Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
YANG’ANANINSO ulosi wa Baibulo mu Yesaya umene umati: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Onani m’mawu a nkhaniyo kuti awo amene akusula malupanga awo ndiwo “anthu ambiri” amene akuyenda m’njira za Mulungu. (Yesaya 2:2-4) Zimenezi zikutanthauza kuti anthu ameneŵa amalambira Yehova Mulungu ndi kumvera malamulo ake. Kodi iwoŵa ndi ayani?
Ayenera kukhala anthu amitundu yosiyanasiyana amene sanangokana zida zankhondo komanso amene ayesayesa kuzula m’maganizo ndi mumtima mwawo mikhalidwe ndi malingaliro amene amachititsa udani ndi kumenyana. (Aroma 12:2) M’malo mwa kupha mnansi wawo, amamkonda. (Mateyu 22:36-39) Kodi mwamvapo za anthu onga amenewo?
Mwinamwake mwamvapo kuti Mboni za Yehova zili ndi ubale wapadziko lonse ndipo zakana kunyamula zida kuti ziphere ena. Tangoganizani: Ngati munthu aliyense padziko lapansi akanakhala ndi malingaliro amenewo, kodi pulanetili silikanakhala kale malo amtendere ndi chisungiko?
Ndithudi, si aliyense amene amalingalira motero. Zili monga momwe Mfumu Solomo analembera pafupifupi zaka 3,000 zapitazo kuti: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu.”—Mlaliki 4:1.
Chiitano kwa Okonda Mtendere
Kodi padzakhaladi dziko lopanda nkhondo? Inde. Kodi lidzakhalako mwa zoyesayesa za anthu? Ayi. Kodi lidzakhalako mwa kutembenuzira anthu ochuluka ku chipembedzo choona? Ayi. Buku la Baibulo la Salmo limayankha kuti: ‘Idzani, penyani ntchito za Yehova, . . . Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.’—Salmo 46:8, 9.
Kodi Yehova Mulungu adzachita bwanji zimenezo? Buku la Miyambo likuyankha kuti: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa [aja amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu] adzalikhidwa m’dziko, achiŵembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.
Chifukwa chachikulu chimene Mulungu sakuchitirapo kanthu patsopano lino ndi ichi: Akupereka mpata kwa anthu wa kuphunzira njira zake kuti ayende m’njira zake. Mtumwi Petro analemba kuti: “[Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Motero, anthu a Mulungu mopanda dyera amathandiza ena kuphunzira za Yehova. Monga momwe Yesaya ananenera, iwo amafuula kuti: “Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, . . . ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake.”—Yesaya 2:3.
“Masiku Otsiriza”
Lembalo mu Yesaya linaneneratunso kuti kuphunzitsidwa kwa anthu njira za mtendere kudzachitidwa mu “masiku otsiriza.” (Yesaya 2:2) Panopo tikukhala ndi moyo mu nthaŵiyo. Mwachionekere, nkhondo za m’zaka za zana lino zikusonyeza kuti tili mu nthaŵiyo.
Pamene ophunzira a Yesu anamfunsa za chimene chidzazindikiritsa mapeto a dongosolo ili la zinthu, iye ananeneratu za “zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11; Mateyu 24:3) Ananenanso kuti: “Pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musawopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo. Pamenepo ananena nawo, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina.”—Luka 21:9, 10.
Ngakhale kuti pakhala nkhondo kwa zaka zikwi zambiri, zaka za zana lino zokha zaona nkhondo ziŵiri zadziko ndipo, malinga ndi ziŵerengero zina, kwenikweni kwachitika nkhondo zazing’ono mazana ambiri. Kuphedwa kwenikweniko kwa anthu mamiliyoni makumi ambiri mu nkhondo m’zaka za zana lino kuli chinthu chowopsa. Malinga ndi kunena kwa magazini a World Watch, mkati mwa zaka 2,000, zaka za zana la 20 zisanafike, pa avareji, nthaŵi imene inapyola kuti anthu miliyoni imodzi afe mu nkhondo inali zaka 50. M’zaka za zana lino, utali wa nthaŵi, pa avareji, imene inapyola kuti anthu miliyoni imodzi afe mu nkhondo inali chaka chimodzi.
Dziko Lopanda Nkhondo
Nkhondo zowopsa za m’zaka za zana lathu, limodzi ndi zochitika zina zambiri zonenedweratu mu ulosi wa Baibulo, zimasonyeza kuti tili pakhomo padziko latsopano lolinganizidwa ndi Mulungu. Chipwirikiti cha dziko lakale chidzasesedwa ndi kuloŵedwa m’malo ndi “dziko latsopano,” mmene mudzakhalitsa mtendere ndi chilungamo. (2 Petro 3:13) Mawu a Mulungu amati: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:9, 11.
Lerolino kuzungulira dziko lonse lapansi, miyandamiyanda ikufunafuna dziko lopanda nkhondo. Posonyeza kuti Mulungu watsimikiza za kukwaniritsa lonjezo lake la kulinganiza dziko lotero, kalekale mneneri wina wa Mulungu analemba kuti: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.”—Habakuku 2:3.
Chotero, mwanzeru ikani chidaliro chanu mwa Mulungu ndi kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo lake lakuti: “Mulungu yekha adzakhala nawo [anthu ake], Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]
Zimene Baibulo Limalonjeza Kaamba ka Dziko Latsopano Limenelo:
Simudzakhala Upandu, Chiwawa, Kapena Kuipa
“[Mulungu] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.”—Salmo 46:9.
“Ochita zoipa adzadulidwa . . . Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti.”—Salmo 37:9, 10.
Anthu Onse Adzakhala Mwamtendere
“Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—Yesaya 9:6, 7.
Dziko Lonse Lidzakhala Paradaiso
Yesu anati: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.
“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Ubale Wapadziko Lonse
“Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.
Kuuka kwa Akufa Okondedwa
“Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29.
Sipadzakhalanso Matenda, Ukalamba, Kapena Imfa
“Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhala- nso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.