Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/1 tsamba 15-20
  • Utsogoleri Wokangalika wa Kristu Lerolino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Utsogoleri Wokangalika wa Kristu Lerolino
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbuye ndi Kapolo Wake
  • Oyang’anira M’dzanja Lamanja la Kristu
  • Kupyolera mwa Mzimu
  • Kupyolera mwa Angelo
  • Chidaliro Chotheratu mu Chitsogozo cha Kristu
  • Kristu Amatsogolera Mpingo Wake
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kuulula Chinsinsi Chopatulika
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • ‘Kapolo Wokhulupirika’ ndi Bungwe Lake Lolamulira
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/1 tsamba 15-20

Utsogoleri Wokangalika wa Kristu Lerolino

“Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha Dongosolo la kachitidwe kazinthu.”​—MATEYU 28:20, NW.

1. Kodi ndi mu njira yotani mmene Kristu anaperekera “chuma chake” kwa ophunzira ake?

PAMENE Kristu anali pafupi kusiya ophunzira ake ndi kubwerera kumwamba mu 33 C.E., iye “anapereka kwa iwo chuma chake.” Ichi chinaphatikizapo kukhala “atumiki m’malo mwa Kristu” ndi kutenga ntchito yolalikira imene iye anaiyamba, kuifutukulira iyo “kumalekezero ake a dziko lapansi.” Asanawasiye iwo, iye anawalangiza iwo “kupanga ophunzira a anthu a mitundu yonse.” Kodi tiri ndi chitsi mikiziro chakuti iye anali wosamalitsa kuti ndimotani mmene iwo anachitira ntchito imeneyi? Ndithudi tiri nacho!—Mateyu 25:14; 2 Akorinto 5:20; Machitidwe 1:8; Mateyu 28:19.

2. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Kristu anali kutsatira mosamalitsa machitachita a mipingo ya zana loyamba?

2 Zaka zoposa 60 pambuyo pa kukwera kwa Kristu kumwamba, iye anasonyeza kuti anakhala akutsatira mosamalitsa machitachita a mipingo Yachikristu padziko lapansi. Mu chivumbulutso choperekedwa kwa mtumwi Yohane, chiwalo cha bungwe lolamulira la mu zana loyamba, Yesu Kristu anatumiza uthenga kwa mipingo isanu ndi iwiri yokhala mu Asia Minor. Kwa isanu ya iyo iye anati: “Ndidziwa ntchito zako.” Ndipo anasonyeza kuti iye anali wozolowerana ndi zimene zinali kuchitika mkati mwa iwiri ina, Smurna ndi Pergamo. Iye anapereka chilimbikitso chachindunji ndi uphungu kwa uliwonse wa mipingoyo. Sipakanakhala chikaikiro m’malingaliro awo ponena za amene anali Mtsogoleri wawo wokangalika.​—Chivumbulutso 1:11; 2:1-3:22.

3. Ndi kwandani kumene mauthenga asanu ndi awiri m’chenicheni anaperekedwa, ndipo nchiyani chimene chimatsimikizira ichi?

3 M’chenicheni, mauthenga asanu ndi awiri amenewo sanali oikidwa malire mu mbali zawo ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Asia. Uphungu wabwino ndi machenjezo amene anali nawo anagwira ntchito ku mipingo yonse, kuyambira ku zana loyamba kufikira ku “tsiku la Ambuye,” kumene tiri tsopano.a Maso a Kristu oyerekezedwa ndi “lawi la moto,” akhala akuyang’anira mopitirira zomwe zakhala zikuchitidwa mkati mwa “mipingo yonse.”​—Chivumbulutso 1:10; 2:18, 23.

Mbuye ndi Kapolo Wake

4. Kodi ndimotani mmene Kristu “anankira ku ulendo” ndipo kenaka kubwereranso “patapita nthawi yaitali”?

4 Pambuyo pa kudziyerekeza iyemwini ndi “munthu, wakunka ulendo, [amene] anaitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake,”Kristu anawonjezera: “Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nawo pamodzi.” (Mateyu 25:14, 19) Mu 33 C.E. Kristu “anayenda ulendo wake kupita kumwamba,” kumene iye anakhala “pa dzanja lamanja la Mulungu.” (1 Petro 3:22) “Patapita nthawi yaitali,” kutsatira kukhazikitsidwa kwake monga Mfumu mu 1914, Kristu anayamba ‘kuchita ufumu pakati pa adani ake’ mwakuponyera Satana ndi ziwanda zake pansi ku dziko lapansi. (Masalmo 110:1, 2; Chivumbulutso 12:7-9) Kenaka anatembenuzira chidwi chake kwa akapolo ake. Nthawi inali itafika ya kuwerengera iwo. Kuposa ndi kale lonse, iye anali Mtsogoleri wawo wokangalika.

5. Kodi ndi liti pamene nthawi ya kuWerengera inafika, ndipo ndimotani mmene okhulupirika anafupidwira?

5 Mbiri yamakono ya anthu a Mulungu imasonyeza kuti nthawi imeneyi ya kuwerengera inabwera mu 1918-19. Fanizo la matalente limachitira chitsanzo mmene Mbuye adzawerengerera otsalira a akapolo ake odzozedwa. Iwo adzayenera kuwerengera aliyense payekha mu njira imene agwiritsira ntchito chuma chawo, “monga mwanzeru zake,” kapena kuthekera kwauzimu. Awo amene anakhala obala zipatso analowa mu chikondwerero cha Mbuye wawo, amene ananena kwa iwo: “Unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono. Ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri.”​—Mateyu 25:15, 20-23.

6. Kodi nchiyani chimene Akristu odzozedwa okhulupirika amenewo anachita monga gulu, ndipo nchiyani chimene Mbuye wawo anawapatsa iwo kusamalira?

6 Akristu odzozedwa oterowo aliyense payekha anapezedwa ali atumiki okhulupirika a Mfumu yolamulira tsopano, ofunitsitsa kupanga ophunzira kaamba ka Mbuye wawo. Iwo onse pamodzi anapezeka kukhala “kapolo” amene Mbuye wawo ananena kuti: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.”—Mateyu 24:45-47.

7. (a) Kodi ndimotani mmene “chuma cha” Kristu chawonjezerekera chiyambire 1914? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Kristu alinso Mtsogoleri wokangalika wa “nkhosa zina”?

7 “Chuma” cha Kristu chachuluka chiyambire 1914. Iye wakhala atavekedwa ndi “mphamvu yaufumu,” yophatikizapo ulamuliro wowonjezereka ndi mathayo okulira. (Luka 19:11, 12 ) lye choyamba anapita kusonkhanitsa otsalira a “ana aufumu,” Akristu odzozedwa 144, 000 “ogulidwa kuchokera pakati pa anthu”kukhala mafumu ndi ansembe ndi iye kumwamba. (Mateyu 13:38; Chivumbulutso 14:1-4; 5: 9, 10) Kenaka, monga mmene chinasonyezedwera mu mbiri kuyambira 1935, iye wakhala akusonkhanitsa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za zimene iye anati: “Izinso ndiyenera kuzitenga.” (Chivumbulutso 7:9, 10; Yohane 10:16) Inde, iye Ali amene amabweretsa “nkhosa” izi, ndipo iye akukhala Mtsogoleri wawo wokangalika. Mosangalatsa, lemba la Chigriki mu tanthauzo lenileni limatanthauza kuti, “Ndi awo amene chiri choyenerera [kwa] ine kuwatsogolera.” Kodi ndimotani mmene iye mokangalika akutsogozera “nkhosa” zake zonse lerolino?

Oyang’anira M’dzanja Lamanja la Kristu

8, 9. (a) Kodi ndi masomphenya otani amene mtumwi Yohane analandira? (b) Kodi nchiyani chimene chidaimiridwa ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri?

8 Mtumwi Yohane, chiwalo cha bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu woyambirira, analandira masomphenya mmene iye “anawona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi, ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga mwana wa munthu . . . Ndipo m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri.” Yesu Kristu analongosola kwa Yohane: “Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziwona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo mipingo isanu ndi iwiri.”​—Chivumbulutso 1:12-20.

9 Kuchitira ndemanga pa ndime imeneyi, bukhu la “Then Is Finished the Mystery of God” limanena kuti: “Kodi ‘angelo’ oterowo ali osawoneka ndi maso? Ayi. Mtumwi Yohane analandira bukhu lonse la Chivumbulutso kuchokera kwa Yesu Kristu kupyolera mwa m’ngelo wa kumwamba, ndipo chingakhale kusalingalira kumbali yake kumakhala akumlemberanso m’ngelo kumwamba, mu malo ake osawoneka. Iwo safuna uthengawu wolembedwa kwa mipingo isanu ndi iwiri ya mu Asia. Tanthauzo lenileni la liwu lakuti ‘m’ngelo’ liri ‘mthenga; wonyamula uthenga.’ . . . Popeza nyenyezi zophiphiritsira zisanu ndi ziwiri zimenezi zikuwonedwa ziri mu dzanja lamanja la Yesu, izo ziri m’chisamaliro chake ndi ulamuliro ndi pansi pa chitsogozo chake, ‘dzanja lamanja’ lake lopatsidwa mphamvu liri lokhoza kutsogoza ndi kutetezera iwo. . .. Ponena za ‘zoikapo nyali zisanu ndi ziWiri* mu masomphenya a ‘m’tsiku la Ambuye’ zinaimira mipingo yonse ya Akristu owona mu tsiku lino, ‘tsiku la Ambuye lenileni chiyambire 1914 C.E., chotero ‘nyenyezi zisanu ndi ziwiri’ zimaimira oyang’anira onse odzozedwa ndi mzimu, odzozedwa onga angelo a mipingo imeneyo lerolino.b—Masamba 102-4.

10. Kodi ndi “chuma” chowonjezereka chotani chimene chaperekedwa ku chisamaliro cha kapolo?

10 Oyang’anira odzozedwa amenewa m’dzanja lamanja la Kristu ali mbali ya “kapolo”amene Iye wamusankha kukhala “woyang’anira chuma chake.” Chifukwa chakuti Mbuye wa kapolo iyemwini wavekedwa ndi mathayo owonjezereka chiyambire 1914, “chuma chake chonse” chiyenera kuphatikizapo zinthu zochuluka zowonjezereka kaamba ka kapolo kusiyana ndi kale. Popeza chinthu chimodzi, monga “atumiki olowa m’malo mwa Kristu,” tsopano otsalira ali atumiki a Mfumu yolamulira yomalamulira pa Ufumu wokhazikitsidwa. (2 Akorinto 5:20) Iwo aikidwa oyang’anira a zinthu zonse zauzimu zomwe ziri za Mbuye wawo padziko lapansi. Iwo ayenera kutumikira m’kukwaniritsa maulosi omwe amagwira ntchito chiyambire chikhazikitsidwe cha Ufumuwo. Ichi chimaphatikizapokulalikira “mbiri imeneyi yabwino ya ufumu . . . mu dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni.” (Mateyu 24:14) Kuposa ndi kalelonse, iwo ayenera kupitiriza kupanga “ophunzira a anthu a mitundu yonse,” chotero kusonkhanitsa “khamu lalikulu” losawerengeka. (Mateyu 28:19, 20; Chivumbulutso 7:9) Inde, “zinthu zofunika za amitundu” zimenezi ziri mbali ya “chuma” chowonjezereka cha Kristu padziko lapansi.​—Hagai 2:7.

11. (a) Kodi nchiyani chimene “chuma” chowonjezereka chimenechi chimayeneretsa? (b) Kodi ndani amene akutsogoza ntchito, ndipo motani?

11 Izi zonse zimatanthauza ntchito yowonjezereka kwa “kapolo,” munda wokulira wa ntchito, wofutukulika m’chenicheni ku “dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” Iyo imafunikiranso malikulu okulira nth zipangizo za nthambi kaamba ka kuyang’anira ntchitoyo ndi kusindikiza ndi kugawira mabukhu kaamba ka kulalikira ndi phunziro laumwini. Mofanana ndi mu zana loyamba, ntchito imeneyi imachitika pansi pa utsogoleri wokangalika wa Yesu Kristu, amene mophiphiritsira ali “pakati pa zoikapo nyali,” kapena mipingo. Iye amatsogolera iwo kupyolera mwa oyang’anira odzozedwa, amene mophiphiritsira akuwasunga “m’dzanja lake lamanja.” (Chivumbulutso 1:13, 16) Mofanana ndi mu nthawi ya Akristu oyambirira, gulu la oyang’anira odzozedwa amenewa limapanga Bungwe Lolamulira lowoneka ndi maso la mpingo wa Kristu padziko lapansi. “Dzanja lamanja” lake lopatsidwa mphamvu limatsogoza amuna okhulupirika amenewo pamene amayang’anira ntchito ya Ufumu.

Kupyolera mwa Mzimu

12, 13. (a) M’chiyang’aniro cha chiwonjezeko chokulira, kodi ndi funso lotani limene limabuka? (b) Kodi ndimotani mmene Kristu amagwiritsirira ntchito mzimu kudzaza zosowa za oyang’anira pakati pa ophunzira ake padziko lapansi?

12 Ndi chiwerengero cha “nkhosa zina” tsopano chikumafika mu chiwerengero chopitirira pa mamiliyoni atatu, olinganizidwa mu mipingo 52, 000, chiri chachidziWikire kuti otsalira odzozedwa amafuna thandizo m’kupereka chisamaliro ku chuma cha padziko lapansi cha Mbuye. Ocheperandi 9, 000, kuphatikizapo alongo ambiri, amadya ziphiphiritso za Chikumbutso, chotero palibe ngakhale wodzozedwa m’modzi pa mpingo uliwonse. Kodi icho chikutanthauza kuti Yesu Kristu sali woyang’anira wa mipingo kumene kulibe “m’ngelo,” wodzozedwa ndi mzimu, kapena ‘nyenyezi’?

13 Kutalitali! Monga mmene tawonera mu nkhani yapitayo, mu zana loyamba Kristu mokangalika anatsogolera mpingo wake kupyolera mwa mzimu woyera. Lerolino iye amagwiritsira ntchito ziwalo zodzozedwa ndi mzimu za Bungwe Lolamulira kuika oyang’anira osankhidwa pakati pa “nkhosa zina”. Awa ayenera kufikiritsa ziyeneretso zofanana ndi akulu odzozedwa, monga mmene zalongosoledwera m’malemba monga ngati 1 Timoteo 3:1-7 ndi Tito 1:5-9. Ziyeneretso za m’Malemba zimenezi zinalembedwa pansi pa chitsogozo cha mzimu woyera. Kuyamikira ndi kuikidwa zimachitidwa pambuyo pa pemphero ndi pansi pa chitsogozo cha mzimu woyera. Kwa akulu osadzozedwa amenewa uphungu wa Paulo umagwira ntchito ndi mphamvu yofananayo, yakuti: “Dzipenyerereni inu eni ndi gululo, limene mzimu woyera wakuikani woyang’anira.” —Machitidwe 20:28, NW.

14. (a) Kodi ndimotani mmene ulosi wa Yesaya 32:1, 2 ukukwaniritsidwira? (b) Kodi ndimotani mmene akulu onse ayenera kugonjerera ku “dzanja lamanja“ la Kristu?

14 Chotero, mu makumi a zikwi za mipingo, Mfumu Yesu Kristu wolamulira wachilungamo akugwiritsira ntchito “nkhosa zina” monga “akalonga” kuchinjiriza “nkhosa” zake kuchokera ku mphepo yauzimu, mkuntho, ndi chilala. (Yesaya 32:1, 2) Mofanana ndi Davide wakale, akulu, kaya odzozedwa kapena “nkhosa zina”, amapemphera kwa Yehova: “Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.” (Masalmo 143:10) Ndipo Yehova amamva pemphero lawo. Kupyolera mwa Mwana wake, lye amapatsa iwo mzimu wake, ndipo Yesu amagwiritsira ntchito njira imeneyi mokangalika kutsogolera ophunzira ake padziko lapansi. Mwachihadwa, akulu onse ayenera kugonjera ku “dzanja lamanja” la kulamulira la Kristu, chitsogozo, ndi chilangizo, zimene iye amachita kupyolera mwa mzimu ndi ziwalo zodzozedwa ndi mzimu za Bungwe Lolamulira.

Kupyolera mwa Angelo

15. Kodi ndi njira ina iti imene Kristu ali nayo ya kutsogozera ophunzira ake padziko lapansi mokangalika?

15 Nkhani yapita inatchula kuti angelo anagwiritsiridwa ntchito mu zana loyamba kutsogoza ndi kuwombola Akristu oyambirira ndi kuwathandiza iwo mu ntchito yawo yolalikira. Kodi chingakhale chanzeru kulingalira kuti Mfumu yathu yolamulira Yesu Kristu sakugwiritsira angelo mu kutsogoza mokangalika ophunzira ake lerolino? Sikuti kokha chikakhala chopanda nzeru koma chikakhalanso chopanda malemba.

16, 17. Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene tiri nacho kuti Kristu akugwiritsira ntchito angelo kututa “ana a ufumu” ndi m’kusonkhanitsa “nkhosa zina”?

16 Molingana ndi fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole, nthawi yotuta idzafika pa “mapeto a dongosolo la kachitidwe ka zinthu,” omwe anayamba mu 1914. Mkati mwa kututa, “ana a ufumu” adzasiyanitsidwa ndi “ana a woipayo.” Kodi ndani amene Mbuye adzagwiritsira ntchito kuchita ntchito yotuta? “Otutawo ali angelo,” Kristu anawonjezera: “Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu ufumu wake zokhumudwitsa zonse ndi anthu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 13:37-41) Kristu amagwiritsira ntchito angelo kuchinjiriza abale ake padziko lapansi.

17 Koma bwanji ponena za “nkhosa zina”? Kodi Kristu amagwiritsira ntchito angelo kusonkhanitsa izo? Motsimikizirika! Fanizo lake la nkhosa ndi mbuzi limati: “Pamene Mwana wa munthu adzaza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake. Ndipo adzasonkhanitsa pamaso pake anthu a mitundu yonse, ndipo iye adzalekanitsa wina ndi mnzake monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:31, 32) Kristu amagwiritsira ntchito angelo ake mu ntchito yolekanitsa imeneyi. Monga mmene m’ngelo anatsogozera mapazi a Filipo kulinga kwa mdindo wa ku Aitiopiya, choteronso pali chitsimikiziro chochuluka lerolino chakuti Kristu akugwiritsira ntchito angelo ake kutsogoza mapazi a Mboni zake kulinga kwa onga nkhosa. Anthu ambiri amavomereza ku chenicheni chakuti iwo anali akupemphera kaamba ka thandizo kokha nthaŵi yochepa Mboni isanagogode pa chitseko chawo.​—Machitidwe 8:26, 27.

Chidaliro Chotheratu mu Chitsogozo cha Kristu

18, 19. Pa maziko a zimene zinawoneka mu zana loyamba, kodi tiri achidaliro cha chiyani?

18 Mu zana loyamba, mikhalidwe nthawi zonse siinazitsogolere iyo yeni ku kugwiritsira ntchito kwa bungwe lolamulira mu Yerusalemu kwa Kristu kuthetsa mavuto achindunji. Pamene Paulo anapatulidwa kumpoto mu Asia Minor ndipo anafuna kudziwa ndi kugawo liti lomwe linayenera kutsegulidwa, Kristu anachitapo kanthu kupyolera mwa mzimu. (Machitidwe 16:6-10) Lerolino Mboni za Yehova ziri ndi chidaliro kuti aliyense wa abale awo amene amakhala opatulidwa kwakanthawi kuchokera ku Bungwe Lolamulira chifukwa cha chizunzo adakali pansi pa utsogoleri wokangalika wa Kristu, kupyolera mwa mzimu ndi chirikizo la ungelo.

19 Kalelo kumbuyo mu nthawi za Akristu oyambirira, zigamulo zina zimene zinapangidwa ndi bungwe lolamulira zingakhale zinali zovuta kuzimvetsetsa panthawiyo. Ichi mosakaikira chingakhale chimene chinachitika pamene Paulo anabwezedwa ku Tariso kapena pamene iye anatumizidwa ku kachisi pambuyo paulendo wake wa umishonale wachitatu. (Machitidwe 9:30; 21:23-25) Komabe, Kristu m’chenicheni anali kumbuyo kwa zigamulo zimenezo. (Machitidwe 22:17-21; 23:11) Lerolino tingakhale ndi chidaliro chakuti chirichonse chimene Kristu angachilole kuwoneka pakati pa ophunzira ake padziko lapansi chiri ndi cholinga china cholemekezeka kumbuyo kwake, monga mmene zinaliri mu zana loyamba,

20. Kodi tiri okhutiritsidwa za chiyani, ndipo kodi nchiyani chimene chiri chigamulo chathu?

20 Chotero, pamene tiwerenga mu Baibulo kuti Kristu “ali mutu wathupi, mpingo,” tiri okhutiritsidwa kuti iye sali Mutu wamba. (Akolose 1:18) Tidziwa, kuchokera ku chokumana nacho, kuti iye ali weniweni, Mutu wokangalika. Pamene tiwerenga bukhu la Machitidwe ndi kuwona ndimotani mmene Kristu anatsogozera zinthu pakati pa Akristu oyambirira, tingawone kuti iye akugwiritsira njira yofananayo lerolino. Timawona chitsimikiziro cha kugwiritsira ntchito kwa Kristu kwa mzimu woyera, angelo, ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi Bungwe lake Lolamulira, kuika akulu oyeneretsedwa mwauzimu. Odalira mu chitsogozo chokangalika cha zinthu cha Kristu, tiri olimba mtima kupitirizabe “kulankhula chowonadi” ndi kumakula mu chikondi “mu zinthu zonse kwa iye amene ali mutu, Kristu. ”​—Aefeso 4:15.

[Mawu a m’munsi]

a Kaamba ka kulongosoledwa kotheratu kwa mauthenga asanu ndi awiri amenewa ndi kugwira ntchito kwawo, onani bukhu la “Then Is Finished the Mystery of God,“ pa mutu 7 mpaka 14, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Kope la December 15, 1971, la Nsanja ya Olonda m’Chingelezi rnamveketaa bwino nsonga iyi mowonjezereka, ikumati: “Mosakaikira, osati kokha mkulu mmodzi, wansembe, woyang’anira kapena mbusa, koma ‘bungwe lonse la akulu* linali limene Ambuye wolemekezedwa, Yesu Kristu, analitcha ‘m’ngelo’ yemwe anaimiridwa ndi nyenyezi ya kumwamba. . . . ‘Bungwe la akulu’ (kapena ansembe) la kumeneko ku Aefeso linayenera kugwira ntchito monga nyenyezi mkupereka kuwala kwauzimu kuchokera kumwamba, pa mpingo umene mzimu woyera unawapanga abusa.”

Nsonga Zazikulu Zoyenera Kukumbukira

◻ Kodi ndi chitsimikiziro chotani chimene tiri nacho kuti Kristu mosamalitsa anatsatira machitachita a mipingo ya zana loyamba?

◻ Kodi ndani amene Kristu anawasankha oyang’anira “chuma” chake, ndipo kodi nchiyani chimene izi zimaphatikiza?

◻ Kodi ndani amene akuimiridwa ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri mu dzanja lamanja la Kristu?

◻ Kodi ndimotani mmene Kristu akugwiritsirira ntchito mzimu woyera, angelo, ndi Bungwe Lolamulira lodzozedwa mu kutsogoza mpingo wake lerolino?

◻ Kodi nchifukwa ninji tingakhalire ndi chidaliro chotheratu mu chitsogozo cha zinthu cha Kristu lerolino?

[Bokosi patsamba 20]

Ziyeso zomwe zimabwera chifukwa cha nkhondo, kuukira kapena chisautso ndi chiletso cha boma zingachipange icho kukhala chosathekera kwa inu kupitiriza kulambira kwa Chikristu mu njira yolinganizika mokwanira. Mikhalidwe ingapangike kuchipangitsa icho kukhala chosathekera kupanga misonkhano ya mpingo yaikulu. Kugwirizana ndi ofesi ya nthambi kungaduke kwakanthawi. Kuchezera kwa oyang’aniraadera kungasokonezedwe. Zofalitsidwa zatsopano sizingaf ike. Ngati zirizonse za zinthu izi zichitika kwa inu, kodi nchiyani chimene inu muyenera kuchita?

Yankho liri: Pansi pa mikhalidweyo, chitani chirichonse chimene mungathe, ndipo kufikira ku ukulu umene mungathe, mu njira ya kulambira koyera. Phunziro laumwini liyenera kukhala lothekera. Kawirikawiri magulu ochepa a abale angasonkhane kaamba ka phunziro m’manyumba. Zofalitsidwa zophunziridwa kale ndi Baibulo ilo leni lingagwiritsiridwe ntchito monga maziko a misonkhano. Musakhale otenthetsedwa mitima kapena odera nkhawa. Mwachisawawa, m’kupita kwa kanthawi mtundu wina wa kulankhulana ndi abale amathayo ungakhazikitsidwe. Bungwe Lolamulira limafunafuna njira za kulankhulizana ndi abale.

Koma ngakhale ngati inu mudzipeza inumwini . wopatulidwa kwa abale anu onse Achikristu, sungani m’maganizo kuti simuli opatulidwa kuchokera kwa Yehova ndi Mwana wake Yesu Kristu.​—Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, tsamba 168.

[Chithunzi patsamba 17]

Kristu mophiphiritsira ali pakati pa mipingo kunyamula oyang’anira mu dzanja lake lamanja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena