Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chololedwa pa Sabata?
NDIPASABATA lina pamene Yesu akuchezetsa sunagoge pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Mwamuna wina wopuwala dzanja lamanja ali pamenepo. Alembi ndi Afarisi akuyang’anitsitsa kutiawone ngati Yesu adzamchiritsa. Potsirizira iwo akufunsa kuti: “Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku lasabata?”
Atsogoleri achipembedzo Achiyuda amakhulupira kuti kuchiritsa kuli kololeka pa Sabata kokha ngati moyo uli paupandu. Mwachitsanzo, iwo amaphunzitsa kuti, pa Sabata sikuli kololeka kukonza fupa kapena kumanga mabandeji pobzyongonyoka. Chotero alembi ndi Afarisi akukaikira Yesu moyesayesa kumpezera chifukwa.
Komabe, Yesu, akuzindikira maganizo awo. Panthawi imodzimodziyo, iye akuzindikira kuti ali ndi lingaliro lonkitsa, ndi losagwirizana ndi malemba ponena za chimene chima phatikizapo kuswa lamulo la tsiku la Sabata loletsa kugwira ntchito Chotero Yesu akuyambitsa chochitika chodzutsa mkangano mwa kuuza mwamuna wopuwala dzanjayo kuti: “Nyamu ka, nuimirire pakatipo.”
Tsopano, potembenukira kwa alembi ndi Afarisi, Yesu akuti: “Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m’dzenje tsiku lasabata, kodi sadzaigwira ndi kuitulutsa?” Popeza kuti nkhosa imaimira chuma choikiziridwa, iwo sakanaisiya m’dzenjemo kufikira tsiku lotsatira, mwinamwake ikanadwala ndi kutayikiridwa ndi mtengo wake. Ndi iko komwe, Malemba amati: “Wolungama asamalira moyo wa choweta chake.”
Akumasonyeza kufananako, Yesu akupitirizabe kuti: “Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkololeka kuchita zabwino tsiku lasabata.” Atalephera kutsutsa ganizo lomvekera bwinolo, lachifundo, atsogoleri achipembedzowo akhala chete.
Mwaukali, kuphatikizapo chisoni chifukwa cha kupusa kwawo kwaliuma, Yesu akuunguzaunguza pa iwo onse. Pamenepo ati kwa mwamunayo: “Tansa dzanja lako.” Ndipo iye akulitansa ndipo dzanjalo lichiritsidwa. Mmalo mwa kukondwera kuti dzanja la munthuyo labwezeretsedwa, Afarisi atuluka mwamsanga nachita chiwembu ndi otsatira chipani cha Herode kupha Yesu. Mwachiwonekere chipani chandale zadziko chimenechi nchopangidwa ndi mamembala a Asaduki achipembedzo. Mwachizolowezi chipani chandale za dziko chimenechi ndi Afarisi amatsutsana poyera, koma ali ogwirizana nganga nga m’kutsutsana kwawo ndi Yesu. Mateyu 12:9-14; Marko 3:1-6; Luka 6:6-11; Miyambo 12:10; Eksodo 20:8-10.
◆ Kodi nchiyani chimene chinali mkhalidwe wa chochitika chotsutsana nacho pakati pa Yesu ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda?
◆ Kodi nchiyani chimene Ayuda anakhulupirira ponena za kuchiritsa pa Sabata?
◆ Kodi ndifanizo lotani limene Yesu anagwiritsira ntchito kutsutsa malingaliro awo olakwa?