Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/15 tsamba 4-7
  • Ntchito Imene Ingakupangeni Kukhala Wachimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Imene Ingakupangeni Kukhala Wachimwemwe
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zisonkhezero Zoyenera?
  • Munthu Anapangidwa Kugwira Ntchito
  • ‘Onani Chabwino’ m’Kuchita Chifuniro cha Mulungu
  • Kugwira Ntchito—Zolimba Pamene Kuli Kwabwino
    Galamukani!—1993
  • Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Sangalalani Chifukwa Chogwira Ntchito Mwakhama
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/15 tsamba 4-7

Ntchito Imene Ingakupangeni Kukhala Wachimwemwe

“NDINAKONDADI ntchito yanga monga wosindikiza,” akutero Antonio mu Genoa, Italy. “Ndinapatsidwa malipiro abwino, ndipo chimenechi chinandipangitsa ine kugwira ntchito maora ambiri moposerapo. M’kokha zaka zoŵerengeka, mosasamala kanthu za msinkhu wanga wauchichepere, ndinakhala munthu wodalirika wa wondilemba ntchito wanga.” Antonio anawoneka kukhala atafikira zonulirapo zimene zimasonkhezera ambiri kugwira ntchito molimba: chuma, malo, ndi ntchito yabwino yomwe iye anasangalala nayo.

Kodi Antonio ‘anali kuwona zabwino m’ntchito zake zonse’? (Mlaliki 3:13) Ndipo kodi ntchito yoteroyo ndithudi inampangitsa iye kukhala wachimwemwe? “Chifukwa cha kukwinjika kochititsidwa ndi kuvutitsidwa maganizo kwa njira yathu ya moyo,” iye akupitiriza tero, “tinayamba kukhala ndi mavuto monga banja. Chimenechi chinatipangitsa ife kusakhala achimwemwe.” Antonio ndipo osatinso mkazi wake sanali achimwemwe mosasamala kanthu za ntchito zawo zokhutiritsa. Bwanji ponena za inu? Kodi ‘mukuwona zabwino m’ntchito zanu zonse’? Kodi ntchito yanu kwenikweni ikukupangani kukhala wachimwemwe?

Zisonkhezero Zoyenera?

Chifukwa chachikulu kaamba ka kugwira ntchito molimba chiri kupeza mkhalidwe. M’maiko ena, anthu amafunikira kugwira ntchito molimba maora ambiri kokha kuti achite nazo. Ena amakhala mu ukapolo usana ndi usiku kotero kuti ana awo akakhale ndi moyo wabwinopo. Chikhalirechobe ena amagwira ntchito mokakamizika kuti akundike chuma.

Leonida mu Philippines anali ndi ntchito ziŵiri. Iye ankagwira ntchito mu banki mkati mwa tsiku ndipo anaphunzitsa pa koleji maora atatu kapena anayi madzulo. Kodi ndalama zapamwambazo zinali zokuyenerera iko? “Nthaŵi zonse ndinkapenyerera koloko,” iye akulongosola tero. “Ndinasungulumwa. Ndinkachichita icho popanda chikhutiritso.”

Ayi, kugwira ntchito kokha kaamba ka ndalama sikumatulukapo m’chikhutiritso chowona ndi chimwemwe. “Usadzitopetse kuti ulemere,” ikupereka uphungu tero Mfumu yanzeru Solomo, “pakuti chuma chimera mapiko, ngati [chiwombankhanga ndipo, NW] ch[i]wuluka mumlengalenga.” (Miyambo 23:4, 5) Ziwombankhanga zina zimanenedwa kukhala zikuwuluka pa liŵiro lofika pa makilomita 130 pa ora limodzi. Chimenechi chimachitira bwino fanizo kufulumira kumene chuma chokundikidwa movutikira chingawulukire. Ngakhale ngati munthu akundika chuma, pamene iye amwalira sangatenge kalikonse kopita nako.​—Mlaliki 5:15; Luka 12:13-21.

Kukhala womwerekera m’kupanga kakhalidwe nthaŵi zina kumabweretsa ngozi zowopsya. Iko kungatsogolere ku chikondi cha pa ndalama. M’zana loyamba, panali gulu la anthu achipembedzo otchedwa Afarisi amene anadziŵika kaamba ka chikondi chawo cha pa ndalama. (Luka 16:14) Monga yemwe kale anali Mfarisi, mtumwi Wachikristu Paulo anali wodziŵa bwino lomwe za njira yawo ya moyo. (Afilipi 3:5) “Koma iwo akufuna kukhala achuma,” akuchenjeza tero Paulo, “amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, . . . nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Inde, “chikondi cha pa ndalama,” kuchita chirichonse ndi zirizonse kaamba ka icho, kungavulaze moyo wa wina. Njira yoteroyo simathera m’chimwemwe.

Kwa ena, chisonkhezero chawo m’kudziikizako iwo eni chiri kukwera makwerero a kutchuka ndi malo. Mosasamala kanthu za icho, iwo pomalizira amayang’anizana ndi zenizeni. “Makanda othamangira,” ikutero magazini ya Fortune, “omwe anadzipereka nsembe m’zaka zawo zoyambirira za m’ma 20 ndi kuchiyambi kwa 30 kuti afikire malo olamulira a pakati amafika ku kuzindikira koipa koma kosapeŵeka kuti, mosasamala kanthu za unyinji wa zotulutsidwa za kugwira ntchito zolimba, sialiyense yemwe adzafika pa malo apamwamba. Atatopetsedwa ndi kuyesayesa kodziikizako, iwo amakhala ndi chiyeso cha kufunsa chifukwa chomwe zonsezo zikuchitikira tero. Nkulimbanirananji mwamphamvu chotero? Ndani yemwe amasamala?”

Moyo wa mwamuna mmodzi woteroyo, Mizumori, unazikidwa pa kupita patsogolo m’dziko. Akumalondola ntchito ya m’malo a umanejala ndi imodzi ya mabanki aakulu koposa mu Japan, iye sanakhale ndi nthaŵi kaamba ka banja lake. Pambuyo pogwira ntchito molimba kwa zaka zoposa 30, umoyo wake unavulala, ndipo iye motsimikizirika sanali wachimwemwe. “Ndinazindikira,” iye akutero, “kuti mpikisano kaamba ka malo pakati pa anthu oyesera kudziŵika monga otchuka uli ‘wachabe ndi kungosautsa mtima.’”​—Mlaliki 4:4.

Koma bwanji ponena za aja onga Antonio, omwe amasangalala ndi ntchito yawo? Atasangalatsidwa ndi ntchito yake, Antonio anapereka nsembe moyo wa banja lake pa guwa lansembe la ntchito. Ena amapereka nsembe umoyo wawo ndipo ngakhale miyoyo yawo, monga kwasonyezedwera ndi imfa za mwadzidzidzi za anthu ambiri otchuka a ku Japan ndi a malo apamwamba ogwira ntchito mopambanitsa. Utumiki wopereka chitsogozo kaamba ka akufa awo modabwitsa unalandira malamya 135 m’tsiku limodzi lokha.

Ena amapereka miyoyo yawo kuthandiza ena. Yesu analimbikitsa mzimu umenewu. (Mateyu 7:12; Yohane 15:13) Kukhala otanganitsidwa m’ntchito yopindulitsa ya kuthandiza ena ndithudi kumabweretsa chimwemwe.​—Miyambo 11:25.

Ngakhale kuli tero, kugwira ntchito kwa maganizo olemekezeka koteroko sikuli komasuka ku kuphophonya. Mwachitsanzo, mfumu ya Chiyuda Uziya inadziloŵetsa m’ntchito ya boma yokumba zitsime m’chipululu. Uziya ayenera kukhala anali ndi phindu la anthu ake m’malingaliro, pamene anali “kufuna Yehova” pa nthaŵi imeneyo ndipo mwachiwonekere analabadira lamulo laumulungu kuti mafumu akhale opanda dyera. (2 Mbiri 26:5, 10; Deuteronomo 17:14-20) Ichi chinakweza chipambano chake cha zankhondo, ndipo “dzina lake linamveka kutali.” Koma pokhala wolimba, anakhala wodzikuza, kutulukapo m’kugwa kwake. (2 Mbiri 26:15-20; Miyambo 16:18) Amene ali wodzipereka kuthandiza ena koma wosonkhezeredwa ndi kudzisangalatsa kwaumwini ndi kunyada angatherenso m’kusweka. Kenaka, nchifukwa ninji aliyense amafuna kugwira ntchito molimba?

Munthu Anapangidwa Kugwira Ntchito

Tingaphunzire zochuluka ponena za ntchito kuchokera kwa mwamuna yemwe anakwaniritsa zabwino zokulira kuposa munthu aliyense anakhalapo pa dziko lapansi. Iye ali Yesu Kristu. (Mateyu 20:28; Yohane 21:25) Pamene iye anafa pa mtengo wozunzirapo, iye anafuula kuti, “Zakwaniritsidwa!” (Yohane 19:30, NW) Moyo wake wa zaka 331/2 unali wokwaniritsa.

Moyo wa Yesu umathandizira kuyankha funso lakuti, “Kodi ndi ntchito yanji imene ingakupangeni kukhala wachimwemwe?” Kunali kukwaniritsa kwa chifuniro cha Atate wake wakumwamba komwe kunambweretsera iye chimwemwe chosayerekezeka. Mofananamo, kuchita chifuniro cha Mlengi wathu kungatipatse kudzimva kwa kukwaniritsa ndi kutipanga ife kukhala achimwemwe. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Iye amadziŵa kapangidwe kathu ndi zosoŵa zathu ngakhale kuposa ndi mmene timachitira.

Pamene Mulungu analenga mwamuna woyamba, Adamu, Iye anampatsa ponse paŵiri ntchito ya manja ndi ya maganizo kuichita. (Genesis 2:15, 19) ‘Pokhala ndi ulamuliro pa’ zolengedwa zina zonse za pa dziko lapansi, Adamu analinso ndi ntchito ya umanejala yakuichita. (Genesis 1:28) Malinga ngati Adamu anamamatira ku kakonzedwe kameneka, ntchito yake inakhalabe ya tanthauzo ndi yaphindu. Mbali yaing’ono iriyonse ya ntchito inatanthauza mwaŵi wina wa kukondweretsa Wam’mwambamwamba.

Ichi, ngakhale kuli tero, sichinapitirize kukhala tero ndi Adamu. Iye anagamulapo kupatuka kuchoka ku kakonzedwe ka Mulungu. Adamu sanasangalatsidwenso m’kuchita chifuniro cha Mulungu koma anafuna kuchita chimene iye anakonda. Iye anachimwira Mlengi. Monga chotulukapo cha chigamulo chake, Adamu, mkazi wake, ndi ana ake onse anali “ogonjetsedwa ku [uchabe, NW].” (Aroma 5:12; 8:20) M’malo mobweretsa chimwemwe, ntchito inakhala chothodwetsa. Chilango cha Mulungu motsutsana ndi Adamu chinaphatikizapo mawu awa: “Nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo: m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:17-19) Ntchito, imene inayenera kulemekezedwa m’kukhala ndi chonulirapo chake chomalizira kukondweretsa Mlengi wa munthu, tsopano inangotanthauza ntchito yowawitsa kokha kuti munthu apeze chakudya chake.

Ndi kumaliza kotani komwe tingapeze kuchokera ku zenizeni zimenezi? Uku: Ntchito yolimba imabweretsa chikhutiritso chosatha ndi chimwemwe kokha pamene tisumika miyoyo yathu pa kuchita chifuno chaumulungu.

‘Onani Chabwino’ m’Kuchita Chifuniro cha Mulungu

Kuchita chifuno chaumulungu kunali ngati chakudya kwa Yesu Kristu​—chinachake chofunikira kusangalala nacho ndi kuchirikiza moyo wake wauzimu. (Yohane 4:34) Kodi ndimotani mmene chisangalalo cha ntchito choterocho chingakhalire chanu?

Inu muyenera kuzindikira “chimene chifuniro cha [Yehova, NW] chiri” kaamba ka inu. (Aefeso 5:17) Chifuniro chake chiri kaamba ka mtundu wa anthu kubwezeretsedwa ku “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21; 2 Petro 3:9) Tsopano ntchito ya kusonkhanitsa ya dziko lonse yokwaniritsa chimenechi ikuchitika. Inu mungakhalenso ndi mbali m’ntchito yokhutiritsa koposa imeneyi. Ntchito yoteroyo motsimikizirika idzakupangani inu kukhala wachimwemwe.

Antonio, wotchulidwa poyambirirapo, pambuyo pake anapeza chikhutiritso ndi chimwemwe. Pamene iye ndi mkazi wake anaika ntchito zawo zakuthupi “zachabe” choyamba m’moyo wawo ndipo anali odziloŵetsa mwakuya mu izo, moyo wawo wauzimu unavutika. Imeneyo ndiyo nthaŵi imene anayamba kukhala ndi mavuto a panyumba. Atazindikira mkhalidwewo, mkazi wake anagamulapo kuleka ntchito yake ndi kuyamba ‘kudziikizako mwamphamvu iyemwini’ m’kuchita ntchito yolalikira ponena za Ufumu wa Mulungu kwa nthaŵi zonse.​—Luka 13:24.

“Mwamsanga,” akutero Antonio, “tinawona kusintha kwakukulu. Panalibenso kukangana kokhazikika. Mtendere unabwerera ku banja lathu.” Mkazi wake anatuta chisangalalo cha kuthandiza ena kupeza chidziŵitso chotanthauza “moyo wosatha.” (Yohane 17:3) Chimwemwe chake chinasonkhezera Antonio kuyesanso chimene kwenikweni chiri chaphindu. Chikhumbo chake cha kutumikira Mulungu ndi mtima wonse chinapambana. Iye anakana chogawira cha kukwezedwa pa ntchito ndi kuchoka ku ntchito yake yakuthupi. Ngakhale kuti kusinthako kunatanthauza kutenga kwake ntchito yochepetsa mokulira, onse aŵiri Antonio ndi mkazi wake ali achimwemwe kukhala akuthera nthaŵi yawo yochulukira koposa mu utumiki Wachikristu, kuchita chifuniro cha Mulungu.

Ndithudi, sionse omwe ali m’malo opanga masinthidwe okulira oterewa. Mizumori, wogwira ntchito ku banki wa ku Japan wotchulidwa poyambirirapo, akusangalala ndi utumiki wake monga mkulu mu mpingo Wachikristu ndipo akuchirikizabe banja lake ndi ntchito yake yakuthupi, kumene ali ndi malo aumanejala. Ngakhale kuli tero, moyo wake suli wozikidwabe pa ntchito yakuthupi koma umazungulira pa kuchita chifuniro cha Mulungu. Ntchito yake yakuthupi iri njira yomwe imam’chirikiza iye ndi kumtheketsa kukwaniritsa cholinga chimenecho. Tsopano kugwira ntchito mwakuthupi nakonso kuli kwa tanthauzo.

Pamene mulimirira kawonedwe kameneka kulinga ku ntchito yanu yolembedwa, inu mosakaikira mudzadziikizako inueni “osati ukapolo wa maso, monga wokondweretsa anthu komatu ndi mtima wa kulinga kumodzi wa kuwopa [Yehova, NW].” (Akolose 3:22) Kuwona mtima koteroko sikungawoneke kukhala kopita patali m’chitaganya cha mpikisano chino, koma, monga mmene Mizumori akuvomerezera, mwa kugwiritsira ntchito maprinsipulo oterowo, inu mudzakhulupiridwa ndi kulemekezedwa. Ngakhale kuti iye analeka kugwira ntchito kaamba ka kukwezedwa pa ntchito, iko kunabwera kwa iye.​—Miyambo 22:29.

Inde, kuika moyo wanu mozungulira kuchita chifuniro cha Mulungu ndiyo mfungulo ya kupeza chimwemwe m’ntchito yolimba. Ndicho chifukwa chake Mfumu yanzeru Solomo anamaliza kuti: “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”​—Mlaliki 3:12, 13.

[Chithunzi patsamba 7]

Kuzika moyo wanu wa banja mozungulira phunziro la Baibulo ndi kuchita chifuniro cha Mulungu kuli mfungulo ku kusangalala ndi zipatso za ntchito yolimba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena