Kodi Muli Ofunitsitsa Kumvetsera kwa Mulungu?
PAMENE tiŵerenga Baibulo, mwamsanga timazindikira kuti mkhalidwe wa anthu m’zana loyamba unali m’njira zambiri wofanana ndi wathu lerolino. Panali chisembwere ndi kusawona mtima kochuluka, makamaka pakati pa anansi achiwerewere a Israyeli, amene chisembwere kaŵirikaŵiri chinali mbali ya chipembedzo. Moyo unali wosatsimikizirika kaamba ka anthu osauka, ndipo panali mavuto a ndale zadziko. Podzafika chaka cha 66 C.E., Israyeli ndi Roma analoŵetsedwa mu nkhondo yeniyeni. M’masiku amenewo, monga mmene ziriri tsopano, anthu anafunikira thandizo.
Mwachipembedzo, kufanana pakati pa masiku amenewo ndi nthaŵi yathu kuli kochuluka. Atsogoleri a chipembedzo Achiyuda anali onyenga. (Mateyu 23:15; Luka 20:46, 47) M’dziko losakhala Lachiyuda, mikhalidwe ya chipembedzo inasintha pa mlingo kuchokera pa kukhulupirira miyambo yakale kufika ku kukhulupirira malaulo ndi chikondi cha chipembedzo chopanda maziko. (Yerekezani ndi Machitidwe 14:8-13; 19:27, 28.) Ngakhale mu mpingo Wachikristu watsopanowo, zonse sizinali bwino. Pamapeto pa zana, mtumwi Yohane anachenjeza kuti: “Onyenga ambiri adatuluka kuloŵa m’dziko lapansi.” (2 Yohane 7) Inde, kubwerera kumbuyokonso, uphungu wonyenga wambiri unaperekedwa pa nkhani ya chipembedzo. Komabe thandizo lodalirika linalipo.
Kodi Mukanamvetsera kwa Yesu?
Yesu anali mmodzi amene anapereka uphungu wabwino m’masiku amenewo. Unali wowumiriza kwenikweni kotero kuti timaŵerenga ichi ponena za chiyambukiro chake: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Koma oŵerengeka pakati pa makamu amenewo m’chenicheni anamvetsera ku chimene iye ananena. Yesu anachita ntchito zozizwitsa ndi kukhazikitsa chitsanzo chabwino cha kakhalidwe kaumulungu ndi mkhalidwe. Komabe, ngakhale atsogoleri olingaliridwa kukhala ophunzira bwinopo anakana kuwona phindu la chimene iye ananena. Chifukwa ninji?
Ku mlingo wokulira, inali nkhani ya kunyada. Ena ananyalanyaza Yesu chifukwa chakuti anali wochokera ku Nazarete. Ena anamkana iye chifukwa chakuti sanapezekeko ku imodzi ya masukulu awo ndipo analibe kugwirizana ndi gulu lolamulira. (Yohane 1:46; 7:12, 15, 47, 48) M’kuwonjezerapo, Yesu nthaŵi zonse sananene chimene anthu anafuna kumva. Iye analankhula kokha chowonadi, ndipo Afarisi, mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri anakwiyitsidwa ndi mawu ake. (Mateyu 15:12-14) Ndithudi, pambuyo pa kulalikira kwa zaka zitatu ndi theka, atsogoleri achipembedzo Achiyuda anapangitsa iye kuphedwa. (Luka 23:20-35) Ndi mwaŵi wotani nanga umene iwo anaphonya, popeza kuti Yesu anali ndi “mawu a moyo wosatha”!—Yohane 6:68.
Ngati inu munakhala m’Yerusalemu pa nthaŵi imeneyo, kodi mukanatsatira atsogoleri achipembedzo ndi khamu lonse? Kapena kodi mukanakhala wotseguka maganizo mokwanira kugwira lingaliro la chimene Yesu anali kunena? Ngati ndi tero, mukanakhala wofanana ndi mkazi wodabwitsa amene Yesu anakumana naye pa maulendo ake.
Wina Yemwe Anamvetseradi
Iye anakumana ndi mkazi ameneyu pamene anali kuyenda kudutsa Samariya. Iye anakhala pansi pambali pa chitsime kuti apume, ndipo mkaziyo anabwera kudzatunga madzi pamene iye anali pamenepo. Sitikudziŵa dzina la mkaziyo, koma Baibulo limalemba kuti Yesu, mosasamala kanthu za kutopa kwake, anatenga mwaŵi wa kulankhula kwa iye ponena za chipembedzo.—Yohane 4:5-15.
Tsopano, panali zifukwa zambiri zimene mkaziyu angakhale anasinkhasinkhira pa kufikira kwa Yesu. Iye anali wa chipembedzo chosiyana—njira yolambirira ya Chisamariya inali yosiyana ndi ya Chiyuda. Ndiponso, Ayuda anapeputsa Asamariya ndi kukana kuyanjana nawo. Kenaka, kachiŵirinso, amuna Achiyuda kaŵirikaŵiri sanali kulankhula ndi akazi omwe anali alendo kwa iwo. (Yohane 4:9, 27) Kuwonjezerapo, mkazi wa Chisamariyayo anali kukhala njira yamoyo ya chisembwere, ndipo iye akanakwiya pa kuthekera kwa kukhala akusulizidwa kapena kukhala ndi machimo ake akuvumbulidwa.—Yohane 4:18.
Ngakhale kuli tero, mmenemo simmene iye anachitira. M’malomwake, iye anafunsa mafunso olingalirika m’kuyankha ku kufikira kwa Yesu kochenjera, kodzutsa chikondwerero. Pamene kukambitsirana kunakula, mkaziyo anafika pa nsonga yovuta, akumalozera ku udani wa chipembedzo womwe unalipo pakati pa Ayuda ndi Asamariya. Yesu anayankha mwachifundo koma mowona mtima, akumawuza mkaziyo kuti: “Inu mulambira chimene simuchidziŵa; ife tilambira chimene tidziŵa.” (Yohane 4:19-22) Koma iye sanakwiyitsidwe. Maganizo ake otseguka anali okonzekera kumva zowonjezereka.
Chotero Yesu anapitiriza ndi chilengezo chofunika koposa chakuti: “Koma ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mumzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.” (Yohane 4:23, 24) Pambuyo pake, mkazi wotseguka maganizo ameneyu anasonyeza chiyamikiro mwa kuwuza anansi ake mofunitsitsa chomwe iye anaphunzira. Iwo, pambuyo pake, anafuna chidziŵitso chowonjezereka mwa kumvetsera ku mawu a Yesu.—Yohane 4:39-42.
Nchiyani chomwe tingaphunzire kuchokera ku ichi? Chabwino, ngati timakhala m’gawo kumene kuli kunyada kokulira kwaufuko, utundu, kapena chipembedzo, ndimotani mmene timavomerezera pamene winawake wa fuko, mtundu, kapena chipembedzo chosiyana atifikira ife? Kodi timakhala chete pamene zinthu zikukambitsiridwa zomwe zingatisonyeze ife kukhala olakwa? Kapena kodi ife, mofanana ndi mkazi wa Chisamariya, timakhala ofunitsitsa kulankhula?
Kodi Mukanamvetsera kwa Paulo?
Winawake yemwe anapereka uphungu wabwino mkati mwa zana loyamba anali mtumwi Paulo. Pa nthaŵi ina Paulo nayenso anali ndi maganizo otsekeka. Iye anavomereza kuti: “Ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira.” (1 Timoteo 1:13) Ngakhale kuli tero, iye analandira chowonadi chonena za Yesu Kristu ndi kuchotsa kunyada kwake. Chitsanzo chake chimasonyeza kuti chowonadi cha Baibulo chingathandize ‘kugwetsa malinga’ mu mtima ngati zinthu zoterozo ziri zovulaza ku ubwino wathu.— 2 Akorinto 10:4.
Pamene iye anakhala Mkristu, Paulo anapita kukafalitsa molimba mtima mbiri yabwino imeneyi anaiphunzira. Ndipo monga momwe chingayembekezedwere, iye anakumana ndi mtundu umodzimodziwo wa kutsekeka maganizo komwe iye pa nthaŵi ina anali nako—koma osati mu mkhalidwe uliwonse. Mu Bereya, kumpoto kwa Grisi, iye anapeza ena ofatsa mtima omwe anali chitsanzo chabwino cha mmene tingamvetserere ku uphungu. Awa anazindikira kulira kwa chowonadi m’mawu a Paulo. Chotero, “iwo analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse.” Koma iwo anali otseguka maganizo, osati onyengeka msanga. Iwo ‘anasanthula m’Malemba masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.’ (Machitidwe 17:11) Iwo anakonda chomwe anamva, ngakhale kuti anafufuza kuwona kwake ndi Baibulo asanalandire kotheratu icho.
“Tsimikizirani Zinthu Zonse”
M’tsiku lathu, Mboni za Yehova zikuwononga nthaŵi yochuluka kuyesayesa kugawana mbiri yabwino ya Ufumu ndi anansi awo a m’zipembedzo zina. Kodi ndi chivomerezo chotani chimene Mboni zimapeza? Anthu ambiri aubwenzi amakhala achimwemwe kuwalandira iwo. Koma oŵerengeka amakana, ndipo ena amakhoza ngakhale kukwiya chifukwa chakuti Mbonizo zimaitanira.
Ichi nchomvetsa chisoni, popeza kuti chimene Mboni za Yehova zimafuna kulankhula ponena za icho chimatchedwa “mbiri yabwino” m’Baibulo. (Mateyu 24:14, NW) M’kuwonjezerapo, iwo amalimbikitsa mkhalidwe wa mtumwi Paulo, yemwe ananena kuti: “Tsimikizirani zinthu zonse; gwiritsani ku chimene chiri chabwino.” (1 Atesalonika 5:21, NW) Ngakhale ngati winawake ali ndi malingaliro amphamvu, motsimikizirika, mofanana ndi anthu a ku Bereya ndi mkazi Wachisamariya, ameneyo ayenera kukhala wotseguka maganizo mokwanira kulankhula ponena za Mulungu ndi ena.
Nchifukwa Ninji Kukhala Wotseguka Maganizo?
Mwachimwemwe, mazana a zikwi za anthu chaka chirichonse akuchita kokha chimenecho. Ambiri aphunzira kuzindikira nzeru imene iri m’Baibulo, ndipo chotulukapo chiri kusintha kwenikweni, kosatha m’miyoyo yawo. Ena kale anali ofanana ndi Janet, mkazi wachichepere wokhala ndi mbiri yaitali ya anam’goneka ndi kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa yemwe pamapeto pake anayesera kudzipha. Lerolino, Janet ali munthu Wachikristu wachimwemwe. Kuphunzira kwake Baibulo kunamthandiza iye kupeza nyonga ya kutsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.”—2 Akorinto 7:1.
Vernon anali chidakwa, ndipo ukwati wake unali m’ngozi ya kusweka. Koma kutsatira uphungu wa Baibulo kunamtheketsa iye kulaka msampha umenewu ndi kukhala wogwirizanitsidwanso ndi mkazi wake. (1 Akorinto 6:11) Debra anali ndi kunyada kwamphamvu kwa ufuko. Koma phunziro la Baibulo ndi kuyanjana ndi anthu Achikristu kunamthandiza kuwongolera kulingalira kwake. (Machitidwe 10:34, 35) Ndipo ndani yemwe akanakhulupirira masinthidwe amene anawoneka m’moyo wa mkazi wadama wachichepere mu Netherlands pamene, tsiku lina, anavomereza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova? Mwamsanga, iye anali Mkritsu wobatizidwa wokhala ndi moyo waudongo ndipo womayang’anira mwa thayo ana ake.
Zokumana nazo zoterozo zimabwerezedwa nthaŵi zambiri pamene anthu amvetsera ku chimene Baibulo likunena. Miyoyo yawo imawongoleredwa m’njira zimene ambiri a iwo sanalingalire konse kukhala zothekera. Chofunika koposa, iwo anapeza unansi ndi Mulungu, kotero kuti angapemphere kwa iye mowona mtima monga “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Ndipo iwo amapeza chiyembekezo chotsimikizirika, chosasweka kaamba ka mtsogolo pamene akukumana ndi chowonadi cha mawu a Yesu akuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
Uwu ndiwo mtundu wa chidziŵitso chimene Mboni za Yehova zimafuna kukambitsirana pamene zikulondola utumiki wawo ndi kuchezera anansi awo. Mwachidziŵikire, iwo adzakhala akukuchezeraninso posachedwapa. Kodi mudzakhala otseguka maganizo mokwanira kumvetsera kwa iwo?
[Chithunzi patsamba 7]
Mkazi Wachisamariya sanalole kunyada kumuletsa kumvetsera kwa Yesu. Kodi muli otseguka maganizo mofananamo?