Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 10/15 tsamba 5-7
  • Masada—Kodi Ili Umboni Wakuti Mesiya Anabwera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masada—Kodi Ili Umboni Wakuti Mesiya Anabwera?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudza kwa Mesiya
  • Malingaliro Achiyuda a Kulamulira kwa Akunja
  • Amesiya Onyenga
  • Uchete wa Akristu a ku Yudeya
  • Masada—Kodi Nchifukwa Ninji Inachitika?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Tapeza Ife Mesiya”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Gawo 10: 537 B.C.E. kupita mtsogolo—Kudikirirabe Mesiya
    Galamukani!—1989
  • “Tapeza Ife Mesiya”!
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 10/15 tsamba 5-7

Masada​—Kodi Ili Umboni Wakuti Mesiya Anabwera?

KUKHETSA mwazi m’dzina la chipembedzo kwakhala mliri wochitika kaŵirikaŵiri m’mbiri. Masada siinali yachilendo, popeza kuti achilikizi ake anali ndi zisonkhezero zamphamvu zachipembedzo. Mutachezera zofukulidwa za Masada, mungawone mabwinja a sunagoge kumene ambanda ankakumana kaamba ka kulambira ndi malo amwambo osambira ogwiritsiridwa ntchito kaamba ka kuyeretsa kwachipembedzo.

Zidutswa za Baibulo zapezedwanso pa Masada. Inu mungazizwe kuti, kodi uthenga wa Baibulo umene ambandawa anali nawo unafanana bwanji ndi umene timaŵerenga m’Baibulo lerolino? Dr. Yigael Yadin, m’bukhu lake lakuti Masada, analemba motere ponena za zotumbidwa zoyambirira zoterozo:

“Kusanthula kofulumira kwa malowo kunatisonyeza panthaŵi yomweyo kuti padali chidutswa chochokera mu Bukhu la Masalmo, ndipo tinakhoza ngakhale kuwona mituyo: chigawocho chinali cha Salmo 81 mpaka Salmo 85. . . . Chinali chotheka kuika deti popanda kukaikira kulikonse. Sichikanakhala chitapita chaka cha 73 AD, chaka chimene Masada inagwa. . . . Chigawo ichi chochokera mu Bukhu la Masalmo, mofanana ndi mipukutu ina yonse ya Baibulo imene tinaipeza pambuyo pake, nchofanana kwenikweni . . . ndi lemba la mabuku Abaibulo amene timagwiritsira ntchito lerolino.”

Mwachiwonekere, ambandawo anakhulupirira kuti Mlembi Waumulungu wa Malemba Achihebri akadalitsa kugalukira kwawo Roma. Monga momwe The Universal Jewish Encyclopedia ikufotokozera kuti: “Changu chopanda maziko cha Ayuda mu Nkhondo Yaikulu yolimbana ndi Roma (66-73 C.E.) chinalimbikitsidwa ndi chikhulupiriro chawo chakuti nyengo ya Mesiya inali pafupi kwenikweni. Kutaikiridwa kwa Kachisi kudangowonjezera ziyembekezo zonena za kudza kwa Mesiya.”

Kudza kwa Mesiya

The Encyclopedia of Religion ikulongosola kuti: “Ayuda okangalika ndi kudza kwa Mesiya kaŵirikaŵiri ankazika kuŵerengera kwawo pa Bukhu la Danieli.” Zowonadi, mneneri Wachihebri Danieli ananeneratu za kudza kwa “Mesiya Mtsogoleri.” (Danieli 9:25, NW) M’zolembedwa zina ziŵiri, Danieli ananena kuti Mesiyayo akakhala Wolamulira wa dziko ndikuti Ufumu Wake ukawononga maboma otsutsa a anthu onse.​—Danieli 2:44; 7:13, 14.

Ayuda ogalukira a m’zaka za zana loyamba analingalira kuti nthaŵi inali itafika ya kukwaniritsidwa kwa masomphenya aulosiwo. Josephus akulongosola kuti: “Chomwe chinawasonkhezera mopambanitsa kupita ku nkhondo, kuposa china chirichonse chinali [chikhulupiriro] chakuti panthaŵi imeneyo winawake wa m’dziko mwawomo akakhala wolamulira wa dziko.” Koma Danieli ananeneratu kuti Mesiya Mtsogoleriyo akayenera ‘kulikhidwa’ choyamba ndikuti pambuyo pa imfa yake Yerusalemu ndi kachisi wake zikawonongedwa ndi ‘anthu a mtsogoleri wina yemwe ankadza.’​—Danieli 9:25, 26, NW.

Malingaliro Achiyuda a Kulamulira kwa Akunja

Yudeya wa m’zaka za zana loyamba anagawidwa pakati pa achuma oŵerengeka ndi osauka ambiri. Ayuda ena achuma, makamaka pakati pa Asaduki ndi Afarisi, ananyadira ulamuliro umene Roma anawalola kukhala nawo padzikolo, ndipo anapeputsa anthu wamba. Motero, iwo anatsutsa lingaliro la kupanga masinthidwe, mmalo mwake analingalira zopanga unansi wamtendere ndi Roma.​—Luka 16:14; 19:45, 46; Yohane 2:14; 7:47-49; 11:47, 48.

Kumbali ina, Ayuda wamba anavutika pansi pa goli la msonkho wa Roma ndi kutsendereza kwa anthu a mtundu wawo. Iwo sanapeze chitonthozo chirichonse m’kukhala pansi pa chomwe chinkatchedwa Pax Romana (Mtendere Wachiroma) koma anafuna masinthidwe. Kupambadzukana kwa zikondwerero kumeneku kunatulukapo mkangano wowopsya wa pachiweniweni. “Gulu lina linaumirira pa kulamulira,” analemba motero Josephus, “linalo pa chiwawa ndi kubera achuma.”

Mwachitsanzo, ambandawo analanda ndi kupha Ayuda anzawo nalungamitsa machitachita auchigaŵenga ameneŵa kukhala chilango kwa Ayuda amene analingaliridwa kuti anagwirizana ndi Roma. Rabi wa m’zaka za zana lachiŵiri, Johanan ben Torta, anapereka chifukwa ichi kaamba ka tsoka lomwe linafikira Ayuda a m’zaka za zana loyamba: “Iwo analakalaka ndalama nadana okha.”

Nkosadabwitsa kuti Ayuda amene analidi owopa Mulungu analakalaka kudza kwa Mesiya, amene anamuyembekezera kuti akagwetsa kulamulira kwa Roma ndikukhazikitsa Ufumu wolungama wa Mulungu. Koma anthu opanda mwambo anagwiritsira ntchito ziyembekezo zimenezi.

Amesiya Onyenga

Pafupifupi chaka cha 33 C.E., mtsogoleri Wachiyuda wotchedwa Gamaliyeli anakumbutsa olamulira anzake a m’Yerusalemu kuti: “Pakuti asanafike masiku ano . . . anauka [Yudase, NW] wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.”​—Machitidwe 5:36, 37.

“Kulembedwa” kumene kunatulukapo kugalukira kwa Yudase kunalinganizidwa mu 6 C.E. ndicholinga chofuna kukweza misonkho ya Roma. Josephus akutiuza kuti Yudase analengeza kuti Ayuda “akatchedwa alideredere ngati akagonjera ku kupereka misonkho kwa Aroma.” Dzina lakuti Yudase limachokera ku dzina lakuti Yuda, kusonyeza kuti anali wochokera ku fuko limene Mesiya ankayembekezeredwa. (Genesis 49:10) “Kalankhulidwe kake kamotomoto ndi kutchuka kwa ziphunzitso zake kunakokera anthu ambiri kutsata miyezo yake, ambiri a iwo ankamulingalira kukhala Mesiya,” ikufotokoza motero Cyclopædia ya McClintock ndi Strong.

Onani kuti Machitidwe 5:37 akusimba kuti otsatira a Yudase ameneyu sanawonongeke naye pamodzi. Gulu lake, mogwirizana ndi katswiri Wachiyuda Gaalya Cornfeld, “linali lamphamvu ndi ziyembekezo za Mesiya.” Kwenikweni, atsogoleri aŵiri a ambandawo, Menahem ndi Eleazara, anali mbadwa zochokera kwa Yudase wa ku Galileya ameneyo. Pakuyambika kwa kupanduka Kwachiyuda mu 66 C.E., Menahem anakonzekeretsa atsatiri ake ndi zida zimene zinasungidwa pa Masada. Kenaka, “iye anabwerera monga mfumu ku Yerusalemu” ndipo “anakhala mtsogoleri wa gulu logalukiralo.” Encyclopaedia Judaica ikuwonjezera kuti: “Kuli pafupifupi kotsimikizirika kuti Menahem [mwana wa] Yuda analingaliridwa kukhala Mesiya.”

Komabe, m’chaka chimodzimodzicho, Menahem anaphedwa ndi ziŵalo za gulu la kugalukira Kwachiyuda lopanduka lotsutsana ndi lake. Atsatiri ake anathaŵira ku Masada, kumene Eleazara anayamba kulamulira ambandawo kufikira 73 C.E. Nkhani yakudzipha ya Eleazara ikumveketsa ziphunzitso zolakwika izi za Yudase, kholo lake loyambirira: “Chiyambire pamenepo, ine ndi mabwenzi anga olimba mtima, tinatsimikiza mtima kusatumikira Aroma kapena munthu wina aliyense koma Mulungu yekha.”

Uchete wa Akristu a ku Yudeya

Kupanduka Kwachiyuda kwa mu 66 C.E. kusanachitike, mipingo Yachikristu idali itakhazikitsidwa mu Yudeya, kuphatikizapodi mpingo wa Yerusalemu. (Machitidwe 9:31) Iyo inapangidwa ndi Ayuda amene anakhulupirira kuti Yesu wa ku Nazarete anali Mesiya amene imfa yake ndi chiukiriro zinali zinanenedweratu. (Machitidwe 2:22-36) Akristu Achiyudawo anakhala achangu m’kufalitsa zikhulupiriro zawo, pamene ankayembekezera mwamtendere kudza kwachiŵiri kwa Mesiyayo, monga wolamulira wa dziko. Yesu adasonyeza kuti akabwerera ‘itapita nthaŵi yaikulu.’​—Mateyu 25:19, 31; 28:19, 20; Machitidwe 1:8-11.

Koma pamene kupanduka Kwachiyuda kunabuka mu 66 C.E., kodi nchiyani chimene chinawachinjiriza Akristu a ku Yudeya amenewo kusatengeka ndi chipambano chake choyambirira? Mosakaikira iwo anakumbukira chenjezo ili la Mbuye wawo: “Onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Yesu adawapatsanso lingaliro lolinganizika la ulamuliro waboma wa Akunja. ‘Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara,’ iye anatero, ‘ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.’ (Marko 12:17) Kuwonjezerapo, Yesu adaneneratu kuti kukadza onyengezera kukhala Mesiya, akumati, “Ndine amene,” ndikuti, “Nthawi yayandikira,” koma iye anachenjeza kuti: “Musawatsate pambuyo pao.”​—Luka 21:8.

Yesu analoseradi zotulukapo za kupanduka Kwachiyudako, akumati: ‘Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo. . . . pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa. Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka ku mitundu yonse ya anthu.’​—Luka 21:20-24.

Chipiyoyo chowopsya cha chiwonongeko chimene chinatsatira kupanduka Kwachiyuda chinali kukwaniritsidwa kozizwitsa kwa ulosi wa Yesu! Komabe, Akristu a ku Yudeya anapulumuka mwa kumvera chenjezo la ‘kuthawira kumapiri.’ Encyclopaedia Judaica ikulongosola kuti: “Kulaliridwa kwa Yerusalemu kochitidwa ndi Tito [mu 70 C.E.] kusanachitike, mudzi wake Wachikristu unasamukira ku Pella.” Mosangalatsa, Pella inali kumpoto, patsinde pa mtandadza wa mapiri a kutsidya lina la Mtsinje wa Yordano ndipo motero anali wolekanitsidwa kotheratu ndi Yudeya ndi Chigwa cha Yordano. “Nkovuta kugwirizanitsa kupulumukaku kukanakhala kuti ulosi wa [Yesu] udalembedwa chochitikachi chitapita kale,” akutero G. A. Williamson m’mawu ake oyamba a bukhu lakuti Josephus​—The Jewish War.

Ndithudi, kupulumuka kwachipambano kwa Akristu a ku Yudeya ndiko umboni wamphamvu wakuti iwo adalidi atsatiri owona a Mesiya. Chimenechi chimadzutsa mafunso ofunika kwambiri. Kodi nchiyani chimene chinali chifuno cha kudza koyamba kwa Mesiya? Ndipo kodi kupanduka kwatsoka Kwachiyuda kukupereka chenjezo lotani kwa ife lerolino, makamaka kagulu ka anthu kamene kakudziŵika monga “Kachikristu”? Mafunso ameneŵa adzafotokozedwa kutsogoloku m’magazine ano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena