Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Fanizo la Matalente?
    Nsanja ya Olonda—2015 | March 15
    • 4, 5. Kodi mbuye wotchulidwa mu fanizoli akuimira ndani ndipo talente imodzi inali yofanana ndi madinari angati?

      4 Werengani Mateyu 25:14-30. Mabuku athu akhala akufotokoza kuti munthu kapena mbuye wotchulidwa mu fanizoli akuimira Yesu. Amafotokozanso kuti iye atapita kumwamba mu 33 C.E., zinali ngati wapita kudziko lina. Mu fanizo lina, Yesu ananena kuti cholinga chopitira kudziko lina chinali ‘kukalandira ufumu.’ (Luka 19:12) Koma iye sanalandire Ufumu atangopita kumene kumwambako.b M’malomwake, ‘anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambira pamenepo, anayembekezera kufikira pamene adani ake anaikidwa monga chopondapo mapazi ake.’—Aheb. 10:12, 13.

  • Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Fanizo la Matalente?
    Nsanja ya Olonda—2015 | March 15
    • d Atumwi atamwalira, Satana anayambitsa mpatuko. Mpatukowo unasokoneza mpingo wachikhristu kwa zaka zambiri. Pa nthawiyi, palibe anthu amene ankapitiriza ntchito imene Yesu anaisiya. Koma izi zinadzasintha ‘m’nthawi yokolola’ kapena kuti m’masiku otsiriza. (Mat. 13:24-30, 36-43) Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, tsamba 9 mpaka 12.

  • Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Fanizo la Matalente?
    Nsanja ya Olonda—2015 | March 15
    • 8. Kodi mbuyeyo ankayembekezera chiyani ngakhale kuti akapolowo anapatsidwa matalente osiyana?

      8 Fanizoli likusonyeza kuti mbuyeyo anapereka matalente 5 kwa kapolo wina, matalente awiri kwa wina ndipo winayo anangomupatsa talente imodzi. (Mat. 25:15) Ngakhale kuti akapolowa analandira matalente osiyana, mbuyeyo ankayembekezera kuti onse achita khama. Choncho tinganene kuti Khristu ankafuna zoti ophunzira ake achite zonse zimene angathe pa ntchito yolalikira. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Akhristu akhala akuchita malonda ndi matalente. Buku la Machitidwe limasonyeza kuti iwo ankachita khama kwambiri pa ntchito yolalikira.d—Mac. 6:7; 12:24; 19:20.

      AKAPOLO AKUCHITA MALONDA NTHAWI YA MAPETOYI

      9. (a) Kodi akapolo awiri okhulupirika anachita bwanji ndi matalente aja ndipo izi zikusonyeza chiyani? (b) Kodi a “nkhosa zina” ayenera kuchita chiyani?

      9 M’nthawi ya mapeto ino, makamaka kuyambira mu 1919, Akhristu odzozedwa okhulupirika akhala akuchita malonda ndi matalente a Ambuye. Mofanana ndi akapolo awiri oyamba aja, Akhristuwa akhala akuchita zonse zimene angathe pa ntchito yawo. Sitinganene kuti amene analandira matalente 5 ndi ndani kapena amene analandira matalente awiri ndi ndani. Chofunika kwambiri n’chakuti mu fanizoli, onse awiri anachita khama n’kuchulukitsa kawiri matalente amene anapatsidwa. Koma kodi anthu amene adzakhale padzikoli ayenera kugwiranso ntchito imene odzozedwa apatsidwa? Fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi limasonyeza kuti anthu amenewa ali ndi mwayi waukulu wothandiza abale a Khristu pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. M’masiku otsiriza ano, magulu awiriwa ali ngati “gulu limodzi.” Onse akugwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu.—Yoh. 10:16.

      10. Kodi mbali yaikulu ya chizindikiro chakuti Yesu akulamulira ndi iti?

      10 Ambuye amayembekezera kuti tizigwira ntchito mwakhama. Tanena kale kuti Akhristu oyambirira ankachitadi zimenezi. Kodi izi n’zimene zikuchitika m’masiku otsiriza ano pamene fanizo la matalente likukwaniritsidwa? Inde. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu okhulupirika akhala akugwira mwakhama kwambiri ntchito yolalikira. Chaka chilichonse, anthu masauzande ambiri amakhala ofalitsa. Izi zachititsa kuti ntchito yolalikira ikhale mbali yaikulu ya chizindikiro chakuti Yesu akulamulira. Ambuye ayenera kuti akusangalala kwambiri.

      Atumiki a Yehova amachita zinthu zosiyanasiyana pa ntchito yolalikira

      Khristu wapereka ntchito yamtengo wapatali kwa atumiki ake (Onani ndime 10)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena