Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • dp mutu 1 tsamba 4-11
  • Buku la Danieli ndi Inu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Buku la Danieli ndi Inu
  • Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • DANIELI—BUKU LAMAKEDZANA KOMA LA NTHAŴI ZAMAKONO
  • DANIELI—WOKONDEKA KWAMBIRI KWA MULUNGU
  • KULENGEZA MAUTHENGA A MULUNGU
  • MITUNDU IŴIRI YA NKHANI, UTHENGA UMODZI
  • Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Danieli
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Danieli—Buku Limene Likuzengedwa Mlandu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Alimbikitsidwa ndi Mthenga Wochokera kwa Mulungu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Samalani Ulosi wa Danieli!
dp mutu 1 tsamba 4-11

Mutu 1

Buku la Danieli ndi Inu

1, 2. (a) Kodi zina mwa zochitika zodabwitsa zosimbidwa m’buku la Danieli la m’Baibulo n’zotani? (b) M’nthaŵi zathu zino, pamabuka mafunso otani ponena za buku la Danieli?

MFUMU yamphamvu ikufuna kunyonga amuna ake anzeru chifukwa alephera kuvumbula ndi kumasulira loto lake lothetsa nzeru. Anyamata atatu omwe akana kulambira fano lalikulu ndi lalitali kwambiri awaponya m’ng’anjo ya moto imene aisonkheza moto wake moŵirikiza koopsa, komabe apulumuka. Phwando la madyerero lili m’kati, mazanamazana a anthu akuona dzanja limene likulemba mawu ozizwitsa pakhoma m’nyumba ya mfumu. Anthu oipa achiwembu achititsa kuti mwamuna wina wokalamba aponyedwe m’dzenje la mikango, koma iye atulukamo wopanda bala lililonse. Mneneri wa Mulungu aona zilombo zinayi m’masomphenya, tanthauzo lake likumafikira m’zaka zikwizikwi zam’tsogolo.

2 Izi ndi zina mwa nkhani zopezeka m’buku la Danieli la m’Baibulo. Kodi n’zofunikadi kuziganizira? Kodi buku lamakedzana limenelo lingakhale ndi kufunika kwanji m’masiku athu ano? N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala za zinthu zimene zinachitika kalekale zaka pafupifupi 2,600 zapitazo?

DANIELI—BUKU LAMAKEDZANA KOMA LA NTHAŴI ZAMAKONO

3, 4. N’chifukwa chiyani anthu ambiri akuda nkhaŵa, ndipo ayeneradi kutero, ponena za tsogolo la mtundu wa anthu?

3 Mbali yaikulu ya buku la Danieli imanena za nkhani ya ulamuliro wa dziko lonse, nkhani yofunika kwambiri lerolino. Pafupifupi wina aliyense angavomereze kuti tikukhala m’nthaŵi zovuta kwambiri. Tsiku ndi tsiku, timamva malipoti omvetsa chisoni kwambiri otikumbutsa kuti mtundu wa anthu ukumiriramirira m’chithaphwi cha mavuto othetsa nzeru, tingatero kunena kwake—ndipo zimenezo zikuchitika mosasamala kanthu kuti pakhala kupita patsogolo kodabwitsa m’zasayansi ndi luso lopanga zinthu.

4 Taganizirani izi: Munthu wakhoza kukayenda pamwezi, koma m’madera ambiri sangathe kuyenda mopanda mantha m’misewu ya dziko lapansi, mudzi wake weniweni. Atha kukongoletsa nyumba ndi zabwino zonse zamakono, koma akulephera kusungitsa mtendere m’mabanja. Ndipo wadzetsa nyengo ya chidziŵitso chankhaninkhani, koma satha kuphunzitsa anthu kukhalira limodzi mwamtendere. Hugh Thomas, polofesa wa mbiri yakale, nthaŵi ina analemba kuti: “Kuchuluka kwa chidziŵitso ndi maphunziro kwaphunzitsa anthu zochepa kwambiri ponena za kudziletsa ndi nzeru ya kukhalira limodzi ndi anthu anzawo.”

5. Kwakukulukulu, kodi ulamuliro wa munthu wakhala ndi zotsatirapo zotani?

5 Poyesa kukhazikitsa bata pang’ono pakati pawo, anthu asonkhana m’magulumagulu napanga maboma a mitundumitundu. Ngakhale ndi choncho, palibe n’limodzi lomwe limene lapatukapo pa choonadi cha mawu a Mfumu Solomo akuti: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 4:1; 8:9) N’zoona kuti olamulira ena akhala ndi zolinga zabwino. Komabe, palibe mfumu iliyonse, pulezidenti, kapena wolamulira wopondereza ena amene angathe kuchotsa matenda ndi imfa. Palibe munthu aliyense amene angabwezeretse dziko lathuli ku Paradaiso amene Mulungu anakhazikitsa poyamba.

6. N’chifukwa chiyani Yehova safunikira chivomerezo cha olamulira aumunthu pofuna kuchita chifuniro chake?

6 Koma kunena za Mlengiyo, iye ali wofunitsitsa komanso wokhoza kuchita zimenezo. Iye safunikira chilolezo cha maboma a anthu kuti achite cholinga chake, pakuti kwa iyeyo “amitundu akunga dontho la m’mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’muyeso.” (Yesaya 40:15) Inde, Yehova ndi Mfumu Yolamulira chilengedwe chonse. Ndicho chifukwa chake ali ndi ulamuliro waukulu kwambiri kupambana wa maboma a anthu. Uli Ufumu wa Mulungu umene udzaloŵa m’malo mwa ulamuliro wonse wa anthu, nudzakhala dalitso lamuyaya kwa mtundu wa anthu. Mwinamwake kulibe kwina kulikonse kumene mfundo imeneyi yamveketsedwa bwino lomwe koposa m’buku la Danieli la m’Baibulo.

DANIELI—WOKONDEKA KWAMBIRI KWA MULUNGU

7. Kodi Danieli anali yani, nanga Yehova anamuona motani?

7 Yehova Mulungu anam’konda kwambiri Danieli, amene anatumikira monga mneneri wake kwa zaka zambiri. Ndithudi, ngakhale mngelo wa Mulungu anatcha Danieli ‘wokondedwa kwambiri.’ (Danieli 9:23) Mawu oyambirira achihebri omasuliridwa kuti ‘wokondedwa kwambiri’ akhoza kutanthauzanso “wokondedwa kwakukulu,” “woŵerengeredwa kwambiri,” kapenanso “wapamtima.” Danieli analidi wapadera m’maso mwa Mulungu.

8. Kodi zinachitika motani kuti Danieli apezeke ku Babulo?

8 Tiyeni mwachidule tilingalire za mikhalidwe yapadera ya mneneri wokondeka ameneyu. Mu 618 B.C.E., Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo, anamangira misasa ya nkhondo Yerusalemu. (Danieli 1:1) Posapita nthaŵi, achinyamata ena achiyuda ophunzira kwambiri anagwidwa natengeredwa ku dziko laukaidi ku Babulo. Pakati pawo panali Danieli. Panthaŵiyo, iyeyo mwinamwake anali ndi zaka pakati pa 13 ndi 19.

9. Kodi ndi maphunziro otani amene anapatsidwa kwa Danieli limodzi ndi Ahebri anzake?

9 Danieli ndi anzakewo Hananiya, Misayeli, ndi Azariya anali pakati pa Ahebri osankhidwa kuti alandire maphunziro a zaka zitatu a “m’mabuku, ndi manenedwe a Akasidi.” (Danieli 1:3, 4) Akatswiri ena amaphunziro amanena kuti maphunziro amenewo sanali chabe kuphunzira chinenero. Mwachitsanzo, Polofesa C. F. Keil ananena kuti: “Danieli ndi anzakewo anaphunzitsidwa nzeru za ansembe a Akasidi ndi amuna ophunzira, zimene anali kuziphunzitsa m’sukulu za m’Babulo.” Choncho Danieli ndi anzakewo anaphunzitsidwa makamaka kuti agwire ntchito za boma.

10, 11. N’zovuta zotani zimene Danieli limodzi ndi anzakewo anakumana nazo, ndipo Yehova anawathandiza motani?

10 Kumeneku kunali kusintha kwa zinthu kwakukuludi pamoyo wa Danieli limodzi ndi anzake aja! Ku dziko la Yuda amakhala pakati pa alambiri a Yehova okhaokha. Koma tsopano anazingidwa ndi anthu olambira milungu yonama ndi milungu yachikazi. Ngakhale ndi choncho, anyamatawo Danieli, Hananiya, Misayeli, ndi Azariya sanachite mantha. Anatsimikiza mtima kuima nji pakulambira koona, poyang’anizana ndi mkhalidwe woyesa chikhulupiriro umenewu.

11 Zimenezo sizinali zopepuka ayi. Mfumu Nebukadinezara anali mlambiri wokangalika wa Maduki, mulungu wamkulu wa Babulo. Zofuna za mfumuyo nthaŵi zina zinali zosavomerezeka m’pang’ono pomwe kwa mlambiri wa Yehova. (Mwachitsanzo, onani Danieli 3:1-7.) Komabe, chitsogozo cha Yehova chosalepheracho nthaŵi zonse chinali pa Danieli limodzi ndi anzakewo. M’kati mwa maphunziro awo a zaka zitatu, Mulungu anawadalitsa ndi “luntha la m’mabuku alionse, ndi nzeru.” Kuwonjezera pamenepo, Danieli anapatsidwanso luntha lozindikira matanthauzo a masomphenya ndi maloto. Nthaŵi ina pamene mfumu inadzapenda anyamata anayiwo, inapeza kuti “anaposa kuŵirikiza nthaŵi khumi ansembe amatsenga ndi alauli onse a mu ufumu wake wonse.”—Danieli 1:17, 20, NW.

KULENGEZA MAUTHENGA A MULUNGU

12. Kodi Danieli anali ndi ntchito yapadera yotani?

12 M’zaka zonsezo zimene anakhala m’Babulo, Danieli anatumikira monga mthenga wa Mulungu kwa Mafumu ngati Nebukadinezara ndi Belisazara. Ntchito ya Danieli inali yovuta kwenikweni. Yehova anali atalola Nebukadinezara kuwononga Yerusalemu, akumam’gwiritsa ntchito ngati chida Chake. Koma m’kupita kwa nthaŵi, Babulonso akawonongedwa. Ndithudi, buku la Danieli limakweza Yehova Mulungu monga Wam’mwambamwamba komanso monga Wolamulira mu “ufumu wa anthu.”—Danieli 4:17.

13, 14. Kodi chinachitika kwa Danieli n’chiyani Babulo atagwa?

13 Danieli anapitiriza kutumikira m’bwalo la mfumu kwa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mpaka pamene Babulo anagwa. Iye anaona ndi maso ake Ayuda ambiri akubwerera ku dziko lakwawo mu 537 B.C.E., ndipo Baibulo silinena kuti iye anatsagana nawo. Iye anali wokangalikabe mpaka m’chaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Koresi, amene anayambitsa Ufumu wa Perisiya. Pofika nthaŵiyo, Danieli ayenera kuti anali atayandikira zaka 100 zakubadwa!

14 Pambuyo pakuti Babulo wagwa, Danieli analemba zochitika zofunika kwambiri pamoyo wake. Zolemba zakezo tsopano zili mbali yofunika kwambiri ya Baibulo Loyera ndipo zimatchedwa buku la Danieli. Koma n’chifukwa chiyani tisamala za m’buku lakalekale limeneli?

MITUNDU IŴIRI YA NKHANI, UTHENGA UMODZI

15. (a) Kodi ndi mitundu iŵiri yotani ya nkhani imene ili m’buku la Danieli la m’Baibulo? (b) Kodi magawo osimba zochitika a m’buku la Danieli angatipindulitse motani?

15 Buku lapaderalo la Danieli lili ndi mitundu iŵiri yosiyana kotheratu ya nkhani—zosimba zochitika, ndi zonenera maulosi. Mbali zonse ziŵirizo za buku la Danieli zikhoza kulimbikitsa chikhulupiriro chathu. Motani? Magawo osimba zochitika—pokhala ena mwa omvekera bwino kwambri m’Baibulo—amatisonyeza kuti Yehova Mulungu adzadalitsa ndi kusamalira anthu okhulupirikabe kwa iye. Danieli limodzi ndi anzake atatu aja anachirimika osagwedera poyang’anizana ndi mayesero oika pachiswe miyoyo yawo. Lerolinonso, onse ofuna kukhalabe okhulupirika kwa Yehova adzapeza nyonga mwa kupenda mosamalitsa chitsanzo chimenecho.

16. Kodi tikutengapo phunziro lanji pa magawo a maulosi a m’buku la Danieli?

16 Magawo a maulosi a Danieli amamanga chikhulupiriro chathu mwa kusonyeza kuti Yehova amadziŵiratu zochitika zam’tsogolo zaka mazanamazana, ngakhale zikwizikwi pasadakhale. Mwachitsanzo, Danieli amafotokoza tsatanetsatane wa zochitika za kukwera ndi kugwa kwa maulamuliro apadziko lonse kuchokera m’nthaŵi ya Babulo mpaka “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) Danieli akutiuzanso za Ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Mfumu yoikidwa ndi Mulungu komanso za olamulira anzake a Mfumuyo “opatulikawo,” akumasonyeza kuti limenelo lidzakhala boma limene lidzalamulira kunthaŵi zomka muyaya. Boma limenelo lidzakwaniritsa chifuniro cha Yehova chonse kulinga ku dziko lathu lapansili ndipo lidzadzetsa madalitso kwa onse ofuna kutumikira Mulungu.—Danieli 2:44; 7:13, 14, 22.

17, 18. (a) Kodi chikhulupiriro chathu chingalimbitsidwe motani mwa kupenda mosamalitsa buku la Danieli? (b) Kodi ndi nkhani iti imene tiyenera kuitsimikizira kaye tisanayambe kuphunzira mozama buku la maulosi limenelo?

17 Mwayinso n’ngwakuti Yehova satibisira zochitika zam’tsogolo. M’mwalo mwake, iye ali “wakuvumbulutsa zinsinsi.” (Danieli 2:28) Mmene tiziphunzira za kukwaniritsidwa kwa maulosi olembedwa m’buku la Danieli, chikhulupiriro chathu m’malonjezo a Mulungu chizimka nachilimbitsidwa nthaŵi zonse. Chitsimikizo chathu chidzalimbirapo kwambiri choti Mulungu adzachita chifuniro chake panthaŵi yake yeniyeni yoikikayo komanso m’njira yoyenerera imene waisankha mwini yekha.

18 Onse amene aphunzira buku la Danieli la m’Baibulo ndi mtima womvera adzakula m’chikhulupiriro. Komabe, tisanayambe kuliphunzira mozama buku limenelo, tifunikira tipende umboni wake pofuna kutsimikiza ngati bukulo lilidi loona. Ofufuza ena atsutsa buku la Danieli, akumanena kuti maulosi ake analembedwa zinthuzo zitachitika kale. Kodi zonena za anthu okayikawo n’zoona? Mutu wotsatira udzayankha funso limeneli.

KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?

• N’chifukwa chiyani buku la Danieli lili la nthaŵi zamakono?

• Kodi Danieli limodzi ndi anzakewo anakaloŵa motani ntchito ya boma ku Babulo?

• Kodi ntchito yapadera ya Danieli ku Babulo inali yotani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ulosi wa Danieli?

[Chithunzi chachikulu patsamba 4]

[Chithunzi chachikulu patsamba 11]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena