Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 11/1 tsamba 8-9
  • Kuloŵa kwa Kristu Kolakika m’Yerusalemu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuloŵa kwa Kristu Kolakika m’Yerusalemu
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Kuloŵa m’Yerusalemu Kwachipambano kwa Kristu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Mfumu Inalowa mu Yerusalemu Itakwera pa Bulu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Amtama Yesu Kuti Ndiye Mesiya ndi Mfumu!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Yafika Nthaŵi”!
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 11/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kuloŵa kwa Kristu Kolakika m’Yerusalemu

M’MAWA motsatira, Sande, Nisani 9, Yesu akuchoka m’Betaniya ndi ophunzira ake ndipo akupita ku Phiri la Azitona kulinga ku Yerusalemu. Mwamsanga, iwo ayandikira Betefage, yokhala pa Phiri la Azitona. Yesu akulangiza aŵiri a ophunzira ake kuti:

“Mukani ku mudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nawo kwa ine. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza.”

Ngakhale kuti poyamba ophunzirawo akulephera kuzindikira kuti malangizo amenewa ali ndi chinachake chochita ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, pambuyo pake iwo akudziŵa chimenecho. Mneneri Zekariya ananeneratu kuti Mfumu yolonjezedwa ya Mulungu ikaloŵa m’Yerusalemu itakwera pa bulu, inde, “ndi mwana wamphongo wa bulu.” Mfumu Solomo nayenso adakwera pa mwana wa bulu pa kudzozedwa kwake.

Pamene ophunzira aloŵa m’Betefage ndi kutenga mwana wa bulu ndi mayi wake, ena oima pafupi akunena kuti: “Muchita chiyani?” Koma pamene awuzidwa kuti nyamazo zinali za Ambuye, amunawo akulola ophunzirawo kupita nazo kwa Yesu. Ophunzirawo ayala zovala zawo pa buluyo ndi mwana wake, koma Yesu akwera pa mwana wa buluyo.

Pamene Yesu akupita ku Yerusalemu, khamu liwonjezereka. Ambiri a anthuwo ayala zovala zawo m’njira, pamene ena akuthyola nthambi za mitengo ndi kuziyala izo. “Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la [Yehova]!” iwo afuula tero. “Mtendere m’mwamba, ndi ulemerero m’mwambamwamba!”

Afarisi ena m’khamulo akwiyitsidwa ndi kulengeza kumeneko ndipo adandaula kwa Yesu kuti: “Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.” Koma Yesu akuyankha kuti: “Ndinena ndi inu, ngati awa akhala chete miyala idzafuula.”

Pamene Yesu akuyandikira ku Yerusalemu, akuwona mzindawo ndi kuyamba kuwulirira, nanena: “Ukadazindikira tsiku iri, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.” Chifukwa cha kusamvera kwake kodzifunira, Yerusalemu ayenera kulipira mtengo, monga mmene Yesu akuneneratu kuti:

“Adani ako [Aroma pansi pa Kazembe Tito] adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwo kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake.” Chiwonongeko chimenechi cha Yerusalemu chonenedweratu ndi Yesu chikuchitikadi zaka 37 pambuyo pake, mu 70 C.E.

Kokha milungu yoŵerengeka poyambirirapo, ambiri m’khamulo anali atawona Yesu akuukitsa Lazaro. Tsopano iwowa akuuzabe ena za chozizwitsacho. Chotero pamene Yesu aloŵa m’Yerusalemu, mzinda wonsewo wasokonezeka. “Ndani uyu?” anthu afuna kudziŵa. Ndipo makamuwo angonenabe kuti: “Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya!” Powona zomwe zikuchitika, Afarisi akukwiya pokhala opanda chochita, namati: “Dziko limutsata.”

Monga mwachizoloŵezi chake pa kuchezera Yerusalemu, Yesu apita ku kachisi kukaphunzitsa. Kumeneko akhungu ndi opunduka adza kwa iye, ndipo awachiritsa! Pamene akulu ansembe ndi alembi awona zinthu zozizwitsa zimene Yesu akuzichita ndi pamene akumva ŵana m’kachisimo akufuula kuti, “Hosana kwa mwana wa Davide,” akwiyitsidwa. “Mulinkumva kodi chimene alikunena awa?” namatsutsa tero.

“Inde,” Yesu akuyankha. “Simunaŵerenga kodi, Mkamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?”

Yesu akupitiriza kuphunzitsa, nayang’anayang’ana pa zinthu zonse m’kachisimo. Mwamsanga kwada. Chotero akuchoka, limodzi ndi 12 enawo, ndi kubwerera pa ulendo wa makilomita atatu kapena kuposapo kupita ku Betaniya. Kumeneko athera usiku wa Sande, mwinamwake m’nyumba ya bwenzi lake Lazaro. Mateyu 21:1-11, 14-17; Marko 11:1-11; Luka 19:29-44; Yohane 12:12-19; Zekariya 9:9.

◆ Kodi ndi liti ndipo ndi mu mkhalidwe wotani umene Yesu akuloŵera m’Yerusalemu monga Mfumu?

◆ Kodi nchofunika kwambiri motani kuti makamu akutamanda Yesu?

◆ Kodi Yesu akudzimva motani pamene awona Yerusalemu, ndipo kodi ndi ulosi wotani umene iye akunena?

◆ Kodi nchiyani chimene chikuchitika pamene Yesu apita ku kachisi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena