Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jr mutu 7 tsamba 81-91
  • “Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”
  • Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZINTHU ZIMENE ZINGAFOOKETSE ATUMIKI A MULUNGU
  • KODI INUYO MUDZATSITSIMUTSA ANTHU OLEFUKA?
  • “Sindingathe Kukhala Chete”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Yehova Anauza Yeremiya Kuti Azilalikira
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
jr mutu 7 tsamba 81-91

Mutu 7

“Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”

1. Kodi inuyo mukufunitsitsa kudzalandira madalitso ati m’dziko lapansi latsopano?

KODI mukamva mawu akuti “dziko latsopano” mumaganizira ena mwa madalitso ooneka amene Mulungu watilonjeza? Mwina mungaganizire zoti mudzakhala ndi chakudya chopatsa thanzi, thupi lanu lidzakhala langwiro, mudzakhala mwamtendere ndi nyama, kapenanso mudzakhala ndi nyumba zabwino. Mwinanso mungatchule mavesi a m’Baibulo amene amakuthandizani kuti muziyembekezera zinthu zimenezi. Koma palinso madalitso ena ofunika kwambiri amene Mulungu adzapereke kwa atumiki ake. Iwo adzakhala ndi moyo wabwino wauzimu komanso sazidzavutika m’maganizo. Popanda madalitso amenewa, anthu sangakhale mosangalala ngakhale atakhala ndi chilichonse.

2, 3. Kodi mabuku amene Yeremiya analemba akutithandiza kuyembekezera madalitso apadera ati?

2 Pamene Mulungu ankauza Yeremiya kuti alosere zoti Ayuda adzabwerera kwawo kuchokera ku Babulo, Mulunguyo ananenanso kuti Ayudawo adzasangalala kwambiri. Baibulo limati: ‘Mudzanyamula maseche ndi kupita kukavina pamodzi ndi anthu amene akuseka.’ (Werengani Yeremiya 30:18, 19; 31:4, 12-14.) Mulungu ananenanso mawu ena amene angakhale olimbikitsa kwa inu. Iye anati: “Ndidzatsitsimutsa wolefuka ndipo ndidzalimbitsa wofooka aliyense.”—Yer. 31:25.

3 Apatu Mulungu analonjeza Ayudawo zinthu zosangalatsa kwambiri. Yehova ananena kuti adzatsitsimutsa wolefuka kapena kuti kulimbikitsa munthu aliyense wofooka. Izi zinachitikadi chifukwa Mulungu amachita zimene walonjeza. Mabuku amene Yeremiya analemba amatitsimikizira kuti nafenso Mulungu adzatitsitsimutsa. Kuwonjezera pamenepo, mabukuwa amatithandiza kuona kuti ngakhale panopa Mulungu angathe kutilimbikitsa kuti tisafooke. Komanso mabuku amenewa akutisonyeza mmene tingalimbikitsire olefuka ndi kuwatsitsimutsa.

4. N’chifukwa chiyani tingamvetse tikaganizira zoti Yeremiya ankakhumudwa kapena kuvutika maganizo?

4 Lonjezo limeneli linali lolimbikitsa kwambiri kwa Yeremiya, ndipo ifenso lingatilimbikitse. N’chifukwa chiyani tikutero? Kumbukirani mfundo imene yatchulidwa m’Mutu 1 wa buku lino yakuti Yeremiya anali “munthu monga ife tomwe” mofanana ndi Eliya. (Yak. 5:17) Ndiyeno ganizirani zina mwa zifukwa zimene zinkachititsa kuti nthawi zina Yeremiya azikhumudwa kapena kuvutika maganizo kumene. Ganiziraninso mmene inuyo mukanamvera zikanakhala kuti mwakumana ndi mavuto amenewo komanso chifukwa chake mukanatha kufooka ndi mavutowo.—Aroma 15:4.

5. Kodi n’chiyani chimene chiyenera kuti chinkafooketsa kwambiri Yeremiya?

5 N’kutheka kuti ena mwa anthu amene ankafooketsa Yeremiya anali a mumzinda wakwawo. Yeremiya anakulira ku Anatoti, mzinda wa Alevi umene unali pa mtunda wa makilomita ochepa kumpoto chakum’mawa kwa Yerusalemu. Ku Anatoti kuyenera kuti kunali anthu amene mneneriyu ankadziwana nawo komanso mwina kunali achibale ake. Yesu ananena kuti mneneri salemekezedwa kwawo, ndipo zinalidi choncho ndi Yeremiya. (Yoh. 4:44) Anthu a mumzindawo analibe chidwi ndi zimene Yeremiya ankanena komanso ankamuchitira chipongwe. Koma si zokhazo, chifukwa nthawi inayake Mulungu ananena kuti ‘anthu a ku Anatoti ankafuna moyo wa Yeremiya.’ Mwaukali, anthuwo ananena kuti: “Usanenere m’dzina la Yehova, ngati ukufuna kuti tisakuphe.” Amenewatu anali mawu oopseza kwambiri, ndipo ankachokera kwa anthu akwawo komanso mwina kwa achibale ake, amene ankayenera kukhala kumbali yake.—Yer. 1:1; 11:21.

Chithunzi patsamba 83

6. Kodi kuganizira nkhani ya Yeremiya ndi “anthu a ku Anatoti” kungakuthandizeni bwanji ngati anzanu akuntchito kapena anthu ena akukutsutsani?

6 Kuganizira zimene Yehova anachitira Yeremiya kungakulimbikitseni ngati anthu oyandikana nawo nyumba, anzanu akusukulu, akuntchito kapena achibale ena akukukakamizani kuti musiye kutumikira Mulungu. M’nthawi ya Yeremiya, Mulungu ananena kuti ‘adzapereka chilango’ kwa anthu a ku Anatoti amene ankatsutsa mneneri wakeyu. (Werengani Yeremiya 11:22, 23.) Mawu olimbikitsa a Mulunguwo ayenera kuti anathandiza kwambiri Yeremiya kuti asafooke pamene anthu akwawo ankamutsutsa. Patapita nthawi, Mulungu anabweretsadi “tsoka pa anthu a ku Anatoti.” Inunso dziwani kuti Yehova akuona zimene otsutsa akukuchitirani ndipo adzawapatsa chilango. (Sal. 11:4; 66:7) Ngati ‘mutapitiriza kuchita’ zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kuchita zinthu zoyenera, mungathandize anthu ena otsutsa kuti tsoka limene likubweralo lisadzawagwere.—1 Tim. 4:16.

M’buku la Yeremiya, n’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu amakhudzidwa ndi mmene anthu ake akumvera mumtima, ndipo zimenezi ziyenera kuti zinathandiza bwanji mneneriyu?

ZINTHU ZIMENE ZINGAFOOKETSE ATUMIKI A MULUNGU

7, 8. Kodi Yeremiya anazunzidwa m’njira ziti, ndipo zimenezi zinamukhudza bwanji?

7 Anthu akwawo kwa Yeremiya sankangoopseza mneneriyu ndi mawu okha. Chitsanzo chimodzi ndi zimene anachita munthu wina wotchuka mu Yerusalemu dzina lake Pasuri, amenenso anali wansembe.a Atamva ulosi wochokera kwa Mulungu, “Pasuri anamenya mneneri Yeremiya ndi kumuika m’matangadza.” (Yer. 20:1, 2) Mawu amenewa ayenera kuti akutanthauza zambiri, osati kungom’menya mbama. Anthu ena akawerenga lembali amaona kuti Pasuri analamula kuti Yeremiya amenyedwe kapena akwapulidwe zikoti 40. (Deut. 25:3) Pamene Yeremiya ankavutika ndi ululu, n’kutheka kuti anthu ankamukuwiza ndi kumunyoza ngakhalenso kumulavulira. Koma si zokhazo. Pasuri analamula kuti Yeremiya aikidwe “m’matangadza” usiku wonse. Mawu achiheberi amene anagwiritsidwa ntchito ponena za kuikidwa m’matangadza, amasonyeza kuti Yeremiya anakhala mopindika. Zoonadi, anthuwo anachitira Yeremiya nkhanza kwambiri pomuika m’matangadza usiku wonse ndipo iye ankamva ululu kwambiri.

8 Kodi zimenezi zinamukhudza bwanji Yeremiya? Iye anauza Mulungu kuti: “Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse.” (Yer. 20:3-7) Nthawi ina iye anafika poganiza zosiya kunenera m’dzina la Mulungu. Koma inu mukudziwa kuti Yeremiya sakanasiya kunenera, ndipo sanasiyedi. Iye sanachite zimenezi chifukwa chakuti uthenga umene Mulungu anam’patsa kuti akalengeze unali “ngati moto woyaka umene autsekera m’mafupa a [Yeremiya],” ndipo ankafunika kulengeza uthengawo poimira Yehova.—Werengani Yeremiya 20:8, 9.

Chithunzi pamasamba 84, 85

9. Kodi kuganizira zimene zinachitikira Yeremiya n’kothandiza bwanji kwa ife?

9 Nkhani imeneyi ingatithandize ngati titayamba kunyozedwa kwambiri ndi anthu amene tikuwadziwa, monga achibale athu, anthu oyandikana nawo nyumba, anzathu akuntchito kapenanso akusukulu. Tisamadabwe ngati nthawi zina timafooka chifukwa chotsutsidwa mwanjira imeneyi. Zimenezi zingachitikenso ngati tikuzunzidwa chifukwa choti tikuchita zinthu zogwirizana ndi kulambira koona. Yeremiya, amene analinso munthu wopanda ungwiro, anakumana ndi mavuto amenewa, ndipotu mmene iye ankamvera ndi mmenenso ife timamvera. Koma tisaiwale kuti Mulungu anathandiza Yeremiya kuti ayambirenso kukhala wolimba mtima ndiponso wosangalala. Yeremiya sanakhale wofooka mpaka kalekale, ndipo ifenso sitiyenera kutero.—2 Akor. 4:16-18.

10. Kodi Baibulo likusonyeza kuti Yeremiya ankamva bwanji mumtima mwake nthawi zina?

10 Nthawi zina Yeremiya ankasinthasintha kwambiri mmene ankamvera mumtima mwake. Kodi mwina inunso nthawi zina zimenezi zimakuchitikirani? Kodi mumaona kuti ndinu wosangalala koma kenako n’kukhala ndi nkhawa komanso chisoni? Nayenso Yeremiya ankakhala wosangalala nthawi zina, ndipo tikuona zimenezi pa Yeremiya 20:12, 13. (Werengani.) Pambuyo pozunzidwa kwambiri ndi Pasuri, Yeremiya anasangalala kwambiri chifukwa anali ngati munthu wosauka amene walanditsidwa “m’manja mwa anthu ochita zoipa.” Mwina inunso nthawi zina mumakhala wosangalala moti mumafuna kutamanda Yehova ndiponso kumuimbira nyimbo. Zimenezi zingachitike pamene mukuona kuti mwalanditsidwa kapena ngati pachitika zinazake zosangalatsa m’moyo wanu kapena mu utumiki wanu wachikhristu. Kunena zoona, zimenezi zimakhala zosangalatsa kwambiri.—Mac. 16:25, 26.

Chithunzi patsamba 86

Kodi tingamve bwanji mumtima chifukwa chotsutsidwa kapena kunyozedwa?

11. Ngati tili ndi vuto loti timasinthasintha mmene tikumvera mumtima mwathu, kodi tizikumbukira chiyani chokhudza Yeremiya?

11 Komabe, popeza ndife opanda ungwiro, timasinthasintha mmene tikumvera mumtima mwathu, ngati mmene zinalili ndi Yeremiya. Pambuyo ponena mawu akuti “imbirani Yehova,” Yeremiya anasintha n’kuyamba kumva chisoni kwambiri ndipo mwina ankagwetsa misozi. (Werengani Yeremiya 20:14-16.) Iye anataya mtima kwambiri moti ankaona kuti zikanakhala bwino akanapanda kubadwa. Ali wokhumudwa choncho, ananena kuti munthu amene analengeza za kubadwa kwake anali womvetsa chisoni ngati mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Choncho tingafunse kuti: Kodi Yeremiya anapitiriza kukhala wokhumudwa? Kodi iye anataya mtima n’kumangoona kuti adzakhala wokhumudwa mpaka kalekale? Ayi sanatero. Zikuoneka kuti iye anayesetsa kuti asakhalenso wokhumudwa ndipo zimenezi zinatheka. Taonani zimene buku la Yeremiya likunena kenako. Pasuri wina amene anali kalonga, anapita kwa Yeremiya atatumidwa ndi Mfumu Zedekiya kuti akamufunse zimene ziwachitikire, chifukwa Ababulo anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu. Yeremiya sanachite mantha, koma analimba mtima n’kulengeza chiweruzo cha Yehova komanso zimene ziwachitikire. (Yer. 21:1-7) Apa n’zoonekeratu kuti Yeremiya anapitiriza kugwira ntchito yake mwakhama monga mneneri.

12, 13. Kodi tingachite chiyani kuti tichepetse vuto lokhumudwa?

12 Atumiki ena a Mulungu masiku ano amasinthasinthanso mmene akumvera mumtima mwawo. Nthawi zina zimenezi zingachitike chifukwa chakuti thupi lawo silikugwira bwino ntchito ndipo dokotala wodziwa bwino ntchito yake angawauze njira zimene zingawathandize kuchepetsa vutolo. (Luka 5:31) Koma ambiri a ife nthawi zina timatha kukhumudwa kapena kusangalala, ndipo zimenezi sizikhala zopitirira muyezo kapena zachilendo. Komanso nthawi zambiri timakhumudwa chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro. Tingakhumudwe chifukwa chotopa kapena ngati munthu amene timam’konda wamwalira. Zimenezi zikatichitikira, tizikumbukira kuti Yeremiya nayenso ankakhumudwa, koma anapitirizabe kukondedwa ndi Mulungu. Kuti tichepetse kukhumudwa, tingafunike kusintha zina ndi zina kuti tizikhala ndi nthawi yokwanira yopuma. Kapena tingafunike kudzipatsa nthawi yokwanira kuti tiiwale imfa ya munthu amene tinkamukonda. Komabe, tiyenera kupitiriza kuchita zinthu zonse zauzimu monga kupezeka pamisonkhano yachikhristu. Zimenezi n’zofunika kwambiri kuti tikhalebe akhama komanso osangalala potumikira Mulungu.—Mat. 5:3; Aroma 12:10-12.

13 Kaya mumakhumudwa mwa apo ndi apo kapena ndi vuto limene limakuchitikirani kawirikawiri, zimene zinachitikira Yeremiya zingakuthandizeni. Monga taonera, nthawi zina Yeremiya ankakhumudwa kwambiri. Koma popeza iye ankakonda Mulungu, sanalole kuti kukhumudwako kumulepheretse kumutumikira mokhulupirika. Pamene adani ake ankamuchitira zinthu zoipa ngakhale kuti iye ankawachitira zinthu zabwino, Yeremiya anadalira ndi kukhulupirira Yehova. (Yer. 18:19, 20, 23) Choncho yesetsani ndi mtima wonse kutsanzira Yeremiya.—Maliro 3:55-57.

Ngati nthawi zina mumakhala wokhumudwa kapena wosasangalala, kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene tikuphunzira m’buku la Yeremiya?

KODI INUYO MUDZATSITSIMUTSA ANTHU OLEFUKA?

14. Kodi kwenikweni Yeremiya analimbikitsidwa ndi ndani?

14 Tingachite bwino kuganizira mmene Yeremiya analimbikitsidwira komanso mmene iye analimbikitsira ena amene anali ‘olefuka.’ (Yer. 31:25) Mneneriyu kwenikweni analimbikitsidwa ndi Yehova. Tangoganizani mmene mungalimbikitsidwire mutamva Yehova akukuuzani kuti: “Ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri . . . Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana, pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’” (Yer. 1:18, 19) M’pomveka kuti Yeremiya anam’tchula Yehova kuti “mphamvu yanga, malo anga achitetezo ndi malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.”—Yer. 16:19.

15, 16. Kodi tikaona mmene Yehova analimbikitsira Yeremiya, tikuphunzirapo chiyani pa zimene ifeyo tingachite polimbikitsa ena?

15 N’zochititsa chidwi kuti Yehova anauza Yeremiya kuti: “Ine ndili ndi iwe.” Kodi pamenepa mukuona zimene mungachite ngati munthu wina amene mukum’dziwa akufunika kulimbikitsidwa? Kungodziwa kuti m’bale kapena mlongo wathu wachikhristu, kapena wachibale wina akufunika kulimbikitsidwa si kokwanira. Kawirikawiri njira yothandiza kwambiri ndi kungokhala limodzi ndi munthu amene akufunika kulimbikitsidwayo. Ndipo izi n’zimene Mulungu anachita ndi Yeremiya. Ndiyeno pakadutsa kanthawi mungamuuze mawu olimbikitsa, koma musalankhule zinthu zambirimbiri. Mawu ochepa amene asankhidwa bwino angakhale othandiza kwambiri chifukwa angamulimbikitse. Simukufunika kunena mawu ogometsa, koma mungagwiritse ntchito mawu osavuta osonyeza kuti mukudera nkhawa Mkhristu mnzanuyo komanso mumamukonda. Mawu otero angamulimbikitse kwambiri.—Werengani Miyambo 25:11.

16 Yeremiya anapempha kuti: “Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga. Ndikumbukireni ndipo mutembenuke ndi kundiyang’ana.” Ndiyeno chinachitika n’chiyani? Mneneriyu anafotokoza kuti: “Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya. Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga.” (Yer. 15:15, 16) Mofanana ndi Yeremiya, munthu amene mukufuna kumulimbikitsayo angafunikenso kumusonyeza chifundo. N’zoona kuti mawu amene munganene sangafanane ndi a Yehova. Komabe, pa zimene mukunenazo mungaphatikizepo mawu a Mulungu. Mfundo za m’Baibulo zimene munganene mochokera pansi pa mtima zingasangalatse kwambiri munthu wokhumudwayo.—Werengani Yeremiya 17:7, 8.

17. Kodi mmene Yeremiya anachitira zinthu ndi Zedekiya komanso Yohanani zikutiphunzitsa mfundo iti yofunika?

17 Onani kuti Yeremiya sanangolimbikitsidwa ndi Mulungu, koma iyenso analimbikitsa ena. Kodi anachita bwanji zimenezi? Pa nthawi ina, Mfumu Zedekiya anauza Yeremiya kuti ankaopa Ayuda amene anagwirizana ndi Ababulo. Mneneriyu ananena mawu olimbikitsa, ndipo anapempha mfumuyi kuti imvere Yehova kuti zinthu ziiyendere bwino. (Yer. 38:19, 20) Yerusalemu atawonongedwa, mumzindawu munangotsala Ayuda ochepa. Pa nthawiyi, mkulu wa asilikali wa Ayudawo dzina lake Yohanani anaganiza zotenga anthuwo kuti apite nawo ku Iguputo. Koma asanachite zimenezi anafunsa kaye malangizo kwa Yeremiya. Mneneriyu anamvetsera zimene Yohanani anafotokoza ndipo kenako anapemphera kwa Yehova. Pambuyo pake, Yeremiya anapereka yankho lolimbikitsa lochokera kwa Yehova, ndipo ananena kuti ngati anthuwo atatsatira malangizo a Mulungu oti akhalebe m’dzikolo, zinthu ziwayendera bwino. (Yer. 42:1-12) Nthawi ziwiri zonsezi, Yeremiya ankamvetsera kaye mwatcheru asananene chilichonse. Izi zikusonyeza kuti kumvetsera n’kofunika kwambiri pamene tikulimbikitsa ena. Muyenera kulola munthu wokhumudwayo kuti afotokoze zakukhosi kwake, ndipo muyenera kumvetsera. Pa nthawi yoyenera mungalankhule mawu olimbikitsa. Izi sizikutanthauza kuti Mulungu adzakuuzani mozizwitsa zoti munene polimbikitsa ena, komabe munganene mfundo zolimbikitsa komanso zopatsa chiyembekezo, zochokera m’Mawu ake.—Yer. 31:7-14.

Chithunzi patsamba 91

18, 19. Kodi m’nkhani ya Arekabu ndi ya Ebedi-meleki tikupezamo zitsanzo zotani za mmene tingalimbikitsire ena?

18 Zedekiya komanso Yohanani sanamvere malangizo olimbikitsa amene Yeremiya anawapatsa, ndipo masiku ano zingaonekenso kuti anthu ena sakumvera malangizo anu. Koma zimenezo zisakufooketseni. Anthu ena anamvera malangizo olimbikitsa amene Yeremiya anawapatsa, ndipo n’kutheka kuti ambiri adzamveranso malangizo anu. Ganizirani chitsanzo cha Arekabu, amene anali gulu la anthu a mtundu wachikeni, ndipo ankagwirizana ndi Ayuda kwa zaka zambiri. Kholo lawo Yehonadabu anawapatsa malamulo oti azitsatira. Limodzi mwa malamulo amenewo linali lakuti iwo asamamwe vinyo chifukwa anali alendo pakati pa Ayudawo. Pamene Ababulo ankaukira mzinda wa Yerusalemu, Yeremiya anatenga Arekabuwo n’kupita nawo m’chipinda chodyera chapakachisi. Potsatira malangizo a Mulungu, Yeremiya anatenga vinyo n’kuwapatsa. Mosiyana ndi Aisiraeli amene sanamvere Mulungu, Arekabuwo anamvera kholo lawo lija komanso anasonyeza kuti ankalilemekeza. Iwo anachita zimenezi pokana kumwa vinyoyo. (Yer. 35:3-10) Yeremiya anawauza mawu oyamikira ochokera kwa Yehova komanso malonjezo a zimene adzawachitire m’tsogolo. (Werengani Yeremiya 35:14, 17-19.) Inuyo mungatengere chitsanzo chimenechi polimbikitsa ena. Ngati n’zotheka, muziyamikira ena mochokera pansi pamtima.

19 Yeremiya nayenso anachita zimenezi kwa Ebedi-meleki, munthu wochokera ku Itiyopiya amene zikuoneka kuti anali nduna ya panyumba ya Mfumu Zedekiya. Mopanda chilungamo, akalonga a ku Yuda anaponya Yeremiya m’chitsime cha matope okhaokha n’kumusiya kuti afere momwemo. Koma Ebedi-meleki anapempha Mfumu Zedekiya kuti amulole kukapulumutsa mneneriyu, ndipo anamuloladi. Munthu wochokera kudziko linayu anachitadi zimenezi, ngakhale kuti anthu akanatha kumuchitira zankhanza. (Yer. 38:7-13) Zimene Ebedi-meleki anachitazi zinapangitsa kuti akalonga a ku Yudawo adane naye, choncho iye ayenera kuti ankada nkhawa chifukwa sankadziwa zimene zingamuchitikire. Yeremiya sanangokhala chete n’kumaganiza kuti pakapita nthawi nkhawa za Ebedi-melekizo zitha. Iye anauza Ebedi-meleki mawu olimbikitsa onena za madalitso amene Mulungu adzam’patse m’tsogolo.—Yer. 39:15-18.

20. Kodi tikhale ndi mtima wofuna kuwachitira chiyani abale athu, ana ndi achikulire omwe?

20 Zoonadi, tikamawerenga buku la Yeremiya, timapeza zitsanzo zabwino kwambiri zosonyeza mmene ifeyo tingachitire zimene mtumwi Paulo analimbikitsa abale a ku Tesalonika kuti azichita. Iye anati: “Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana . . . Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.”—1 Ates. 5:11, 28.

Kodi mwaphunzira mfundo ziti m’buku la Yeremiya zimene mukufuna kuzigwiritsa ntchito pamene mukuyesetsa kulimbikitsa anthu olefuka?

a Pa nthawi ya ulamuliro wa Zedekiya, kunali munthu winanso wotchedwa Pasuri amene anali kalonga. Pasuri ameneyu ndi yemwe anapempha mfumu kuti Yeremiya aphedwe.—Yer. 38:1-5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena