Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
“[Yehova] aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.”—SALMO 46:9.
1. Kodi mu ulosi wa Yesaya tikupezamo lonjezo lotani labwino kwambiri lamtendere?
“NTCHITO ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthaŵi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” (Yesaya 32:17, 18) Ati kukongola kwake lonjezo limeneli! Ndi lonjezo la mtendere weniweni umene Mulungu adzadzetsa.
2, 3. Fotokozani mtendere weniweni.
2 Komano, kodi mtendere weniweni nchiyani? Kodi ndiwo chabe kusakhalako kwa nkhondo? Kapena wangokhala nyengo pamene mitundu ikukonzekera nkhondo yotsatira? Kodi mtendere weniweni ndi maloto okhaokha? Amenewo ndiwo mafunso amene tikufuna mayankho ake odalirika. Choyamba, mtendere weniweni ukusiyana kutali ndi maloto. Mtendere umene Mulungu walonjeza ukuposa chilichonse chimene dzikoli lingaganizire. (Yesaya 64:4) Suuli mtendere wa zaka zingapo kapena zaka makumi angapo. Uli wosatha! Ndipo suuli mtendere wa anthu angapo amwaŵi—umakhudza kumwamba ndi dziko lapansi, angelo ndi anthu. Umafika anthu a mitundu yonse, mafuko, manenedwe, ndi maonekedwe. Ulibe malire, zopinga, ndipo sulephera.—Salmo 72:7, 8; Yesaya 48:18.
3 Mtendere weniweni umatanthauza mtendere masiku onse. Umatanthauza kuti muzidzuka mmaŵa uliwonse popanda kuganiza za nkhondo, popanda kuda nkhaŵa za mtsogolo mwanu, mtsogolo mwa ana anu, ngakhale mtsogolo mwa adzukulu anu. Umatanthauza mtendere weniweni wa maganizo. (Akolose 3:15) Umatanthauza kusakhalakonso kwa upandu, kutheratu kwa chiwawa, kusaswekanso kwa mabanja, kusakhalakonso kwa anthu opanda nyumba, kusakhalakonso kwa anthu anjala kapena ozizidwa, ndi kutheratu kwa mantha ndi zokhumudwitsa. Ndipotu, mtendere wa Mulungu umatanthauza dziko lopanda matenda, zopweteka, chisoni, kapena imfa. (Chivumbulutso 21:4) Tili ndi chiyembekezo chabwino chotani nanga cha kusangalala ndi mtendere weniweni kosatha! Kodi umenewu sindiwo mtundu wa mtendere ndi chimwemwe umene tonsefe tikulakalaka? Kodi sindiwo mtundu wa mtendere umene tiyenera kuupempherera ndi kuugwirira ntchito?
Zoyesayesa Zolephereka za Munthu
4. Kodi mitundu yayesayesa kuchitanji ponena za mtendere, ndipo patuluka zotani?
4 Kwa zaka mazana ambiri, anthu ndi mitundu alankhula za mtendere, akangana za mtendere, asainirana mapangano a mtendere mazana ambiri. Kodi patsatiranji? Pazaka 80 zapitazi, sipanakhaleko nthaŵi imene panalibe mtundu wina kapena gulu lina limene likumenya nkhondo. Mwachionekere, mtendere wawazemba anthu. Choncho funso ndi ili, Kodi nchifukwa ninji kulimbikira konse kwa munthu kukhazikitsa mtendere padziko lonse kwalephera, ndipo nchifukwa ninji munthu sangathe kudzetsa mtendere weniweni wachikhalire?
5. Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zonse kulimbikira kwa munthu kudzetsa mtendere kwalephera?
5 Yankho lapafupi nlakuti anthu sanayang’ane kwa munthu yemwe ali woyenera kudzetsa mtendere weniweni. Mosonkhezeredwa ndi Satana Mdyerekezi, anthu apanga mabungwe amene amakhalanso ndi zofooka zawo ndi zoipa zawo—umbombo wawo ndi chikhumbo chawo cha kukhala pamalo apamwamba, kukhumbitsa kwawo mphamvu ndi kudziŵika. Iwo apita kusukulu zapamwamba nakhazikitsa mabungwe opereka thandizo ndi timagulu ta aphungu, angolinganiza njira zambiri zoponderezera ndi zowononga. Kodi anthu atsogozedwa kuti? Kodi iwo ayang’ana kuti?
6, 7. (a) Kodi bungwe la League of Nations linadzipangira mbiri yotani? (b) Kodi bungwe la United Nations lili ndi mbiri yotani?
6 Kalelo mu 1919 mitundu inadalira bungwe la League of Nations kuti ndilo lidzakhazikitsa mtendere wachikhalire. Chiyembekezo chimenecho chinasweka pamene Mussolini analanda Ethiopia mu 1935 ndi pamene nkhondo yachiŵeniŵeni inaulika ku Spain mu 1936. Bungwe limenelo linangozimiririka mu 1939 pamene Nkhondo Yadziko II inaulika. Umene ankati mtenderewo sunathe ndi zaka 20 zomwe.
7 Bwanji nanga za bungwe la United Nations? Kodi lapereka chiyembekezo chenicheni chilichonse cha mtendere wachikhalire wa padziko lonse? Kutalitali. Nkhondo zoposa 150 zamenyedwa kuyambira pamene linakhazikitsidwa mu 1945! Ndiye chifukwa chake Gwynne Dyer, wophunzira za nkhondo ndi zochititsa zake wa ku Canada, anafotokoza kuti UN lili “bungwe la opha nyama zakutchire popanda chilolezo amene aikidwa kukhala osunga nyama zakutchirezo, osati bungwe la oyera mtima,” ndi kuti lili “bungwe lopanda mphamvu kumene anthu amangodziŵa kukamba basi.”—Yerekezerani ndi Yeremiya 6:14; 8:15.
8. Ngakhale akambitsirana za mtendere, kodi mitundu yakhala ikuchitanji? (Yesaya 59:8)
8 Ngakhale kuti amakambitsirana za mtendere, mitundu ikupitirizabe kupanga zida. Nthaŵi zambiri maiko amene amachirikiza misonkhano ya mtendere ndiwo amenenso amakhala patsogolo kupanga zida. Kufunitsitsa mapindu a malonda m’maiko ameneŵa kumawasonkhezera kupanga zida zakupha, kuphatikizapo mabomba oipa otchera pansi amene chaka chilichonse amapha kapena kulemaza anthu wamba pafupifupi 26,000, achikulire ndi ana. Umbombo ndi ukatangale ndizo zimawasonkhezera. Ziphuphu zimayendera limodzi ndi malonda a zida a padziko lonse. Andale ena amalemerera pamenepa.
9, 10. Kodi akatswiri akudziko anenanji ponena za nkhondo ndi zoyesayesa za anthu?
9 Mu December 1995, katswiri wa physics wa ku Poland ndipo wopata mphoto ya Nobel Prize for Peace Joseph Rotblat anapempha mitundu yonse kusiya mpikisano wa zida. Iye anati: “Njira yokha yoletsera [mpikisano wina wa zida] ndiyo kuletseratu nkhondo.” Kodi muganiza kuti zimenezi zidzachitika? Kuyambira mu 1928 kumka mtsogolo, mitundu 62 inasaina pangano la Kellogg-Briand Pact, mmene anati nkhondo sindiyo njira yothetsera mikangano. Nkhondo Yadziko II inasonyeza bwino lomwe kuti panganolo linali lopanda pake.
10 Kunena zoona, nkhondo yakhala chopunthwitsa chosatha panjira m’mbiri ya munthu. Monga analembera Gwynne Dyer kuti, “nkhondo yakhala mkhalidwe waukulu pa kutsungula kwa anthu, ndipo yakhala ndi mbiri yaitali mofananadi ndi kutsungulako.” Inde, pafupifupi kutsungula konse ndi maufumu onse akhala ndi ngwazi zake za nkhondo zolemekezeka, magulu ake a nkhondo achikhalire, nkhondo zake zotchuka, sukulu zake zopatulika za nkhondo, ndi nkhokwe zake za zida. Komabe, zaka zathu za zana lino zadziŵika ndi nkhondo zoposa zina zonse, ponse paŵiri pakuwonoga kwake ndi kutayitsa kwake miyoyo.
11. Kodi atsogoleri a dziko anyalanyaza mbali iti yofunika pa kufunafuna kwawo mtendere?
11 Nzoonekeratu kuti atsogoleri a dziko anyalanyaza nzeru yofunika ya pa Yeremiya 10:23 yakuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Popanda Mulungu, sipangakhale mtendere weniweni. Kodi ndiye kuti zonsezi zikutanthauza kuti nkhondo njosapeŵeka m’chitaganya chotsungula? Kodi zikutanthauza kuti mtendere—mtendere weniweni—wangokhala maloto chabe?
Kudziŵa Chochititsa Nkhondo Chenicheni
12, 13. (a) Kodi Baibulo limavumbulanji ponena za chochititsa chenicheni chosaoneka cha nkhondo? (b) Kodi Satana wachotsa motani maganizo a anthu panjira yeniyeni yothetsera mavuto a dzikoli?
12 Kuti tiyankhe mafunso amenewo, tifunikira kudziŵa bwino zimene zimachititsa nkhondo. Baibulo limanena zomveka kuti mngelo wopanduka Satana ndiye “wambanda” ndi “wabodza” woyambirira ndi kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (Yohane 8:44; 1 Yohane 5:19) Kodi wachitanji kuti achirikize machenjera ake? Timaŵerenga pa 2 Akorinto 4:3, 4 kuti: “Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawaŵalire.” Satana amachita zonse zotheka kuchotsa maganizo a anthu pa Ufumu wa Mulungu monga chothetsera mavuto a dzikoli. Amachititsa anthu khungu ndi kuwapandutsa kupyolera m’nkhani zochititsa magaŵano za khalidwe, zandale, ndi zachipembedzo, kuchititsa zimenezi kuoneka ngati zofunika kwambiri kuposa ulamuliro wa Mulungu. Mwachitsanzo, titenge utundu umene wabuka posachedwa padziko lonse.
13 Satana Mdyerekezi amachirikiza utundu ndi ufuko, chikhulupiriro chakuti dziko lako, fuko, kapena mtundu wako upambana wa ena. Chidani chozama chimene anthu anapondereza kwa zaka mazana ambiri chikubukanso ndi kusonkhezera nkhondo zambiri. Federico Mayor, mkulu wa bungwe la UNESCO, anachenjeza za mkhalidwewo kuti: “Ngakhale kumene mkhalidwe wakulekererana unali chizoloŵezi, kuopa alendo kwayamba kuonekera kwambiri, ndipo mawu okondera kapena atsankhu la fuko amene anaoneka ngati akale akumveka kaŵirikaŵiri.” Kodi pakhala zotulukapo zotani? Kuphana kochititsa kakasi m’dziko lomwe kale linali Yugoslavia ndi kuphana kwa mafuko ku Rwanda zili ziŵiri chabe za zochitika zimene zamveka dziko lonse.
14. Kodi Chivumbulutso 6:4 chimaisonyeza motani nkhondo ndi zotulukapo zake m’nthaŵi yathu?
14 Baibulo linalosera kuti m’nthaŵi ya mapeto a dongosolo ili la zinthu, kavalo wofiira, wophiphiritsira nkhondo, adzakhuphuthuka padziko lonse lapansi. Pa Chivumbulutso 6:4 timaŵerenga izi: “Anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.” Chiyambire 1914 tamuona wapakavalo wophiphiritsira ameneyu ‘akuchotsa mtendere,’ ndipo mitundu yapitirizabe kumenyana m’nkhondo.
15, 16. (a) Kodi chipembedzo chachitanji m’nkhondo ndi kuphana? (b) Kodi Yehova amaziona motani zinthu zimene zipembedzo zachita?
15 Sitinganyalanyaze mbali ya chipembedzo m’nkhondo zimenezi ndi m’kuphanaku. Mbiri ya anthu yakhala yokhathamira ndi mwazi makamaka chifukwa cha chisonkhezero chosokeretsa cha chipembedzo chonyenga. Katswiri wa zaumulungu wachikatolika Hans Küng analemba kuti: “Palibe amene angakane kuti m’mawu oipa, ndi owononga, [zipembedzo] zachirikiza zimenezo ndipo zidakachirikizabe kwambiri. Kulimbana kochuluka, nkhondo zamwazi, inde ‘nkhondo zachipembezo’ zili mlandu wake; . . . ndipo zimenezi zikuphatikizapo nkhondo zadziko ziŵirizo.”
16 Kodi Yehova Mulungu amaiona bwanji mbali ya chipembedzo chonyenga pakuphana ndi nkhondo? Kuzenga mlandu chipembedzo chonyenga kwa Mulungu, kolembedwa pa Chivumbulutso 18:5 kumati: “Machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.” Kugwirizana kwa chipembedzo chonyenga ndi olamulira a ndale za dziko kwachititsa liwongo lalikulu la mwazi, mulu waukulu wa machimo, wakuti Mulungu sangaunyalanyaze konse. Kwatsala pang’ono kuti achotsepo chopunthwitsa chimenechi panjira ya mtendere weniweni.—Chivumbulutso 18:21.
Njira ya Mtendere
17, 18. (a) Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira kuti mtendere wachikhalire ngwotheka si maloto wamba? (b) Kodi Yehova watani kale kutsimikiza kuti mtendere weniweni udzabwera?
17 Ngati anthu, kupyolera m’mabungwe onga United Nations, sangadzetse mtendere weniweni ndi wokhalitsa, kodi mtendere weniweni udzachokera kuti, ndipo udzabwera motani? Kodi kukhulupirira kuti mtendere wosatha uli wotheka kwangokhala maloto basi? Iyayi, makamaka ngati tiyang’ana kwa munthu woyenera wopereka mtendere. Ndipo ameneyo ndani? Salmo 46:9 limayankha mwa kutiuza kuti Yehova “aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.” Ndipo Yehova wayamba kale njira yothetsera nkhondo ndi kukhazikitsa mtendere weniweni. Motani? Mwa kukhazika Kristu Yesu pa mpando wake wa Ufumu mu 1914 ndi mwa kuchirikiza mkupiti waukulu koposa wa maphunziro a mtendere m’mbiri ya munthu. Mawu aulosi a pa Yesaya 54:13 amatitsimikiza kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.”
18 Ulosi umenewu umasonyeza choonadi cha mawu akuti chochitika chimatsata chochititsa—ndiko kuti, chochitika chilichonse chili ndi chochititsa. Panopa, chiphunzitso cha Yehova—chochititsa—chimasintha anthu okonda nkhondo kukhala anthu okonda mtendere okhala pamtendere ndi Mulungu. Chochitikacho ndicho kusintha kwa mtima kumene kumachititsa anthu kukhala okonda mtendere. Chiphunzitso chimenechi chimene chimasintha mitima ya anthu ndi maganizo awo chikufalikira ngakhale tsopano padziko lonse pamene mamiliyoni akutsanzira chitsanzo cha “Kalonga wa Mtendere,” Yesu Kristu.—Yesaya 9:6.
19. Kodi Yesu anaphunzitsanji ponena za mtendere weniweni?
19 Ndipo kodi Yesu anaphunzitsanji ponena za mtendere weniweni? Sanangolankhula za mtendere pakati pa mitundu komanso za mtendere pakati pa anthu m’maunansi awo ndi za mtendere wa mumtima umene chikumbutima chabwino chimapereka. Pa Yohane 14:27, timaŵerenga mawu a Yesu kwa otsatira ake kuti: “Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.” Kodi mtendere wa Yesu unali wosiyana motani ndi uja wa dziko?
20. Kodi Yesu adzaubweretsa motani mtendere weniweni?
20 Choyamba, mtendere wa Yesu unali wogwirizana kwambiri ndi uthenga wake wa Ufumu. Iye anadziŵa kuti boma lolungama lakumwamba, lopangidwa ndi Yesu ndi olamulira anzake a 144,000, lidzathetsa nkhondo ndi osonkhezera ake. (Chivumbulutso 14:1, 3) Anadziŵa kuti lidzadzetsa mikhalidwe yamtendere ya paradaiso amene analonjeza wochita zoipa uja amene anafera pambali pake. Yesu sanamlonjeze malo mu Ufumu wakumwamba, koma anati: “Indetu, ndinena ndi iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43, NW.
21, 22. (a) Kodi mtendere weniweni umaphatikizapo chiyembekezo chotani chabwino kwambiri ndi cholimbikitsa? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikaone dalitsolo?
21 Yesu anadziŵanso kuti Ufumu wake udzatonthoza onse olira amene asonyeza chikhulupiriro mwa iye. Mtendere wake umaphatikizapo chiyembekezo chabwino kwambiri ndi cholimbikitsa cha chiukiriro. Kumbukirani mawu ake olimbikitsa opezeka pa Yohane 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”
22 Kodi mukufunitsitsa kuti nthaŵiyo ifike? Kodi munatayapo okondedwa anu mu imfa? Kodi mukulakalaka kuwaonanso? Pamenepo landirani mtendere umene Yesu akukupatsani. Khalani ndi chikhulupiriro chonga chija cha Marita, mlongo wa Lazaro, yemwe anati kwa Yesu: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” Koma taonani yankho la Yesu lokondweretsa kwa Marita: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse. Kodi ukhulupirira ichi?”—Yohane 11:24-26.
23. Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu nchofunika kuti tipeze mtendere weniweni?
23 Inunso mungakhulupirire lonjezo limenelo ndi kupindula nalo. Motani? Mwa kupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu. Taonani mmene mtumwi Paulo anagogomezerera kufunika kwa chidziŵitso cholongosoka: “Sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso [“chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso [“m’chidziŵitso cholongosoka,” NW] cha Mulungu.” (Akolose 1:9, 10) Chidziŵitso cholongosoka chimenechi chidzakukhutiritsani kuti mtendere weniweni udzachokera kwa Yehova Mulungu. Ndiponso chidzakuuzani zimene muyenera kuchita tsopano kuti mugwirizane ndi wamasalmo ponena kuti: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.”—Salmo 4:8.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchifukwa ninji nthaŵi zonse kulimbikira kwa munthu kudzetsa mtendere kwalephera?
◻ Kodi chochititsa nkhondo chenicheni nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji mtendere wachikhalire si maloto wamba?
◻ Kodi mtendere weniweni udzachokera kuti?
[Chithunzi patsamba 8]
Mtendere weniweni si maloto ayi. Ndi lonjezo la Mulungu
[Chithunzi patsamba 10]
Chiyambire 1914 wokwera kavalo wofiira wophiphiritsira wachotsa mtendere padziko lapansi
[Chithunzi patsamba 11]
Kodi chipembedzo ndi UN zingadzetse mtendere?
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi cha UN