Mutu 4
Yesu Anabwera ndi Uthenga Wolimbikitsa
1. Kodi uthenga umene Yohane analemba ukupita kwa ndani, ndipo masiku ano ndani amene ayenera kuchita chidwi ndi uthengawu?
ALIYENSE amene amasonkhana ndi mpingo wa anthu a Mulungu masiku ano ayenera kuchita chidwi ndi uthenga umene uli m’mavesi otsatirawa. M’mavesi amenewa muli uthenga wosiyanasiyana ndipo ndi wofunika kwambiri panopa chifukwa “nthawi yoikidwiratu ili pafupi.” (Chivumbulutso 1:3) Tikatsatira mfundo za uthenga umenewu tidzapeza madalitso osatha. Uthengawu ukuyamba ndi mawu akuti: “Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7 ya m’chigawo cha Asia. Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa ‘Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,’ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7 yokhala pamaso pa mpando wake wachifumu. Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu.”—Chivumbulutso 1:4, 5a.
2. (a) Kodi “7” amaimira chiyani? (b) Kodi uthenga wopita ku “mipingo 7” ukugwiranso ntchito kwa ndani m’tsiku la Ambuye?
2 Apa Yohane akulembera “mipingo 7” imene yatchulidwa mu ulosiwu m’mavesi akutsogoloku. M’buku la Chivumbulutso, “7” ndi nambala imene yatchulidwa mobwerezabwereza. Nambalayi imasonyeza kuti zinthu ndi zokwanira, makamaka zinthu zokhudza Mulungu ndi mpingo wake wa Akhristu odzozedwa. Popeza kuti chiwerengero cha mipingo ya anthu a Mulungu padziko lonse chawonjezereka mpaka kufika masauzande ambiri m’tsiku la Ambuye, sitikukayikira kuti uthenga umene ukupita ku “mipingo 7” ya Akhristu odzozedwa, ukugwiranso ntchito kwa anthu onse a Mulungu masiku ano. (Chivumbulutso 1:10) Choncho, uthenga wa Yohane ndi wofunika kwambiri kumipingo yonse ya Mboni za Yehova ndiponso kwa anthu onse amene amasonkhana ndi Mboni kulikonse padziko lapansi.
3. (a) Kodi mawu oyamba a Yohane akusonyeza kuti “kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere” zimachokera kuti? (b) Kodi ndi mawu ati a mtumwi Paulo amene akufanana ndi mawu oyamba a Yohane?
3 “Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere” ndi makhalidwe osangalatsa kwambiri, makamaka tikadziwa kumene makhalidwewa akuchokera. Makhalidwewa amachokera kwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa yemwenso ndi “Mfumu yamuyaya,” amene wakhalapo “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (1 Timoteyo 1:17; Salimo 90:2) Mtumwi Yohane anatchulanso “mizimu 7.” Zimenezi zikutanthauza kuti mzimu woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, ikugwira ntchito mokwanira. Mzimu woyerawu umachita zimenezi ukamathandiza anthu kumvetsa ulosi ndiponso kuthandiza anthu onse amene akutsatira zimene ulosiwo ukunena kuti apeze madalitso. Uthenga wa Yohane ukusonyezanso kuti “Yesu Khristu” ali ndi udindo wofunika kwambiri. Ponena za iye, Yohane analemba kuti: “Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.” (Yohane 1:14) Choncho, m’mawu ake oyambirira, Yohane analemba mfundo zofanana ndi zimene mtumwi Paulo anatchula pomaliza kalata yake yachiwiri yopita kumpingo wa ku Korinto. Iye anati: “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu, chikondi cha Mulungu, komanso mzimu woyera umene mukupindula nawo limodzi, zikhale nanu nonsenu.” (2 Akorinto 13:14) Tiyeni tiyesetse kuti mawu amenewa azigwiranso ntchito kwa aliyense wa ife amene amakonda choonadi masiku ano.—Salimo 119:97.
“Mboni Yokhulupirika”
4. Pofotokoza za Yesu Khristu, kodi Yohane anagwiritsa ntchito mayina ati, ndipo n’chifukwa chiyani mayina amenewa ali oyenerera?
4 Yesu ndi waulemerero kwambiri m’chilengedwe chonse ndipo amaposedwa ndi Yehova yekha basi. Yohane anazindikira zimenezo ndipo anafotokoza za Yesu kuti ndi “‘Mboni Yokhulupirika,’ ‘Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,’ ndiponso ‘Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.’” (Chivumbulutso 1:5b) Mofanana ndi mwezi kumwamba, iye wakhazikika monga Mboni yaikulu kwambiri yotsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu. (Salimo 89:37) Atatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa yake yansembe, iye anali munthu woyamba kuukitsidwa n’kupatsidwa moyo wauzimu umene sungafe. (Akolose 1:18) Tsopano Yesu ali ndi Yehova kumwamba ndipo wakwezedwa kuposa mafumu onse a padziko lapansi. Wapatsidwanso “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18; Salimo 89:27; 1 Timoteyo 6:15) M’chaka cha 1914, iye anaikidwa kukhala Mfumu yolamulira pakati pa mitundu ya anthu padziko lapansi.—Salimo 2:6-9.
5. (a) Kodi Yohane anapitiriza bwanji kuyamikira Ambuye Yesu Khristu? (b) Ndani amene amapindula ndi mphatso ya moyo wangwiro wa Yesu, ndipo kodi Akhristu odzozedwa ali ndi mwayi wapadera wotani?
5 Yohane anapitiriza kuyamikira Ambuye Yesu Khristu ndi mawu omutamanda akuti: “Kwa iye amene amatikonda, amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo, n’kutipanga kukhala mafumu ndi ansembe kwa Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya. Ame.” (Chivumbulutso 1:5c, 6) Yesu anapereka moyo wake wangwiro n’cholinga choti anthu amene amam’khulupirira adzakhale ndi moyo wangwiro. Inunso amene mukuwerenga bukuli mukhoza kudzakhala ndi moyo wangwiro umenewo. (Yohane 3:16) Koma imfa yansembe ya Yesu inatsegula njira yoti Akhristu odzozedwa, monga Yohane, alandire madalitso apadera. Mulungu amawaona Akhristu amenewa kuti ndi olungama chifukwa cha nsembe ya Yesu ya dipo. Mofanana ndi Yesu, anthu a m’kagulu ka nkhosa sakhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi, ndipo anabadwanso mwa mzimu wa Mulungu. Iwo akuyembekezera kudzaukitsidwa ndi kudzakhala mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Yesu Khristu mu Ufumu wake. (Luka 12:32; Aroma 8:18; 1 Petulo 2:5; Chivumbulutso 20:6) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri, ndipo m’pake kuti Yohane analankhula mosangalala kuti ulemerero komanso mphamvu ndi za Yesu.
“Akubwera ndi Mitambo”
6. (a) Kodi Yohane analengeza chiyani ponena za ‘kubwera ndi mitambo’ kwa Yesu, ndipo kodi iye ayenera kuti anakumbukira ulosi uti wa Yesu? (b) Kodi Yesu “akubwera” motani, ndipo ndani amene mkwiyo waukulu udzawagwere padziko lapansi?
6 Kenako Yohane analengeza mosangalala kuti: “Taonani! Akubwera ndi mitambo, ndipo diso lililonse lidzamuona, ngakhalenso anthu amene anamulasa. Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye. Ame.” (Chivumbulutso 1:7) N’zosakayikitsa kuti Yohane atamva zimenezi anakumbukira ulosi umene Yesu ananena m’mbuyomu wokhudza mapeto a nthawi ino. Mu ulosi umenewo Yesu anati: “Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni, ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:3, 30) Choncho mawu akuti Yesu “akubwera” sakutanthauza kuti akubwera moonekera, koma iye akubwera mwanjira yakuti akuyamba kuika maganizo ake onse pa ntchito yopereka chiweruzo cha Yehova ku mitundu ya anthu. Zimenezi zidzasintha zinthu kwambiri padziko lapansi, ndipo popeza kuti “mafuko onse a padziko lapansi” akana kuvomereza kuti Yesu ndi mfumu, “mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse” udzawagwera.—Chivumbulutso 19:11-21; Salimo 2:2, 3, 8, 9.
7. Kodi “diso lililonse,” ngakhale la anthu osamvera, ‘lidzaona’ bwanji Yesu?
7 Usiku womaliza umene Yesu anali ndi ophunzira ake, anawauza kuti: “Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso.” (Yohane 14:19) Nanga kodi mawu akuti “diso lililonse lidzamuona,” akutanthauza chiyani? Sitingayembekezere kuti adani a Yesu adzamuonadi ndi maso awo, chifukwa Yesu atakwera kumwamba, mtumwi Paulo ananena kuti tsopano Yesu “amakhala m’kuwala kosafikirika,” ndipo “palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.” (1 Timoteyo 6:16) Apa n’zoonekeratu kuti ponena kuti diso lililonse “lidzamuona,” Yohane ankatanthauza kuti anthu “adzazindikira” kuti iye alipo. Zimenezi n’zofanana ndi mmene tingaonere kapena kuzindikira makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso, m’zinthu zimene analenga. (Aroma 1:20) Mawu akuti Yesu “akubwera ndi mitambo” akutanthauza kuti iye sadzaoneka ndi maso, mofanana ndi mmene dzuwa silionekera likabisika ndi mitambo. Koma ngakhale dzuwa libisike ndi mitambo, timadziwabe kuti lilipo chifukwa timaona kuwala. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti Ambuye Yesu sangaoneke ndi maso, adzaonekera ngati ‘moto walawilawi, pamene adzabwezera chilango kwa anthu osamvera uthenga wabwino wonena za iye.’ Pamene akulandira chilangocho, anthu osamverawo ‘adzamuona’ kapena kuti ‘adzazindikira’ kuti iye alipo.—2 Atesalonika 1:6-8; 2:8.
8. (a) Kodi ndani amene ‘analasa Yesu’ mu 33 C.E., ndipo ndani amene akumulasa masiku ano? (b) Popeza kuti panopa Yesu salinso padziko lapansi, kodi anthu ‘angamulase’ bwanji?
8 ‘Ngakhalenso anthu amene analasa Yesu, adzamuona.’ Kodi anthu amenewa ndi ndani? Pamene Yesu ankaphedwa mu 33 C.E., asilikali achiroma anamulasa. Petulo anasonyeza kuti si asilikali achiroma okhawo amene anali ndi mlandu wopha Yesu, koma ngakhalenso Ayuda anali ndi mlandu chifukwa pa Pentekosite, iye anauza ena mwa Ayudawo kuti: “Yesu ameneyu, amene inu munam’pachika, Mulungu anamuika kukhala Ambuye ndi Khristu.” (Machitidwe 2:5-11, 36; yerekezerani ndi Zekariya 12:10; Yohane 19:37.) Aroma ndi Ayuda amenewo anamwalira kalekale zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Choncho masiku ano, anthu amene ‘akumulasa’ akuimira mayiko ndi mitundu ya anthu amene amasonyeza chidani chofanana ndi chimene Aroma ndi Ayudawo anasonyeza pamene ankapachika Yesu. Panopa Yesu salinso padziko lapansi. Koma otsutsa akamazunza anthu a Mboni za Yehova amene amachitira umboni za Yesu, kapena akamagwirizana ndi anthu amene akuzunza Mbonizo, amakhala ngati ‘akulasa’ Yesu.—Mateyu 25:33, 41-46.
“Alefa ndi Omega”
9. (a) Kodi ndani amene analankhula, ndipo analankhula kangati m’buku lonse la Chivumbulutso? (b) Kodi pamene Yehova anadzitchula kuti “Alefa ndi Omega” komanso “Wamphamvuyonse,” zinkatanthauza chiyani?
9 Tsopano panachitika zinthu zodabwitsa kwambiri. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, analankhula. M’pake kuti Yehova analankhula koyambirira m’masomphenyawa, chifukwa iye ndi Mlangizi Wamkulu ndiponso uthenga wa m’buku la Chivumbulutso unachokera kwa iyeyo. (Yesaya 30:20) Mulungu wathu analengeza kuti: “Ine ndine Alefa ndi Omega . . . Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 1:8) M’buku la Chivumbulutso, Yehova analankhula katatu kuchokera kumwamba, ndipo aka n’koyamba. (Onaninso Chivumbulutso 21:5-8; 22:12-15) Akhristu a m’nthawi ya atumwi akanadziwa mosavuta kuti alefa ndi chilembo choyamba ndipo omega ndi chomaliza pa afabeti ya zilembo zachigiriki. Podzitchula kuti alefa ndi omega, Yehova anatsindika mfundo yakuti sipanakhalepo Mulungu wina wamphamvuyonse ndipo sipadzakhalanso wina koma iye yekha. Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu adzasonyeza kuti iye yekha ndiye Mulungu woona ndipo palibe amene adzakayikirenso zimenezi mpaka muyaya. Adzasonyezanso kwamuyaya kuti iye yekha ndi Mulungu Wamphamvuyonse, Wolamulira Wamkulu Koposa m’chilengedwe chonse.—Yerekezerani ndi Yesaya 46:10; 55:10, 11.
10. (a) Kodi tsopano Yohane anadzifotokoza bwanji, ndipo pa nthawiyi anali kuti? (b) Ndani amene ayenera kuti anathandiza pa ntchito yotumiza kumipingo mpukutu umene Yohane analemba? (c) Kodi kawirikawiri chakudya chauzimu chimaperekedwa bwanji masiku ano?
10 Yohane anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova athandiza kuti zinthu ziyende bwino ndipo anauza akapolo anzake kuti: “Ine Yohane, m’bale wanu ndi wogawana nanu masautso a Yesu, mu ufumu ndi m’kupirira, ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.” (Chivumbulutso 1:9) Yohane anali atamangidwa pachilumba cha Patimo chifukwa cha uthenga wabwino. Pa nthawiyi iye anali wokalamba ndipo ankapirira mavuto ambiri limodzi ndi abale ake, komanso anali ndi chiyembekezo champhamvu chakuti adzalamulira nawo mu Ufumu umene anali kuuyembekezera. Yohane ali pachilumbacho anaona masomphenya oyamba a m’buku la Chivumbulutso. N’zosakayikitsa kuti masomphenya amenewo anamulimbikitsa kwambiri, monga mmene Akhristu odzozedwa amalimbikitsidwira masiku ano akamaona kukwaniritsidwa kwake. Sitikudziwa kuti Yohane anatumiza bwanji mpukutu wa buku la Chivumbulutso kumipingo, popeza kuti pa nthawiyi iye anali atamangidwa. (Chivumbulutso 1:11; 22:18, 19) Angelo a Yehova ayenera kuti anathandiza kuti mpukutuwu utumizidwe, monga mmene nthawi zambiri amathandizira Mboni za Yehova zokhulupirika masiku ano zimene zikutumikira Mulungu m’mayiko amene ntchito yawo ndi yoletsedwa. Mboni zimenezi zimatetezedwa ndi angelo kuti zithe kutumiza chakudya chauzimu chapanthawi yake kwa abale awo amene ali ndi njala ya choonadi.—Salimo 34:6, 7.
11. Kodi masiku ano Akhristu odzozedwa ali ndi mwayi wapadera uti wofanana ndi umene Yohane anali nawo?
11 Yohane ayenera kuti anayamikira kwambiri mwayi umene anali nawo wogwiritsidwa ntchito ndi Yehova ngati njira yake yolankhulira ndi mipingo. Masiku anonso, Akhristu odzozedwa amayamikira kwambiri mwayi wopereka “chakudya” chauzimu “pa nthawi yoyenera” kwa anthu a Mulungu. (Mateyu 24:45) Tikukupemphani kuti mukhale m’gulu la anthu olandira chakudya chauzimu cholimbikitsa chimenechi, chomwe chingakuthandizeni kuti mudzalandire mphoto yapadera kwambiri ya moyo wosatha.—Miyambo 3:13-18; Yohane 17:3.
[Bokosi patsamba 21]
Kulandira Chakudya Chauzimu M’nthawi Zovuta
M’masiku otsiriza ano, pamene Mboni za Yehova zikuzunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ambiri, Mbonizo zimafunika kwambiri kulandira chakudya chauzimu kuti zikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Kawirikawiri, pa nthawiyi Mboni zimalandirabe chakudya chokwanira, ndipo nthawi zambiri zimenezi zimatheka chifukwa Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake modabwitsa kwambiri.
Mwachitsanzo, pamene Hitler ankalamulira dziko la Germany, Mboni zinkakopera ndi kugawa mobisa magazini a Nsanja ya Olonda, omwe pa nthawiyo anali oletsedwa ndi atsogoleri ankhanza achipani cha Nazi. Mumzinda wa Hamburg, apolisi a Gestapo analowa mwadzidzidzi m’nyumba imene anthu a Mboni ankagwirira ntchito yokopera magaziniwo. Nyumbayi inali yaing’ono, ndipo zinali zosatheka kubisa chilichonse kuti munthu asaone. Makina olembera anali m’kabati, ndipo zipangizo zina zimene ankagwiritsa ntchito pokopera magaziniwo zinali m’chidebe chosungamo mbatata chimene chinali m’chipinda chapansi. Komanso kuseri kwa chidebecho kunali sutikesi yodzaza ndi magazini. Aliyense ankangoganiza kuti katundu ameneyu aonedwa ndi apolisiwo. Koma chinachitika n’chiyani? Mmene wapolisi anatsegulira kabatiyo, zinamuchititsa kuti asaone makina olemberawo. Pofotokoza zimene zinachitika m’chipinda chapansi chija, mwiniwake nyumbayo anati: “Apolisi atatu anaima pakati penipeni pa chipindacho, ndipotu pamenepo m’pamene panali chidebe chija ndipo kuseri kwake kunali sutikesi yodzaza ndi magazini a Nsanja ya Olonda. Koma palibe amene ankaoneka kuti waona zinthu zimenezi. Zinkangokhala ngati onsewo achititsidwa khungu.” Chifukwa chakuti Mulungu anawateteza mwanjira imeneyi, eniake a nyumbayo anapitiriza kupereka chakudya chauzimu kwa Akhristu anzawo m’nthawi yovuta ndi yoopsa imeneyo.
M’zaka za m’ma 1960, panali nkhondo yapachiweniweni pakati pa dziko la Nigeria ndi dera la Biafra limene linkafuna kuima palokha. Popeza kuti dera la Biafra linali mkati mwenimweni mwa dziko la Nigeria, njira yokha yotulukira kapena kulowa m’derali inali kuyenda pa ndege kudzera pabwalo linalake. Choncho Mboni za ku Biafra sizikanathanso kulandira chakudya chauzimu. Kenako chakumayambiriro kwa chaka cha 1968, akuluakulu a boma a ku Biafra anatumiza munthu wawo wogwira ntchito m’boma kuti azikagwira ntchito yofunika kwambiri ku Ulaya, ndipo wina anamutumiza kubwalo la ndege la ku Biafra komweko. Anthu awiri amenewa anali a Mboni za Yehova, ndipo aliyense anapezeka kuti ali pamalo amene akanathandiza kuti chakudya chauzimu chizilowa m’dera la Biafra. Anthu awiriwa anazindikira kuti amene wachititsa zimenezi ayenera kuti ndi Yehova. Choncho, anadzipereka kugwira ntchito yovuta ndiponso yoopsa yotumiza chakudya chauzimu ku Biafra. Iwo anachita zimenezi nthawi yonse ya nkhondo. Mmodzi wa iwo ananena kuti: “N’zoonekeratu kuti zimenezi zinatheka ndi mphamvu ya Mulungu, chifukwa munthu sakanakwanitsa kuti zonsezi zitheke.”
[Tchati patsamba 19]
Manambala Ophiphiritsa a M’buku la Chivumbulutso
Nambala Tanthauzo Lophiphiritsa
2 Amasonyeza kuti nkhani inayake ndi yotsimikizirika.
(Chivumbulutso 11:3, 4; yerekezerani ndi Deuteronomo 17:6.)
3 Amasonyeza kutsindika. Amasonyezanso mphamvu kapena
kukula kwa chinthu. (Chivumbulutso 4:8; 8:13;16:13, 19)
4 Amasonyeza kuti chinthu chimapezeka paliponse kapena kuti mbali zonse zinayi za chinthu chinachake n’zofanana.
6 Amasonyeza kupanda ungwiro, chinthu chimene sichili bwino, kapena chinthu choopsa.
(Chivumbulutso 13:18; yerekezerani ndi 2 Samueli 21:20.)
7 Amasonyeza kukwanira, makamaka pa nkhani yokhudza Yehova ndi zolinga zake.
Komanso amasonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zonse
ndipo amaika malire pa zimene walola kuti Satana achite. (Chivumbulutso 1:4, 12, 16; 4:5; 5:1, 6; 10:3, 4; 12:3)
10 Amasonyeza kuti chinthu ndi chathunthu kapena chokwanira,
makamaka zinthu za padziko lapansi.
12 Amasonyeza gulu limene Mulungu walikhazikitsa,
kumwamba kapena padziko lapansi.
24 Amasonyeza kuti njira imene Yehova amachitira zinthu m’gulu lake ndi yokwanira bwino kwambiri
ndipo imathandiza kukwaniritsa zolinga zake. (Chivumbulutso 4:4)
Manambala ena otchulidwa m’buku la Chivumbulutso si ophiphiritsa. Nthawi zambiri, nkhani imene muli manambalawo ingatithandize kudziwa ngati manambalawo ndi ophiphiritsa kapena ayi. (Onani Chivumbulutso 7:4, 9; 11:2, 3; 12:6, 14; 17:3, 9-11; 20:3-5.)