Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jy mutu 2 tsamba 12-tsamba 13 ndime 10
  • Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Analemekezedwa Asanabadwe
  • Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nkhani Yofanana
  • Alemekezedwa Asanabadwe
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Gabirieli Anaonekera kwa Mariya
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mngelo Afikira Mariya
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
jy mutu 2 tsamba 12-tsamba 13 ndime 10
Mariya wakwera pabulu; Pamene Mariya akulowa m’nyumba mwa Elizabeti, Elizabetiyo akumva kuti mwana amene ali m’mimba mwake akudumpha mosangalala; Mariya akuthandiza Elizabeti kugwira ntchito zapakhomo

MUTU 2

Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

LUKA 1:34-56

  • MARIYA ANAPITA KUKACHEZA KWA MBALE WAKE ELIZABETI

Mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti adzabereka mwana wamwamuna yemwe adzamupatse dzina lakuti Yesu ndipo adzalamulira monga Mfumu mpaka kalekale. Zimenezi zinadabwitsa Mariya moti anafunsa kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, pakuti sindinagonepo ndi mwamuna?”—Luka 1:34.

Gabirieli anayankha kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:35.

Pofuna kumuthandiza Mariya kuti akhulupirire zimene ankamuuzazo, Gabirieli ananenanso kuti: “M’bale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka, nayenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake, ndipo uno ndi mwezi wa 6. Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena, sizilephereka.”—Luka 1:36, 37.

Zimene Mariya anayankha zinasonyeza kuti anavomereza zimene Gabirieli ananena, chifukwa anayankha kuti: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.”—Luka 1:38.

Gabirieli atangochoka, Mariya anayamba kukonza ulendo woti akacheze kwa Elizabeti, yemwe ankakhala ndi mwamuna wake Zekariya cha kumapiri a ku Yudeya pafupi ndi Yerusalemu. Kuchokera ku Nazareti kukafika kumene Elizabeti ankakhala unali ulendo wa masiku atatu kapena 4.

Kenako Mariya anafika kunyumba ya Zekariya. Pamene ankalowa n’kupereka moni kwa Elizabeti, mzimu woyera unafika pa Elizabeti ndipo ananena kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse. N’chodalitsidwanso chipatso cha mimba yako! Koma zatheka bwanji kuti dalitso limeneli lindigwere? Zatheka bwanji kuti mayi wa Mbuye wanga abwere kwa ine? Waona nanga! Pamenetu mawu a moni wako alowa m’makutu mwangamu, ndithu khanda ladumpha mosangalala kwambiri m’mimba mwangamu.”—Luka 1:42-44.

Mariya anayankha mosangalala kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova. Ndipo mzimu wanga sungaleke kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga. Chifukwa waona malo otsika a kapolo wake. Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wodala. Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu.” Ngakhale kuti anapatsidwa mwayi wobereka mwana wa Mulungu, Mariya anapereka ulemu wonse kwa Mulungu. Ananena kuti: “Dzina lake ndi loyera. Chifundo chake chakhala pa amene amamuopa ku mibadwomibadwo.”—Luka 1:46-50.

Mariya anapitiriza kulemekeza Mulungu ndipo ananena mawu omwe ndi ulosi kuti: “Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsira kutali odzikweza m’zolinga za mitima yawo. Watsitsa anthu amphamvu zawo pamipando yachifumu, ndipo wakweza anthu wamba. Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino, amene anali ndi chuma wawapitikitsa chimanjamanja. Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli. Wachita zimenezi posonyeza kuti akukumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo kwamuyaya, monga momwe anauzira makolo athu akale, Abulahamu ndi mbewu yake.”—Luka 1:51-55.

Mariya akuthandiza Elizabeti kugwira ntchito zapakhomo

Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi pafupifupi itatu ndipo ayenera kuti pa nthawi imeneyi ankamuthandiza ntchito zosiyanasiyana. Zimenezi zinali zothandiza kwambiri kwa Elizabeti chifukwa anali atangotsala pang’ono kubereka. Nthawi imene azimayi okhulupirikawa, omwe anatenga pakati mothandizidwa ndi Mulungu, anakhalira limodzi inali yosangalatsa komanso yapadera kwambiri.

Chochititsanso chidwi n’chakuti Yesu anayamba kulemekezedwa ngakhale asanabadwe. Mariya atangofika kunyumba kwa Elizabeti, Elizabeti anatchula mwana amene anali m’mimba mwa Mariyayo kuti “Mbuye wanga,” ndipo nthawi yomweyo mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti ‘anadumpha mosangalala kwambiri.’ Koma nkhani zakutsogoloku zikusonyeza kuti zimene zinachitika pa nthawi imeneyi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ena anachitira Mariya komanso mwana amene anali atatsala pang’ono kubereka.

  • Kodi Gabirieli ananena chiyani chomwe chinathandiza Mariya kumvetsa mmene adzakhalire ndi pakati?

  • Kodi Yesu analemekezedwa bwanji asanabadwe?

  • Kodi Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa nthawi yaitali bwanji ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena