MUTU 22
Ophunzira 4 Anakhala Asodzi a Anthu
MATEYU 4:13-22 MALIKO 1:16-20 LUKA 5:1-11
YESU ANAITANA OPHUNZIRA KUTI AZIMUTSATIRA NTHAWI ZONSE
ASODZI A NSOMBA ANAKHALA ASODZI A ANTHU
Yesu atathawa anthu a ku Nazareti omwe ankafuna kumupha anapita mumzinda wa Kaperenao. Mzindawu unali pafupi ndi nyanja ya Galileya yomwe inkadziwikanso kuti “nyanja ya Genesarete.” (Luka 5:1) Zimenezi zinakwaniritsa ulosi womwe unalembedwa m’buku la Yesaya wakuti anthu okhala m’mbali mwa nyanja ya Galileya adzaona kuwala kwakukulu.—Yesaya 9:1, 2.
Atafika ku Galileya, Yesu anapitiriza kulalikira kuti: “Ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Kenako Yesu anakumananso ndi ophunzira ake 4 aja. Ophunzira amenewa ndi amene ankayenda ndi Yesu koma atachoka ku Yudeya n’kubwerera kwawo anayambanso kugwira ntchito yawo yopha nsomba. (Yohane 1:35-42) Koma tsopano imeneyi inali nthawi yoti ayambe kuyenda ndi Yesu nthawi zonse ndi cholinga choti awaphunzitse mmene angamalalikirire kuti adzapitirize ntchitoyi iye atabwerera kumwamba.
Pamene Yesu ankayenda m’mbali mwa nyanja anaona Simoni Petulo ndi m’bale wake Andireya komanso anthu ena akutsuka maukonde awo. Yesu anapita pomwe panali anthuwo n’kukwera m’boti la Petulo kenako anamuuza kuti akankhire botilo m’madzi. Botilo litayenda pang’ono, Yesu anakhala pansi n’kuyamba kuphunzitsa khamu la anthu limene linali m’mbali mwa nyanjayo mfundo za choonadi zokhudza Ufumu.
Kenako Yesu anauza Petulo kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” Koma Petulo ananena kuti: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse. Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.”—Luka 5:4, 5.
Ataponya maukondewo, anapha nsomba zambiri moti maukonde aja anayamba kung’ambika. Nthawi yomweyo anaitana anzawo amene anali m’boti lina lapafupi kuti adzawathandize. M’kanthawi kochepa, maboti awiriwo anadzaza ndi nsomba ndipo anayamba kumira. Ataona zimenezi, Petulo anagwadira Yesu n’kunena kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano, chifukwa ndine munthu wochimwa.” Koma Yesu anamuyankha kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”—Luka 5:8, 10.
Kenako Yesu anaitana Petulo ndi Andireya n’kuwauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.” (Mateyu 4:19) Anaitananso asodzi ena awiri, omwe anali ana a Zebedayo ndipo mayina awo anali Yakobo ndi Yohane. Nawonso anayamba kutsatira Yesu nthawi yomweyo. Choncho anthu 4 amenewa anasiya ntchito yawo yopha nsomba ndipo anakhala ophunzira oyambirira a Yesu.