Tumikirani Yehova ndi Cholinga Chimodzi
“Kenaka ndidzatembenuzira kwa anthu chinenero choyera, kuti iwo akaitanire pa dzina la Yehova, kumtumikira iye ndi cholinga chimodzi.”—ZEFANIYA 3:9, American Standard Version.
1, 2. (a) Yehova tsopano akubweretsa kukwaniritsidwa kwa ulosi uti? (b) Ulosi umenewo umadzutsa mafunso otani?
YEHOVA MULUNGU akuchita chinachake lerolino chimene anthu okha sangathe kuchikwaniritsa. Zinenero zina 3,000 zikulankhulidwa m’dziko lino logawanikana, koma Mulungu tsopano akubweretsa kukwaniritsidwa kwa ulosi uwu: “Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa anthu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.”—Zefaniya 3:9, NW.
2 Kodi nchiyani chimene chiri “chinenero choyera” chimenechi? Ndani amene amalankhula icho? Ndipo kodi nchiyani chimene chimatanthauza ‘kutumikira Mulungu mogwirizana’?
Amalankhula “Chinenero Choyera”
3. Nchiyani chimene chiri “chinenero choyera,” ndipo nchifukwa ninji awo amene akulankhula icho sali ogawanikana?
3 Pa tsiku la Pentekoste ya 33 C.E., mzimu woyera wa Mulungu unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu Kristu, kuwapatsa iwo mphamvu ya kulankhula m’chinenero chimene anali asanachiphunzirepo. Ichi chinawatheketsa iwo kuuza anthu amalilime ambiri “zinthu zazikulu za Mulungu.” Yehova mwakutero anayamba kubweretsa anthu amafuko onse m’chigwirizano. (Machitidwe 2:1-21, 37-42) Pamene Akunja okhulupirira pambuyo pake anakhala otsatira a Yesu, atumiki a Mulungu m’chenichenidi anali amalilime ambiri, anthu amitundu yambiri. Ngakhale kuli tero, iwo sanagawanitsidwepo ndi malire audziko, chifukwa onse amalankhula “chinenero choyera.” Ichi ndi chinenero cha onse cha chowonadi cha m’Malemba chonenedweratu pa Zefaniya 3:9. (Aefeso 4:25) Awo olankhula “chinenero choyera” sali ogawanikana koma “amalankhula mogwirizana,” akumakhala “moyenerera ogwirizana m’malingaliro amodzi ndi m’mzera umodzi wa kulingalira.”—1 Akorinto 1:10, NW.
4. Ndimotani mmene Zefaniya 3:9 amalozera ku kugwirizana kwa malilime ndi mafuko ambiri, ndipo ndi kuti kumene icho chikupezeka lerolino?
4 “Chinenero choyera” chinayenera kutheketsa anthu amitundu yonse ndi mafuko kutumikira Yehova “mogwirizana,” m’lingaliro lenileni, ‘ndi phewa limodzi.’ Iwo akatumikira Mulungu “ndi chigwirizano chimodzi” (The New English Bible); “ndi cholinga chimodzi” (The New American Bible); kapena “ndi chigwirizano cha onse chimodzi ndi phewa limodzi logwirizana.” (The Amplified Bible) Malembedwe ena amaŵerengedwa kuti: “Kenaka ndidzatembenuza milomo ya anthu onse kukhala yoyera, kuti iwo akaitanire pa dzina la Yehova ndi kugwirizana mu utumiki wake.” (Byington) Kugwirizana kwa malilime ambiri ndi mitundu yambiri kumeneku mu utumiki wa Mulungu kukupezeka kokha pakati pa Mboni za Yehova.
5. Ndi ku kugwiritsiridwa ntchito kotani kumene Mboni za Yehova ziri zokhoza kuika chinenero cha munthu aliyense?
5 Popeza onse a Mboni za Yehova amalankhula “chinenero choyera” cha chowonadi cha m’Malemba, iwo ali okhoza kugwiritsira ntchito chinenero chirichonse cha munthu kukugwiritsira ntchito kokwezeka koposa—kulemekeza Mulungu ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. (Marko 13:10; Tito 2:7, 8; Ahebri 13:15) Chiri chosangalatsa chotani nanga kuti “chinenero choyera” choterocho chikutheketsa anthu a magulu onse amafuko kutumikira Yehova ndi cholinga chimodzi!
6. Ndimotani mmene Yehova amawonera anthu, koma nchiyani chimene chidzakhala chothandiza ngati mlingo wa tsankho ulipo mu mtima mwa Mkristu wina?
6 Pamene Petro anali kuchitira umboni kwa Korneliyo ndi kwa Akunja ena, iye ananena kuti: “Ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho, koma m’mtundu uliwonse iye wakuwopa iye ndi kuchita chilungamo ali wolandirika kwa iye.” (Machitidwe 10:34, 35, By) Mogwirizana ndi malembedwe ena, Yehova “sali Wolemekeza anthu,” “sasiyanitsa pakati pa anthu,” ndipo “sasonyeza kukondera.” (The Emphatic Diaglott; Phillips; New International Version) Monga atumiki a Yehova, tiyenera kuwona anthu a magulu onse amafuko monga mmene iye amachitira. Koma bwanji ngati mlingo wa tsankho utsalira mu mtima wa Mkristu wina? Chotero chidzakhala chathandizo kudziŵa mmene Mulungu wathu wopanda tsankho amachitira ndi atumiki ake a mtundu uliwonse, fuko, anthu, ndi manenedwe.—Onaninso Galamukani! ya November 8, 1984, masamba 3-11 (Chingelezi).
Ali Zofunika
7. Mogwirizana ndi unansi ndi Mulungu, ndimotani mmene Mkristu mmodzi samasiyanirana ndi wina wa mtundu kapena fuko lina?
7 Ngati muli mboni yobatizidwa ya Yehova, mwachidziŵikire panthaŵi ina munali ‘kulira ndi kuusa moyo pa zonyansa zonse’ zimene zimachitika m’dongosolo iri loipa. (Ezekieli 9:4) Munali ‘akufa m’machimo anu,’ koma Mulungu mwachifundo anakukokani inu kwa iyemwini kupyolera mwa Yesu Kristu. (Aefeso 2:1-5; Yohane 6:44) M’njira zimenezi, simunasiyane ndi ena omwe tsopano ali akhulupiriri anzanu. Iwo nawonso anavutitsidwa ndi kuipa, anali ‘akufa m’machimo awo,’ koma anakhala olandira achifundo cha Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. Ndipo mosasamala kanthu za fuko lathu kapena utundu, chiri kokha mwachikhulupiriro kuti aliyense wa ife tsopano ali ndi kaimidwe ndi Yehova Mulungu monga mboni zake.—Aroma 11:20.
8. Ndimotani mmene Hagai 2:7 akukwaniritsidwira tsopano?
8 Mawu a ulosi a Hagai 2:7 amatithandiza ife kuwona mmene tiyenera kuwonera akhulupiriri anzathu amitundu ina yosiyana. Pamenepo Yehova ananena kuti: “Ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndipo zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” Kukwezedwa konenedweratu kwa chipembedzo choyera kumeneku kukuchitika pakachisi wowona wa Mulungu, mabwalo akulambira kwake. (Yohane 4:23, 24) Koma nchiyani chimene chiri “zinthu zofunika za amitundu”? Izo ziri zikwi za okonda chilungamo omwe akuvomereza mwachiyanjo ku ntchito yolalikira Ufumu. Kuchokera ku mitundu yonse ndi mafuko, iwo akupita ku ‘phiri la nyumba ya Yehova,’ kukhala mboni zake zobatizidwa ndi mbali ya mitundu yonse ya “khamu lalikulu.” (Yesaya 2:2-4; Chivumbulutso 7:9) Awo amene akulemekeza Yehova monga mbali ya gulu lake la padziko lapansi ali oyera, oyera mwa makhalidwe, anthu aumulungu—ofunika kwenikwenidi. Ndithudi, chotero, Mkristu aliyense wowona ayenera kufuna kusonyeza chikondi cha ubale kwa ofunika onse amenewo olandiridwa kwa Atate wathu kumwamba.
Umunthu Wawo ndi Watsopano
9. Ngakhale ngati kale sitinali kulingalira bwino ponena za alendo, nchifukwa ninji zinthu ziyenera kukhala zosiyana tsopano pamene tiri Akristu?
9 Abale ndi alongo athu auzimu kuzungulira padziko lapansi alinso ofunika chifukwa iwo alabadira uphungu wa ‘kuchotsa umunthu wakale ndi ntchito zake ndi kudziveka iwo eni ndi umunthu watsopano.’ “Kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka [iwo] ukupangidwa kukhala watsopano mwa chifaniziro cha iye amene anaulenga, pamene palibe m’Griki kapena m’Yuda, mdulidwe kapena kusadulidwa, wotchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse m’zonse.” (Akolose 3:9-11, NW) Ngati munthu kalelo sanali kulingalira bwino ponena za Ayuda, Agriki, kapena ena ake akunja kwa iye, zinthu ziyenera kukhala zosiyana tsopano popeza iye ali Mkristu. Mosasamala kanthu za fuko, mtundu, kapena mwambo, awo okhala ndi “umunthu watsopano” amakulitsa ndi kusonyeza chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, kudzichepetsa, ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Ichi chimawagwirizanitsa iwo kwa alambiri anzawo a Yehova.
10. Ngati tiyesera kupanga ndemanga zongopita zopanda chiyanjo ponena za akhulupiriri anzathu a fuko kapena mtundu wina, ndimotani mmene Tito 1:5-12 angatithandizire?
10 Mosiyana ndi atumiki a Yehova, anthu ena a kudziko amapanga ndemanga zokhumudwitsa ponena za anthu a chiyambi cha ufuko chosiyana ndi chawo. Nkulekelanji, ponena za anthu ake enieni, mneneri wa chiKrete kamodzi ananena kuti: “Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zirombo zoipa, aumbombo”! Mtumwi Paulo anakumbutsidwa za mawu amenewo pamene chinakhala choyenerera kuletsa aphunzitsi onyenga pakati pa Akristu pa chisumbu cha Krete. Koma Paulo ndithudi sanali kunena kuti: ‘Akristu onse a chiKrete ali amabodza ndi oipa, aulesi, ndi aumbombo.’ (Tito 1:5-12) Ayi, popeza Akristu samalankhula mosalimbikitsa za ena. M’kuwonjezerapo, ambiri a Akristu a ku Krete amenewo anali atavala “umunthu watsopano,” ndipo ena anayeneretsedwa mwauzimu kaamba ka kuikidwa monga akulu. Ichi chimafunikira kulingalira kosamalitsa ngati tayesedwa kupanga ndemanga zongopita zopanda chiyanjo ponena za abale ndi alongo athu auzimu a fuko kapena mtundu wapadera.
Lingalirani Ena Kukhala Apamwamba
11. Ngati tsankho la mtundu wina uliwonse liripo mu mtima mwa Mkristu, nchiyani chimene angachite?
11 Kumbali ina, ngati Mkristu anali watsankho ku fuko limodzi kapena mtundu, iye mwinamwake angasonyeze ichi ndi mawu kapena kachitidwe. Kenaka, ichi chingapangitse malingaliro opwetekedwa, makamaka mu mpingo wopangidwa ndi anthu achiyambi cha mafuko osiyanasiyana. Motsimikizirika, palibe Mkristu amene angafune kuika chitsenderezo choterocho pa umodzi wa anthu a Mulungu. (Masalmo 133:1-3) Chotero ngati tsankho lirilonse liripo mu mtima wa Mkristu, iye angachite bwino kupemphera kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.”—Masalmo 139:23, 24.
12. Nchifukwa ninji sitiyenera kudzikweza mwa ife eni kapena mwa ena a chiyambi cha fuko lathu?
12 Chiri chabwino kutenga kawonedwe kenikeni kuti tonsefe tiri anthu opanda ungwiro omwe sitikanakhala nkomwe ndi kaimidwe ndi Mulungu ngati sichinali chifukwa cha nsembe ya Yesu Kristu. (1 Yohane 1:8–2:2) Nchiyani, chotero, chimene chimatipangitsa ife kusiyana ndi ena? Popeza tiribe chirichonse chimene sitinalandire, nchifukwa ninji tiyenera kudzikweza mwa ife eni kapena mwa ena a chiyambi cha fuko lathu?—Yerekezani ndi 1 Akorinto 4:6, 7.
13. Ndimotani mmene tingagawirireko ku umodzi wa mu mpingo, ndipo nchiyani chimene chingaphunziridwe kuchokera ku Afilipi 2:1-11?
13 Tingagawire ku umodzi wa mu mpingo ngati tizindikira ndi kusonyeza chiyamikiro kaamba ka mikhalidwe yabwino ya ena. Mtumwi Wachiyuda Paulo anapereka kwa tonsefe chakudya cholingalira pamene iye anauza Afilipi Akunja kuti: “Kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi; musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima yense ayese anzake omposa iye mwini.” Kawonedwe koyenera kwa ife kakusonyeza kulinga kwa anthu anzathu a fuko lirilonse kapena mtundu kanachitiridwa chitsanzo ndi Yesu Kristu. Ngakhale kuti iye anali cholengedwa champhamvu chauzimu, iye “anakhala m’mafanizidwe a anthu” ndipo anadzichepetsa iyemwini kufikira imfa pamtengo wozunzirapo kaamba ka anthu ochimwa a fuko ndi mtundu uliwonse. (Afilipi 2:1-11) Monga atsatiri a Yesu, chotero kodi ife sitiyenera kukhala okonda, odzichepetsa, ndipo omvera chifundo, tikumazindikira kuti ena ali otiposa ife?
Mvetserani ndi Kupenya
14. Ndimotani mmene tingathandizidwire kulingalira ena monga apamwamba kuposa ife?
14 Tingathandizidwe kulingalira ena kukhala otiposa ngati ife timamvetseradi pamene iwo alankhula ndipo mosamalitsa kupenya khalidwe lawo. Mwachitsanzo, ife mowona mtima tingafunikire kuvomereza kwa ife eni kuti mkulu mnzathu—mwinamwake wa fuko lina—watiposa ife mkuthekera kwa kupereka uphungu wokhutiritsa m’Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Tingazindikire kuti uli uzimu wake, osati kwenikweni kalankhulidwe kake kapena njira ya kulankhula, imene yamtheketsa iye kupeza zotulukapo zabwino m’kuthandiza akhulupiriri anzake kukhala olengeza a Ufumu ofikapo. Ndipo chiri chodziŵikiratu kuti Yehova akudalitsa zoyesayesa zake.
15. Nchiyani chimene tingadziŵe pamene timvetsera ku ndemanga za alambiri anzathu?
15 Pamene ticheza ndi abale ndi alongo athu kapena kumvetsera ku ndemanga zawo pa misonkhano, tingazindikire kuti ena a iwo ali ndi kumvetsetsa kwabwinoko kwa zowonadi zina za m’Malemba kuposa mmene tichitira. Tingazindikirenso kuti chikondi chawo cha ubale chimawoneka champhamvupo, iwo amawoneka kukhala ndi chikhulupiriro choposa, kapena iwo amapereka chitsimikiziro cha kukhulupirira kwawo kokulira mwa Yehova. Chotero kaya iwo ali a chiyambi cha gulu lathu la fuko kapena ayi, amatisonkhezera ife kuchikondano ndi ntchito zabwino, kuthandiza kulimbikitsa chikhulupiriro chathu, ndi kutifulumiza ife kukhulupirira mokwanira koposa mwa Atate wathu wa kumwamba. (Miyambo 3:5, 6; Ahebri 10:24, 25, 39) Yehova mwachidziŵikire watikokera ife kufupi ndi iwo, ndipo momwemonso tiyenera kutero.—Yerekezani ndi Yakobo 4:8.
Adalitsidwa ndi Kuchirikizidwa
16, 17. Chitirani chitsanzo nsonga yakuti Yehova sali wa tsankho m’kudalitsa atumiki ake a mtundu kapena fuko lirilonse.
16 Yehova sali wa tsankho m’kudalitsa atumiki ake a mtundu uliwonse kapena fuko. Mwachitsanzo, lingalirani dziko la Brazil. Sikunali kuchokera kwa amishonale achilendo koma kuchokera ku milomo ya amalinyero asanu ndi atatu a chiBrazil kuti anthu mu Brazil choyamba anamva uthenga wa Ufumu chifupifupi m’chaka cha 1920. Dalitso la Mulungu lakhala lodziŵikiratu, popeza kuti podzafika chaka cha utumiki cha 1987, panali chiŵerengero chapamwamba cha olengeza Ufumu cha 216,216 m’dziko limenelo la nzika 141,302,000—chiŵerengero cha wofalitsa mmodzi kwa 654.
17 Lingalirani chitsanzo china cha dalitso laumulungu. Mu April 1923 mboni za Yehova ziŵiri zakuda zochokera ku chisumbu cha Caribbean cha Trinidad zinatumizidwa kukalengeza uthenga wa Ufumu ku West Africa. Chotero zinachitika kuti Mbale ndi Mlongo W. R. Brown anatumikira kumeneko kwa zaka zochulukira, iye akumakhala wodziŵika monga “Baibulo Brown.” Iwo “anabzyala” ndipo “Mulungu anazipangitsa kukula” pamene enanso anagwira ntchito m’gawo lalikulu limenelo. (1 Akorinto 3:5-9) Lerolino, olengeza Ufumu akufika pa chiŵerengero choposa 32,600 mu Ghana ndipo oposa 133,800 mu Nigeria mokha.
18, 19. Perekani zitsanzo za mmene mungatsimikizirire kuti Mulungu wathu wopanda tsankho amachirikiza atumiki ake amafuko ndi mitundu yonse.
18 Yehova samadalitsa kokha atumiki ake a mitundu yonse ndi mafuko komanso amawachirikiza iwo. Mwachitsanzo, lingalirani nkhani za mboni za Yehova za chiJapan ziŵiri. Pa June 21, 1939, Katsuo Miura ndi mkazi wake anagwidwa mopanda chilungamo, ndi kuikidwa m’ndende, ndi kulekanitsidwa ndi mwana wawo wamwamuna wa zaka zisanu zakubadwa, yemwe anasamaliridwa ndi agogo ake a akazi. Mlongo Miura anamasulidwa pambuyo pa miyezi isanu ndi itatu, koma Mbale Miura anasungidwa kwa zaka zoposa ziŵiri asanayambe kuzengedwa mlandu. Iye anavutika ndi kusakhalitsidwa bwino, anapezedwa wa mlandu, ndipo analandira chilango cha zaka zisanu. M’ndende ya mu Hiroshima, Mulungu anamchirikiza iye kupyolera mwa Malemba omwe anapereka chitonthozo chosalephera ndi mphamvu. Mwa chowoneka kukhala chozizwitsa, Mbale Miura anapulumuka pa August 6, 1945, pamene bomba la atomu linaphulitsa ndende yake. Miyezi iŵiri pambuyo pake, iye anali wokhoza kugwirizananso ndi mkazi wake ndi mwana kumpoto kwa Japan.
19 Mkati mwa Nkhondo ya Dziko II, chizunzo champhamvu chinakumanizidwa ndi Mboni za Yehova m’maiko ambiri. Mwachitsanzo, Robert A. Winkler anali mbale mmodzi wa chiGerman yemwe anavutika m’misasa ya chibalo ya chiNazi mu Germany ndi mu Netherlands. Chifukwa chakuti iye anakana kupereka Mboni zinzake, iye anamenyedwa mwankhalwe kotero kuti sanakhoze kuzindikiridwa. Koma iye analemba: “Malingaliro a malonjezo a Yehova akuthandiza wina mu mtundu uliwonse wa mavuto anandipatsa ine chitonthozo ndi mphamvu ya kupirira zonsezi. . . . Loŵeruka ndinali nditamenyedwa ndi a Gestapo, ndipo pa Lolemba lotsatira ndinayenera kufunsidwa ndi iwo kachiŵirinso. Nchiyani chimene chikachitika tsopano ndipo nchiyani chimene ndikachita? Ndinatembenukira kwa Yehova m’pemphero, kukhulupirira m’malonjezo ake. Ndinadziŵa kuti ichi chinatanthauza kugwiritsira ntchito machenjera ankhondo ya teokratiki kaamba ka ntchito ya Ufumu ndi chinjirizo la abale anga Achikristu. Chinali chiyeso chachikulu kwa ine kuchipirira ndipo pofika tsiku la khumi ndi zisanu ndi ziŵiri ndinatoperatu, koma ndinayamikira Yehova kuti m’mphamvu yake ndinali wokhoza kupirira chiyeso chimenechi ndi kusunga umphumphu wanga.”—Masalmo 18:35; 55:22; 94:18.
Oyamikira kaamba ka Ubale Wathu
20. Ndimotani mmene ulemu wathu kaamba ka akhulupiriri anzathu a fuko ndi mtundu uliwonse ungawonjezedwere?
20 Mosakaikira, Yehova amadalitsa ndi kuchirikiza mboni zake za mtundu uliwonse ndi fuko. Iye alibe tsankho, ndipo monga atumiki ake odzipereka, tiribe chodzikhululukira kapena chifukwa cha kusonyezera tsankho. M’kuwonjezerapo, ulemu wathu kaamba ka abale ndi alongo athu a fuko ndi mtundu uliwonse udzawonjezeka ngati tilingalira njira m’zimene iwo aliri apamwamba kwa ife. Nawonso amagwiritsira ntchito nzeru ya kumwamba, yomwe siipanga kusiyanitsa koma imatulutsa chipatso chabwino koposa. (Yakobo 3:13-18) Inde, ndipo kukoma mtima kwawo, kuolowa manja, chikondi, ndi mikhalidwe ina yaumulungu imatipatsa ife zitsanzo zabwino.
21. Nchiyani chimene tiyenera kugamulapo kuchita?
21 Ndi oyamikira chotani nanga mmene tiyenera kukhalira, chotero, kaamba ka ubale wathu wa mafuko ambiri, mitundu yambiri! Ndi thandizo ndi dalitso la Atate wathu wakumwamba, lolani kuti ife “timtumikire mogwirizana” m’chikondi cha ubale ndi ulemu kwa onse. Ndithudi, chiyenera kukhala chikhumbo chathu cha mtima wonse ndi cholinga chathu champhamvu cha kutumikira Yehova ndi cholinga chimodzi.
Nchiyani Chomwe Chiri Ndemanga Zanu?
◻ Nchiyani chimene “chinenero choyera” chimatheketsa atumiki a Yehova a magulu a mafuko onse kuchita?
◻ Ndimotani mmene Hagai 2:7 akukwaniritsidwira lerolino, ndipo ndimotani mmene ichi chiyenera kuyambukirira kawonedwe kathu ka atumiki ena a Mulungu?
◻ Ndimotani mmene Afilipi 2:3 angayambukirire unansi wathu ndi anthu a fuko ndi mtundu uliwonse?
◻ Ngati timvetsera ndi kupenya, nchiyani chimene tidzazindikira ponena za akhulupiriri anzathu a chiyambi cha mtundu wina?
[Zithunzi patsamba 17]
Anthu a fuko ndi mtundu uliwonse akulemekeza Yehova ndi cholinga chimodzi
[Chithunzi patsamba 18]
Mvetserani mosamalitsa ndi kukhala openyerera. Mudzasonkhezeredwa ndi chikondi ndi chikhulupiriro chowonekera m’mawu ndi zochita za mboni zina za Yehova