Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Atumwi Anapempha Chizindikiro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Zimene Zikutidziŵitsa Kuti Armagedo Ili Pafupi
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kudziwa Zoona Zokhudza Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Yesu tsopano akudziŵa deti la Armagedo?

Zichita ngati nzanzeru kuganiza kuti akulidziŵa.

Ena angadabwe chifukwa chake pali funsoli. Mwina nchifukwa cha ndemanga ya Yesu yopezeka pa Mateyu 24:36: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” Onani mawu akutiwo “kapena Mwana.”

Vesi limeneli ndi mbali ya yankho la Yesu ku funso la atumwi lakuti: “Zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha [kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthuli nchiyani, NW]?” (Mateyu 24:3) Mu ulosi wake wotchuka tsopano wonena za maumboni amene akupanga “chizindikiro,” ananeneratu za nkhondo, njala, zivomezi, chizunzo cha Akristu oona, ndi zinthu zina padziko lapansi zimene zidzasonyeza kukhalapo kwake. Mwa chizindikiro chimenechi otsatira ake adzatha kuzindikira kuti chimaliziro chinali pafupi. Iye anafanizira kuyandikira kumeneku ndi nthaŵiyo pamene mtengo wa mkuyu uyamba kuphukira, kusonyeza kuti chilimwe chili pafupi. Anawonjezera kuti: “Chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo.”​—Mateyu 24:33.

Koma Yesu sananene nthaŵi yeniyeni pamene mapeto adzafika. M’malo mwake, ananena zimene timaŵerenga pa Mateyu 24:36. Umo ndimo mmene Revised Nyanja (Union) Version imanenera ndipo ma Baibulo ambiri amakono amanena chimodzimodzi. Komabe, matembenuzidwe ena akale alibe “kapena Mwana.”

Mwachitsanzo, Douay Version yachikatolika imati: “Koma za tsikulo ndi ola palibe amene adziŵa, osati angelo kumwamba, koma Atate okha.” King James Version imanenanso chimodzimodzi. Kodi nchifukwa ninji mawu akuti “kapena [kapena, ngakhale] Mwana” anasiyidwa, ngakhale kuti amapezeka pa Marko 13:32? Chifukwa chakuti kalelo kuchiyambi cha zaka za zana la 17 pamene matembenuzidwe aŵiriwo anakonzedwa, malembo apamanja amene otembenuza anagwiritsira ntchito, analibe mawuwo. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi malembo apamanja ambiri akale achigiriki atulukiridwa. Ameneŵa, amene ali oyandikana kwambiri ndi nthaŵi ya zolembedwa zoyambirira za Mateyu, ali ndi mawu akuti “kapena Mwana” pa Mateyu 24:36.

Mokondweretsa, Jerusalem Bible yachikatolika imaphatikizapo mawuwo, ndi mawu amtsinde onena kuti Vulgate yachilatini inasiya mawuwo “mwina mwake pa zifukwa za ziphunzitso.” Eyatu! Otembenuza kapena okopa okhulupirira Utatu angakhale atayesa kusiya mawu amene amasonyeza kuti Yesu sanadziŵe zimene Atate wake anadziŵa. Kodi ndi motani mmene Yesu sanakadziŵira mfundo ina yake ngati kuti iyeyo ndi Atate wake omwe anali mbali za Mulungu wokhala ndi mbali zitatu?

Mofananamo, A Textual Commentary on the Greek New Testament, yolembedwa ndi B. M. Metzger, imati: “M’maumboni [malembo apamanja] ambiri a Mateyu, kuphatikizapo zolembedwa za pambuyo pake za Byzantine mulibe mawu akuti ‘kapena Mwana.’ Komanso, maumboni abwino koposa a mitundu ya zolembedwa a Alexandria, the Western, ndi a Caesarea ali ndi mawuwo. Kusiya mawu amenewo chifukwa cha vuto la chiphunzitso chimene limachititsa mwinamwake ndiko kumene kumachititsa kuti awawonjezere pa” Marko 13:32.​—Kanyenye ngwathu.

“Maumboni abwino koposa” amenewo a malembo apamanja akale amachirikiza kaŵerengedwe kamene kamasonyeza kuwonjezereka koyenerera kwa chidziŵitsocho. Angelo sanadziŵe ola la mapeto; ngakhalenso Mwana; koma Atate okha. Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 20:23, pamene anavomereza kuti analibe ulamuliro wopereka malo apamwamba mu Ufumuwo, koma Atate anali nawo ulamuliro umenewo.

Chotero, mawu a Yesu iye mwini amasonyeza kuti padziko lapansi sanali kudziŵa deti la ‘mapeto a dziko.’ Kodi iye walidziŵa kuyambira pamenepo?

Chivumbulutso 6:2 chimafotokoza Yesu kukhala atakwera kavalo woyera akutulukira “wolakika kuti alakike.” Ndiyeno pakubwera apakavalo oimira nkhondo, njala, ndi miliri, zonga zimene taziona kuyambira pamene Nkhondo Yadziko I inayamba mu 1914. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti mu 1914, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, amene adzatsogolera m’nkhondo ikudzayo pa kuipa kwa padziko lapansi. (Chivumbulutso 6:3-8; 19:11-16) Popeza Yesu tsopano wapatsidwa mphamvu monga amene adzalakika m’dzina la Mulungu, kukuoneka kuti Atate wake wamuuza pamene mapeto adzafika, pamene “adzalakika.”

Ifeyo padziko lapansi sitinauzidwe detilo, chotero mawu a Yesu akugwirabe ntchito kwa ife: ‘Yang’anirani, dikirani; pakuti simudziŵa nthaŵi yake. . . . Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.’​—Marko 13:33-37.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena