Ikani Mulungu Patsogolo m’Moyo Wanu Wabanja!
BOB NDI JEAN—okwatirana otchulidwa m’nkhani yapitawo—sanasudzulane. Mmalomwake, anakambitsirana mavuto awo ndi minisitala Wachikristu. Iye mwamsanga anazindikira kuti chochititsa mavuto awo chachikulu chinali kusiyana kwa makulidwe awo.
Mwachitsanzo, popeza kuti Bob anachokera m’banja la ochita malonda ndi ogwira ntchito zotsika ndipo iye ankagwira ntchito yamanja yolimba, ankafuna chakudya cham’mawa chogwira pamimba m’mawa uliwonse. Jean, yemwe anachokera m’banja la antchito zapamwamba, anangomkonzera khofi ndi mkate wowotcha (uja amati thositi). Choncho mkangano wa chakudya cham’mawa unakula kukhala nkhondo yeniyeni!
Bob ndi Jean anafunikira kuwongolera kulankhulana kwawo. Komabe, chochititsa kupsinjika kwawo chenicheni chinakulakulabe. “Kodi mumalingalirana mogwirizana ndi 1 Akorinto 13:4?” adafunsa motero minisitalayo. Lemba la m’Baibulo limenelo limati: ‘Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.’ Vesi lotsatira limanena kuti chikondi ‘sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa.’ Onse aŵiri Bob ndi Jean adali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito mawu ameneŵa muunansi wawo.
Mavuto a okwatiranaŵa anafunikira kwakukulukulu mankhwala auzimu. Popeza kuti Bob ndi Jean ankakhumba kukhala ndi unansi wabwino ndi Mulungu, koposa zonse iwo adafunikira kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo ndi kuzindikira kuti ‘akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwira ntchito chabe.’ (Salmo 127:1) Mavesi 3 mpaka 5 amanena za kumanga banja. Ndipo chipambano chachikulu koposa m’kupititsa patsogolo chimwemwe chapanyumba chimabwera mwakuika Mulungu patsogolo m’moyo wabanja.—Aefeso 3:14, 15.
Zoloŵetsedwamo m’Kuika Mulungu Patsogolo
Kuika Mulungu patsogolo m’moyo wanu wabanja kumatanthauza zambiri kuposa mwambi wakuti, “Banja limene limapempherera pamodzi nlogwirizana.” Mogwirizana ndi magazini akuti Family Relations, ambiri amakhulupirira kuti “chipembedzo chimakhozetsa kuchitirana mwaubwino m’banja ndipo chimakulitsa chikhutiro cha moyo cha ziŵalo zake.” Koma kungopembedza sikofanana ndi kuika Mulungu patsogolo. Anthu ambiri amakhala ndi chipembedzo kokha chifukwa cha chizoloŵezi, mwambo wa banja, kapena ubwino wa mayanjano. Mulungu amakhala ndi chisonkhezero chochepa m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Chofunika kwambiri, sizipembedzo zonse zomwe ndi ‘mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu.’—Yakobo 1:27.
Kuti timuike Mulungu patsogolo m’moyo wathu wabanja, ifeyo ndi okondedwa athu tiyenera kulambira Yehova, “Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,” mogwirizana ndi ziyeneretso zake. (Salmo 83:18) Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anati: ‘Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:23, 24) Kuti timlambire Yehova Mulungu “mumzimu,” utumiki wathu wopatulika kwa iye uyenera kusonkhezeredwa ndi mtima wodzaza ndi chikondi ndi chikhulupiriro. (Marko 12:28-31; Agalatiya 2:16) Kumlambira Yehova ‘m’chowonadi’ kumafuna kuti tikane zinyengo zachipembedzo ndikulabadira kotheratu chifuniro chake chovumbulidwa m’Baibulo. Sitingathe kuika Yehova Mulungu patsogolo pokhapo ngati chipembedzo chathu chimafitsa miyezo yake.a Kodi ndi iti ina ya miyezo imeneyi? Ndipo ndimotani mmene kuigwiritsira ntchito kungapindulitsire banja lanu?
Kuika Mulungu Patsogolo Monga Mwamuna
Pa 1 Akorinto 11:3, Baibulo limati: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” Ngati ndinu mwamuna, muli ndi thayo lopatsidwa ndi Mulungu lakukhala wopanga zosankha wamkulu m’banja lanu. Koma chimenechi sichimakupatsani chiphaso chokhalira wopondereza kapena wotsendereza.
Baibulo limalimbikitsa amuna kulingalira maganizo a akazi awo pamene akupanga zosankha zimene zimawakhudza. (Yerekezerani ndi Genesis 21:9-14.) Ndithudi, Malemba amatilimbikitsa tonsefe ‘kupenyerera, osati mokondwera ndi zinthu zathu zokha, komanso mokondwera ndi zija za ena.’ (Afilipi 2:2-4, NW) Pamene malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo sakuloŵetsedwamo, mwamuna Wachikristu kaŵirikaŵiri adzagonjera ku zokonda mkazi wake. Pokhala ndi chikondwerero chaumwini mwa mkazi, iye adzatsimikiziranso kuti sakusenzetsa mkazi mathayo ochulukitsa. Mwachitsanzo, iye angamthandize ntchito zapanyumba, makamaka ngati amagwira ntchito yolembedwa.
Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu [achitira mpingo, NW].’ (Aefeso 5:28, 29) Yesu Kristu amachitira ziŵalo za mpingo mwanjira yachikondi.
Chofunikanso ndicho uphungu wa mtumwi Petro wakuti: ‘Amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.’ (1 Petro 3:7) Kodi sikolamitsa maganizo kuzindikira kuti kuchitira mkazi mwanjira yopanda chikondi kungaletse mapemphero a mwamuna? Inde, mwamuna ayenera kuchita ndi mkazi wake mwanjira yachikondi ngati Mulungu ati amve ndi kuyankha mapemphero ake.
Kuika Mulungu patsogolo kumayambukiranso unansi wa bambo ndi ana ake. Iye ayenera kukhala nayo nkhaŵa yeniyeni ponena za mkhalidwe wawo wauzimu. Chikhalirechobe, kufufuza kwakukulu kwa ku United States kunasonyeza kuti, theka lokha la amuna ndiwo adanena kuti “kukhala ndi phande m’phunziro la Malemba kapena kukambitsirana kwa m’magulu” kunali ‘kofunika koposa m’kupita patsogolo kwauzimu kwa mabanja awo.’ Enawo anatchula zinthu zonga “kupenyerera kapena kumvetsera ku mautumuki achipembedzo oulutsidwa” kapena ‘kulingalira pa tanthauzo la moyo.’
Komabe, Baibulo limauza atate kuti: ‘Musakwiitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha [Yehova, NW].’ (Aefeso 6:4) Pakati pa Mboni za Yehova, atate amayembekezeredwa kutsogolera m’kulambira kwa banja. Mwakuchititsa maphunziro Abaibulo abanja mokhazikika, kupezeka kumisonkhano Yachikristu, ndi kulabadira zofunika zina Zamalemba, amuna oterowo amaika Mulungu patsogolo m’moyo wabanja.
Kuika Mulungu Patsogolo Monga Mkazi
Ngati ndinu mkazi, mutha kuika Mulungu patsogolo mwakuchirikiza mwamuna wanu m’ntchito yake monga mutu wa banja. Baibulo limati: “Akazi inu, mudzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.” (Akolose 3:18) Ichi chingakhale chovutirapo ngati mwamuna salankhuzika kapena ngwankhokera m’kutsogolera kulambira kwa banja. Mulimonse mmene zingakhalire, kusumika maganizo pa zifooko zake nthaŵi zonse kapena, choipirapobe, kumchitira mwano kukangokulitsa chipsinjo m’banja.
Miyambo 14:1 imati: ‘Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake.’ Njira imodzi imene mkazi wokwatiwa wanzeru angaikire Mulungu patsogolo ndi ‘kumanga banja lake’ ndiyo kukhala wogonjera kwa mwamuna wake. (1 Akorinto 11:3) Pokhala ndi ‘chilangizo chachifundo chiri pa lilime lake,’ iye amapeŵa kukhala wosuliza mwamuna wake mosayenerera. (Miyambo 31:26) Iye amayesayesa mwamphamvu kuchititsa zosankha za mwamuna wake kukhala zachipambano.
Njira ina imene mkazi wokwatiwa angaikire Mulungu patsogolo ndiyo kukhala mkazi wochitachita. Ndithudi, ngati iye ayenera kugwira ntchito yakuthupi, iye angasoŵeke kaya nthaŵi kapena nyonga yofunikira kusamala nyumba yake molingana ndi mmene akukhumbira. Iye angayeseyesebe kukhala monga “mkazi wangwiro” amene Baibulo limamfotokoza kuti: ‘Ayang’anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi.’—Miyambo 31:10, 27.
Chofunika koposa, mkazi ayenera kuika kulambira Mulungu patsogolo m’moyo wake. Anthu ambiri ofika pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova kwa nthaŵi yoyamba amathirira ndemanga pa maonekedwe audongo a ana. Ntchito ya mkazi pambali imeneyi njamtengo wapatali koposa. Koma iye ayeneranso kugwirira ntchito pakusungitsa mkhalidwe wake wauzimu mwa pemphero, phunziro, ndi utumiki kwa Mulungu.
Kuika Mulungu Patsogolo Monga Achichepere
Nkhani yopezeka mu Adolescent Counselor imati: “Ana akhoterera kukhala ndi mzimu ndi malingaliro omwe awachititsa kulamulira makolo awo. . . . Pokhala m’chitaganya chogogomezera ndi kuthokoza chisangalalo cha pomwepo ndi chuma chakuthupi, achichepere amakhala ndi mzimu wakuti ‘ndikuchifuna tsopanoli.’” Ngati ndinu wachichepere, kodi umenewo ndiwo mzimu wanu?
Akolose 3:20 amati: ‘Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.’ Wachichepere amene amawona kumvera koteroko kukhala chiyeneretso chaumulungu adzagwirizana ndi makolo ake. Mwachitsanzo, iye sadzawanyoza mwamseri mwakuyanjana ndi anzake akusukulu amene iwo samavomereza; kapena sadzayesayesa mwachinyengo kuchititsa aliyense wa makolo ake kutsatira njira yake. (Miyambo 3:32) Mmalomwake, wachichepere aliyense amene amaika Mulungu patsogolo m’moyo adzagonjera ku chitsogozo chachikondi cha makolo.
Sungani Mulungu Patsogolo!
Mosasamala kanthu za malo omwe tingakhale nawo m’banja, tifunikira kuika Mulungu patsogolo m’moyo ndi kukulitsa unansi wathithithi ndi iye. Kodi inuyo ndi banja lanu mumachita zimenezo?
Mu “masiku otsiriza” anowa, tonsefe tikuyang’anizana ndi “nthawi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Komabe, nkotheka kupita patsogolo mwauzimu ndi kupulumuka mapeto a dongosolo lazinthu liripoli. (Mateyu 24:3-14) Mwakuchita mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo, inuyo ndi banja lanu mungakhale ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso. (Luka 23:43; Yohane 17:3; Chibvumbulutso 21:3, 4) Inde, izi zingakhale choncho ngati muika Mulungu patsogolo m’moyo wanu wa banja.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Mutu 22 wa bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 5]
Mkazi wangwiro amayamikiridwa zedi
[Chithunzi patsamba 7]
Baibulo limalimbikitsa amuna kutsogolera m’kulambira kwa banja