Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 7/1 tsamba 3-4
  • Mkwiyo—Kodi Iwo Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkwiyo—Kodi Iwo Nchiyani?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kutulutsa Mkwiyo
  • Magwero a Mkwiyo
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Nthaŵi Zonse Kumakhala Kulakwa Kukwiya?
    Galamukani!—1994
  • Kusamalira Mkwiyo—Wanu ndi wa Ena
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kupsa Mtima Kumabweretsa Mavuto
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 7/1 tsamba 3-4

Mkwiyo​—Kodi Iwo Nchiyani?

“MWAKUTSEKEREZA mPhatso yanu yopatsidwa ndi Mulungu ya mkwiyo, mukudzipha inu mwini.” Inachenjeza motero nkhani yogwidwa mawu mu magazini ya Newsweek. Kwa zaka zambiri, mwachiwonekere, akatswiri ambiri odziwa za maganizo atchukitsa lingaliro lakuti mkwiyo wosasonyezedwa ungapangitse kusokonezeka koteroko monga ngati kukwera kwa mwazi, nthenda ya mtima, kupsyinjika, kudera nkhawa, ndi uchidakwa.

Baibulo, kumbali ina, lakhala litachenjeza kwa zaka zikwi: “Leka kupsya mtima, nutaye mkwiyo.” (Masalmo 37:8) Kupeza kwa magwero amatenda kwa Baibulo kuli kofika pansonga: “Usakangaze kukwiya mumtima mwako: pakuti mkwiyo ugona m’chifukwa cha zitsiru.”​—Mlaliki 7:9, King James Version.

Ndani amene ali olondola, akatswiri a kudziko kapena Baibulo? Kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri mkwiyo? Kodi kutulutsa mkwiyo kuli kwabwino kwa ife?

Kutulutsa Mkwiyo

“Mkwiyo” liri liwu la chisawawa lolongosola maganizo amphamvu kapena kuvomereza ku kusasangalatsidwa ndi kutsutsana. Pali mawu enanso, amene amavumbulutsa ukulu wa mkwiyo kapena mmene wasonyezedwera. Ukali umasonyeza mkwiyo wamphamvu. Kulunda kungakhale kosakaza. Kuvutika mtima kungalozere ku kukwiya chifukwa chamagwero achilungamo. Ndipo kuzaza kawirikawiri kumasonyeza kubwezera kapena chilango.

Kawirikawiri mkwiyo umakhala wachindunji: Tiri okwiya ponena za chinachake. Koma mmene timasonyezera mkwiyo kapena kuchita ndi iwo kumapanga kusiyana kwakukulu.

Mosangalatsa, ngakhale kuti akatswiri ena amakakamira kuti kutulutsidwa kwa mkwiyo kuli kopindulitsa, maphunziro aposachedwa a ukatswiri wa za maganizo akusonyeza kuti anthu ambiri amene amadzilola iwo eni kusonyeza mkwiyo amavutika ndi kudzimva kukhala otsika, kupsyinjika, kuvutika kwa kudzimva kukhala ndi mlandu, udani womakulakula, kapena kudera nkhawa. Mkuwonjezerapo, “kuchichotsa icho pa chifuwa panu,” kapena “kuuzira mpweya,” komwe mwinamwake kumatsagana ndi kubuka kwa mkwiyo, kufuula, kulira, kapena ngakhale kuyamba kwa kuthupi, kawirikawiri kumayambitsa mavuto ochuluka kuposa amene kumathetsa. Munthu wokwiya amakwiya moposerapo, ndipo malingaliro a kupwetekedwa amamangirira mwa ena.​—Miyambo 30:33; Genesis 49:6, 7.

Pamene tifuula ndi kulira mu mkwiyo, ife kawirikawiri sitimapeza mapindu omwe tinayembekezera chifukwa chakuti munthu winayo kawirikawiri amayambidwa kubwezera. Mwachitsanzo, tangoyerekezani kuti pamene munali kuyendetsa galimoto yanu, woyendetsa galimoto wina anachita chinachake chokukwiyitsani inu. Mkuvomereza, mufuula ndi kuyimba belu lanu. Kutulutsa mkwiyo wanu mopepuka kumayambitsa cholinga cha ukali wanu kubwezera. Nthawi zina, ngozi zatulukapo kuchokera kukhalidwe loterolo. Mwachitsanzo, mwamuna wina mu Brooklyn, New York, anaphedwa pamene anali kukangana ponena za malo oimikapo galimoto mu khwalala. Baibulo limaunikira vutolo pamene limati: “Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa.” (Miyambo 29:22) Chiri chanzeru chotani nanga kutsatira uphungu: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse”!​—Aroma 12:17, 18.

Chotero, kutulutsa mkwiyo wathu sikumatithandiza ife mwa mayanjano. Koma kodi chiri chabwino kwa ife mwakuthupi? Unyinji wa asing’anga amaliza kuti sichiri tero. Maphunziro asonyeza kuti anthu amene ali oyedzamira ku kusonyeza mkwiyo ali ndi miyezo yapamwamba kwambiri ya kukwera kwa mwazi. Ena amasimba kuti mkwiyo umatulutsa kuvutika kwa mtima, kupweteka kwa mutu, kamfuno, chizungulire, kapena kuvutika mu kulankhula. Kumbali ina, Mpatsi wa moyo wathu akulongosola: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Yesu anati: “Odala ali akuchita mtendere, chifukwa adzatchedwa ‘ana a Mulungu.’”​—-Mateyu 5:9.

Magwero a Mkwiyo

Magwero ena a mkwiyo ali kuyambidwa kwa kudzimva kwathu kukhala wapamwamba, kusuliza kwaumwini, kutukwana, kuchita ndi anthu mosayenerera, ndi kupsya mtima kosalungamitsidwa. Pamene anthu ali okwiya, iwo amapereka uthenga wogogomezeredwa: “Ukuwopsyeza chimwemwe ndi chisungiko changa! Ukupweteka kunyada kwanga! Iwe ukundichotsera ine ulemu wanga! Ukundiderera!”

Nthawi zina anthu amagwiritsira ntchito mkwiyo monga chophimbira cha chinachake. Mwachitsanzo, mnyamata wa zaka 14 m’mzinda wa New York kawirikawiri anali mu mkhalidwe wokwiya ndipo nthawi zonse anali kuchita ndewu. Ndi thandizo la dokotala, mnyamatayo kenaka anavomereza: “Sindinganene nkomwe kuti, inde, ndikufuna thandizo, ndikufuna wina wake kulankhula naye . . . Mantha ako ali akuti anthu sadzakukonda iwe.” Chotero, chimene iye anafuna kwenikweni chinali chisamaliro ndi chikondi.

Anthu okwatirana mu California anali mu mkhalidwe wamkwiyo nthawi iriyonse pamene mkaziyo anachezera mnzake wamkazi. Mkhalidwe wamkwiyo wa mwamuna wake unayambitsa kuvomereza kofananako mwa mkazi wake. Pagawo lakupereka uphungu, mwamunayo kenaka anauza mkazi wake chinachake chimene anali asanawuuzepo aliyense ndi kale lomwe. Pamene mkazi wake anapita kwina kwake popanda iye, ngakhale kwakanthawi kochepa, mkati mwake anali wa mantha kuti mwinamwake angamusiyiretu iye chifukwa chakuti atate wake anamuthawa iye pamene anali wamng’ono. Pamene mkaziyo anamvetsetsa chifukwa chenicheni cha mkwiyo wa mwamuna wake​—mantha akusiyidwa—​chinamuthandiza iye kuchotsa mkwiyo wake pa iye ndikumutsimikizira iye za chikondi chake.

Chotero, mkwiyo ungakhale chizindikiro. Mu mikhalidwe yoteroyo, mwa kuzindikira magwero ake enieni, tingaphunzire kuchita ndi iwo moyenerera.

[Chithunzi patsamba 4]

Asing’anga ambiri amaliza kuti kutulutsa mkwiyo kuli koipa kaamba ka umoyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena