Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 June tsamba 8
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Kwambiri Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Kwambiri Yehova
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Makolo—Kodi Ana Anu Akukula Mwauzimu?
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 June tsamba 8
Yosefe ndi Mariya akuphunzitsa Yesu ndi abale ake pa nthawi ya chakudya

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Kwambiri Yehova

Makolo achikhristu amafunitsitsa kuona ana awo akukula n’kukhala atumiki okhulupirika a Yehova. Iwo angathandize anawo kuchita zimenezi ngati atayesetsa kumawaphunzitsa kuyambira ali aang’ono. (Deut. 6:7; Miy. 22:6) Kuchita zimenezi sikophweka, koma makolo amapeza madalitso ambiri ngati amaphunzitsa bwino ana awo.​—3 Yoh. 4.

Makolo angaphunzire zambiri kuchokera kwa Yosefe ndi Mariya. Chaka ndi chaka iwo ‘ankakonda kupita ku Yerusalemu, ku chikondwerero cha pasika,’ ngakhale kuti ulendowu unkafunika ndalama komanso unali wautali. (Luka 2:41) N’zoonekeratu kuti ankaona kuti zinthu zokhudza kulambira ndi zofunika kwambiri m’banja lawo. Masiku anonso makolo ayenera kuchita zilizonse zomwe angathe pophunzitsa ana awo mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso kuwasonyeza chitsanzo chabwino m’zochita zawo.​—Sal. 127:3-5.

KODI MUKUDZIWA?

Ngakhale kuti Yesu anakulira m’banja lokonda Yehova, abale ake ena sankamukhulupirira mpaka pamene Yesuyo anafa. (Yoh. 7:5; Mac. 1:14) Kenako abale ake awiri, Yakobo ndi Yuda analemba nawo mabuku a m’Baibulo odziwika ndi mayina awo.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANAGWIRITSA NTCHITO MWAYI UMENE ANALI NAWO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi a Jon ndi a Sharon Schiller anasonyeza bwanji kuti ankaika zinthu za Ufumu pa malo oyamba pamene ankalera ana awo?

  • Kodi makolo angatani kuti azipereka malangizo komanso chilango kwa mwana aliyense mogwirizana ndi mmene mwanayo alili?

  • Kodi makolo angakonzekeretse bwanji ana awo kuti asamagonje akamayesedwa?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene gulu la Yehova latulutsa zimene mumagwiritsa ntchito pothandiza ana anu kuti azikonda kwambiri Yehova?

Banja la a Schiller

Muziika zinthu zokhudza kulambira pa malo oyamba m’banja lanu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena