Lamulo la Makhalidwe Abwino—Kodi Ilo Nchiyani?
“TAWONANI! Sindivutitsa anansi anga. Malinga ndi mmene ndidziŵira, iwo angachite chimene amafuna. Ndithudi, ngati iwo anali m’mavuto, ndingachite zomwe ndingathe kuwathandiza.” Kodi kameneko ndiko kalingaliridwe kanu? Pamene masoka akantha, ntchito zachifundo ndi kupanda dyera zingawonekere, kaŵirikaŵiri modabwitsa ambiri. Koma kodi zimenezi nzokwanira?
Ngati ndinu kholo, mosakaikira mwalangiza ana anu kupeŵa kukwiyitsa anzawo oseŵera nawo. Ambirife tiri ndi zipsyera za ku uchichepere wathu zosonyeza kuti kunyalanyaza chitsogozo chimenecho kumabweretsa kubwezera. Inde, taphunzira nzeru ya mwambi wowunikiridwa ndi wanthanthi Wakum’mawa Confucius: “Chimene simukufuna kuti chichitidwe kwa inu, musachichite kwa ena.” Ngakhale ndi tero, kodi mumadziŵa kuti imeneyi iri njira ina yotsika ndi yosachitira ena ya lodziŵika kukhala Lamulo la Makhalidwe Abwino?
Lamulo Lakuchitira Ena
Mogwirizana ndi Webster’s New Collegiate Dictionary, “lamulo la makhalidwe abwino” likulongosoledwa kukhala “lamulo la makhalidwe a mwambo lolozera ku [Mateyu] 7:12 ndi [Luka] 6:31 ndipo limanena kuti munthu ayenera kuchita kwa ena monga mmene akafunira ena kumchitira.” Yang’anani m’bokosi lomwe liri pansi pa tsambali ndi kulingalira mmene matembenuzidwe a Baibulo osiyanasiyana a Mateyu chaputala 7, vesi 12 amalolera ubwino wa lamulo la makhalidwe abwino lotsogoza limeneli kuwonekera.
Chonde onani kuti ngakhale kuti mawuwo amasiyana pa matembenuzidwe amodzi ndi ŵena, lamulolo liri lakuchitira ena. Ndiiko komwe, monga mmene Yesu analingalirira poyambirirapo pa Ulaliki wa pa Phiri kuti: “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.” (Mateyu 7:7, 8) Kupempha, kufuna, kugogoda, onseŵa ali machitidwe akuchitira ena. “Chifukwa chake zinthu zirizonse,” Yesu anapitiriza akumati, “mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”—Mateyu 7:12.
Baibulo limasonyeza kuti ophunzira a Yesu nawonso anavomereza kukhalira moyo lamulo limodzimodzili. (Aroma 15:2; 1 Petro 3:11; 3 Yohane 11) Ngakhale ndi tero, nzachisoni kuti mkhalidwe wamakono wa maunansi a anthu umachitira umboni kuti m’mbali zonsezi, anthu, kaya odzinenera kukhala Akristu kapena ayi, samalitsatira. Kodi chimenechi chimatanthauza kuti lamulo limeneli la makhalidwe a mwambo silikugwiranso ntchito? Kapena kodi ilo n’lachikale?
[Bokosi patsamba 3]
“Chitani kwa anthu ena zonse zimene mukafuna kuti akuchitireni.”—The Holy Bible, lotembenuzidwa ndi R. A. Knox.
“Chitirani anthu ena mongadi mmene mungakondere kuchitiridwa ndi iwo.”—The New Testament in Modern English, lolembedwa ndi J. B. Phillips.
“Chirichonse chimene mumalakalaka kuti ena achite kwa inu ndi kaamba ka inu, moterodi chitani nanunso kwa iwo.”—The Amplified New Testament.
“Chitirani ena zonse zimene mufuna kuti akuchitireni.”—The New Testament in the Language of Today, lolembedwa ndi W. F. Beck.
“Pamenepa m’mbali zonse, chitirani anthu anzanu monga mmene mukafunira iwo kukuchitirani.”—The Four Gospels, lotembenuzidwa ndi E. V. Rieu.
“Muyenera kuzoloŵera kuchita ndi ena monga mmene mungakondere iwo kuchita nanu.”—The New Testament, lolembedwa ndi C. B. Williams.