Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 10/8 tsamba 19-21
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuphunzira Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuphunzira Baibulo?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukwaniritsa Zosoŵa Zanu Zauzimu
  • Kupeza Njira Yolondola
  • Thandizo m’Kuyandikira kwa Mulungu
  • Mphotho ya Kuyesayesa Kwanu
  • Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Mulungu?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 10/8 tsamba 19-21

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuphunzira Baibulo?

“PAMENE ndabwera kuchoka kusukulu, sindimafunanso kuphunzira. Ndimafuna kupita kunja kukaseŵera ndi mabwenzi anga!” Kameneko ndiko kanali kayankhidwe ka wachichepere wotchedwa Ken ku lingaliro lakuti adzithera nthaŵi ina akuphunzira Baibulo.

Mofanana ndi achichepere ambiri, mwinamwake inu simunachite zambiri m’phunziro laumwini Labaibulo. Mwinamwake mumakhulupirira Baibulo kukhala Mawu a Mulungu. Mungakhale mumapezeka pamisonkhano Yachikristu. Koma mungaganize kuti mumadziŵa kale zimene Baibulo limaphunzitsa. Kapena mungamazizwe kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji ndiyenera kuphunzira Baibulo? Kodi ndidzapatanji ku kuyesayesa kwangako?’

Kukwaniritsa Zosoŵa Zanu Zauzimu

Kufunsa mafunso oterowo sikolakwa kapena kupanda ulemu. Mosemphana kwenikweni, iko kungasonyeze kuti mukuyamba kuzindikira chimene Yesu anachitcha ‘chosowa [chanu] chauzimu.’ (Mateyu 5:3, NW) Uku sindiko kufunafuna kopanda phindu. Monga momwe The New English Bible ikumasulira vesili, uko kuli “kufuna Mulungu”—kufuna kudziŵa Mulungu mwathithithi ndi kumvetsetsa zifuno zake. Mwachitsanzo, pamene munali mwana wamng’ono, makolo anu angakhale anakuphunzitsani chowonadi choyambirira cha Baibulo. Mwinamwake munavomereza zimene anakuuzanizo mosakaikira konse. Koma pamene munakula, inu mungakhale munafuna “kutsimikizira zinthu zonse”—kudziŵa ngati zimene mwaphunzitsidwazo nzowona kapena ayi.—1 Atesalonika 5:21, NW.

Pamenepo kachiŵirinso, mwinamwake simunaleredwe m’banja lopembedza. Kodi ichi chikutanthauza kuti mulibe chosoŵa chauzimu? Kutalitali! Talingalirani za mkhalidwe m’dziko lina kumene kusakhulupirira Mulungu kwakhala kukuchilikizidwa kwa nthaŵi yaitali. M’zaka zaposachedwapa achichepere akumeneko asonyeza chikondwerero chachikulu m’chipembedzo. Munthu wina wobukitsa kutsutsa chipembedzo anasonya chala, pakati pa zinthu zina, ku “kulephera kwa osakhulupirira Mulungu kupereka mayankho okhutiritsa ku mafunso onena za tanthauzo la kugwiritsidwa mwala ndi kuvutika m’moyo.” Mungadzipeze inu eninu mukufunsa mafunso ofananawo—umboni wakuti muli ndi chosoŵa chauzimu.

Komabe, sizipembedzo zonse zimene zimapereka mayankho okhutiritsa. Mwachitsanzo, Manish wachichepere analeredwa monga Mhindu, wokhulupirira milungu mamiliyoni ambiri. Komabe, iye akuvomereza kuti: “Ndinayamba kukaika kuti, ‘Kodi Mulungu ndiye yani?’” Ndipo achichepere ambiri amene aleredwera m’zipembedzo za Chikristu Chadziko apeza kufufuza mayankho okhutiritsa kukhalanso kopusitsa. Kodi tinganke kuti? Yesu Kristu akuyankha kuti: ‘Mawu anu [a Mulungu] ndi chowonadi.’—Yohane 17:17.

Chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu, Baibulo, chingakhutiritse ludzu lanu la chowonadi chauzimu. Icho chidzayankha mafunso anu onena za kuzindikira Mulungu, zifukwa za mikhalidwe yadziko imene ilipoyi, ndiziyembekezo zanu za mtsogolo. Kunena zowona, mungakhale munaleredwa ndi makolo amene ndi Mboni za Yehova, ndipo inu mungaganize kuti mukudziŵa kale ‘chowonadi’ kumlingo winawake. Koma kodi mukhoza “kuzindikira . . . kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama” kwa chowonadi cha Baibulo, kapena kodi chidziŵitso chanu nchapamwamba pokha? (Aefeso 3:18) Ngati ndemanga yomalizirayo ikunena za inu, pamenepo mufunikira ‘kuzindikira chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro,’ mwakuphunzira Baibulo mokwanira.—Aroma 12:2.

Kupeza Njira Yolondola

Kodi munayamba mwapatsidwapo njira yolakwa kunka kumalo kumene mukufuna? Nthaŵi ndi kuyesayesa kotaikako kungakhale kokhumudwitsa. Komabe, miyoyo yonse ya anthu ambiri achichepere ikulinga kunjira yolakwayo! Baibulo limati: ‘Iripo njira yowoneka kwa mwamuna ngati yowongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa.’—Miyambo 14:12.

Mwachitsanzo, talingalirani za nkhani ya chisembwere chakugonana. Msungwana wina wa zaka 14 zakubadwa anati: “Palibe chinthu chabwino. Iwo ali kokha malingaliro osiyana.” Kunena zowona, chikhumbo chakulawa kugonana nchamphamvu, makamaka pamene mudakali wachichepere. Koma ngati sichilamuliridwa, chikhumbo chimenechi chingakutsogolereni ku “njira za imfa.” Chaka chirichonse, achichepere 2.5 miliyoni a ku U.S. amagwidwa ndi matenda opatsirana mwakugonana. Asungwana ambiri achichepere amakhala amayi asadakwatiwe—kapena amapha makanda awo mwakuchotsa mimba! Ndipo ngakhale kuti mimba kapena matenda angapeŵedwe, kugonana ukwati usanakhale nthaŵi zonse kumabweretsa kupanda chiyanjo cha Mulungu.—1 Atesalonika 4:3.

Pamenepo kodi nkumakhumudwiranji mu “njira za imfa”? Baibulo limapereka chitsogozo chachindunji chokuthandizani ‘kuthawa zilakolako za unyamata.’ (2 Timoteo 2:22) Ichi chimaphatikizapo ‘kufetsa,’ osati zilakolako zachibadwa za unansi wakugonana muukwati wolemekezeka, koma zikhumbo zakugonana kwachisembwere. (Akolose 3:5) Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kukwaniritsa chimenechi. Kungakupatseni mphamvu yamakhalidwe yokuthandizani kuthawa pa zoipa—ngakhale ngati choipacho chingawoneke kukhala chosangalatsa. Iko kungakhoze ‘kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa anyamata [kapena anamwali] kudziwa ndi kulingalira’ kotero kuti apeŵe mikhalidwe imene ingatsogolere ku mkhalidwe wachisembwere.—Miyambo 1:4.

Dan wachichepere ali mmodzi amene wapindula ndi kuphunzira Baibulo. Pamene akuvomereza kuti achichepere achisembwere amawoneka kukhala ndi zosangalatsa, iye akuti wawonanso “makanda akubadwa kunja kwa ukwati, matenda opatsana mwakugonana, ndi mavuto ena ambiri.” Iye akufunsa kuti: “Ndikanakhala kuti sindinaphunzire Baibulo, kodi ineyo ndikanakhala ndikutani?” Baibulo lingakupulumutseni nanunso ku “njira za imfa.”

Thandizo m’Kuyandikira kwa Mulungu

Pamene kuli kwakuti achichepere ambiri lerolino amati amakhulupirira Mulungu, chikhulupiriro cha Mulungu weniweni chimatha pamene achichepere akukula. Nkhani ya m’magazine a Adolescence inalongosola kuti kwa achichepere ena, “lingaliro la Mulungu nlosatsimikizirika.” Zipembedzo zambiri zapangitsa Mulungu kuwoneka kukhala wosakhalako mwakubisa nsonga yakuti Mulungu ali ndi dzina. Ndiiko komwe, kodi mungadzimve motani kukhala woyandikira kwa munthu amene simum’dziŵa dzina?

Komabe, Baibulo limavumbula kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, likumaligwiritsira ntchito nthaŵi zoposa 7,000! (Salmo 83:18) Kudziŵa dzina limenelo kumatsegula njira kwa inu ya kukhala ndi unansi waumwini ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Koma ichi chimatanthauza zambiri osati kokha kukhala ndi chikondwerero wamba m’Baibulo. 1 Mbiri 28:9 imati: “Ukamfunafuna Iye udzampeza.” Ichi chikutanthauza kukumba m’Malemba kuyesayesa kudziŵa Yehova mwathithithi.

Kodi mwachita tero? Mwachitsanzo, kodi mungalongosole chifukwa chake Baibulo limalankhula za Yehova kukhala ali ndi “maso,” “makutu,” “nkhope,” ndi “mkono”? (1 Petro 3:12; Ezekieli 20:33) Kodi Baibulo silimanena kuti “Mulungu ndiye mzimu”? (Yohane 4:24) Kapena kodi mumazindikira mlingo umene Mulungu aliri ndi kuthekera kwa kukuwonani, kudziŵa zimene mukufuna kunena ngakhale musanazinene? (Salmo 139:4) Ndipo kodi bwanji ponena za mikhalidwe yaikulu ya Yehova, chikondi, nzeru, chilungamo, ndi mphamvu? Kodi mungalongosole chimene chinali chisonyezero chachikulu koposa cha chikondi cha Mulungu? (Yohane 3:16) Kodi mumadziŵa kusiyana pakati pa mzimu wa Mulungu ndi mphamvu yake? (Mika 3:8) Kodi mungatsimikizire kuti Mulungu ali ndi malingaliro—ndipo kuti nkotheka kukwiitsa malingaliro ake?—Salmo 78:40.

Pali njira imodzi yokha yoyankhira mafunso amenewo—mwakuphunzira Baibulo. Luther wachichepere waphunzira kuti “mwakuphunzira Mawu Ake, ndingakhoze ‘kuona’ umunthu wa Yehova ndi mtundu wa munthu amene iye ali.” (Yerekezerani ndi Yobu 42:5.) Mofananamo Jaquella wafikira pakudziŵa bwino Mulungu. Mwakuphunzira Baibulo, iye wafikira pa kuyamikira “kuti Yehova angachilikize chimene amanena. Pamene alonjeza chinthu, iye samaswa lonjezo lake; iye samanama.”—Tito 1:2.

Mphotho ya Kuyesayesa Kwanu

Kuphunzira Baibulo kumaloŵetsamo kuyesayesa ndi kupereka nsembe nthaŵi yanu ina yaufulu. Kuyamba kungakhale kovuta ndipo mwinamwake kungabweretse chitonzo chochokera kwa banja ndi mabwenzi. Koma yang’anani pa mphotho zake. Kuphunzira Baibulo kokhazikika kwathandiza Paula. Iye akuti, ndapanga “unansi wathithithi ndi Yehova, abale anga Achikristu, ndi banja langa.” Sandy akuti kunamthandiza “kukulitsa chikumbumtima” chimene chimavomereza ngakhale ku zinthu zazing’ono. Iye akuti: “Ndingalingalire za malemba kapena malamulo amakhalidwe abwino amene amanditheketsa kusankha zimene ndingapenyerere pa TV.” Ndipo kodi mukumukumbukira Ken amene watchulidwa kuchiyambi kwa nkhani ino? Iye anayamba kuŵerenga Baibulo mwakaŵirikaŵiri ndipo akuti: “Kuchuluka kumene ndinaŵerenga ndiko kuchuluka kumene ndinasangalatsidwa nalo, ndipo zinamvekeranso kukhala zanzeru mowonjezereka.” Ken anafulumizidwa kukhala mtumiki wobatizidwa wa Mulungu.

Kodi bwanji osaphunzira Baibulo mosamalitsa? Kuwoneni kukhala chitokoso. Afunseni makolo anu kapena chiŵalo cha mpingo wakumaloko wa Mboni za Yehova kukuthandizani kuyamba. Khalani wotsimikiza mtima ndipo musaleke. Gwiritsirani ntchito zimene mukuphunzira. Ndipo kumbukirani kuti: ‘Iye wopenyerera m’lamulo langwiro natero chipenyerere adzakhala wodala m’kuchita kwake.’—Yakobo 1:25.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

Kodi ‘mukuzindikira . . . kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama’ kwa chowonadi cha Baibulo, kapena kodi chidziŵitso chanu nchapamwamba pokha?

[Chithunzi patsamba 21]

mpingo Wachikristu angakuthandizeni kuyamba ntchito yoŵerenga Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena