Kodi Mumafunafuna Chuma Chobisika?
“Chisomo ndi mtendere ziwonjezeke kwa inu mwa chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.”—2 PETRO 1:2, “NW.”
1, 2. Kodi ndi nsonga ziti zimene zimapangitsa golidi kukhala wamtengo ndi wodula?
KODI nchifukwa ninji golidi ali wodula chotero? Iye ali kokha chitsulo chofeŵa, komabe phindu lake limafika m’mazana a madola pa ounce imodzi. Zowona, iye akhoza kupangidwa m’chinthu chirichonse ndipo angapangidwe kukhala chovala chokongola chonga mphete kapena chibangiri. (1 Timoteo 2:9; Yakobo 2:2) Komabe, ngati munasoŵa m’chipululu, mukumavutika ndi njala ndi ludzu, inu simukanamudya kapena kumumwa. Mu mkhalidwe woterowo mtanda wa mkate kapena mbale ya mpunga ndi madzi akumwa zikakhala zamtengo kwenikweni kuposa golidi.
2 Pamenepo, kodi nchifukwa ninji golidi akuyanjidwa kukhala wamtengo koposa? Kokha chinthu chimodzi, iyo simapezekapezeka ndipo ngwovuta kupeza. Mwachitsanzo, pamene m’godi Empire wa golidi unatsekedwa kumpoto kwa California mu 1957 chifukwa chakuti sunali kutulutsanso phindu, ogwira ntchito mumgodimo ankakumba utali wa mamita oposa 1,500 mozondoka koma anayeneranso kutsika makilomita atatu mopindika kuti afikire golidiyo. Pa nsonga imeneyo, mtengo wapamwamba wa golidi unapangitsa kuyesayesa kwa kalavula gaga kwa kupitirizabe kufunafuna kukhala koyenerera.
3. Kodi ndi chuma chiti chimene tingafunefune?
3 Ngakhale ndi tero, ife tingakumbe kaamba ka chinachake cha mtengo kwenikweni kuposa golidi. Kodi icho nchiyani? Mfumu yanzeru Solomo inapereka yankho zaka 3,000 zapitazo: “Ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukafunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuwopa Yehova [ndipo udzapeza chidziŵitso chenicheni cha Mulungu, NW].” Tangolingalirani anthu wamba kukhala okhoza kupeza “chidziŵitso chenicheni cha Mulungu”!—Miyambo 2:3-5.a
Chifukwa Chimene Onse Amafunikira Chidziŵitso Cholongosoka
4. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuphatikizidwa m’chidziŵitso cholongosoka cha Mkristu?
4 Chiyambire nthaŵi ya Kristu, chidziŵitso chofunika koposa chimenecho chafutukuka kuphatikiza zochulukira kuposa zimene zinalipo kwa amuna ndi akazi Achihebri okhulupirika a m’nthaŵi zakale. Monga mmene Paulo analongosolera kuti: “Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wavumbulutso [la chidziŵitso cholongosoka cha iye, NW]; ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima.”—Aefeso 1:17, 18.
5. Kodi nchifukwa ninji odzozedwa afunikira kupereka chisamaliro chokhazikika ku chidziŵitso chawo cha chifuno cha Mulungu?
5 Kumbuyoko, uwu unali uphungu wachindunji kwa abale opatulika odzozedwa a Kristu, ndipo udakali tero lerolino. Monga mbali yachiwiri ya “mbewu” yolonjezedwa, ameneŵa ali chandamali chapadera cha kupatutsa kwauzimu kwa Satana. (Agalatiya 3:26-29; Aefeso 6:11, 12) Makamaka odzozedwa, ayenera kupanga kuitanidwa kwawo kukhala kotsimikizirika mwa kusanyalanyaza mphatso yaulere ya chisomo cha Mulungu. Chimenecho ndicho chifukwa chake ayenera kulimbitsa chuma chawo chauzimu mwa kukonzanso chidziŵitso chawo cholongosoka cha chifuno cha Mulungu ndi Mawu.—Aefeso 3:7; Ahebri 6:4-6; 2 Petro 1:9-12.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji tonsefe timafunikira chidziŵitso cholongosoka, mosasamala kanthu kaya chiyembekezo chathu nchakumwamba kapena cha padziko lapansi? (b) Kodi nchiyani chimene chimafunikira kuti tipeze chidziŵitso cholongosoka?
6 Kodi bwanji ponena za awo amene chiyembekezo chawo chiri moyo wosatha padziko lapansi? Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika kwa iwo? Chifukwa chakuti palibe milingo ya umphumphu Wachikristu, ngati kuti panali miyezo yapamwamba kwa odzozedwa, amene ali ndi chiyembekezo chakumwamba, kuposa kwa nkhosa zina, amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. (Yohane 10:16; 2 Petro 3:13) Miyezo Yachikristu imagwira ntchito mofananamo kwa onse. Kaamba ka chifukwa chimenecho, tonsefe tifunikira kuikamonso mphamvu m’mabatiri athu auzimu ndi chidziŵitso cholongosoka pa maziko okhazikika. Koma nthaŵi ndi kuyesayesa nzoloŵetsedwamo. Tiyenera kudziloŵetsa m’kukumba kwauzimu, monga ngati kwa chuma chobisika.—Salmo 105:4, 5.
Kupeza Nthaŵi Yokumba
7. (a) Kodi ndi zovuta zotani zomwe ziripo zimene zingasokoneze kupeza kwathu chidziŵitso cholongosoka? (b) Kodi nchiyani chimene chingakhale chotulukapo cha kunyalanyaza uzimu?
7 Anthu ambiri lerolino amakhala ndi miyoyo yotanganitsidwa, ndipo monga Akristu timawoneka kukhala otanganitsidwa kwenikweni ndi ndandanda zathu za misonkhano ya Baibulo, utumiki wakumunda, ntchito yakuthupi, ntchito yapanyumba, ntchito ya kusukulu, ndi zina zotero kuposa onse. Komabe, monga mmene timandandalitsira nthaŵi tsiku lirilonse kuti tidye, choteronso tiyenera kuika pambali nthaŵi ya kudyetsa maganizo athu ndi uzimu wathu. Sinali ndemanga yopanda pake imene Yesu anapanga pamene anagwira mawu Deuteronomo 8:3 kuti: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Ngati tinyalanyaza uzimu wathu, tikunyalanyaza mapindu athu auzimu ndi chiyembekezo chathu chamtsogolo. Kenaka tingayambe kupatuka ndi kugwa. Chotero kodi ndimotani mmene tingapezere nthaŵi ya phunziro laumwini lokhazikika la Baibulo?
8. Kodi ndi uphungu Wamalemba wotani umene umatipatsa kayang’anidwe kabwino ka phunziro laumwini?
8 Mawu a mtumwi Paulo ali oyenereradi: “Yang’anitsitsani kuti mmene muyendera simonga opanda nzeru koma monga anthu anzeru, mukumadzipezera nthaŵi, chifukwa masiku ali oipa. Chifukwa cha ichi lekani kukhala osalingalira, koma pitirizani kuzindikira chimene chiri chifuno cha Yehova.” Tingakhozedi kuzindikira chimene chiri chifuno cha Yehova ngati titchera khutu ku Mawu ake kupyolera m’phunziro lathu laumwini. Ndipo chimenecho chimatanthauza kuti tiyenera ‘kupeza nthaŵi’ kapena ‘kugwiritsira bwino koposa nthaŵi yathu.’—Aefeso 5:15-17; Phillips.
9. Kodi nkuti kumene tingakhale tikuwonongera nthaŵi yathu imene ingawomboledwe kaamba ka phunziro laumwini? Perekani zokumana nazo zaumwini.
9 Titasanthula ntchito zathu zopanda pake za tsiku ndi tsiku, kodi timapeza kuti yochulukira ya nthaŵi yathu yapambali imawonongedwa motani? Kodi ndi kutsogolo kwa wailesi yakanema? Chiwiya chochititsa tondovi chimenecho chingabe nthaŵi iriyonse kuchokera pa maola aŵiri kufika ku asanu m’moyo wathu madzulo aliwonse! Kodi panokha mumathera maola angati patsiku mukupenyerera wailesi yakanema? Kaŵirikaŵiri, zimene zimawonetsedwa mwa chigogomezero chake pa chiwawa ndi kugonana, ziri zonyonyotsoka. Ndipo kaŵirikaŵiri zimalinganizidwira kudzutsa “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo uno.” (1 Yohane 2:15-17) Komabe, ambiri alibe mphamvu yodziletsa kuti azime wailesi yakanema. Inde, chopangidwa chamakonochi chingadye chuma chathu cha mtengo koposa, nthaŵi.
10. Kodi nchifukwa ninji chiri chofunika chotero lerolino kuti tigwiritsire ntchito nthaŵi yathu mwanzeru?
10 Ngati ndife owona mtima kwa ife eni, tidzazindikira kuti kaŵirikaŵiri nchotheka kuwombola nthaŵi kaamba ka zochita zofunika zonga ngati phunziro Labaibulo. Ndipo phunziro laumwini Labaibulo limene limatsogolera ku chidziŵitso cholongosoka liri lofunika kwa Mkristu m’nthaŵi zovuta zino. Komabe, pokhala ndi 41,000 ochotsedwa chaka chatha, chiri chowonekera kuti abale ndi alongo ambiri anyalanyaza uzimu wawo. Kuvala ndi kusungabe “zida zonse za Mulungu” sikuli kokha maseŵera. Monga mmene zimakhalira ndi msilikali amene wavala zida zenizeni zankhondo, iyo imakhala ntchito yatsiku ndi tsiku.—Aefeso 6:10-18; Aroma 1:28-32; 2 Timoteo 3:1.
11. Kodi ndi chitsanzo chotani chimene banja la Beteli limakhazikitsa m’kukhala olinganizidwa kaamba ka phunziro labanja?
11 Kuzungulira dziko lonse ziŵalo za mabanja a Beteli zoposa 9,000 pa nthambi 95 za Watch Tower Society zimakhala ndi phunziro lawo labanja madzulo aliwonse pa Lolemba. Iwo amaphunzira Nsanja ya Olonda m’kukonzekera msonkhano wa kothera kwa mlungu, ndipo nthaŵi zambiri amakhalanso ndi nkhani ya Baibulo kapena phunziro la m’kalasi kaamba ka ziŵalo zatsopano za banjalo. Inde, usiku wa Lolemba uli wa phunziro labanja la Beteli dziko lonse. Kodi ndi iti imene iri nthaŵi ya phunziro lanu laumwini kapena labanja?—Ahebri 10:24, 25.
Zipangizo ndi Mmene Mungazigwiritsire Ntchito
12. Kodi ndi ziti zimene ziri mbali zina zapadera za phunziro za New World Translation of the Holy Scriptures—With References?
12 Mongadi mmene wamumgodi amakhalira ndi zipangizo kaamba ka ntchito yake, choteronso tiri ndi zipangizo zimene tingakumbire mgodi wa golidi wa Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, lingalirani New World Translation of the Holy Scriptures—With References. Iyo pakali pano yafalitsidwa mu chinenero cha Chidutch, Chingelezi, Chifrench, Chigerman, Chiitalian, Chijapanese, Chipwitikizi, ndi Chispanya. Chotero, Mboni za Yehova zambiri ziri nacho chipangizo chamtengo cha kupezera chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu woona. Bukhu la Baibulo limeneli lirinso ndi zikwi za zilozero za m’danga lapakati ndi mawu a m’munsi ochulukira. Lirinso ndi mawu othera a masamba 36 okhala ndi chidziŵitso chatsatanetsatane pa mafunso ofunika a Baibulo osiyanasiyana.b
13. Kodi ndi mbali zosangalatsa zotani zimene zaperekedwa ponena za kugwiritsira ntchito kwa “chidziŵitso” ndi “chidziŵitso cholongosoka” m’Malemba Achihebri ndi Malemba Achigriki?
13 Kumbuyo kwake, Reference Bible iri ndi ndandanda yaikulu ya “Bible Words Indexed” (Mawu a Baibulo Oikidwa Motsatizana Bwino). Kodi imeneyo tingaigwiritsire ntchito motani? Mutafufuza kope lanu kaamba ka mawu akuti “accurate knowledge” (chidziŵitso cholongosoka), mudzapeza malemba khumi ondandalitsidwa. Koma palibe n’limodzi lomwe la awa lomwe liri m’Malemba Achihebri. Kodi chimenecho chimatanthauza kuti Malemba Achihebri samagogomezera kufunika kwa chidziŵitso choterocho? Ayi. Popeza kuti pansi pa liwu lakuti “knowledge” (chidziŵitso), pali zilozero 24, kuphatikizapo 18 zochokera m’Malemba Achihebri. Komabe, chinenero Chachihebri chiribe liwu lapadera kaamba ka “chidziŵitso cholongosoka.” Chotero, monga mmene mudzawonera kuchokera mu zilozerozo, iyo nthaŵi zina imagogomezera kufunika kwa choposadi chidziŵitso chachisawawa mwa kugwirizanitsa “chidziŵitso” ndi mawu onga ngati “kuzindikira” ndi “kudziŵa” kapena kulankhula za chidziŵitso kukhala “chochuluka.”—Danieli 1:4; 12:4; Yeremiya 3:15.
14. Kodi ndi mfundo zosangalatsa zotani zimene ziripo pansi pa “chidziŵitso” mu Insight on the Scriptures?
14 Monga mmene tinaphunzirira m’nkhani yapitayo, Baibulo Lachigriki linaika kusiyana kwamachenjera pakati pa milingo iŵiri ya chidziŵitso. Ndipo pamene tikukumba, tikufuna kudziŵa zochulukira ponena za kusiyana pakati pa mawu aŵiri ameneŵa pamene akugwira ntchito kwa Akristu. Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso, gnoʹsis, ndi chidziŵitso cholongosoka, e·piʹgno·sis, ziri zofunika kwa Akristu? Kodi nkuti kumene tingapeze yankho? M’bukhu lanazonse la Baibulo Insight on the Scriptures. Ndi nyumba yachuma chotani nanga imene mavolyumu ameneŵa ali! Yang’anani mutu wakuti “Knowledge” (Chidziŵitso). Pamenepo mudzapeza nkhani yathunthu yonena za mawu amene tikulingalira ndi mawu ena ogwirizana nawo nzeru, kumvetsetsa, kuzindikira, ndi luntha la kuganiza. Ndipo tapeza “golidi” yonseyi, chidziŵitso chimenechi, mwa kungogwiritsira ntchito zothandizira za Baibulo zoŵerengeka! Koma pali zowonjezereka.—Salmo 19:9, 10.
15. Kodi ndi zipangizo zina zofufuzira zotani zimene tiri nazo, ndipo kodi zingagwiritsiridwe ntchito motani?
15 Ngati munafuna kuyamba phunziro lakuya kwenikweni la liwu lakuti “chidziŵitso” ndi mawu ogwirizana nalo, inu mungagwiritsire ntchito Zosonyezera za mabukhu a Watch Tower Society, zomwe ziripo m’zinenero zingapo. Mongadi mmene tapezera mutu wakuti chidziŵitso, inu mungatsatire njira yofananayo pa mazanamazana a nkhani zina. Tangolingalirani chuma cha chidziŵitso chimene chimapezeka pansi pa dzina la Yehova! Ndi chidziŵitso cholongosoka cha mwana alirenji chotani nanga chimene chiripo ponena za Mfumu Ambuye wa chilengedwe chaponseponse!—Salmo 68:19, 20; Machitidwe 4:24.
16. Kodi Malemba amanenanji ponena za kufufuza?
16 Pokhala ndi izi limodzi ndi zothandizira phunziro zina zofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society, ndi “chuma chobisika” chokongola chotani nanga chimene tingapeze! Kodi mukufuna “golidi”? Kodi mukuganiza kuti ndi waphindu? Kodi mudzakhala ndi nthaŵi yakumkumba?—Miyambo 2:1-5.
Kodi Ndani Amene Amatsogolera M’kukumba Kwauzimu?
17. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipeze chidziŵitso cha Mulungu ndi Kristu?
17 Kodi ndi iti imene iri mfungulo yopezera chidziŵitso cha mtengo chimenechi cha Mulungu ndi Kristu? Chisonkhezero—chikhumbo cha kufuna kaimidwe kovomerezedwa ndi Yehova ndi Mwana wake ndi chilakolako cha kulandira mphatso ya moyo wosatha. Yesu anachiika mwanjira iyi: “Pitirizanibe kupempha, ndipo mudzapatsidwa; pitirizanibe kufunafuna, ndipo mudzapeza; pitirizanibe kugogoda, ndipo mudzatsegulidwa. Pakuti yense wakupempha alandira, ndi wakufunayo apeza, ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.” Koma onani lamulo lake. Yesu ananena kuti, ‘Pitirizanibe kupempha, kufunafuna, ndi kugogoda.’ Sichiri chinthu chochitidwa kamodzi kwatha. Kufunafuna chidziŵitso kuyenera kukhala koumirira.—Mateyu 5:6; 7:7, 8, NW.
18. M’banja, kodi ndani yemwe ayenera kutsogolera m’kufunafuna chidziŵitso cholongosoka, ndipo nchifukwa ninji?
18 M’banja Lachikristu, ndani amene ayenera kutsogolera m’kukumba chidziŵitso cholongosoka? Paulo akuyankha kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova].” Inde, makolo, makamaka atate, ayenera kutsogolera m’kusonyeza chiyamikiro cha mapindu auzimu. Ndipo chimenecho chimatikumbutsanso za kufunika kwa makonzedwe okhazikika amene banja lingayembekezere ndi kuyang’ana kutsogolo.—Aefeso 6:4.
19. Kodi nthaŵi zophunzira za banja zingapangidwe motani kukhala zosangalatsa? Kodi nkuti kumene kuli kuzoloŵera kwa banja lanu?
19 Nthaŵi za phunziro la banja zingapangidwe kukhala zosangalatsa. Mwachitsanzo, ngati muli ndi ana, bwanji osawalola iwo kusankha mutu wa nkhani ndipo kenaka kuwagaŵira iwo kukafufuza m’mabukhu osiyanasiyana molingana ndi msinkhu wawo ndi luntha. Kenaka pambuyo pa ola limodzi kapena kuposapo, khalani pamodzi ndi kuwona chimene aliyense wapeza pa nkhani yogaŵiridwa. Ngati pali concordance, wachichepere angaŵerenge nthaŵi zimene liwu linalake limawonekera m’Malemba Achihebri ndi Malemba Achigriki. Mwinamwake wachikulirepo angasanthule ngale m’mavolyumu a Insight. Makolo amadziŵa kuthekera kwa ana awo ndi utali wa kutchera kwawo khutu ndipo ayenera kumangirira kukambitsiranako pa nsonga zimenezo. Khalani wosawumirira pachimodzi ndi woyamikira. Limbikitsani banja lanu m’kukumba kwawo kwauzimu—ndipo khalani ndi cholinga chabwino.
Kukumba Ndi Cholinga Chabwino
20. Kodi ndi cholinga choipa chotani chimene tiyenera kupeŵa m’phunziro lathu laumwini?
20 Kufatsa kuli ubwino Wachikristu. (Miyambo 11:2; 1 Timoteo 2:9) Pamenepa, kodi tiyenera kumaphunzira ndi cholinga chofuna kudzitukumula ndi zimene taziphunzira? Kapena kodi tiyenera kuwonetsera poyera chidziŵitso chathu ndipo mwinamwake kusonyeza ena kukhala mbuli? Kapena kodi tiyenera kubukitsa kumasulira kwathukwathu kapena zolinga? Paulo analangiza kuti: “Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagaŵira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.”—Aroma 12:3.
21, 22. Kodi chidziŵitso chathu cholongosoka chiyenera kutiyambukira motani?
21 Kuyesayesa kwa mtima wonse ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka kungatsogolere ku chikhulupiriro, ubwino, kudziletsa, chipiriro, kudzipereka kwaumulungu, chiyanjo chaubale, ndi chikondi. Petro anasonyeza kufunika kwa zimenezi pamene analemba kuti: “Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye wathu Yesu Kristu.”—2 Petro 1:2-8.
22 Chidziŵitso chathu chiyenera kuyambukira mtima. Chiyenera kutifulumiza kusonyeza chikondi cha Mulungu ndi cha mnansi ndi kukhala Akristu ophulapo kanthu mumkhalidwe wathu ndi utumiki. Ichi chidzatulukapo umodzi ndi kumvetsetsa kokwanira kwa chitsanzo cha Kristu. (Aefeso 4:13) Ndi mphotho yabwino chotani nanga ya kufunafuna chuma chobisika!
[Mawu a M’munsi]
a Mosangalatsa, pa Miyambo 2:5 mawu akuti “chidziŵitso chenicheni cha Mulungu” amapezeka mu Septuagint Yachigriki kukhala e·piʹgno·sis, kapena “chidziŵitso cholongosoka,” kumodzi kwa kugwiritsira ntchito kusanu ndi kutatu kwa liwu Lachigriki limenelo mu Septuagint.
b Kaamba ka kulongosola kwatsatanetsatane kwa mmene mungapezere zochulukira kuchokera mu Reference Bible, onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1986, masamba 28-31.
Mafunso Olingalirapo
◻ Mogwirizana ndi Mfumu Solomo, kodi nchiyani chimene chiri chamtengo kwenikweni kuposa chuma chobisika?
◻ Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika koposa kwa odzozedwa ndi kwa nkhosa zina?
◻ Kodi ndimotani mmene tingapezere nthaŵi ya phunziro laumwini?
◻ Kodi ndi zipangizo zapadera zotani zimene tiri nazo zokumbira chidziŵitso cholongosoka?
◻ Kodi ndani yemwe ayenera kutsogoza paphunziro labanja, ndipo kodi tiyenera kuphunzira ndi cholinga chotani?