Kuzindikira Kufooka, Kuipa, ndi Kulapa
TCHIMO ndi chinthu chimene Akristu amadana nacho—kupereŵera pa miyezo yolungama ya Yehova. (Ahebri 1:9) Mwachisoni, tonsefe timachimwa nthaŵi ndi nthaŵi. Tonsefe timalimbana ndi kufooka kobadwa nako ndi kupanda ungwiro. Komabe, kaŵirikaŵiri ngati tiulula machimo athu kwa Yehova ndi kuyesayesa moona mtima kusawabwerezanso, tingamfikire ndi chikumbumtima choyera. (Aroma 7:21-24; 1 Yohane 1:8, 9; 2:1, 2) Tikuyamikira Yehova kuti, pamaziko a nsembe ya dipo, amalandira utumiki wathu wopatulika mosasamala kanthu za kufooka kwathu.
Ngati wina agwera m’tchimo lalikulu chifukwa cha chifooko chakuthupi, mwamsanga amafunikira kuŵetedwa mogwirizana ndi njira yolongosoledwa pa Yakobo 5:14-16 kuti: “Pali wina kodi adwala [mwauzimu] mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo . . . ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe.”
Pamene Mkristu wodzipatulira achita tchimo lalikulu, kanthu kena koposa kuulula chabe kwaumwini kwa Yehova kamafunikira. Akulu ayenera kutenga masitepe akutiakuti, popeza kuti chiyero kapena mtendere wa mpingo zaikidwa pachiswe. (Mateyu 18:15-17; 1 Akorinto 5:9-11; 6:9, 10) Akulu afunikira kudziŵa kuti: Kodi munthuyo ali wolapa? Kodi nchiyani chimene chinatsogolera ku tchimolo? Kodi linangochitika chifukwa cha kufooka kwa kamodzi kamodzi? Kodi kunali kuchita tchimo kwachizoloŵezi? Kuzindikira zimenezi sikumakhala nthaŵi zonse kopepuka kapena koonekeratu ndipo kumafuna chidziŵitso chakuya.
Komabe, bwanji ngati tchimolo lachitidwa chifukwa cha kulondola njira ya kuchita choipa ndi makhalidwe oipa? Pamenepo, thayo la akulu nloonekeratu. Polangiza za kusamalira milandu yaikulu mumpingo wa Akorinto, mtumwi Paulo anati: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:13) Anthu oipa alibe malo mumpingo Wachikristu.
Kupima Kufooka, Kuipa, ndi Kulapa
Kodi akulu angadziŵe motani pamene munthu ali wolapa?a Limeneli sifunso lopepuka. Mwachitsanzo, talingalirani za Mfumu Davide. Iye anachita chigololo ndiyeno, mbanda yeniyeni. Komabe, Yehova anamlola kukhalabe ndi moyo. (2 Samueli 11:2-24; 12:1-14) Ndiyeno talingalirani za Hananiya ndi Safira. Iwo anayesa kunyenga atumwi mwa kunama, akumanamizira kukhala ooloŵa manja koposa mmene analiridi. Tchimo lalikulu? Inde. Kodi linali lowopsa mofanana ndi mbanda ndi chigololo? Kutalitali! Komabe, Hananiya ndi Safira analipira ndi miyoyo yawo.—Machitidwe 5:1-11.
Kodi nchifukwa ninji panakhala ziweruzo zosiyana? Davide anagwera m’tchimo lalikulu chifukwa cha kufooka kwakuthupi. Pamene zimene anachita zinaikidwa pamaso pake, iye analapa, ndipo Yehova anamkhululukira—ngakhale kuti analangidwa kwakukulu ndi mavuto a m’nyumba yake. Hananiya ndi Safira anachimwa mwa kulinganiza mwadala kunyenga mpingo Wachikristu ndipo motero ‘anachitira chinyengo mzimu woyera ndi Mulungu.’ Zimenezo zinakhala umboni wa mtima woipa. Chifukwa chake, iwo anaweruzidwa mowopsa kwambiri.
M’zochitika ziŵiri zonsezo Yehova anapereka chiweruzo, ndipo chiweruzo chake chinali cholondola chifukwa iye akhoza kusanthula mtima. (Miyambo 17:3) Akulu aumunthu sangathe kuchita zimenezo. Motero kodi ndimotani mmene akulu angazindikirire kuti tchimo lalikulu lili kwenikweni umboni wa chifooko osati kuipa?
Kwenikweni, tchimo lililonse nloipa, koma si ochimwa onse amene ali oipa. Machimo ofanana angakhale umboni wa chifooko mwa munthu wina ndi umboni wa kuipa mwa wina. Ndithudi, kaŵirikaŵiri kuchita tchimo kumaloŵetsamo mlingo winawake wa ziŵiri zonsezo kufooka ndi kuipa kwa wochimwayo. Chinthu china chodziŵira ndicho mmene wochimwayo akuonera chimene wachita ndi chimene akufuna kuchita ponena za icho. Kodi akusonyeza mzimu wa kulapa? Akulu amafunikira chidziŵitso chakuti aone zimenezi. Kodi angapeze motani chidziŵitso chimenecho? Mtumwi Paulo analonjeza Timoteo kuti: “Lingilira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziŵitso m’zonse.” (2 Timoteo 2:7) Ngati akulu modzichepetsa ‘amalingalira’ pa mawu ouziridwa a Paulo ndi olemba Baibulo ena, adzapeza chidziŵitso chofunikira kuti awaone mwa njira yoyenera awo amene amachimwa mumpingo. Ndiyeno, zigamulo zawo zidzasonyeza kalingaliridwe ka Yehova, osati ka iwo eni.—Miyambo 11:2; Mateyu 18:18.
Kodi zimenezi zimachitidwa motani? Njira ina ndiyo ya kupenda za mmene Baibulo limalongosolera anthu oipa ndi kuona kaya ngati malongosoledwewo akuyenerera munthu amene mukuchita naye.
Kuvomereza Mlandu ndi Kulapa
Anthu oyamba kusankha njira yoipa anali Adamu ndi Hava. Ngakhale kuti anali angwiro ndi odziŵa bwino lomwe lamulo la Yehova, iwo anapandukira ulamuliro wa Mulungu. Pamene Yehova anawafunsa zimene anachita, mayankho awo ngofunikira kudziŵa—Adamu anaimba mlandu Hava, ndipo Hava anaimba mlandu njoka! (Genesis 3:12, 13) Yerekezerani zimenezi ndi kudzichepetsa kwakukulu kwa Davide. Pamene anchititsidwa kuyang’anizana ndi machimo ake aakuluwo, anavomereza mlandu ndi kupempha chikhululukiro, akumati: “Ndinachimwira Yehova.”—2 Samueli 12:13; Salmo 51:4, 9, 10.
Akulu angachite bwino kulingalira zitsanzo ziŵiri zimenezi pamene akusamalira nkhani za tchimo lalikulu, makamaka ngati ali munthu wamkulu. Kodi wochimwayo—mofanana ndi Davide pamene anakhutiritsidwa za tchimo lake—akuvomereza mlandu mosazengereza ndi kuyang’ana kwa Yehova ndi mtima wolapa kuti amthandize ndi kumkhululukira, kapena kodi iye akuyesayesa kupeputsa chimene wachita, mwinamwake akumatulira munthu wina mlanduwo? Zoona, munthu amene wachimwa angafune kufotokoza chimene chinamtsogolera ku machitidwe ake, ndipo pangakhale mikhalidwe, kaya yakumbuyo kapena yapanthaŵiyo, imene akulu angafunikire kuipenda posankha mmene angamuthandizire. (Yerekezerani ndi Hoseya 4:14.) Koma iye ayenera kuvomereza kuti iye ndiye amene anachimwa ndi kuti iye ndiye ali ndi mlandu kwa Yehova. Kumbukirani kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18.
Kumachita Choipa
M’buku la Masalmo, muli zilozero zambiri za anthu oipa. Malemba oterowo angathandize kwambiri akulu kuzindikira kaya munthuyo ali kwenikweni woipa kapena wofooka. Mwachitsanzo, talingalirani pemphero louziridwa la Mfumu Davide lakuti: “Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi awo, koma mumtima mwawo muli choipa.” (Salmo 28:3) Onani kuti anthu oipa akutchulidwa monga “ochita zopanda pake.” Munthu amene amachimwa chifukwa cha kufooka kwakuthupi ali wothekera kuleka atangozindikira kuipa kwake. Komabe, ngati munthu ‘amachita’ choipa kwakuti chikhala mbali ya moyo wake, chimenechi chingakhale umboni wa mtima woipa.
Davide anatchula mkhalidwe wina wa kuipa m’vesi limenelo. Mofanana ndi Hananiya ndi Safira, munthu woipa amalankhula zinthu zabwino ndi pakamwa pake koma ali ndi zinthu zoipa mumtima mwake. Iye angakhale wonyenga—mofanana ndi Afarisi a m’tsiku la Yesu omwe ‘anaonekera olungama pamaso pa anthu, koma mkati anali odzala ndi chinyengo ndi kusayeruzika.’ (Mateyu 23:28; Luka 11:39) Yehova amadana ndi chinyengo. (Miyambo 6:16-19) Ngati munthu wina mwachinyengo ayesa kukana machimo ake aakulu ngakhale pamene akulankhula ndi komiti yachiweruzo, kapena angovomereza monyinyirika kokha zimene enawo akudziŵa kale, koma osaulula zonse, zimenezi zingakhalenso umboni wa mtima woipa.
Mwano wa Kusawopa Yehova
Zinthu zina zimene zimasonyeza munthu woipa zalongosoledwa m’Salmo 10. Mmenemo timaŵerenga kuti: “Podzikuza woipa apsereza waumphaŵi; . . . anyoza Yehova.” (Salmo 10:2, 3) Kodi ndimotani mmene tiyenera kuonera Mkristu wodzipatulira amene ali wodzikuza ndi wosawopa Yehova? Ndithudi, amenewa ali maganizo oipa. Munthu amene achimwa chifukwa cha kufooka, atazindikira tchimo lake kapena litasonyezedwa kwa iye, amalapa ndi kuyesayesa zolimba kuwongolera moyo wake. (2 Akorinto 7:10, 11) Kumbali ina, ngati munthu achimwa chifukwa cha mkhalidwe waukulu wa kusawopa Yehova, nanga nchiyani chidzamletsa kubwereranso kaŵirikaŵiri panjira yake yochimwayo? Ngati ali wodzikuza ngakhale kuti anapatsidwa uphungu mumzimu wachifatso, kodi ndimotani mmene angakhalire ndi kudzichepetsa kofunikira kuti alape moona mtima?
Tsopano talingalirani mawu a Davide apatsogolo pang’ono, m’salmo limodzimodzilo: “Woipa anyozeranji Mulungu, anena m’mtima mwake, Simudzafunsira?” (Salmo 10:13) M’kakonzedwe ka mpingo Wachikristu, munthu woipa amadziŵa kusiyana kwa chabwino ndi choipa, koma samazengereza kuchita choipa ngati aganiza kuti akhoza kuzemba chilango. Malinga ngati adziŵa kuti sizidzaululika, iye amakhala waufulu kuchita zikhoterero zake zochimwazo. Mosiyana ndi Davide, ngati machimo ake avumbuluka, adzachita machenjera akuti apeŵe chilango. Munthu woteroyo amakhala wopanda ulemu kwenikweni kwa Yehova. “Palibe kuwopa Mulungu pamaso pake. . . . Choipa saipidwa nacho.”—Salmo 36:1, 4.
Kuvulaza Ena
Kaŵirikaŵiri, tchimo la munthu mmodzi limayambukira anthu ambiri. Mwachitsanzo, wachigololo amachimwira Mulungu; amavutitsanso mkazi wake ndi ana; ngati wochimwa naye ali wokwatiwa, iye amavutitsanso banja la mkaziyo; ndipo amawononganso dzina labwino la mpingo. Kodi ndimotani mmene iye amaonera zonsezo? Kodi akusonyeza chifundo chochokera mumtima limodzi ndi kulapa kwenikweni? Kapena kodi akusonyeza mzimu wolongosoledwa mu Salmo 94 kuti: “Adzitamandira onse ochita zopanda pake. Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholandira chanu. Amapha wamasiye ndi mlendo, nawapha ana amasiye. Ndipo amati, Yehova sachipenya, ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira”?—Salmo 94:4-7.
Mwachionekere, machimo osamaliridwa mumpingo sadzaloŵetsamo mbanda ndi kupha. Komabe, mzimu wosonyezedwa panopa—mzimu wakukhala wofunitsitsa kuvutitsa ena kaamba ka phindu laumwini—ungakhale woonekeratu pamene akulu afufuza mchitidwe wolakwawo. Izinso, ndizo kunyada, chizindikiro cha munthu woipa. (Miyambo 21:4) Nzosiyana kotheratu ndi mzimu wa Mkristu woona, amene amafunitsitsa kudzimana kaamba ka mbale wake.—Yohane 15:12, 13.
Kugwiritsira Ntchito Zitsogozo Zaumulungu
Zitsogozo zoŵerengeka zimenezi cholinga chake sindicho kuika malamulo. Komabe, zimapatsa lingaliro la zinthu zina zimene Yehova amaziona kukhaladi zoipa. Kodi pali kukana mlandu wa cholakwa chochitidwacho? Kodi wochimwayo wanyalanyaza kotherathu uphungu wakumbuyoku pa nkhani imodzimodziyo? Kodi pali chizoloŵezi chozama cha kuchita cholakwa chachikulu? Kodi wochita cholakwayo akusonyeza kunyalanyaziratu lamulo la Yehova? Kodi wapanga kuyesayesa kwa kubisa cholakwacho, mwinamwake akumanyenga ena panthaŵi imodzimodziyi? (Yuda 4) Kodi zoyesayesa zoterozo zikukulirakulira pamene cholakwacho chivumbuluka? Kodi wochimwayo akusonyeza kusadera nkhaŵa konse za chivulazo chimene wachita kwa ena ndi pa dzina la Yehova? Bwanji ponena za mkhalidwe wake wa maganizo? Pambuyo pakuti uphungu wokoma mtima wa Malemba waperekedwa, kodi iye ali wodzikuza kapena wouma khosi? Kodi alibe chikhumbo chochokera mumtima cha kupeŵa kubwereza cholakwacho? Ngati akuluwo aona zinthu zoterozo, zimene zimasonyeza mwamphamvu kusoŵeka kwa mtima wakulapa, iwo angagamule kuti machimo ochitidwawo ali umboni wa kuipa osati kufooka chabe kwa thupi.
Ngakhale pochita ndi munthu wooneka kukhala ndi zikhoterero zoipa, akulu samaleka kumlimbikitsa kulondola chilungamo. (Ahebri 3:12) Anthu oipa angalape ndi kusintha. Ngati sizikanakhala motero, nanga nchifukwa ninji Yehova analimbikitsa Aisrayeli kuti: “Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa”? (Yesaya 55:7) Mwinamwake, mkati mwa kuzenga mlandu, akulu adzazindikira kusintha mumtima mwake kosonyezedwa ndi mzimu ndi mkhalidwe wa maganizo wa kulapa.
Ngakhale panthaŵi ya kuchotsa munthu, akulu, monga abusa, adzamlimbikitsa kulapa ndi kuyesayesa kubwerera m’chiyanjo cha Yehova. Kumbukirani “woipayo” mu Korinto. Mwachionekere iye anasintha njira yake, ndipo Paulo pambuyo pake anavomereza kubwezeretsedwa kwake. (2 Akorinto 2:7, 8) Talingaliraninso Mfumu Manase. Iye anali woipa kwenikweni, koma pamene analapa potsirizira pake, Yehova anavomereza kulapa kwakeko.—2 Mafumu 21:10-16; 2 Mbiri 33:9, 13, 19.
Zoona, lilipo tchimo limene silimakhululukidwa—tchimo lochimwira mzimu woyera. (Ahebri 10:26, 27) Yehova yekha ndiye amagamula kuti munthu wachita tchimo loterolo. Anthu alibe ulamuliro wa kuchita zimenezo. Thayo la akulu ndilo kusunga mpingo uli woyera ndi kuthandiza kuwonjola ochimwa olapa. Ngati iwo achita zimenezo ndi chidziŵitso ndi kudzichepetsa, akumalola zigamulo zawo kusonyeza nzeru ya Yehova, pamenepo, Yehova adzadalitsa mbali imeneyi ya kuŵeta kwawo.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zochulukirapo, onani Nsanja ya Olonda ya March 1, 1982, masamba 17-20; Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 772-4.
[Chithunzi patsamba 29]
Hananiya ndi Safira ananyenga mzimu woyera, akumasonyeza kuipa kwa mtima