Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 10/1 tsamba 4-8
  • Dziŵani Yehova—Mulungu wa Umunthu Wake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziŵani Yehova—Mulungu wa Umunthu Wake
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova ndi Mose ‘Kupenyana Maso’
  • Yehova​—Mulungu wa Eliya wa Umunthu Wake
  • Kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera kwa Paulo
  • Kukhala Wokana Mulungu Sikumatsekereza Chidwi cha Yehova
  • Mmene “Wauchitsiru” Amaonera Mulungu
  • Machenjezo Kuchokera kwa Mulungu Wathu wa Umunthu Wake
  • Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mudzakhulupirika Monga Eliya?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Analimbikitsidwa ndi Mulungu Wake
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha?
    Phunzitsani Ana Anu
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 10/1 tsamba 4-8

Dziŵani Yehova​—Mulungu wa Umunthu Wake

POYEREKEZA lingaliro la Ahindu la Mulungu ndi la zipembedzo zina, Dr. S. Radhakrishnan wa ku India anaona kuti: “Mulungu wa Aisrayeli ndi wa mtundu wina. Ali ndi umunthu wake ndipo m’mbiri yonse wakhala akuchita zinthu ndipo ali ndi chidwi ndi kusintha ndiponso zogwa mwadzidzidzi zadziko lotukuka kumene lino. Ndi Munthu yemwe amatha kulankhulana nafe.”

Dzina lachihebri la Mulungu wa m’Baibulo ndi יהוה, kaŵirikaŵiri lotembenuzidwa kuti “Yehova.” Ali pamwamba pa milungu ina yonse. Kodi timadziŵanji ponena za iye? Kodi ankachita motani ndi anthu m’nthaŵi za Baibulo?

Yehova ndi Mose ‘Kupenyana Maso’

Ubwenzi ‘wopenyana maso’ unalipo pakati pa Yehova ndi mtumiki wake Mose, ngakhale kuti Mose sanali kumuona kwenikwenidi Mulungu. (Deuteronomo 34:10; Eksodo 33:20) Pa unyamata wake, mtima wa Mose unali pa Aisrayeli, amene panthaŵiyo anali muukapolo ku Igupto. Anakana moyo wake monga mmodzi wa a m’nyumba ya Farao, “nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu.” (Ahebri 11:25) Zotsatira zake, Yehova anapatsa Mose mwaŵi wapadera.

Monga mmodzi wa a m’nyumba ya Farao, “Mose anaphunzira nzeru zonse za Aigupto.” (Machitidwe 7:22) Koma kuti atsogolere mtundu wa Aisrayeli, anafunikira kukulitsa mikhalidwe ya kudzichepetsa, kudekha, ndi chifatso. Izi anazichita panthaŵi yomwe anali mbusa ku Midyani kwa zaka 40. (Eksodo 2:15-22; Numeri 12:3) Yehova, ngakhale anakhalabe wosaoneka, anadziulula iye mwini ndiponso zifuno zake kwa Mose, ndipo kupyolera mwa angelo Mulungu anapereka Malamulo Khumi kwa iye. (Eksodo 3:1-10; 19:3-20:20; Machitidwe 7:53; Ahebri 11:27) Baibulo limatiuza kuti “Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake.” (Eksodo 33:11) Ndithudi, Yehova mwiniyo anati: “Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa.” Ndi ubwenzi wabwino chotani umene Mose mwaumwini anali nawo ndi Mulungu wake wosaoneka koma wokhala ndi umunthu wake!​—Numeri 12:8.

Kuwonjezera pa mbiri yoyambirira ya mtundu wa Israyeli, Mose analemba Chilamulo pamodzi ndi mbali zake zina zonse. Anapatsidwanso mwaŵi wina wamtengo wapatali​—uja wolemba buku la Genesis. Ku mapeto kwa buku limenelo kunali mbiri yodziŵika bwino kwa banja lake motero yosavutirapo kulemba. Koma nanga nkuti kumene Mose anapeza tsatanetsatane wa mbiri yoyambirira ya munthu? Mwina Mose anali ndi zolembedwa zakale, zimene azigogo ake anasunga zomwe ankaonerapo. Mwinanso zitheka kuti wina adamulongosolera pakamwa tsatanetsatane wake kapena Yehova anamvumbulutsira mwachindunji. Anthu oopa Mulungu a m’mibadwo yonse avomereza za ubwenzi umene Mose anali nawo ndi Mulungu wake pankhani imeneyi.

Yehova​—Mulungu wa Eliya wa Umunthu Wake

Mneneri Eliya nayenso anadziŵa Yehova kuti ali ndi umunthu wake. Eliya anali wachangu pa kulambira koyera ndipo anatumikira Yehova mosasamala kanthu zakuti anadedwa ndi kutsutsidwa koopsa ndi alambiri a Baala, mulungu wamkulu wa kachisi wa Akanani.​—1 Mafumu 18:17-40.

Ahabu, Mfumu ya Israyeli, ndi mkazi wake, Yezebeli, anafuna kupha Eliya. Poopera moyo wake, Eliya anathaŵira ku Beereseba, kumadzulo kwa Nyanja ya M’chere. Kumeneko anayendayenda m’chipululu napemphera kuti afe. (1 Mafumu 19:1-4) Kodi Yehova anali atamtaya Eliya? Kodi Iye sanali kumfunanso mtumiki wake wokhulupirika? Mwina Eliya analingalira choncho, koma anali wolakwa chotani nanga! Pambuyo pake, Yehova analankhula naye motsitsa mawu kumfunsa kuti: “Uchitanji pano, Eliya?” Atamsonyeza mochititsa nthumazi mphamvu zoposa za chilengedwe, “Anamdzera mawu akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?” Yehova mwaumwini anasonyeza chidwi chimenechi mwa Eliya kuti alimbikitse mtumiki wake wokhulupirikayo. Mulungu anali ndi ntchito yambiri yoti Eliyayo aichite, ndipo anavomera chiitano chimenecho ndi mtima wonse! Eliya anatsiriza utumiki wake mokhulupirika, kuyeretsa dzina la Yehova, Mulungu wake wokhala ndi umunthu wake.​—1 Mafumu 19:9-18.

Ataukana mtundu wa Aisrayeli, Yehova sanalankhulenso mwachindunji kwa atumiki ake padziko lapansi. Izi sizitanthauza kuti chidwi chake kwa iwo chidatha. Mwamzimu wake woyera, ankawatsogolerabe ndi kuwalimbitsa mu utumiki wake. Mwachitsanzo, lingalirani za mtumwi Paulo, wotchedwa kuti Saulo poyamba.

Kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera kwa Paulo

Saulo anachokera ku Tariso, mzinda wotchuka ku Kilikiya. Makolo ake anali Ahebri, koma anabadwa monga nzika ya Roma. Komabe analeredwa monga mwa zikhulupiriro zolimba za Afarisi. Pambuyo pake, ku Yerusalemu, anali ndi mpata wophunzira “pamapazi a Gamaliyeli,” mphunzitsi wodziŵika wa Chilamulo.​—Machitidwe 22:3, 26-28.

Chifukwa cha changu cha Saulo cholakwika pamwambo wachiyuda, anagwirizana nawo pakuzunza otsatira a Yesu Kristu. Anavomereza ngakhale kuphedwa kwa Stefano, Mkristu woyamba wofera chikhulupiriro chake. (Machitidwe 7:58-60; 8:1, 3) Pambuyo pake anavomereza kuti ngakhale kuti poyamba anali wamwano ndi wolondalonda ndiponso wachipongwe, “[anamchitira] chifundo, popeza [anazichita] wosazindikira, wosakhulupirira.”​—1 Timoteo 1:13.

Saulo analimbikitsidwa ndi chilakolako chenicheni cha kutumikira Mulungu. Pambuyo pa kutembenuka kwa Saulo panjira ya ku Damasiko, Yehova anamgwiritsira ntchito mwamphamvu. Hananiya, wophunzira wachikristu wakale, anatsogozedwa ndi Kristu woukitsidwayo kukamthandiza. Pambuyo pake Paulo (dzina lachiroma limene Saulo anadziŵika nalo monga Mkristu) anatsogozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova kukachita utumiki wautali ndiponso wobala zipatso kumbali za Ulaya ndi Asia Minor.​—Machitidwe 13:2-5; 16:9, 10.

Kodi chitsogozo chofananacho cha mzimu woyera chingadziŵidwe lerolino? Inde, chikhoza kudziŵidwa.

Kukhala Wokana Mulungu Sikumatsekereza Chidwi cha Yehova

Joseph F. Rutherford anali pulezidenti wachiŵiri wa Watch Tower Society. Anabatizidwa mu 1906 kukhala Wophunzira Baibulo​—dzina lomwe Mboni za Yehova zinali kudziŵika nalo nthaŵiyo​—anaikidwa kukhala phungu wa zamalamulo wa Sosaite chaka chotsatira, ndipo anakhala pulezidenti wake mu January 1917. Komabe, panthaŵi ina loya wachinyamata ameneyu anali wokana Mulungu. Kodi anakhala motani mtumiki wakhama wachikristu wa Yehova motero?

Mu July 1913, Rutherford anatumikira monga tcheyamani wa msonkhano wa International Bible Students Association umene unachitidwira ku Springfield, Massachusetts, U.S.A. Mtolankhani wa nyuzipepala ya kumeneko The Homestead, adamfunsa mafunso Rutherford, ndipo makambitsiranowo analembedwa mu lipoti lofalitsa za msonkhanowo.

Rutherford anafotokoza kuti panthaŵi imene anakonzekera kukwatira, anali ndi zikhulupiriro za chipembedzo cha Baptist, koma za yemwe amati adzakhale mkazi wakeyo zinali za Presbyterian. Pamene pasitala wa Rutherford ananena kuti “mkaziyo adzapita kumoto wa helo chifukwa sanamizidwe ndi kuti iye adzapita kumwamba chifukwa anamizidwa, malingaliro ake abwino anasintha ndipo anakhala wokana Mulungu.”

Rutherford anafufuza mosamalitsa kwa zaka zingapo kuti amangenso chikhulupiriro chake mwa Mulungu wa umunthu wake. Iye anati, anagwiritsira ntchito ganizo lakuti “chomwe sichingakhutiritse maganizo sichiyenera kukhutiritsa mtima.” Akristu “ayenera kutsimikizira kuti Malemba amene amakhulupirira ndi oona,” Rutherford analongosola choncho, nawonjeza kuti: “Ayenera kudziŵa maziko a zimene akukhulupirira.”​—Onani 2 Timoteo 3:16, 17.

Inde, nzotheka ngakhale lerolino kwa munthu wokana Mulungu ndi yemwe amati Mulungu sadziŵika kufufuza Malemba ndi kukhala ndi chikhulupiriro ndi kukulitsa ubwenzi wathithithi ndi Yehova Mulungu. Ataphunzira Baibulo mosamalitsa mogwiritsira ntchito chofalitsa cha Watch Tower cha Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, wachinyamata wina anavomera kuti: “Pamene ndinayamba phunziroli, sindinali kukhulupirira mwa Mulungu, koma tsopano ndapeza kuti kudziŵa Baibulo kwasintha maganizo anga onse. Ndayamba kumdziŵa Yehova ndi kumkhulupirira.”

Mmene “Wauchitsiru” Amaonera Mulungu

“Sizinachitikepo kwa wolemba Chipangano Chakale [Malemba Achihebri] kuyesa kufufuza kapena kutsutsa za kukhalapo kwa Mulungu,” akutero Dr. James Hastings mu A Dictionary of the Bible. “Malinga ndi malingaliro adziko lakale sanakane kukhalapo kwa Mulungu, kapena kupanga makani kuti apeze umboni wake. Chikhulupirirocho chinali chachibadwa m’maganizo a munthu ndipo chinali cha anthu onse.” Komabe, nzoona kuti izi sizikutanthauza kuti anthu onse panthaŵiyo anali oopa Mulungu. Ayi ndithu. Salmo 14:1 ndi 53:1 onsewo amatchula za ‘chitsiru,’ kaya monga King James Version imanenera, “wopusa,” amene amati mumtima mwake, “Kulibe Mulungu.”

Kodi chitsiru chimenechi, chokana kukhalapo kwa Mulungu ndi munthu wamtundu wanji? Sikuti sadziŵa zimenezo ayi. M’malo mwake, liwu lachihebri na·valʹ limasonya munthu wopanda khalidwe. Profesa S. R. Driver, m’ndemanga zake za mu The Parallel Psalter, akuti vuto “sikuti nkulephera kuganiza, koma kusazindikira khalidwe labwino ndi zachipembedzo, kupandiratu kuzindikira kapena nzeru.”

Wamasalmo akupitiriza kulongosola za kunyonyotsoka kwa khalidwe kumene kumabwera monga chotsatirapo cha maganizo ameneŵa: “Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.” (Salmo 14:1) Dr. Hastings akutsiriza kuti: “Pokhulupirira kuti kulibe Mulungu m’dziko ndi kuti kulibe chilango, anthu akhala oipa ndipo achita zosayenera.” Poyera amatsatira mapulinsipulo osaopa Mulungu ndipo amanyalanyaza Mulungu wokhala ndi umunthu wake amene alibe naye khumbo lokhala oŵerengeredwa mlandu. Koma maganizo otere ndi opanda nzeru ndi opanda pake masiku ano monga momwe analili pamene wamasalmo analemba mawu ake zaka 3000 zapitazo.

Machenjezo Kuchokera kwa Mulungu Wathu wa Umunthu Wake

Tiyeni tsopano tibwerere ku mafunso amene tadzutsa m’nkhani yathu yoyamba. Nchifukwa ninji anthu ambiri amalephera kugwirizanitsa Mulungu wa umunthu wake ndi mavuto amene achuluka m’dzikowa lerolino?

Baibulo lili ndi uthenga wa ‘anthu olankhula atagwidwa ndi Mzimu Woyera.’ (2 Petro 1:21) Ilo lokha limatiululira Mulungu wa umunthu wake, Yehova. Komanso limatichenjeza ife za munthu woipa, wosaoneka kwa anthu, amene ali ndi mphamvu zotsogolera kalingaliridwe ka anthu​—Satana Mdyerekezi. Eetu, nanga ngati sitikhulupirira mwa Mulungu wa umunthu wake, ndiye tingakhulupirire bwanji kuti kulinso Mdyerekezi, kapena Satana, waumunthu?

Mouziridwa mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Pambuyo pake Yohane anati: “Tidziŵa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mawu ameneŵa amagwirizana ndi a Yesu, amene Yohane iyemwini analemba mu Uthenga wake Wabwino: “Mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine.”​—Yohane 14:30.

Malemba ameneŵa ndi otalikirana chotani nanga ndi zimene anthu masiku ano amakhulupirira! “Kukamba za Mdyerekezi mwachionekere ndi kwachikale masiku ano. Masiku athu a kukayikakayika ndiponso a sayansi, apangitsa Satana kupumula,” inatero Catholic Herald. Koma Yesu ananena mwamphamvu kwa anthu aja amene anali ncholinga chomupha kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita.”​—Yohane 8:44.

Kalongosoledwe ka Baibulo ka mphamvu za Satana nkomveka. Limanena bwino chifukwa chake, ngakhale kuti anthu ambiri ali ndi cholinga chomakhala mumtendere ndi mogwirizana, udani, nkhondo, ndiponso ziwawa zopanda pake, monga momwe zinachitikira ku Dunblane (kotchulidwa pa masamba  3 ndi 4) zili mbwee m’dziko. Ndiponso, sikuti Satana ali yekha mdani amene tiyenera kulimbana naye. Baibulo limapereka machenjezo owonjezereka ponena za adyerekezi, kapena ziŵanda​—zolengedwa zauzimu zoipa zomwe zinagwirizana ndi Satana kalekale kuti zisokeretse ndi kuvutitsa mtundu wa anthu. (Yuda 6) Yesu Kristu anakumana ndi mphamvu za mizimu imeneyi nthaŵi zambiri, ndipo anatha kuzigonjetsa.​—Mateyu 12:22-24; Luka 9:37-43.

Mulungu woona, Yehova, wakonza zochotsapo kuipa padziko lapansi pano ndipo potsiriza kuchotseratu zochita za onse Satana ndi ziwanda zake. Pogwiritsira ntchito chidziŵitso chathu cha Yehova, tingakhale ndi chikhulupiriro ndi chidaliro cholimba m’malonjezo ake. Iye amati: “Ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.” Ndithudi Yehova ndi Mulungu wa umunthu wake kwa onse amene amamdziŵa, kumlambira, ndi kumtumikira. Tikhoza kuyang’ana kwa iye, iye yekhayo, kaamba ka chipulumutso chathu.​—Yesaya 43:10, 11.

[Chithunzi patsamba 7]

Chozokotedwa cha m’zaka za zana la 18 chosonyeza Mose akulemba Genesis 1:1 mouziridwa

[Mawu a Chithunzi]

Kuchokera mu The Holy Bible la J. Baskett, Oxford

[Chithunzi patsamba 8]

Yesu Kristu anagonjetsa ziŵanda nthaŵi zambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena