Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 155
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kupereka kumene Mulungu amasangalala nako
  • Kupereka kumene Mulungu sasangalala nako
  • “Mulungu Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Muli ndi Mzimu Wopatsa?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yehova Amakonda Opatsa Mokondwerera
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Ubwino wa Mtima Wopatsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 155
Bambo wanyamula kabokosi koti muli mphatso

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kupatsa?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala opatsa. Koma limanena kuti tizichita zimenezi ndi zolinga zabwino komanso osati mokakamizika. Limasonyeza kuti kupatsa koteroko kumakhala ndi zotsatira zabwino kwa wolandira ngakhalenso kwa woperekayo. (Miyambo 11:25; Luka 6:​38) Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

  • Kupereka kumene Mulungu amasangalala nako

  • Kupereka kumene Mulungu sasangalala nako

  • Mavesi a m’Baibulo amene amanena za kupatsa

Kupereka kumene Mulungu amasangalala nako

Mulungu amasangalala tikamapatsa ena zinthu mwa kufuna kwathu. Baibulo limanena kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”​—2 Akorinto 9:7.

Kupereka ndi mtima wonse ndi mbali ya “kupembedza” kumene Mulungu amavomereza. (Yakobo 1:27) Yehova amasangalala ndi munthu yemwe amathandiza anthu omwe akufunikira thandizo. Yehova amaona kuti munthuyo akumukongoza iyeyo. (Miyambo 19:17) Ndipo Baibulo limanena kuti Mulungu adzabweza yekha ngongoleyo.​—Luka 14:12-​14.

Kupereka kumene Mulungu sasangalala nako

Ngati munthu akupereka n’cholinga choti apezepo kenakake. Mwachitsanzo:

  • Pofuna kudzionetsera.​—Mateyu 6:2.

  • Pofuna kuti nayenso adzapatsidwe kenakake.​—Luka 14:12-14.

  • Pofuna kugula chipulumutso.—Salimo 49:6, 7.

Ngati akupereka pofuna kuthandizira zinthu zomwe Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, si nzeru kupatsa munthu ndalama kuti akayendere juga kapena akagulire mankhwala osokoneza bongo komanso kuti akamwe mowa n’kuledzera. (1 Akorinto 6:9, 10; 2 Akorinto 7:1) Ndiponso si zomveka kupereka ndalama kwa munthu amene angathe kugwira ntchito n’kudzipezera yekha zinthu zofunika koma amachita ulesi.​—2 Atesalonika 3:10.

Ngati zikulepheretsa woperekayo kusamalira banja lake. Baibulo limanena kuti amuna okwatira ayenera kusamalira mabanja awo. (1 Timoteyo 5:8) Choncho sizingakhale zoyenera kuti mwamuna azipereka zinthu zambiri kwa anthu ena mpaka banja lake kumasowa zinthu zina zofunikira. Ndipotu Yesu anadzudzula anthu amene ankalephera kusamalira makolo awo okalamba n’kumanena kuti chuma chawo chonse ndi “mphatso yoperekedwa kwa Mulungu.”​—Maliko 7:​9-​13.

Mavesi a m’Baibulo amene amanena za kupatsa

Miyambo 11:25: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.”

Mfundo yake: Kupatsa kumapindulitsa onse, wolandira ndi wopereka yemwe.

Miyambo 19:17: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.”

Mfundo yake: Yehova amaona kuti ali ndi ngongole kwa anthu amene amasonyeza mtima wopatsa kwa anthu ovutika, ndipo akulonjeza kuti adzawabwezera zimene anachitazo.

Mateyu 6:2: “Pamene ukupereka mphatso zachifundo, usalize lipenga muja amachitira onyenga . . . kuti anthu awatamande.”

Mfundo yake: Tisamapereke mphatso pongofuna kuti tidzionetsere kwa anthu.

Machitidwe 20:35: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”

Mfundo yake: Kupereka mphatso ndi mtima wonse kumathandiza munthu kukhala wosangalala.

2 Akorinto 9:7: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”

Mfundo yake: Mulungu amasangalala tikamapereka mphatso mwa kufuna kwathu, osati mokakamizika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena