Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 December tsamba 5
  • Mbali Yatsopano pa Misonkhano ya Mkati mwa Mlungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mbali Yatsopano pa Misonkhano ya Mkati mwa Mlungu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mungazime Nyali Yofuka?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kuloŵa kwa Kristu Kolakika m’Yerusalemu
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuloŵa m’Yerusalemu Kwachipambano kwa Kristu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mfumu Inalowa mu Yerusalemu Itakwera pa Bulu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 December tsamba 5
Buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu la mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi la Study Edition la pa intaneti

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mbali Yatsopano pa Misonkhano ya Mkati mwa Mlungu

Kuyambira m’mwezi wa January 2018, pa misonkhano ya mkati mwa mlungu padzakhala gawo lokhala ndi mfundo, zithunzi, mavidiyo ndi zinthu zina. Zinthu zimenezi zikupezeka mu Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi la Study Edition la pa intaneti. Tidzakhala ndi gawoli ngakhale kuti tilibe Baibulo la Study Edition m’chinenero chathu. Sitikukayikira kuti zinthu zimenezi zidzakuthandizani kwambiri pokonzekera misonkhano. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti zidzakuthandizani kuti muyandikire Atate wathu wachikondi Yehova.

MFUNDO ZIMENE NDIKUPHUNZIRA

Mbaliyi ili ndi zotithandiza kudziwa zinthu zokhudza chikhalidwe, malo komanso mawu omwe agwiritsidwa ntchito m’mavesi ena a m’Baibulo.

Mateyu 12:20

Nyale yofuka: Kale, nyale zambiri zomwe ankagwiritsa ntchito zinkakhala zoumba ndipo ankaikamo mafuta a maolivi. Nyalezi zinkakhala ndi kachingwe komwe kankayaka chifukwa cha mafutawo. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “nyale yofuka,” angatanthauze chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima ndipo lawi lake likuzilala kapena lazima. Ulosi wa pa Yesaya 42:3 unkasonyeza kuti Yesu adzakhala wachifundo ndipo sadzazimitsa chiyembekezo cha anthu odzichepetsa komanso oponderezedwa.

Mateyu 26:13

Ndithu: Mawu achigiriki akuti a·menʹ omwe anachokera ku mawu achiheberi, amatanthauza kuti “zikhale momwemo” kapena “zoonadi.” Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito mawu amenewa pofuna kutsimikizira kuti zimene wanena, walonjeza kapena kulosera ndi zoona komanso zodalirika. Zikuoneka kuti m’Baibulo lonse, ndi Yesu yekha amene anagwiritsa ntchito mawu akuti “ndithu,” kapena kuti ame, m’njira imeneyi. Mawu amene ananenedwa motsatizana (a·menʹ a·menʹ), monga mmene zili mu Uthenga Wabwino wa Yohane, anamasuliridwa kuti “ndithudi.”​—Yoh. 1:51.

ZITHUNZI NDI MAVIDIYO

Mbaliyi ili ndi zithunzi, mavidiyo opanda mawu komanso mavidiyo amakatuni ofotokoza nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo.

Betefage, Phiri la Maolivi ndi Yerusalemu

Vidiyo yachiduleyi ikusonyeza njira yochokera m’mudzi wotchedwa Betefage, umene panopa umadziwika kuti et-Tur. Njirayi inayenda kuchokera m’mudziwu n’kukadutsa pamwamba pa Phiri la Maolivi kulowera ku Yerusalemu. Mudzi wa Betaniya unali chakum’mawa kwa Betefage m’mbali mwa Phiri la Maolivi. Akakhala ku Yerusalemu, Yesu ndi ophunzira ake ankakagona ku Betaniya, komwe panopa kuli tawuni ya el-ʽAzariyeh (El ʽEizariya), lomwe ndi dzina lachiarabu lotanthauza “Kwawo kwa Lazaro.” Zikuoneka kuti Yesu ankakagona kunyumba kwa Marita, Mariya ndi Lazaro. (Mat. 21:17; Maliko 11:11; Luka 21:37; Yoh. 11:1) Akamapita ku Yerusalemu, Yesu ayenera kuti ankadutsa njira imene yasonyezedwa m’vidiyoyi. Pa Nisani 9 mu 33 C.E., pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu atakwera bulu n’kudutsa pa Phiri la Maolivi, ayenera kuti ankachokera ku Betefage.

Njira imene Yesu ankadutsa akamachokera ku Betaniya kupita ku Yerusalemu
  1. Njira yochokera ku Betaniya kupita ku Betefage

  2. Betefage

  3. Phiri la Maolivi

  4. Chigwa cha Kidironi

  5. Kachisi wa Paphiri

Msomali M’fupa Lachidendene

Msomali m’fupa lachidendene

Ichi ndi chithunzi chongoyerekezera chosonyeza msomali wautali masentimita 11.5 (mainchesi 4.5) utalowa mufupa lachidendene. Fupa lenileni linapezeka m’chaka cha 1968, pamene anthu ena ankafukula zinthu zakale chakumpoto kwa Yerusalemu ndipo zikuoneka kuti fupali ndi la m’nthawi ya Aroma. Fupa lokhala ndi msomali limeneli ndi umboni wakuti pa nthawiyo ankagwiritsa ntchito misomali akamapha anthu powakhomerera pamtengo. Msomaliwu uyenera ndi wofanana ndi umene asilikali achiroma anagwiritsa ntchito pokhomerera Yesu pamtengo. Fupali linapezeka m’bokosi linalake lamwala, lomwe munaikidwa mafupa a munthu wina amene anaphedwa. Zimenezi zikusonyeza kuti munthu akaphedwa mochita kukhomereredwa pamtengo ankaikidwanso m’manda.​—Mat. 27:35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena