Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/15 tsamba 32
  • Dziko Lonse Lidzakhala ndi Chakudya Chokwanira Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lonse Lidzakhala ndi Chakudya Chokwanira Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/15 tsamba 32

Dziko Lonse Lidzakhala ndi Chakudya Chokwanira Motani?

“MWINA kuchita kwathu khama kuti tikhale ndi chakudya chochuluka chimene takhala nacho zaka zambiri m’zana lino sikudzaphula kanthu,” akutero Lester Brown, pulezidenti wa bungwe la Worldwatch Institute ku Washington, D.C. Malinga ndi magazini ya New Scientist, kumayambiriro a 1995, chakudya chomwe chinali m’nkhokwe za dziko chinatsika kuposa kale kufikira matani 255 miliyoni​—chokwanira kudyetsa dziko lonse masiku 48 okha. Zaka zapitazi pamene chakudya m’nkhokwe chinatsika kufika poti nkudyetsa anthu masiku osakwanira 60, nkhokwezo zinali kudzalanso, zinthu zitawongokera. Koma tsopano bungwe la Worldwatch likukayika ngati mphamvu ya dziko lapansi ingabwezeretsenso zotayikazo.

Pokhala ndi zaka zitatu zimene ulimi sunayende bwino ndiponso ndi maiko ambiri omatukuka amene akupatsa zifuyo zokolola zawo, pali dzinthu dzochepa za osauka amene amazifuna monga chakudya chawo chachikulu. Magazini ya New Scientist ikuchenjeza kuti ngati mkhalidwewo susamalidwa msanga, anthu okwanira mamiliyoni chikwi chimodzi amene amatayira ndalama zawo zosachepera 70 peresenti pachakudya angayambe kufa ndi njala.

Baibulo linalosera kuti am’dziko lapansi panthaŵi yathu adzaona “njala.” (Luka 21:11) Komabe Mulungu akudziŵa za mavutowo. Inde, nkhaŵa yake pansautso ya munthu idzaonekadi pamene Ufumu wake udzayamba kulamulira dziko lapansi. Panthaŵiyo, ‘dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.’ “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.” (Salmo 67:6; 72:16) Ndiyeno mawu awa aulosi onena za Mlengi adzakwaniritsidwa: “Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira . . . Zigwa zakutidwa ndi tirigu.”​—Salmo 65:9, 13.

Kodi lonjezo lodabwitsa limenelo likukukopani? Kodi mukufuna kudziŵa mmene mungakhaliremo m’dzikolo? Ndiye funsani Mboni za Yehova kuti zikuuzeni zambiri ponena za Paradaiso wolonjezedwayo nthaŵi yotsatira imene zidzafika pakhomo panu. Ngati mufuna kuti wina akabwere kunyumba kwanu kudzachita nanu phunziro la Baibulo laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka, 10101, kapena kukeyala yoyenera pandandanda ya patsamba 2.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Chithunzithunzi chophatikizidwa: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena