Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Nchifukwa ninji Yesu ananena kuti mtembenuki wa Afarisi “anamsandutsa mwana wa gehena woposa iwo kaŵiri”?
Mwachiwonekere, Akunja omwe anatembenuzidwa ku gulu la mpatuko la Chiyuda la Afarisi anali osamva kwambiri. Ena a iwo kumbuyoko angakhale anali opanda chivomerezo cha Mulungu, koma pa kukhala Afarisi, iwo anakhala osavomerezedwa kuŵirikiza kaŵiri, motsimikizirika kukhala pa ulendo wa ku chiwonongeko m’gehena.
Chigwa cha Hinomu chinali kum’mwera/kum’mwera cha kumadzulo kwa malinga a Yerusalemu. Panthaŵi zina chinagwiritsiridwa ntchito kaamba ka kulambira mafano ndi kupereka nsembe anthu. (2 Mbiri 28:1-3; 33:1-6; Yeremiya 32:35) Chotero anakhala malo otaya zinyalala, kuphatikizapo matupi a aupandu owonedwa monga osayenera kaamba ka kuikidwa ndi chiyembekezo cha chiukiriro.—Yerekezani ndi Mateyu 5:22.
The New Bible Dictionary (yolembedwa ndi J. D. Douglas, 1962) imanena kuti ‘chigwa cha Hinomu chinali kunja kwa Yerusalemu, kumene ana anali kuperekedwa nsembe ndi moto kwa Moleki. Icho chinakhala chisonyezero chaulosi cha chiweruzo ndipo kenaka chilango chotheratu.’ Jesuit John L. McKenzie, m’bukhu lake la Dictionary of the Bible (1965), akuwonjezera kuti: “Chifukwa cha [malo opatulika a mwambo a nsembe za anthu] amenewa Yeremiya anatemberera malowo ndipo ananeneratu kuti iwo adzakhala malo a imfa ndi chiwonongeko (7:32; 19:6 ff). Chigwachi chalozeredwako, osati ndi dzina mu Ye[saya] 66:24, monga malo kumene matupi akufa a anthu otsutsana ndi Yahweh anataidwa . . . M’mabukhu a chirabi, ngakhale kuli tero, moto wosatha suli kwenikweni chilango chosatha . . . [Gehena] ali malo kumene oipa amawonongedwa thupi ndi moyo, chimene mwinamwake chimafuula lingaliro la kuchotseratu (Mat 10:28).”
Pamene tiŵerenga mbiri zonga ngati Mateyu 15:1-8; Yohane 8:12-19, 31-41; 9:13-34; 11:45-53, tingamvetsetse nchifukwa ninji Yesu ananena kuti Afarisi anayenera chiwonongeko, chochitidwira chitsanzo ndi Gehena. Zowonadi, ena angalape ndi kupeza chivomerezo cha Mulungu, koma monga gulu, iwo ali oyenera chiwonongeko chosatha. Kristu ananena kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo mmene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa gehena woposa inu kaŵiri.”—Mateyu 23:15.
Zochuluka kotero kwa Ayuda a Chifarisi, koma ndimotani mmene awo amene adzakhala atembenuki adzakhalira ‘ana a gehena kuŵirikiza kaŵiri’ kuposa Afarisi? Atembenuki amenewa sanali Akunja omwe anali chabe omverera chifundo Ayuda kapena ngakhale awo omwe anatembenuzidwa ndipo anadulidwa. (Luka 7:2-10; Marko 7:24-30; Machitidwe 8:26-34; 10:1, 2) Ayi, Yesu sanali kulankhula ponena za atembenuki kupita ku Chiyuda koma atembenuki opita ku Chifarisi chonyenga. Nchiyani chimene mkhalidwe wawo unakhala?
Ena a iwo poyamba angakhale anali olakwa kwakukulu kapena alambiri opanda maziko a milungu ya ziwanda, chotero kukhala opanda chiyanjo koposa ndi Mulungu. Mwinamwake ena anali ngakhale m’mzera wa ku Gehena chifukwa iwo mwanjira ina yake analakwa motsutsana ndi mzimu wa Mulungu. (Mateyu 12:32) Ngati mkhalidwe wawo pamaso pa Yehova unali usanafike pa mlingo umenewo, iwo anatenga sitepi yopita ku mkhalidwe woipitsitsa. Iwo anatembenukira ku kutsatira mlingo wonkitsa wa Afarisi. Atembenuki amenewa anadzimiza iwo eni m’miyambo yonyenga ndi kawonekedwe konkitsa komwe kanalamulira mkhalidwe uliwonse wabwino ndi chowonadi chomwe atembenuki ena kupita ku Chiyuda angakhale anachipeza. Mwachiwonekere, atembenuki a Chifarisi amenewa anakhala onkitsa kuposa aphunzitsi awo oweruzidwawo. Chotero ngati Afarisi a Chiyuda anali “ana a gehena,’ atembenuki amenewa anali otero mowonjezereka kapena, monga mmene Yesu anachilongosolera icho, kuŵirikiza kaŵiri.
[Mapu/Chithunzi patsamba 31]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
MAPU A YERUSALEMU WA MU ZAKA ZA ZANA LOYAMBA
MBALI YA KACHISI
CHIGWA CHA HINOMU
(GEHENA)
[Chithunzi]
Mbali ya Chigwa cha Hinomu lerolino
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.