ya angelo ake. (Genesis 18:21, 22; 19:1) Iye anatenganso nthaŵi ya kutsimikizira Abrahamu kuti iye sakachita mosalungama.​—Genesis 18:23-32.

7. Kodi ndimaphunziro otani amene akulu otumikira pamakomiti achiweruzo angaphunzire m’zitsanzo za njira ya Yehova ya kuweruza?

7 Kodi akulu lerolino angaphunzirenji m’zitsanzo zimenezi? M’chochitika cha Adamu ndi Hava, Yehova anasonyeza chikondi ndi kudera nkhaŵa kaamba ka awo amene, ngakhale kuti anali ndi unansi ndi opalamulawo, anali opanda liwongo m’nkhaniyo. Iye anasonyeza chifundo kumbadwa za Adamu ndi Hava. M’chochitika cha Kaini, Yehova anawoneratu ngozi imene Kaini analimo nalingalira naye mokoma mtima, akumayesa kuchitapo kanthu kupewetsa kuchitidwa kwa tchimo. Ngakhale pambuyo pa kumuweruzira kukukhala wothawathawa, Yehova anali wokoma mtima kwa Kaini. Ndiponso, Yehova anapereka chiweruzo pambadwo wa Chigumula chisanakhale kokha pambuyo pa kusonyeza chipiriro cha kuleza mtima kwakukulu. Poyang’anizana ndi kuipa kouma khosi, Yehova “anavutika mumtima mwake.” Iye anali wachisoni kuti anthu anapandukira ulamuliro wake wolungama ndi kuti iye anakakamizika kuwaweruza mowatsutsa. (Genesis 6:6; yerekezerani ndi Ezekieli 18:31; 2 Petro 3:9.) M’chochitika cha Sodomu ndi Gomora, Yehova anachitapo kanthu kokha pambuyo pa kutsimikizira maumboni. Ndizitsanzo zabwino kopambana chotani nanga kwa awo amene lerolino afunikira kusamalira milandu yachiweruzo!

Oweruza Aumunthu m’Nthaŵi za Makolo Akale

8. Kodi ndimalamulo aakulu a Yehova ati amene anadziwidwa m’nthaŵi ya makolo akale?

8 Ngakhale kuti mwachiwonekere panalibe malamulo olembedwa panthaŵiyo, chitaganya cha makolo akale chinali chozolowerana ndi malamulo aakulu a Yehova, ndipo atumiki ake anali ndi thayo la kuwasunga. (Yerekezerani ndi Genesis 26:5.) Chochitika cha mu Edene chinali chitasonyeza kufunika kwa kumvera ndi kugonjera kuufumu wa Yehova. Chochitika cha Kaini chinavumbula kutsutsa kwa Yehova kuchita mbanda. Mwamsanga pambuyo pa Chigumula, Mulungu anapatsa mtundu wa anthu malamulo onena za kupatulika kwa moyo, kuchita mbanda, chilango cha imfa, ndi kudya mwazi. (Genesis 9:3-6) Yehova anatsutsa mwamphamvu chigololo m’chochitika chophatikizapo Abrahamu, Sara, ndi Abimeleki, mfumu ya Gerari, pafupi ndi Gaza.​—Genesis 20:1-7.

9, 10. Kodi ndizitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti dongosolo lachiweruzo linalipo m’chitaganya cha makolo akale?

9 M’masiku amenewo mitu yamabanja inachita ngati oweruza ndipo inasamalira mavuto okhudza lamulo. Ponena za Abrahamu Yehova anafotokoza kuti: “Ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro.” (Genesis 18:19) Abrahamu anasonyeza kupanda dyera ndi luntha pothetsa mkangano wapakati pa abusa a nkhosa zake ndi za Loti. (Genesis 13:7-11) Akumachita monga mutu wa fuko ndi woweruza, Yuda anaweruza mpongozi wake Tamara kuti akamponye miyala ndi kuphedwa ndi kutenthedwa, akumakhulupirira kuti iye anali hule. (Genesis 38:11, 24; yerekezerani ndi Yoswa 7:25.) Komabe, atamva maumboni onse, anamlengeza kukhala wolungama kwambiri kuposa iyemwini. (Genesis 38:25, 26) Nkofunika kwambiri chotani nanga kumva maumboni onse musanagamule poweruza mlandu!

10 Bukhu la Yobu likutchula osati mwachindunji za dongosolo lachiweruzo nilisonyeza kufunika kwa chiweruzo chopanda tsankhu. (Yobu 13:8, 10; 31:11; 32:21) Yobu iyemwiniyo akulankhula za nthaŵi pamene iye anali woweruza wolemekezedwa amene anakhala pachipata chamzinda kuweruzira ndi kutetezera mkazi wamasiye ndi mwana wamasiye. (Yobu 29:7-16) Chotero, pali umboni wakuti mkati mwa chitaganya cha makolo akale, “akulu” anali kuchita monga oweruza pakati pa mbadwa za Abrahamu ngakhale asanatuluke mu Igupto ndipo mpambo wa malamulo wochokera kwa Mulungu usanaperekedwe kumtundu wa Israyeli. (Eksodo 3:16, 18) Kunena zowona, zofunika za pangano Lachilamulo zinaperekedwa ndi Mose kwa “akulu,” kapena madoda, a Israyeli, amene anaimira anthuwo.​—Eksodo 19:3-7.

Dongosolo Lachiweruzo la Israyeli

11, 12. Malinga ndi akatswiri Abaibulo aŵiri, kodi nchiyani chimene chinasiyanitsa dongosolo lachiweruzo la Israyeli ndi lija la mitundu ina?

11 Kuperekedwa kwa chilungamo m’Israyeli kunali kosiyana kwambiri ndi michitidwe yalamulo imene inali kutsatiridwa m’mitundu yozungulira. Panalibe kusiyana pakati pa lamulo la milandu wamba ndi lamulo la milandu ya zaupandu. Onse aŵiri anasanganizidwa ndi malamulo amakhalidwe abwino ndi achipembedzo. Kulakwira mnansi wa munthuwe kunali kulakwira Yehova. M’bukhu lake lakuti The People and the Faith of the Bible, wolembayo André Chouraqui akulemba kuti: “Mwambo wachiweruzo wa Ahebri umasiyana ndi uja wa anansi awo, osati kokha m’kufotokozedwa kwake kwa zolakwa ndi zilango komanso tanthauzo lake lenileni la malamulowo. . . . Tora [Chilamulo] siyolekana ndi moyo watsiku ndi tsiku; imalamulira mkhalidwe ndi zochitika zonse za moyo watsiku ndi tsiku mwa kupereka madalitso kapena matemberero. . . . M’Israyeli . . . kuli pafupifupi kosatheka kusiyanitsa bwino lomwe ntchito zachiweruzo za mumzinda. Zinabisidwa m’chigwirizano cha moyo wodalira kotheratu pa kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu wamoyo.”

12 Mkhalidwe wapadera umenewu unapangitsa kusamaliridwa kwa nkhani zachiweruzo mu Israyeli kukhala pamlingo wapamwamba kwambiri koposa kwa m’mitundu imene inaliko panthaŵiyo. Katswiri wa Baibulo wotchedwa Roland de Vaux akulemba kuti: “Mosasamala kanthu ndi mmene lingafananire mumpangidwe ndi mawu lamulo la Aisrayeli, nlosiyana kwambiri ndi malamulo a Kummawa a ‘mapangano’ ndi nkhani za ‘malamulo’ awo. Ilo ndilamulo lachipembedzo. . . . Palibe lamulo la Akummawa limene lingayerekezeredwe ndi lamulo la Aisrayeli, limene likunenedwa kuti lonse lathunthu nlolembedwa ndi Mulungu. Ngati liri, ndipo kaŵirikaŵiri limasanganiza, malamulo amakhalidwe ndi madzoma, zimenezi ziri chifukwa chakuti limafotokoza mbali zonse za Chipangano chaumulungu, ndi chifukwa chakuti Chipangano chimenechi chinalamulira maunansi a munthu ndi mnzake limodzi ndi maunansi awo ndi Mulungu.” Nzosadabwitsa kuti Mose anafunsa kuti: “Mtundu waukulu wa anthu ndiuti, wakukhala nawo malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lerolino?”​—Deuteronomo 4:8.

Oweruza m’Israyeli

13. Kodi Mose anali chitsanzo chabwino kwambiri m’mbali ziti kwa akulu lerolino?

13 Pokhala ndi dongosolo lachiweruzo lapamwamba chotere, kodi ndimunthu wamtundu wanji amene anafunika kukhala monga woweruza? Ponena za woweruza woyambirira weniweni woikidwa m’Israyeli, Baibulo limafotokoza kuti: “Koma munthuyo Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Iye sanali wodzidalira mopambanitsa. (Eksodo 4:10) Ngakhale kuti anafunikira kuweruza anthu, panthaŵi zina anakhala nkhoswe yawo pamaso pa Yehova, akumamchonderera kuti awakhululukire ndipo ngakhale kudzipereka kuti aphedwe mmalo mwawo. (Eksodo 32:11, 30-32) Iye mwandakatulo anafotokoza kuti: “Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho amvula pazitsamba.” (Deuteronomo 32:2) Koposa ndi kuweruza anthu modalira pa nzeru za iyemwini, iye analengeza kuti: “Akakhala nawo mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu ndi malamulo ake.” (Eksodo 18:16) Pamene anali ndi chikaikiro, anapereka nkhaniyo kwa Yehova. (Numeri 9:6-8; 15:32-36; 27:1-11) Mose anali chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu amene lerolino ‘amaweta Mpingo wa Mulungu’ ndi kupanga zosankha zachiweruzo. (Machitidwe 20:28) Unansi wawo ndi abale awo mofananamo utsimikiziretu kukhala “ngati mvula yowaza pamsipu.”

14. Kodi ziyeneretso zauzimu zinali zotani kaamba ka amuna oikidwa ndi Mose kuweruza m’Israyeli?

14 M’kupita kwanthaŵi Mose anali wosakhoza kusenza yekha thayo losamalira nkhani zachiweruzo kaamba ka anthuwo. (Eksodo 18:13, 18) Iye analandira lingaliro la mpongozi wake la kupeza chithandizo. Kachiŵirinso, kodi ndianthu amtundu wanji amene anasankhidwa? Timaŵerenga kuti: “Dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuwopa Mulungu, amuna owona, akudana nalo phindu lachinyengo; . . . Ndipo Mose anasankha amuna amtima, mwa Aisrayeli onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi. Ndipo anaweruza anthu nthaŵi zonse; mlandu wakuwalaka amabwera nawo kwa Mose, ndi milandu yaing’ono yonse amaweruza okha.”​—Eksodo 18:21-26.

15. Kodi nziti zimene zinali ziyeneretso za awo otumikira monga oweruza m’Israyeli?

15 Tikhoza kuwona kuti msinkhu suunali chogamulira chokha chosankhira amuna oti akhale oweruza. Mose anafotokoza kuti: “Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu mwa mafuko anu.” (Deuteronomo 1:13) Mose anali wozolowerana bwino lomwe ndi zimene Elihu wachichepere anafotokoza zaka zambiri pasadakhale kuti: “Akulu sindiwo eni nzeru, ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo.” (Yobu 32:9) Ndithudi, awo oikidwa anafunikira kukhala amuna “ozindikira bwino.” Koma koposa zonse iwo anafunikira kukhala amuna okhoza, owopa Mulungu, odalirika, amene anadana nalo phindu lachinyengo ndi amene anali anzeru ndi aluntha. Chotero, kukuwonekera kukhala kwachiwonekere, kuti “akulu akulu” ndi “akapitawo” otchulidwa pa Yoswa 23:2 ndi 24:1 sanali osiyana ndi “akulu” otchulidwa m’mavesi amodzimodziwo koma anasankhidwa pakati pawo.​—Wonani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 549.

Kupereka Chiweruzo Cholungama

16. Kodi tiyenera kuwonanji lerolino ponena za malangizo amene Mose anapereka kwa oweruza oikidwa chatsopano?

16 Ponena za malangizo operekedwa kwa oweruza oikidwa amenewa, Mose anati: “Ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; aang’ono ndi aakulu muwamvere mmodzimodzi; musamawopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakulakani mubwere nawo kwa ine [Mose], ndidzaumva.”​—Deuteronomo 1:16, 17.

17. Kodi ndani amene anaikidwa monga oweruza, ndipo kodi ndichenjezo lotani limene Mfumu Yehosafati anawapatsa?

17 Ndithudi, nkhani inkafika kwa Mose kokha m’nthaŵi ya moyo wake. Chotero makonzedwe owonjezereka anapangidwa oti nkhani zovuta ziperekedwe kwa ansembe, Alevi, ndipo makamaka oweruza oikidwa. (Deuteronomo 17:8-12; 1 Mbiri 23:1-4; 2 Mbiri 19:5, 8) Kwa oweruza amene anawaika m’mizinda ya Yuda, Mfumu Yehosafati anafotokoza kuti: “Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; . . . Muzitero ndi kuwopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro. Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m’midzi mwawo, . . . muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.”​—2 Mbiri 19:6-10.

18. (a) Kodi ndimalamulo amakhalidwe abwino ena ati amene oweruza m’Israyeli anafunikira kugwiritsira ntchito? (b) Kodi oweruza anafunikira kukumbukira chiyani, ndipo kodi ndimalemba ati amene amasonyeza zotulukapo za kuiwala kwawo zimenezi?

18 Pakati pa malamulo amakhalidwe amene oweruza m’Israyeli anayenera kugwiritsira ntchito panali otsatirapowa: chiweruzo chofanana kwa wolemera ndi wosauka (Eksodo 23:3, 6; Levitiko 19:15); kupanda tsankhu kotheratu (Deuteronomo 1:17); kusalandira ziphuphu. (Deuteronomo 16:18-20) Oweruza anafunikira kukumbukira mosalekeza kuti zimene iwo anali kuweruza zinali nkhosa za Yehova. (Salmo 100:3) Kunena zowona, chimodzi cha zifukwa zimene Yehova anakanira Israyeli wakuthupi chinali chakuti ansembe awo ndi abusa analephera kuweruza mwachilungamo ndipo anachita ndi anthu mwankhanza.​—Yeremiya 22:3, 5, 25; 23:1, 2; Ezekieli 34:1-4; Malaki 2:8, 9.

19. Kodi kupenda miyezo ya Yehova ya chiweruzo cholungama cha m’Nyengo Yathu isanakhale nkwaphindu lotani kwa ife, ndipo kodi nchiyani chimene chidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?

19 Yehova samasintha. (Malaki 3:6) Kupendedwa mwachidule kumeneku kwa njira imene chiweruzo chinayenera kuperekedwera m’Israyeli ndi mmene Yehova analingalilira kukanidwa kulikonse kwa chilungamo kuyenera kupangitsa akulu amene lerolino ali ndi thayo la kupanga zosankha zachiweruzo kuima kaye ndi kuganiza. Chitsanzo cha Yehova monga Woweruza, ndi dongosolo lachiweruzo limene anakhazikitsa m’Israyeli, zinapereka malamulo amakhalidwe amene amapereka chitsanzo cha kupereka chiweruzo mkati mwa mpingo Wachikristu. Tidzawona zimenezi m’nkhani yotsatira.

Mafunso Akupenda

◻ Kodi ndimotani mmene njira ya Yehova ya kuweruza ingafotokozedwere mwachidule?

◻ Kodi ndimotani mmene njira ya Yehova inachitidwira chitsanzo m’zochita zake ndi Kaini ndi mbadwo wa Chigumula chisanachitike?

◻ Kodi ndani amene anachita monga oweruza m’nthaŵi za makolo akale, ndipo motani?

◻ Kodi nchiyani chimene chinasiyanitsa dongosolo lachiweruzo la Israyeli ndi lija la mitundu ina?

◻ Kodi ndiamuna amtundu wotani amene anaikidwa monga oweruza m’Israyeli, ndipo kodi ndimalamulo amakhalidwe abwino otani amene iwo anayenera kutsatira?

[Chithunzi patsamba 10]

M’nthaŵi za makolo akale ndi m’Israyeli, akulu oikidwa anapereka chiweruzo pachipata chamzinda

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena