-
“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”Nsanja ya Olonda—2013 | January 1
-
-
Abele anabadwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anthu analengedwa. Yesu ananena za Abele kuti anakhalapo “pamene dziko linakhazikika.” (Luka 11:50, 51) Pamenepa Yesu sankanena dziko lenileni koma ankatanthauza anthu amene anali ndi chiyembekezo choti adzawomboledwa. Ngakhale kuti Abele anali munthu wachinayi kukhalapo, zikuoneka kuti iye anali woyamba kuonedwa ndi Mulungu kuti angawomboledwe.a Choncho n’zoonekeratu kuti Abele sanakule ndi anthu achitsanzo chabwino.
-
-
“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”Nsanja ya Olonda—2013 | January 1
-
-
a Palembali mawu akuti “pamene dziko linakhazikika” amanena za kuberekana kwa anthu, choncho lembali likunena za ana a anthu oyambirira. Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena za Abele, kuti anakhalapo “pamene dziko linakhazikika” pomwe woyamba kubadwa anali Kaini? N’chifukwa choti zochita za Kaini zinasonyeza kuti anali wopandukira Yehova Mulungu. Mofanana ndi makolo ake, zikuoneka kuti Kaini sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa komanso kuwomboledwa ku uchimo ndi imfa.
-