Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ulaliki Wotchuka Koposa Onse Operekedwapo
CHOCHITIKACHO ndicho chimodzi cha zosaiwalika koposa m’mbiri ya Baibulo: Yesu wakhala m’mphepete mwa phiri akukamba Ulaliki wake Wapaphiri wotchukawo. Malowo ndiwo pafupi ndi Nyanja ya Galileya, mwinamwake moyandikana ndi Kapernao. Yesu anali atatha usiku wathunthu kupemphera kwa Mulungu, ndipo m’mawa motsatira anali atasankha ophunzira ake 12 kukhala atumwi. Pamenepo, limodzi ndi iwo onse, anali atafika pamalo athyathyathya amenewa paphiripo.
Podzafika nthawi ino, mukanalingalira kuti Yesu akakhala wotopa kwambiri ndipo akafuna kugona pang’ono. Koma makamu aakulu akumtsatira, ena achokera mtunda wakutali ku Yudeya ndi Yerusalemu, mailosi 60 kapena 70 (100 mpaka 110 km). Ena achokera kumbali yanyanja ku Turo ndi Sidoni chakumpoto. Iwo adza kudzamva Yesu ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo. Palinso anthu ovutidwa ndi ziwanda.
Pamene Yesu akutsika, anthu odwala akumka chifupi naye kukamkhudza, ndipo akuwachiritsa onse. Pambuyo pake, Yesu mwachiwonekere akukwera pamalo otumphuka paphiripo. Pamenepo iye akukhala pansi nayamba kuphunzitsa khamu lotakata pamalo odikha pamaso pake. Ndipo tangokulingalirani! Tsopano mulibe ngakhale munthu mmodzi mwa omvetsera amene akudwala nthenda yowopsa!
Anthu akulakalaka kumva mphunzitsi amene ali wokhoza kuchita zozizwitsa zimenezi. Komabe, Yesu akupereka ulaliki wake kwakukulukulu kaamba ka phindu la ophunzira ake, amene mwinamwake asonkhana momkweteza moyandikana naye koposa. Koma, kuti ifenso tipindule, Mateyu ndi Luka aulemba.
Cholembedwa cha Mateyu cha ulaliki wapaphiri chiri chachitali pafupifupi kuwirikiza nthawi zinayi kuposa cha Luka. Ndiponso, zigawo zimene Mateyu walemba, Luka akuzinena ngati kuti zinanenedwa ndi Yesu panthawi ina mkati mwa uminisitala wake, monga momwe kungawonedwere mwa kuyerekezera Mateyu 6:9-13 ndi Luka 11:1-4, ndi Mateyu 6:25-34 ndi Luka 12:22-31. Komabe siziyenera kukhala zodabwitsa. Mwachiwonekere Yesu anaphunzitsa zinthu zimodzimodzizo nthawi yoposa imodzi, ndipo Luka anasankha kulemba zina za ziphunzitso zimenezi mu mpangidwe wosiyana.
Chimene chimapangitsa ulaliki kukhala wopindulitsa kwambiri sindicho kokha kuzama kwa zonenedwamo zauzimu koma kukhweka ndi kumvekera bwino mmene chowonadi chimenecho chinaperekedweramo. lye anatchula zokumana nazo zodziwika nagwiritsira ntchito zinthu zozolowereka kwa anthu, motero anapangitsa mfundo zake kuzindikirika mosavuta ndi onse amene akufunafuna moyo wabwino m’njira ya Mulungu. M’makope athu otsatira tidzapenda zina za zinthu zimene adanena. Luka 6:12-20; Mateyu 5:1, 2.
◆ Kodi ulaliki wotchuka koposa wa Yesu unaperekedwera kuti, kodi ndani amene analipo, ndipo kodi nchiyani chimene chidachitika mwamsanga usanakambidwe?
◆ Kodi nchifukwa ninji sikuli kodabwitsa kuti Luka akulemba ziphunzitso zina za ulaliki mu mpangidwe wina?
◆ Kodi nchiyani chimene chimapangitsa ulaliki wa Yesu kukhala wopindulitsa kwambiri?