Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 5/1 tsamba 15-20
  • Lankhulani Chinenero Choyera ndi Kukhala ndi Moyo Kosatha!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lankhulani Chinenero Choyera ndi Kukhala ndi Moyo Kosatha!
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungaphunzirire Chinenero Choyera
  • Kuloŵerera kwa Zodetsedwa
  • Chinenero Choyera Chimvedwa Padziko Lonse
  • Kuchigwiritsira Ntchito Kapena Kuchitaya
  • Tikhalabe Ogwirizanitsidwa
  • Chinenero Choyera cha Mitundu Yonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Mumalankhula Bwino “Chinenero Choyera”?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Khalani Ogwirizana mwa Chinenero Choyera
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kulankhula “Chinenero Choyera”
    Imbirani Yehova Zitamando
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 5/1 tsamba 15-20

Lankhulani Chinenero Choyera ndi Kukhala ndi Moyo Kosatha!

‘Funani Yehova, . . . funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’​—ZEFANIYA 2:3.

1. (a) Kodi ndinjira zotani zimene ophunzira amagwiritsira ntchito kuphunzira chinenero chachilendo? (b) Kodi nkuchilankhuliranji chinenero choyera?

OPHUNZIRA angaphunzire lilime latsopano mwakugwiritsira ntchito njira ya galamala kapena njira ya chinenero cholankhulidwa. Mwanjira ya galamala, iwo mwachisawawa amagwiritsira ntchito mabuku ophunzirira namaphunzira malamulo a galamala. Mwanjira ya chinenero cholankhulidwa, iwo amatsanzira dongosolo la mamvekedwe ndi mawu olankhulidwa ndi mphunzitsi wawo. Njira zonse ziŵirizo zimagwiritsiridwa ntchito pophunzira “chinenero choyera.” Ndipo nchofunika kwambiri kuti tilankhule chinenero chimenechi ngati tikuyembekezera ‘kubisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’​—Zefaniya 2:1-3; 3:8, 9.

2. Kodi tingaphunzire motani zimene zingatchedwe malamulo a galamala wa chinenero choyera?

2 Bukhu lalikulu lophunzirira logwiritsiridwa ntchito kuphunzira chinenero choyera ndilo Baibulo. Kuliphunzira mwakhama ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo kumakuphunzitsani zimene zingatchedwe malamulo a galamala wa chinenero choyera. Phunziro Labaibulo lapanyumba lochititsidwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova ndilo chiyambi chabwino. Kwa odzipereka kale kwa Mulungu, kuphunzira Malemba kokhazikika ndi kwakhama nkofunika. Koma kodi pali njira zapadera zogwira mtima zophunzirira chinenero choyera? Ndipo kodi ndi mapindu otani omwe amatuluka m’kuchilankhula?

Mmene Mungaphunzirire Chinenero Choyera

3. Kodi ndi njira imodzi iti yophunzirira chinenero choyera?

3 Njira imodzi yophunzirira chinenero choyera ndiyo kugwirizanitsa chowonadi chimene mukuphunzira ndi mfundo zimene mumazidziŵa kale, monga momwe wophunzira chinenero angagwirizanitsire mopita patsogolo malamulo a galamala osiyanasiyana. Mwachitsanzo, panthaŵi ina mungakhale munadziŵa kuti Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu, koma munadziŵa zochepa ponena za ntchito zake. Kuyambira pamenepo, phunziro Labaibulo lingakhale lakuphunzitsani kuti Kristu tsopano akulamulira monga Mfumu yakumwamba ndikuti mkati mwa Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, anthu omvera adzafikitsidwa kuungwiro. (Chibvumbulutso 20:5, 6) Inde, kugwirizanitsa malingaliro atsopano ndi ophunziridwa kale kumawongolera kumvetsetsa kwanu kwa chinenero choyera.

4. (a) Kodi ndi njira ina iti yophunzirira ‘malamulo a galamala’ wa chinenero choyera, ndipo kodi ndi nkhani ya m’Baibulo iti imene yagwiritsiridwa ntchito kufotokoza mwafanizo zimenezi? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Gideoni ndi amuna ake mazana atatu anachitapo kanthu? (c) Kodi nkhani ya Gideoni imatiphunzitsanji?

4 Njira ina yophunzirira ‘malamulo a galamala’ wa chinenero choyera ndiyo kuyerekezera zochitika za m’Baibulo. Kufotokoza mwafanizo: Yesani ‘kuwona ndi kumva’ nkhani yolembedwa pa Oweruza 7:15-23. Tawonani! Woweruza Wachiisrayeli Gideoni wagaŵa makamu ake m’magulu atatu lirilonse lokhala ndi amuna zana limodzi. Mumdima, iwo mwakachetechete akutsika kuchokera pa Phiri la Giliboa nazinga msasa wa Amidyani ogonawo. Kodi ngokonzekeretsedwa mokwanira, mazana atatu ameneŵa? Osati mwa zida zankhondo. Eya, iwo akasekedwa monyodola ndi ankhondo odzitukumula! Mwamuna aliyense ali kokha ndi lipenga, mbiya yaikulu ya madzi, ndi muuni mkati mwa mbiyayo. Koma tamverani! Chizindikiro chitaperekedwa, amuna zana limodzi amene ali ndi Gideoni akuwomba malipenga awo ndi kuswa mbiya zawo za madzizo. Achitanso motero mazana aŵiri enawo. Pamene onse akweza miuni yawo m’mwamba, mukuwamva akufuula kuti: ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni!’ Ha, izi zikuwachititsa mantha Amidyani chotani nanga! Iwo atuluka chadzandidzandi m’mahema awo, akutong’ola maso awo olema ndi tulo powopa malaŵi omwe akuunikira zinthu zowoneka mwachimbuuzi ndi zochititsa mantha. Pamene Amidyaniwo ayamba kuthaŵa, amuna a Gideoni apitirizabe kuliza malipenga awo, ndipo Mulungu awakanthanitsa okha okha adaniwo. Ha, ndi phunziro lalikulu chotani nanga la chinenero choyera! Mulungu akhoza kupulumutsa atumiki ake popanda gulu lankhondo laumunthu. Kuwonjezerapo, ‘Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu.’​—1 Samueli 12:22.

5. Kodi ndimotani mmene misonkhano Yachikristu ingatithandizire kuyenga malankhulidwe athu?

5 Pamene ophunzira aphunzitsidwa lilime lachilendo kupyolera mwa njira yakulankhula, amayesayesa kubwereza mamvekedwe ndi mawu a mphunzitsi molondola. Ndi mwaŵi wabwino chotani nanga umene ulipo wakulankhula chinenero choyera pa misonkhano Yachikristu! Kumeneko timamva ena akulankhula m’chinenero chimenecho cha chowonadi cha Malemba, ndipo tingapatsidwe mwaŵi wakuthirira ndemanga enife. Kodi timachita mantha kuti mwina tidzalankhula chinachake cholakwika? Lolani kuti chimenecho chisakhale nkhaŵa yathu yaikulu, popeza kuti chophophonya chimene chimawongoleredwa mokoma mtima ndi mkulu wotsogoza pa msonkhano woterowo monga Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu ndi mlungu chingayenge malankhulidwe athu. Chifukwa chake, pezekanipo ndikukhala ndi phande mokhazikika m’misonkhano Yachikristu.​—Ahebri 10:24, 25.

Kuloŵerera kwa Zodetsedwa

6. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyana koteroko pakati pa Mboni za Yehova ndi magulu azipembedzo a Chikristu Chadziko?

6 Awo amene amabukitsa chifuniro cha Yehova ndi kulengeza Ufumu wake wakumwamba amalankhula chinenero choyera monga Mboni zake. Amadziŵikitsa dzina lake ndikumtumikira “mogwirizana,” kapena ndi malingaliro amodzi. (Zefaniya 3:9, NW) Chinkana kuti zipembedzo za Chikristu Chadziko zili nalo Baibulo, izo sizimalankhula chinenero choyera kapena kuitanira padzina la Mulungu m’chikhulupiriro. (Yoweli 2:32) Iwo alibe uthenga wogwirizana wozikidwa pa Malemba. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti amaika miyambo yachipembedzo, nthanthi zadziko, ndi kukhulupirika ku ndale zadziko pamwamba pa Mawu a Mulungu. Zifuno zawo, ziyembekezo, ndi njira zonse nzadziko lino loipa.

7. Kodi ndi kusiyana kotani kwa pakati pa Mboni za Yehova ndi zipembedzo zonyenga kosonyezedwa pa 1 Yohane 4:4-6?

7 Chikristu Chadziko​—kwenikweni, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga​—sichimalankhula chinenero chofanana monga momwe Mboni za Yehova zimachitira. Mokondweretsa, kwa amene amalankhula chinenero choyera, mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Inu ndinu ochokera mwa Mulungu; . . . ndipo [munawalaka anthuwo, NW]; pakuti iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m’dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m’dziko lapansi; mwa ichi alankhula monga ochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera. Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife.’ (1 Yohane 4:4-6) Atumiki a Yehova alaka aphunzitsi onyenga chifukwa chakuti Mulungu, amene akhala mwa anthu ake, ‘aposa [Mdyerekezi, amene] akukhala m’dziko lapansi,’ chitaganya cha anthu chosalungama. Popeza kuti ampatuko ‘amachokera m’dziko lapansi’ ndipo ali ndi mzimu wake woipa, iwo ‘alankhula monga ochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera.’ Koma anthu onga nkhosa amamvetsera kwa awo ochokera kwa Mulungu, namazindikira kuti anthu a Yehova amalankhula chinenero choyera cha chowonadi cha m’Baibulo choperekedwa kupyolera m’gulu lake.

8. Kodi munthu wosayeruzikayo ndani?

8 Chipanduko chachikulu chinanenedweratu, ndipo ‘chinsinsi cha kusayeruzika’ chidayamba kale kugwira ntchito m’zaka za zana loyamba C.E. M’kupita kwa nthaŵi, anthu amene analandira​—kapena kutenga​—malo akuphunzitsa mumpingo anaphunzitsa ziphunzitso zambiri zonyenga. Chinenero chawo chinali kutalitali ndi kukhala choyera. Chotero panabuka “munthu wosayeruzika” wachiungwe, atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko, ononomera ku miyambo yonyenga yachipembedzo, nthanthi zadziko, ndi ziphunzitso zopanda malemba.​—2 Atesalonika 2:3, 7.

Chinenero Choyera Chimvedwa Padziko Lonse

9. Kodi nzochitika zachipembedzo zotani zomwe zidalipo mkati mwa zaka za zana la 19?

9 Anthu owopa Mulungu ochepa okha ndiamene ‘ankalimbanira chikhulupiriro chopatsidwa kwa oyera mtima.’ (Yuda 3) Kodi okhulupirira oterowo akapezeka kuti? Kwa zaka mazana ambiri, chipembedzo chonyenga chinasunga makamu ameneŵa mumdima wauzimu, koma Mulungu anawadziŵa oŵerengekawo omwe adali ndi chivomerezo chake. (2 Timoteo 2:19) Ndipo kenaka, pakati pa masinthidwe a m’zaka za zana la 19 m’zamalonda, zamaindasitale, ndi m’zamayanjano, panabuka mawu osiyana ndi babele wachisawawa wa chisokonezo chachipembedzo chonyenga. Magulu aang’ono anayesa kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi ndi kulosera kubwera kwachiŵiri kwa Yesu, koma sionse analankhula chinenero choyera.

10. Kodi ndi gulu la “kubwera kwachiŵiri” liti limene Mulungu anasankha kulankhula chinenero choyera, ndipo nchifukwa ninji kuli kowonekeratu kuti dzanja la Yehova lakhalabe nawo?

10 Komabe, mu 1879, zinawonekera poyera kuti ndi mawu ati onena za “kubwera kwachiŵiri” omwe anasankhidwa ndi Yehova kulankhula chinenero choyera monga Mboni zake. Panthaŵiyo kagulu kakang’ono kophunzira Baibulo kotsogozedwa ndi Charles Taze Russell kankakumana m’Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A. Iwo anakhala otsimikiza kuti kubwera kwachiŵiri kwa Yesu kukayambitsa kukhalapo kwake kosaoneka ndi maso, kuti nthaŵi ya nsautso ya dziko idali patsogolo, ndikuti zimenezi zikatsatiridwa ndi Kulamulira kwa Kristu kwa Zaka Chikwi kumene kukabwezeretsa Paradaiso padziko lapansi, ndi moyo wamuyaya kaamba ka anthu omvera. Mu July 1879 Ophunzira Baibulo ameneŵa anayamba kufalitsa magazini omwe tsopano akutchedwa Nsanja ya Olonda. Makope 6,000 okha ndiwo anagaŵiridwa a kope loyamba. Koma “dzanja la [Yehova, NW]” lidali ndi Mboni zimenezo, chifukwa chakuti magazini ameneŵa tsopano akufalitsidwa m’zinenero 111, ndi avareji yakusindikizidwa yoposa pa 15,000,000 kope lirilonse.​—Yerekezerani ndi Machitidwe 11:19-21.

11, 12. Kodi ndi mfundo zina ziti za chowonadi cha Malemba zomvetsedwa bwino ndi awo olankhula chinenero choyera?

11 Kupyolera m’Baibulo ndi mabuku a Mboni za Yehova, makamaka ndi kulengeza mbiri yabwino kwa Akristu achangu amenewa, chinenero choyera chadziŵika padziko lonse lapansi. Ndipo ndimadalitso aakulu chotani nanga amene ochilankhula akusangalala nawo! Mmalo monena kuti ‘Mulungu ndi Mulungu, Kristu ndi Mulungu, ndipo Mzukwa Woyera ndi Mulungu’ m’chinenero chachinsinsi cha Utatu, iwo amagwirizana ndi kaimidwe ka Baibulo kakuti Yehova ndiye Wamkulukulu, Yesu Kristu monga wocheperapo ali Mwana Wake, ndipo mzimu woyera uli mphamvu yogwira ntchito yozizwitsa ya Mulungu. (Genesis 1:2; Salmo 83:18; Mateyu 3:16, 17) Olankhula chinenero choyera amadziŵa kuti munthu sanasinthike kuchokera ku mtundu wa moyo wotsika koma analengedwa ndi Mulungu wachikondi. (Genesis 1:27; 2:7) Iwo amazindikira kuti moyo umaleka kukhalako paimfa​—mfundo yomwe imachotsapo kuwopa akufa. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Helo amadziŵidwa kukhala manda wamba a anthu, osati malo achizunzo cha moto okonzedwa ndi mulungu wankhalwe. (Yobu 14:13) Iwo amadziŵanso kuti chiukiriro nchiyembekezo choperekedwa ndi Mulungu cha akufa.​—Yohane 5:28, 29; 11:25; Machitidwe 24:15.

12 Awo olankhula chinenero choyera amasonyeza ulemu kaamba ka mwazi ndi moyo. (Genesis 9:3, 4; Machitidwe 15:28, 29) Iwo amazindikira kuti moyo wapadziko lapansi wa Kristu ndiwo mtengo wadipo wolipiridwa kaamba ka anthu omvera. (Mateyu 20:28; 1 Yohane 2:1, 2) Iwo samapemphera kwa “oyera mtima,” podziŵa kuti mapemphero awo ayenera kulunjikitsidwa kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. (Yohane 14:6, 13, 14) Popeza kuti Mawu a Mulungu amatsutsa kulambira mafano, iwo samagwiritsira ntchito mafano m’kulambira kwawo. (Eksodo 20:4-6; 1 Akorinto 10:14) Ndipo amapeŵa maupandu a ziŵanda chifukwa chakuti amakana kukhulupirira mizimu, kotsutsidwanso m’Baibulo.​—Deuteronomo 18:10-12; Agalatiya 5:19-21.

13. Kodi nchifukwa ninji awo olankhula chinenero choyera sakuchita mantha?

13 Atumiki a Yehova, omwe amalankhula chinenero choyera, samachita mantha ndi pamene afika m’nyengo ya nthaŵi. Yehova wawaphunzitsa kuti iwo akukhala ‘m’nthaŵi ya chimaliziro,’ ndi Yesu alipo monga mzimu wosawoneka waulemerero. (Danieli 12:4; Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5; 1 Petro 3:18) Pokhala ndi magulu ankhondo akumwamba kumbuyo kwake, Kristu ali pafupi kuloŵa m’nkhondo yopereka chiweruzo cha Mulungu motsutsana ndi dongosolo lazinthu liripoli. (Danieli 2:44; Chibvumbulutso 16:14, 16; 18:1-8; 19:11-21) Inde, ndipo awo olankhula chinenero choyera ngotanganitsidwa ndi kulengeza mbiri yabwino yakuti Ufumu wa Mulungu wokhala pansi pa Kristu posachedwapa udzabweretsa madalitso aakulu kwa anthu onse omvera padziko lapansi laparadaiso. (Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14; Mateyu 6:9, 10; 24:14; Luka 23:43) Inde zonsezo, ndipo tangopapasa pamwamba pokha! Ndithudi, chinenero choyera ndicho chinenero chamtengo wapatali, cholemera koposa padziko lapansi!

14. Kodi ndi mapindu ena otani amene olankhula chinenero choyera akusangalala nawo?

14 Mapindu omwe olankhula chinenero choyera amasangalala nawo amaphatikizapo “mtendere wa Mulungu” umene umachinjiriza mitima ndi mphamvu zakulingalira. (Afilipi 4:6, 7) Iwo amamvera malamulo a Baibulo, omwe amapititsa patsogolo thanzi, chimwemwe, ndi chikhutiro chochokera m’kukondweretsa Yehova. (1 Akorinto 6:9, 10) Inde, ndipo olankhula chinenero choyera ali ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu.​—2 Petro 3:13.

Kuchigwiritsira Ntchito Kapena Kuchitaya

15. Kodi mudzapindula motani ndi chidziŵitso chabwino cha chinenero choyera?

15 Ngati mufuna kudzalankhula chinenero choyera m’dziko latsopano, muyenera kuchidziŵa bwino lomwe kwakuti chikhale chinenero chimene mumalingaliriramo. Pamene munthu akuphunzira chinenero, poyamba amalingalira m’chinenero chake kenaka nkumatembenuzira malingaliro ake m’chinenero chatsopanocho. Koma pamene akhala waluso mokulirapo m’chinenero chatsopanocho, amayamba kulingalirira m’chinenerocho mosafunikira mchitidwe wakutembenuza. Mofananamo, kupyolera m’phunziro lakhama, mungakhale ndi chidziŵitso chabwino choterocho cha chinenero choyera kwakuti mudzadziŵa mmene mungagwiritsirire ntchito malamulo ndi miyezo ya Baibulo kuthetsa mavuto ndikukhalabe pa “njira ya moyo.”​—Salmo 16:11.

16. Kodi nchiyani chimene chingachitike ngati simumagwiritsira ntchito chinenero choyera mokhazikika?

16 Muyenera kuchigwiritsira ntchito mokhazikika chinenero choyera, mukapanda kutero mudzataikiridwa luso lakuchilankhula bwino. Tifotokoze mwafanizo: Zaka zambiri zapitazo, ena aife tinaphunzira chinenero chachilendo. Tingakumbukire mawu ena achinenerocho koma mwachiwonekere tataikiridwa luso lathu la icho chifukwa chakuti sitimachigwiritsira ntchito mokhazikika. Zofananazo zingachitike ndi chinenero choyera. Ngati sitikuchigwiritsira ntchito mokhazikika, tingataikiridwe luso lathu la icho, ndipo chimenecho chikakhala ndi zotulukapo zangozi mwauzimu. Chifukwa chake tiyeni tichilankhule mokhazikika pamisonkhano ndi muuminisitala Wachikristu. Zochitachita zimenezi, zotsagana ndi phunziro laumwini, zidzatikhozetsa kulankhula zinthu molondola m’chinenero choyera. Ndipo chimenecho nchofunika chotani nanga!

17. Kodi nchiyani chimene chimafotokoza mwafanizo kuti kulankhula kungakhale kopulumutsa moyo kapena kwakupha?

17 Kulankhula kungakhale kopulumutsa moyo kapena kwakupha. Izi zinasonyezedwa mkati mwa kukangana kwa pakati pa mtundu Wachiisrayeli wa Efraimu ndi Woweruza Yefita wa ku Gileadi. Kuti awadziŵe Aefraimu oyesa kuthaŵa kuwoloka Mtsinje wa Yordano, Agileadiwo anagwiritsira ntchito liwu lopyolera lakuti “Shiboleti,” lomwe lidali ndi mamvekedwe oyambira akuti “shi.” Amuna a Efraimu anadziulula okha kwa alonda Achigileadi pa madoko a Yordano mwakunena kuti “Siboleti” mmalo mwa “Shiboleti,” kutchula molakwa mamvekedwe oyambirira a liwulo. Monga chotulukapo, Aefraimu 42,000 anaphedwa! (Oweruza 12:5, 6) Mofananamo, zimene atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko angaphunzitse zingamveke zofanana ndi chinenero choyera kwa awo osazoloŵerana bwino lomwe ndi chowonadi cha Baibulo. Koma kulankhula mwanjira ya chipembedzo chonyenga kudzatsimikizira kukhala kwakupha pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.

Tikhalabe Ogwirizanitsidwa

18, 19. Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la Zefaniya 3:1-5?

18 Posonya kwa Yerusalemu wakale wosakhulupirika ndi mnzake wamakono, Chikristu Chadziko, Zefaniya 3:1-5 amati: ‘Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza! Sanamvera mawu, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wake. Akalonga ake mkati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa. Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe awo anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo. Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m’mawa ndi m’mawa awonetsera chiweruzo chake poyera, chosasoŵa kanthu; koma wosalungama sadziŵa manyazi.’ Kodi mawu amenewo amatanthauzanji?

19 Onse aŵiri Yerusalemu wakale ndi Chikristu Chadziko chamakono anampandukira Yehova ndikudziipsa okha ndi kulambira konyenga. Kuchita zoipa kwa atsogoleri awo kunatulukapo kupondereza. Mosasamala kanthu ndi machenjezo obwerezabwereza a Mulungu, iwo sanamvetsere ndipo sanayandikire kwa iye. Akalonga awo akhala mikango yolusa, nanyalanyaza chilungano mouma khosi. Mofanana ndi mimbulu yolusa, oweruza awo aluluza chilungamo. Ansembe awo ‘aipsa malo opatulika, napotoza chilamulo’ cha Mulungu. Chotero Yehova ali pafupi ‘kusonkhanitsa amitundu ndi kumemeza maufumu, kotero kuti awatsanulire kulunda kwake, mkwiyo wake wonse waukali.’​—Zefaniya 3:8.

20. (a) Kodi muyenera kuchitanji kuti mukapulumuke pa tsiku la mkwiyo wa Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene mungakhalire ndi chiyembekezo chakusangalala ndi madalitso amuyaya ochokera kwa Mulungu?

20 Tsiku la mkwiyo wa Yehova likufika mofulumira. Chotero, kuti mupulumuke kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu, phunzirani ndikulankhula chinenero choyera osachedwa. Ndikokha mwakutero mpamene mungapeze chitetezo ku ngozi yauzimu tsopano ndi ku tsoka la dziko lonse lomafika mofulumira. Mboni za Yehova zikulengeza tsiku la mkwiyo wa Mulungu ndi uthenga wosangalatsa wa Ufumu wake. Ha, iwo amakondwa chotani nanga polankhula za ulemerero wa ufumu wake! (Salmo 145:10-13) Gwirizanani nawo, ndipo mukhoza kuyembekezera kusangalala ndi moyo wamuyaya ndi madalitso ena ochokera kwa Woyambitsa chinenero choyera, Mfumu Ambuye Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndi njira zina ziti zophunzirira chinenero choyera?

◻ Kodi nchifukwa ninji kulankhula chinenero choyera kuli kopindulitsa?

◻ Kodi nchiyani chimene chingachitike ngati simumagwiritsira ntchito chinenero choyera mokhazikika?

◻ Kodi ndimotani mmene munthu angapulumukire pa tsiku la mkwiyo wa Yehova ndi kusangalala ndi madalitso amuyaya?

[Chithunzi patsamba 16]

Gideoni ndi amuna ake akuomba malipenga awo ndi kukweza miuni yawo

[Chithunzi patsamba 18]

Kuchokera 1879 kunka mtsogolo kunavumbulidwa poyera kuti Charles Taze Russell ndi anzake ankagwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kupititsa patsogolo chinenero choyera

[Zithunzi patsamba 20]

Kodi ndinu ogwirizana ndi Mboni za Yehova m’kulankhula chinenero choyera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena