-
Tonsefe Tikhale Ogwirizana Ngati Yehova ndi YesuNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | June
-
-
CHIKONDI NDI KUDZICHEPETSA ZINGATHANDIZE KUTHETSA TSANKHO
8. Kodi ndi mfundo iti imene imathandiza kuti Akhristu azigwirizana? Fotokozani.
8 Yesu anauza otsatira ake mfundo imene ingathandize kuti tizigwirizana kwambiri. Iye anati: “Nonsenu ndinu abale.” (Werengani Mateyu 23:8, 9.) Tinganene kuti tonsefe ndife “abale” chifukwa tonsefe ndi ana a Adamu. (Mac. 17:26) Koma pali chifukwa chinanso. Yesu ananena kuti ophunzira ake anali ngati abale ndi alongo chifukwa choti onse ankaona kuti Yehova ndi Atate wawo wakumwamba. (Mat. 12:50) Chinanso n’chakuti anakhala ngati banja limodzi lauzimu chifukwa choti chikondi ndi chikhulupiriro zinkawathandiza kukhala ogwirizana. N’chifukwa chake atumwi akamalemba makalata awo ankakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti ‘abale ndi alongo’ pofotokoza za Akhristu anzawo.—Aroma 1:13; 1 Pet. 2:17; 1 Yoh. 3:13.a
-
-
Tonsefe Tikhale Ogwirizana Ngati Yehova ndi YesuNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | June
-
-
a Mawu oti “abale” angagwiritsidwenso ntchito ponena za alongo. Mwachitsanzo, Paulo ananena m’kalata yake yopita kwa Aroma kuti akulembera “abale.” Koma mawu amenewa ankatanthauzanso alongo chifukwa ena mwa alongowo anawatchula mayina awo. (Aroma 16:3, 6, 12) Ndipotu Nsanja ya Olonda yakhala ikugwiritsa ntchito mawu oti ‘abale ndi alongo’ pofotokoza za Akhristu.
-