Chifukwa Chake Ena Amabadwanso
“KUSIYAPO ngati aliyense abadwanso, iye sangathe kuwona ufumu wa Mulungu.” (Yohane 3:3, NW) Mawu amenewo achititsa ponse paŵiri nthumanzi ndi kudabwitsa anthu ambiri chiyambire pamene Yesu Kristu anawalankhula zoposa zaka 1,900 zapitazo.
Kuti tipeze lingaliro lolondola la mawu a Yesu onena za kubadwanso, choyamba tiyenera kuyankha mafunso awa: Kodi chifuno cha Mulungu kaamba ka anthu nchiyani? Kodi nchiyani chimene chimachitikira moyo pa imfa? Kodi Ufumu wa Mulungu unalinganizidwira kuchitanji?
Chifuno cha Mulungu kwa Anthu
Munthu woyamba, Adamu, analengedwa ali mwana waumunthu wangwiro wa Mulungu. (Luka 3:38) Yehova Mulungu sanalinganize konse kuti Adamu ayenera kufa. Adamu ndi mkazi wake, Hava, anali ndi chiyembekezo chakubala banja laumunthu lopanda uchimo limene likakhala kosatha ndi kudzaza dziko lapansi la paradaiso. (Genesis 1:28) Imfa sinali mbali ya chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka mwamuna ndi mkazi. Inadudukira anthu kokha monga chotulukapo chachipanduko motsutsana ndi lamulo la Mulungu.—Genesis 2:15-17; 3:17-19.
Chipanduko chimenechi chinadzutsa nkhani zazikulu za makhalidwe abwino, monga ngati kuyenera kwa ulamuliro wa Mulungu ndi kukhoza kwa anthu kukhala okhulupirika ku malamulo ake. Nthaŵi ikafunika kuthetsa nkhani zimenezi. Koma chifuno cha Yehova Mulungu kaamba ka anthu sichinasinthe, ndipo iye sangathe kulephera zinthu zimene alinganiza kuchita. Iye akulinganiza kotheratu kudzaza dziko lapansi ndi banja laumunthu langwiro limene lidzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. (Salmo 37:29; 104:5; Yesaya 45:18; Luka 23:43) Tiyenera kukumbukira chowonadi chamaziko chimenechi pamene tipenda mawu a Yesu onena za kubadwanso.
Kodi Chimachitika Nchiyani ku Moyo pa Imfa?
Mosazindikira zimene mzimu woyera wa Mulungu unavumbulira olemba Baibulo, anthanthi aku Girisi anayesayesa mwaphamphu kupeza tanthauzo m’moyo. Sakakhoza kukhulupirira kuti munthu analinganizidwira kukhala moyo zaka zochepekera zokha, kaŵirikaŵiri m’mikhalidwe yomvetsa chisoni, ndiyeno kufa. Mwanjirayi analondola. Koma m’zotsimikiza zawo ponena za ziyembekezo za munthu pambuyo pa imfa, anali olakwa. Anatsimikiza kuti kukhalapo kwa munthu kunapitirizabe mumpangidwe wina pambuyo pa imfa, kuti mkati mwa munthu aliyense munali moyo wosakhoza kufa.
Ayuda ndi odzinenera kukhala Akristu anasonkhezeredwa ndi malingaliro otero. Bukhu lotchedwa Heaven—A History limati: “Paliponse pamene Ayuda obalalikawo anakumana ndi anzeru Achigiriki, lingaliro la kusakhoza kufa kwa moyo linabuka.” Bukhulo limawonjezera kuti: “Ziphunzitso za Agiriki zonena za moyo zinakhomerezeka kosatha pa Ayuda ndipo potsirizira pake pa ziphunzitso za Akristu. . . . Mwakupanga mlumikizo wapadera wanthanthi ya Plato ndi mwambo wa Baibulo, Philo [wanthanthi Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba waku Alesandriya] analambulira njira Akristu anzeru apambuyo pake.”
Kodi Philo anakhulupirira chiyani? Bukhu limodzimodzilo likupitiriza kuti: “Kwa iye, imfa imabwezeretsa moyo kumkhalidwe wake woyambirira, munthuyo asanabadwe. Popeza kuti moyo unachokera kudziko la mizimu, moyo m’thupilo umakhalako kokha mwachidule, kaŵirikaŵiri mumkhalidwe watsoka.” Komabe, ‘mkhalidwe wa Adamu asanabadwe, unali wakuti iye kunalibeko. Mogwirizana ndi cholembedwa cha Baibulo, Mulungu sanalinganize konse kusamutsa kochitika kokha kumka kumkhalidwe wina pa imfa, monga ngati kuti dziko lapansi linali kokha malo okonzekererapo moyo wapamwamba kapena wotsikirapo.
Chikhulupiriro chakuti moyo wa munthu ngwosakhoza kufa sichimaphunzitsidwa m’Mawu ouziridwa ndi mzimu a Mulungu, Baibulo. Silimagwiritsira ntchito liwu lakuti “moyo wosakhoza kufa” ngakhale kamodzi kokha. Ilo limanena kuti Adamu analengedwa monga moyo, osati ndi moyo. Genesis 2:7 amati: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.” Anthu sanakhale konse ndi chiyembekezo kaya chakukhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena chizunzo chosatha m’moto wa helo. Baibulo limasonyeza kuti moyo, kapena munthu, amene amafa samazindikira kanthu bi. (Salmo 146:3, 4; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Chotero, anthanthi amamatira ku lingaliro lotsutsana ndi malemba ponena za moyo. Tifunikira kuchenjera ndi malingaliro osocheza amene akakhoza kudodometsa kuzindikira kwathu mawu a Yesu onena za kubadwanso.
Obadwanso Akalamulira monga Mafumu
Yesu anauza Nikodemo kuti awo amene ‘abadwanso amaloŵa mu ufumu wa Mulungu.’ (Yohane 3:3-5) Kodi Ufumu umenewo nchiyani? M’chinenero chophiphiritsira pachiyambiyambi cha mbiri ya anthu, Yehova Mulungu anaulula chifuno chake chakugwiritsira ntchito “mbewu” yapadera—wolamulira alinkudza—kuphwanya mutu wa Chinjoka choyambirira, Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:15; Chivumbulutso 12:9) Monga momwe kwavumbulutsidwira mopita patsogolo m’Malemba, “mbewu” imeneyi imadziŵika monga Yesu Kristu, amene akulamulira ndi olamulira anzake m’chisonyezero chapadera cha ulamuliro wa Mulungu, Ufumu Waumesiya. (Salmo 2:8, 9; Yesaya 9:6, 7; Danieli 2:44; 7:13, 14) Umenewu uli Ufumu wa kumwamba, boma lakumiyamba limene lidzalemekeza uchifumu wa Yehova ndi kuwombola anthu ku ukapolo wauchimo ndi imfa.—Mateyu 6:9, 10.
Ogwirizana ndi Yesu monga olamulira pamodzi naye ndiwo a 144,000 amene agulidwa kuchokera mwa anthu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4) Mulungu wasankha ena kuchokera pa banja laumunthu lopanda ungwiro la Adamu kukhala “opatulika a wam’mwambamwamba,” amenewa amene akulamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu Waumesiya. (Danieli 7:27; 1 Akorinto 6:2; Chivumbulutso 3:21; 20:6) Amuna ndi akazi amenewa amaika chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, amene adanena kuti iwo “akabadwanso.” (Yohane 3:5-7, NW) Kodi ndimotani ndipo nchifukwa ninji kubadwa kumeneku kumachitika?
Anthu amenewa abatizidwa m’madzi monga otsatira a Kristu. Mulungu wawakhululukira machimo awo pamaziko ansembe yadipo la Yesu, wawalengeza kukhala olungama, ndipo wawalandira monga ana ake auzimu. (Aroma 3:23-26; 5:12-21; Akolose 1:13, 14) Kwa oterowo mtumwi Paulo akunena kuti: “Munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nawo, kuti, Abba, Atate. Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso oloŵa nyumba; inde oloŵa nyumba ake a Mulungu, ndi oloŵa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zoŵawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.”—Aroma 8:15-17.
Monga otsatira a Kristu, amenewa akhala ndi kubadwa kwatsopano, kapena chiyambi chatsopano, m’moyo. Kwachititsa chikhutiro chakuti iwo akakhala ndi phande m’choloŵa cha Yesu chakumwamba. (Luka 12:32; 22:28-30; 1 Petro 1:23) Mtumwi Petro anafotokoza kubadwanso m’njira iyi: “Monga mwa chifundo chake [cha Mulungu] chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’mwamba inu.” (1 Petro 1:3, 4) Moyo watsopano umenewu kumwamba umatheketsedwa kwa anthu amenewa chifukwa chakuti Mulungu amawaukitsa monga momwe anaukitsira Yesu.—1 Akorinto 15:42-49.
Bwanji za Dziko Lapansi?
Zimenezi sizitanthauza kuti anthu onse omvera potsirizira pake adzabadwanso ndi kusamuka padziko lapansi kumka kumwamba. Lingaliro lolakwika limeneli linali lofanana ndi limene linali ndi anthanthi onga Philo, amene analingalira kuti “moyo m’thupilo [suli] kanthu koma kuti ngwachidule, kaŵirikaŵiri mumkhalidwe watsoka.” Komatu panalibe cholakwika ndi zolengedwa zapadziko lapansi zoyambirira za Yehova Mulungu.—Genesis 1:31; Deuteronomo 32:4.
Moyo wa anthu sunalinganizidwire konse kukhala wachidule ndi womvetsa chisoni. Yesu Kristu ndi awo amene amabadwanso kukatumikira monga mafumu ndi ansembe limodzi naye kumwamba adzachotsa zotulukapo zovulaza zonse zachipanduko cha Satana. (Aefeso 1:8-10) Kupyolera mwa iwo monga ‘mbewu ya Abrahamu,’ yolonjezedwayo ‘mitundu yonse yadziko lapansi idzadzidalitsadi.’ (Agalatiya 3:29; Genesis 22:18) Kwa anthu omvera zimenezi zidzatanthauza moyo padziko lapansi la paradaiso, losiyana kwambiri ndi moyo wachidule, wodzala ndi chisoni ulipowu.—Salmo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:1-4.
Kodi Adzapindula ndani?
Pakati pa awo amene adzapindula ndi kakonzedwe ka Mulungu kakudalitsira anthu padzakhala akufa oukitsidwa amene asonyeza chikhulupiriro munsembe ya dipo la Yesu. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Unyinji wa iwo sunaphunzirepo za Mulungu ndi Kristu ndipo chifukwa chake sunasonyeze chikhulupiriro mwa Yesu. Oukitsidwawo adzaphatikizaponso anthu okhulupirika onga Yohane Mbatizi, amene anafa imfa ya Yesu isanachitike imene inatsegula njira ya moyo wakumwamba. (Mateyu 11:11) Kuwonjezera pa amenewa, ‘khamu lalikulu lochokera mwa mtundu uliwonse achapa miinjiro yawo naiyeretsa m’mwazi wa mwanawankhosa,’ Yesu Kristu. Iwo akulabadira mwachiyanjo kuntchito yolalikira Ufumu imene tsopano ikutsogozedwa ndi “abale” a Yesu obadwanso ndipo adzapulumuka nkhondo ya Mulungu ya Armagedo kukhala ndi moyo padziko lapansi loyeretsedwa. (Chivumbulutso 7:9-14; 16:14-16; Mateyu 24:14; 25:31-46) Chifukwa chake, m’kakonzedwe ka Mulungu, mamiliyoni adzapulumutsidwa, ngakhale kuti iwo sanabadwenso kuti alamulire ndi Kristu kumiyamba.—1 Yohane 2:1, 2.
Kodi inu mudzakhala pakati pa awo amene adzalandira choloŵa cha moyo padziko lapansi la Paradaiso? Mungathe ngati musonyeza chikhulupiriro munsembe ya Yesu Kristu ndi kugwirizana mokangalika ndi mpingo Wachikristu wowona. Uwo sunaipitsidwe ndi nthanthi koma wakhalabe “mzati ndi mchirikizo wa chowonadi.” (1 Timoteo 3:15; yerekezerani ndi Yohane 4:24; 8:31, 32.) Pamenepo mungathe kuyang’anira mtsogolo kunthaŵi yabwino pamene ana obadwanso a Mulungu akulamulira kumwamba ndi pamene ana onse a padziko lonse lapansi a Mulungu abwezeretsedwera ku ungwiro padziko lapansi lokongola la paradaiso. Chotero gwiritsitsani mwaŵi wanu kuti mupeze moyo m’dziko latsopano la madalitso osatha limenelo.—Aroma 8:19-21; 2 Petro 3:13.
[Chithunzi patsamba 6]
Adamu sanapatsidwe konse chiyembekezo kaya cha moyo kumwamba kapena chizunzo chosatha m’moto wa helo