Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 1 tsamba 5-9
  • Kulankhula Mawu Okondweretsa a Choonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Mawu Okondweretsa a Choonadi
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhala ndi Kalankhulidwe Kabwino Tsiku ndi Tsiku
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kodi Ndinu “Chitsanzo . . . M’kalankhulidwe”?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 1 tsamba 5-9

Phunziro 1

Kulankhula Mawu Okondweretsa a Choonadi

1-3. Kodi chinenero cha anthu chinayamba motani, ndipo chinakula motani?

1 Yehova ali Mlengi wamkulu wa chinenero. Thamo lonse liyenera kupita kwa iye kaamba ka njira yodabwitsa imeneyi ya kulankhulana pakati pa zolengedwa zaluntha. Ndipo popeza kuti zonse zimene Mulungu amachita zili zabwino, tiyenera kukhala otsimikiza kuti mphatso yake ya chinenero kwa munthu pachiyambipo inali imodzi mwa ‘mphatso zangwiro’ zotchulidwa m’Baibulo pa Yakobo 1:17. Ponena za kulankhula kwa munthu, Ludwig Koehlar, katswiri pa mawu, analemba kuti: “Zimene zimachitika polankhula, mmene malingaliro amadzutsira mzimuwo, . . . kukhala mawu, sititha kumvetsa. Kulankhula kwa munthu ndi chinsinsi; ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo yozizwitsa.”

2 Chotero, Adamu polengedwa anapatsidwa mpambo wa mawu. Analinso ndi luso lopanga mawu atsopano. Anapatsidwadi mphatso ya luso la kulankhula bwino mogwira mtima. Sanangokhoza kumveketsa maganizo ake ndi mawu abwino, komanso anali wokhozanso kumvetsa bwino chilankhulidwe. Tikudziŵa zimenezi chifukwa Mulungu analankhula ndi Adamu, akumam’patsa malangizo akutiakuti. Adamunso analankhulana ndi Hava.—Gen. 1:27-30; 2:16-20.

3 Komabe, pamene kuipa kunakula kwambiri padziko lapansi, pa nsanja ya Babele, Mulungu anasokoneza kalankhulidwe ka anthu. (Gen. 11:4-9) N’chifukwa chake lerolino pali zinenero zambiri, ndipo zochuluka ndi malankhulidwe osiyanasiyana. Zina mwa zinenero zimenezo zimalankhulidwa ndi mitundu yaing’ono ndipo zina ndi mamiliyoni ambiri a anthu. Kalankhulidwe ka munthu, mofanana ndi munthu mwiniyo, katalikirana kwambiri ndi ungwiro wake wa poyambirira. Kaŵirikaŵiri munthu wagwiritsa ntchito kulankhula kufalitsira mabodza ndi kupandutsira anthu ena kuwachotsa kwa Mulungu.

4. Kodi luso lathu la kulankhula tiyenera kuligwiritsa ntchito motani?

4 Koma ife, monga atumiki a Yehova tikufuna kuti tigwiritse ntchito luso la kulankhula mwa njira yoyenera. Tili ndi mwayi wolankhula ndi anthu za Mulungu woona ndi kuwauzako za uthenga wake wokondweretsa wonena za moyo wamuyaya m’dziko latsopano lolungama. Buku lino lotchedwa Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase lakonzedwa kuti litithandize kuchita zimenezo bwino lomwe.

5, 6. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti zimene tilankhula zikhale zoona zokhazokha?

5 Kulankhula Mawu a Choonadi. Kugwiritsa ntchito koyenera luso la kulankhula kumafuna kuti chimene tilankhula chikhale choona nthaŵi zonse, chogwirizana kwathunthu ndi Mawu a Mulungu. Bodza silingathe kupereka thanzi lauzimu kwa omvetsera. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analangiza mwanzeru kuti: “Khala nachobe chitsanzo cha mawu olamitsa amene unamva kwa ine.” Chifukwa chiyani? Chifukwa “chitsanzo cha mawu olamitsa” chimenecho chinachokera kwa Mulungu. (2 Tim. 1:13, NW) Paulo anachenjeza kuti ena ‘akalubza dala pachoonadi,’ koma iye anasonyeza kuti chinthu choyenera ndicho ‘kulalikira mawu,’ Mawu a Mulungu. Chotero, tiyenera kutsata Mawu a Mulungu a choonadi, akhale maziko a zonse zimene timalalikira ndi kuphunzitsa.—2 Tim. 4:1-5.

6 Timadziŵa bwino lomwe kuti mawu oyenera olankhulidwa panthaŵi yake akhoza kuika munthu panjira ya ku moyo wosatha kapena kumthandiza kukhalabe panjira ya moyo. (Miy. 18:21; Yak. 5:19, 20) Choncho, kugwiritsa ntchito mawu koyenera n’kofunika kwambiri kwa aliyense wa atumikife, ndipo Sukulu ya Utumiki Wateokalase imagogomeza zimenezo.

7-9. Ndi mawu a mtundu wotani amene kaŵirikaŵiri amakhala ogwira mtima kwambiri?

7 Kusankha Mawu. Ntchito ya mawu ndiyo kupereka malingaliro kuchokera m’maganizo a wolankhula kumka kwa omvetsera ake. Izi zingatheke bwino kokha ngati wolankhulayo asankha mawu opereka malingaliro ake molondola komanso amene omvetsera ake amawamva mosavuta. Kusankha bwino mawu kumakhala kovuta poyamba. Ngakhale Mfumu yanzeru Solomo, mlaliki wa Israyeli, “anatchera khutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri. Mlalikiyo anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mawu oona.” (Mlal. 12:9, 10) Chotero, tifumikira khama la maganizo, kupenda ndi kulingalira bwino kuti tipeze mawu okondweretsa. Vesi 11 la chaputala cha Baibulo chimodzimodzicho, limasonyeza kugwira mtima kwake kwa mawu osankhidwa bwino. “Mawu a anzeru” akuyerekezedwa ndi “zisonga” zimene zimatosera nazo anthu ndi kuwasonkhezera kuyenda pamsewu wa ku moyo.

8 Njira yoyamba yofunika kuphunzira ndiyo kusankha mawu osavuta. Kuti kulankhula kumveke bwino, mawu safunikira kukhala ocholoŵana kapena ovuta. Kunena zoona, kusankha mawu osavuta ndiko kiyi ya kumvetsa ndi kukumbukira kwambiri zinthu. Kodi mawu angafeŵe ndi kukhalabe okopa kuposa mawu oyambirira a Baibulo aŵa: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi”? Simungawaiŵale ayi. N’chimodzimodzinso ndi mawu omaliza a mlaliki wanzeruyo amene anawanena atamaliza kusinkhasinkha kwake konse: “Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlal. 12:13.

9 Tifunikira kupeŵa mawu amene amaphimba choonadi cha Mulungu chomvekera bwino. Sitiyenera ‘kudetsa uphungu ndi mawu opanda nzeru.’ (Yobu 38:2) Pakuti adzamva ndani nazindikira “ngati lipenga lipereka mawu osazindikirika”?—1 Akor. 14:8.

10, 11. Ndi motani mmene Yesu alili chitsanzo chathu polankhula?

10 Ife tonse tingapindule ndi chitsanzo chabwino cha Kristu Yesu. Mawu ake ndi mafanizo ake osavuta onena za zochitika zozoloŵereka pamoyo ankawakhudza kwambiri omvetsera ake. Kumbukirani nkhani imene anaikamba paphiri pafupi ndi Kapernao, yofotokozedwa m’machaputala 5 mpaka 7 a Uthenga Wabwino wa Mateyu. Kodi ali mawu okometsera koma ovuta kumva? Ayi. Kapena mawu ovuta kudziŵa tanthauzo lenileni? Kutalitali. Yesu anasumika maganizo pa kuloŵetsa choonadi m’maganizo mwa anthuwo kuti chisonkhezere mitima yawo. Analidi ndi maganizo a Atate wake, Yehova. Ponena za kulankhula, iye ndiye chitsanzo chabwino koposa kwa atumiki onse a Yehova.

11 Tisachepetse konse mphamvu yaikulu ya mawu omvekera bwino, osavuta komanso osankhidwa bwino a choonadi. Iwo atha kukondweretsa munthu, kum’sonkhezera ndi kum’fulumiza kuchitapo kanthu. Ponena za malankhulidwe a Yesu, nkhani ya pa Luka 4:22 imatiuza kuti omvetserawo “onse anam’chitira iye umboni nazizwa ndi mawu a chisomo akutuluka m’kamwa mwake.” Atumwi akenso anapeza omvetsera ambiri omwe anachita chidwi. Zinalidi choncho mosasamala kanthu kuti Ayuda otchuka a panthaŵiyo anaona atumwiwo kukhala anthu “osaphunzira ndi opulukira.” (Mac. 4:13) Kodi chinawakhozetsa zimenezo n’chiyani? Anaphunzira njira yawo kwa Mbuyawo, Kristu. Kodi zimenezo sizolimbikitsa kwambiri kwa atumiki a Mulungu lerolino, aang’ono ndi achikulire omwe?

12. Kodi makolo angathandize motani ana awo kuphunzira kalankhulidwe kabwino?

12 Makolo angathandize kwambiri ana awo kuti azilankhula bwino. Kulankhula kwabwino kwa tsiku ndi tsiku panyumba kungaphunzitsidwe mwa chitsanzo komanso mwa kulangiza. Mapulinsipulo a Baibulo, amene ayenera kutsogolera kalankhulidwe ka munthu, angathe kukhomerezedwa m’maganizo mwa ana. (Deut. 6:6-9) Mabanja ambiri amakambirana lemba la tsiku la Baibulo kwa mphindi zingapo m’maŵa uliwonse kuchokera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku, ndipo panthaŵi zina amaŵerengera pamodzi Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Kameneka ndiko kaphunzitsidwe kabwino ka banja, kamawonjezera mawu atsopano pa mawu amene akuwadziŵa kale ndi kusonyeza mmene mawuwo anganenedwere mokondweretsa polankhula ndi ena mogwira mtima. Ndiponso mwa njira imeneyi, banja limakhala ndi maganizo a Yehova pankhani zosiyanasiyana, ndipo kalankhulidwe kawo kadzasonyeza zimenezo.

13-16. Kuti aliyense wa ife apindule mokwanira ndi Sukulu ya Utumiki Wateokalase, kodi tiyenera kuchitanji payekhapayekha?

13 Kupita patsogolo mwa kutenga mbali mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Mothandizidwa ndi maphunziro operekedwa m’Buku Lolangiza lino, tonsefe amene moona mtima tikufuna kupita patsogolo mu utumiki tidzathandizidwa kugwiritsa ntchito “mawu okondweretsa . . . mawu oona.” Mosasamala kanthu za msinkhu kapena mlingo wa maphunziro anu akusukulu, ngati mudalira chitsogozo cha Yehova ndi mzimu wake mutha kuwongolera ndi kupita patsogolo mu utumiki wachikristu. Koma n’kofunika kuti inu mwini muikirepo khama. Mukulimbikitsidwa ‘kusamalitsa izi; kukhala mu izi; kuti kukula mtima kwanu [‘kupita kwanu patsogolo,’ NW] kuonekere kwa onse.’—1 Tim. 4:15.

14 Khama lofunikira kwa aliyense wa ife limaphatikizapo kumafika nthaŵi zonse pamisonkhano yonse ya mpingo ya anthu a Yehova, ndi kuonetsetsa kuti tikutsata zimene timaphunzira. Makamaka pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase pamaperekedwa chithandizo kotero kuti mungathe kutsatira chilangizo cha mtumwi Paulo chakuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”—2 Tim. 2:15.

15 Munthu aliyense, mwamuna kapena mkazi, wam’ng’ono kapena wachikulire, amene amafika pamisonkhano ya mpingo angalembetse ndi kupindula ndi sukulu imeneyi. Mutha kulembetsa kaya ndinu wobatizidwa kapena ayi. Amene mwinamwake sanaphunzire kwambiri kusukulu ayenera kukumbukira kuti Mulungu anaoneratu kuti uthenga wa Ufumu sudzalandiridwa ndi ambiri amene ali anzeru mwa thupi, apamwamba, ndi ophunzira kopambana m’zadziko. (1 Akor. 1:26-29) Komanso iye anadziŵiratu kuti ambiri amene ali onyozeka mwa lingaliro la dziko akaulandira ndi kuulalikiranso kwa ena ofuna choonadi. Mwa kulembetsa m’sukulu imeneyi ndi mwa kutsatira mokhulupirika maphunziro ake mudzatsogozedwa ku chidziŵitso chimene chidzakutheketsani kulankhula mawu okondweretsa a choonadi kwa anthu oona mtima. Zimenezi zidzalimbikitsa inuyo komanso aja akumva inu.

16 Koposa zonse, mwa kukhala wophunzira mwakhama maphunziro ameneŵa mudzakhala mukufunafuna, mwa mawu ndi machitidwe, chimene Mfumu Davide wa Israyeli anapempha: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.” (Sal. 19:14) Mkristu aliyense ayenera kukhala ndi chikhumbo champhamvu cha kukhala wokhoza kulankhula bwino, nthaŵi zonse akumagwiritsa ntchito mawu amene adzakondweretsa Mlengi. Sukulu ya Utumiki Wateokalase idzakuthandizani kuchifikira cholinga chimenecho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena