Pomalizira Pake—Chilungamo kwa Onse
“Tidzayesetsa kumvetsera m’njira yatsopano . . . kwa anthu ovulazidwa, anthu ankhaŵa, anthu amene anataya chiyembekezo chakuti adzamvedwa. . . . Chimene chatsala ndicho kutsatira malamulo: kuonetsetsa pomalizira pake kuti monga momwe anthu onse amabadwira ndi ulemerero wolingana pamaso pa Mulungu, onse amabadwa ndi ulemerero wolingana pamaso pa anthu.”—Pulezidenti wa dziko la United States, Richard Milhous Nixon, mawu ake oyamba pamwambo womlumbiritsa, January 20, 1969.
PAMENE mafumu, mapulezidenti, ndi nduna zazikulu ayamba udindo wawo, iwo amakonda kukamba za chilungamo. Richard Nixon, pulezidenti wakale wa United States, anachitanso chimodzimodzi. Koma mawu ake onenedwa mwalusowo amakhala opanda pake powapenda ndi zimene zinachitikadi. Ngakhale kuti analonjeza ‘kutsatira malamulo,’ Nixon pambuyo pake anapezedwa ndi mlandu wa kuswa malamulo ndipo anamkakamiza kuchoka paudindo wake. Papita zaka makumi atatu tsopano ndipo ‘anthu ovulazidwa, ankhaŵa, ndi otaya chiyembekezo’ akufuulabe kuti amvedwe.
Kumvetsera anthu ameneŵa ndi kusamalira zosoŵa zawo nkovuta, monga momwe atsogoleri osaŵerengeka ofunadi kuchitapo kanthu apezera. Mawu akuti ‘chilungamo kwa onse’ akhala cholinga chovuta kuchikwaniritsa. Ngakhale zili motero, zaka mazana ambiri zapitazo, lonjezo lina linaperekedwa limene tiyenera kulimvetsera—lonjezo lapadera lonena za chilungamo.
Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Mulungu anatsimikizira anthu Ake kuti adzawatumizira “mtumiki” amene Mulungu iyemwini adzasankha. “Ndaika mzimu wanga pa Iye,” anawauza motero Yehova. ‘Iye adzadzetsera amitundu chiweruziro [“chilungamo,” NW].’ (Yesaya 42:1-3) Kulibe wolamulira waumunthu amene angapereke chilengezo chachikulu ngati chimenecho, chimene chingatanthauze kuti kudzakhala chilungamo chosatha kwa mtundu uliwonse. Kodi tingalikhulupirire lonjezo limeneli? Kodi cholinga chachilendo chimenechi chingakwaniritsidwe?
Lonjezo Limene Tingalikhulupirire
Lonjezo limakhala lodalirika monga momwe wolonjezayo alili. Panopo, si wina koma Mulungu Wamphamvuyonse amene akulengeza kuti “mtumiki” wake adzakhazikitsa chilungamo padziko lonse lapansi. Mosiyana ndi andale, Yehova samangolonjeza mwachabe. ‘Iye sakhoza kunama,’ limatitsimikizira motero Baibulo. (Ahebri 6:18) “Chimene ndasankha kuchita chidzachitika,” akutero Mulungu motsimikizira.—Yesaya 14:24, Today’s English Version.
Mbiri ya “mtumiki” wosankhidwa wa Mulungu, Yesu Kristu, ikulimbitsanso chidaliro chathu palonjezo limenelo. Uyo amene angakhazikitse chilungamo ayenera kukonda chilungamo ndi kutsatira chilungamo. Yesu anasiya mbiri yabwino kwambiri monga munthu amene ‘anakonda chilungamo ndi kudana nacho choipa.’ (Ahebri 1:9) Zimene iye ananena, makhalidwe ake, ndipo ngakhale mmene anafera, zonse zinapereka umboni wakuti analidi munthu wolungama. Pa imfa ya Yesu, msilikali wina wachiroma, amene mwachionekere anaona Yesu akuzengedwa mlandu ndi kuphedwa, anasonkhezereka kunena kuti: “Zoonadi munthu uyu anali wolungama.”—Luka 23:47.
Kuwonjezera pa kutsatira chilungamo iyemwini, Yesu anatsutsa chisalungamo chimene chinali chofala kwambiri m’tsiku lake. Iye anachita zimenezi mwa kuphunzitsa chilungamo chenicheni kwa aliyense wofuna kumva, osati mwa kuukira boma kapena mwa chipanduko. Ulaliki wake wa pa Phiri ndiwo mafotokozedwe aluso a mmene chilungamo choona chiyenera kuchitidwira.—Mateyu, machaputala 5-7.
Yesu anachita zimene anaphunzitsa. Iye sananyansidwe ndi anthu ovutika akhate, “anthu onyozeka” pakati pa Ayuda. M’malo mwake, analankhula nawo, kuwakhudza, ndiponso ngakhale kuwachiritsa. (Marko 1:40-42) Anthu onse amene anakumana nawo, kuphatikizapo osauka ndi otsenderezeka, anali ofunika kwa iye. (Mateyu 9:36) Iye anawauza kuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.”—Mateyu 11:28.
Chachikulu kwambiri nchakuti Yesu sanadzilole kugwera m’chisalungamo chomzinga kapena kukwiya nacho. Iye sanabwezere choipa pachoipa. (1 Petro 2:22, 23) Ngakhale pamene anali kumva ululu waukulu, iye anapemphera kwa Atate wake wakumwamba kaamba ka asilikali enieniwo amene anampachika. Iye anati: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.” (Luka 23:34) Ndithudi, Yesu ‘anafotokoza bwino za chilungamo kwa akunja.’ (Mateyu 12:18, NW) Chitsanzo cha Mwana weniweniyo wamoyo wa Mulungu ndiye umboni waukulu koposa wakuti Mulungu akufuna kukhazikitsa dziko lachilungamo.
Chisalungamo Chingathetsedwe
M’dziko lamakonoli mulinso umboni weniweni wakuti chisalungamo chingathetsedwe. Mboni za Yehova, aliyense payekha, komanso monga gulu, zimayesetsa kugonjetsa tsankhu, kusankhana mafuko, ndi chiwawa. Talingalirani za chitsanzo chotsatirachi.
Pedroa ankakhulupirira kuti kuukira ulamuliro ndiyo njira yokha yodzetsera chilungamo ku Basque Country, chigawo cha ku Spain komwe ankakhala. Pofuna kuchita zimenezi iye analoŵa m’gulu lauchigaŵenga limene linakamphunzitsa zausilikali ku France. Atamaliza maphunziro ake, analangizidwa kulinganiza gulu lauchigaŵenga kuti akaphulitse mudzi wa apolisi. Pamene apolisi anamgwira, gulu lake linali litayamba kale kukonzekera ndi mabomba. Anakhala m’ndende miyezi 18, koma ngakhale pamene anali m’ndendemo iye anapitirizabe ndale zake, kunyanyala nawo chakudya ndiponso panthaŵi ina kudzicheka pamfundo za manja ake.
Pedro ankaganiza kuti anali kumenyera chilungamo. Kenako anadziŵa Yehova ndi zolinga zake. Pamene Pedro anali m’ndende, mkazi wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo pamene anamasulidwa, mkazi wakeyo anamuitanira ku msonkhano wina wa Mboni za Yehova. Iye anasangalala kwambiri ndi chochitikacho kotero kuti anapempha kuti akhale ndi phunziro la Baibulo, phunziro limene linamchititsa kusinthiratu maganizo ake ndi njira yake ya moyo. Pomalizira pake, mu 1989, Pedro ndi mkazi wake anabatizidwa.
“Ndikuthokoza Yehova kuti sindinaphepo aliyense pazaka zomwe ndinali chigaŵenga,” Pedro akutero. “Tsopano ndimagwiritsira ntchito lupanga la mzimu wa Mulungu, Baibulo, pouza anthu uthenga wa mtendere weniweni ndi chilungamo—uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” Osati kale kwambiri, Pedro, amene tsopano akutumikira monga mkulu mumpingo wa Mboni za Yehova, anachezera mudzi uja wa apolisi umene anafuna kuuwononga. Panthaŵiyi anapitako kuti akalalikire uthenga wamtendere m’mabanja a pamudzipo.
Mboni za Yehova zimasintha motero chifukwa chakuti zikufunitsitsa dziko lolungama. (2 Petro 3:13) Ngakhale kuti zimalikhulupirira kotheratu lonjezo la Mulungu lakuti adzadzetsa dzikolo, izo zimadziŵa kuti ziyeneranso kutsatira chilungamo. Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti Mulungu amafuna kuti tichite mbali yathu.
Kubzala Mbewu za Chilungamo
Zoonadi, tikakumana ndi chisalungamo, tingalire kuti: “Ali kuti Mulungu wa chilungamo?” Kumeneko kunali kulira kwa Ayuda a m’tsiku la Malaki. (Malaki 2:17, NW) Kodi Mulungu anamva dandaulo lawo? Ayi, koma ‘linamlemetsa’ chifukwa chakuti, kuwonjezera pazinthu zina, iwo eniwo sanakhulupirike kwa akazi awo amene anali atakalamba, kuwasudzula pankhani zazing’onong’ono. Yehova anasonyeza kusamala kwake za ‘akazi a ubwana wawo, amene anawachitira chosakhulupirika, chinkana iwo ndiwo anali anzawo, akazi a pangano lawo.’—Malaki 2:14.
Kodi tingadandauledi za chisalungamo ngati ife enife tikuchita chisalungamo? Ndithudi, ngati tiyesa kutsanzira Yesu mwa kuchotsa tsankhu ndi kusankhana mafuko m’mitima mwathu, mwa kukhala achikondi kwa onse, ndiponso mwa kusabwezera choipa pachoipa, tidzasonyeza kuti timakondadi chilungamo.
Ngati tikufuna kututa chilungamo, Baibulo limatiuza ‘kubzala m’chilungamo.’ (Hoseya 10:12) Chipambano chilichonse pa kugonjetsa chisalungamo mumtima nchofunika kwambiri kaya chikhale chaching’ono motani. Monga momwe Martin Luther King, Wamng’ono, analembera m’kalata yake yotchedwa Letter From Birmingham Jail, “chisalungamo cha kwina kulikonse chimadodometsa chilungamo kwina kulikonse.” Awo amene ‘akufuna chilungamo’ ndiwo anthu amene Mulungu amasankha kuti adzaloŵe m’dziko lake latsopano lolungama limene lili pafupi kudza.—Zefaniya 2:3.
Sitingamange chiyembekezo chathu cha chilungamo pamaziko osalimba a malonjezo a anthu, komabe tingakhulupirire mawu a Mlengi wathu wachikondi. Ndiye chifukwa chake Yesu anauza otsatira ake kuti apitirizebe kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze. (Mateyu 6:9, 10) Yesu, Mfumu yoikidwa ya Ufumuwo, “adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.”—Salmo 72:12, 13.
Ndithudi, chisalungamo chidzatha. Ulamuliro wa Kristu padziko lonse lapansi udzathetsa chisalungamo kosatha, monga momwe Mulungu akutitsimikizirira kudzera mwa mneneri wake Yeremiya kuti: “Nthaŵi ilinkudza pamene ndidzakwaniritsa lonjezo limene ndinalonjeza . . . Panthaŵiyo ndidzasankha mbadwa yolungama ya Davide kukhala mfumu. Mfumuyo idzachita choyenera ndi cholungama m’dziko lonse.”—Yeremiya 33:14, 15, TEV.
[Mawu a M’munsi]
a Dzina lasinthidwa.