Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 9/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchita Ntchito Zabwino pa Sabata
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Amakonda Anthu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Pita Ukasambe M’dziwe la Siloamu”
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 9/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi anthu odwala ndi opunduka m’chenicheni nachiritsidwadi m’madzi ovundulidwa a Betesda, monga mmene Yohane 5:2-7 akusonyezera? Ndipo ngati ndi tero, ndi mwamphamvu yanji imene zozizwitsa zoterozo zinachitikira?

M’chenicheni, mbiri ya pa Yohane 5:2-9 simakhazikitsa kaya ngati unyinji wa kuchiritsa kozizwitsa kunawoneka pa thamanda m’Yerusalemu wakale. Chozizwitsa chokha chomwe tingakhale otsimikiza kuti chinachitika pamenepo chinali chija chochitidwa ndi Yesu Kristu pamene iye anachiritsa munthu yemwe kwa zaka 38 anakhala akudwala. Tingalandire chozizwitsa chimenechi, popeza ripoti la ichi liri m’Malemba owuziridwa. (2 Timoteo 3:16) Koma ambiri m’Yerusalemu kubwerera m’nthaŵi imeneyo anakhulupirira kuti zozizwitsa zina zinawoneka pa malo amenewo, mongadi mmene ambiri amakhulupirira lerolino kuti kuchiritsa kozizwitsa kumawoneka pa malo a zipembedzo.

Dziŵani chimene Baibulo likunena, ndi chimene ilo kwenikweni silinena: “Koma pali thamanda m’Yerusalemu pa chipata cha nkhosa lotchedwa mu Chihebri Betesda, liri ndi makumbi asanu. Mmenemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala.​—Koma panali munthu wina apo ali nkudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. Yesu pa kuwona ameneyu ali kugona, ndipo anadziŵa kuti anatha nthaŵi yaikulu pamenepo, ananena naye: ‘Ufuna kuchiritsidwa kodi?’ Wodwalayo anayankha: ‘Ambuye, ndiribe wondivika ine m’thamanda paliponse madzi avundulidwa; koma mmene ndirinkudza ine wina atsika ndisanatsike ine.’ Yesu ananena naye: ‘Tawuka, yalula mphasa yako nuyende.’ Ndipo pomwepo munthuyo anachira, nayalula mphasa yake nayenda.”​—Yohane 5:2-9.

Thamanda lolozeredwakolo linali pafupi ndi “chipata cha nkhosa,” chimene mwachiwonekere chinali kumpoto cha kum’mawa kwa Yerusalemu kufupi ndi phiri la kachisi. (Nehemiya 3:1; 12:39) Zofukulidwa za posachedwapa zavumbula umboni wa matamanda aŵiri akale, ndi zidutswa za madanga ndi maziko zomwe zinasonyeza nyumba yokhala ndi makumbi okhalako inaliko kumeneko mu nthaŵi za Herodi, monga mmene Yohane 5:2 akunenera. Koma kodi nchiyani chimene anthu kubwerera nthaŵi imenyo anaganiza kuti chinachitika pano?

Onani mzera wodukizawo m’kugwidwa mawu kwa pamwambapo kwa Yohane 5:2-9. MaBaibulo ena amaphatikiza ndime yowonjezereka yomwe imatchedwa Yohane 5:4. Kuwonjezera kumeneko kumanena chinachake chonga ichi: “Pakuti mngelo wa Ambuye ankabwera pa thamandapo nthaŵi ndi nthaŵi ndi kuvundula madzi; woyambirira kupitamo pambuyo pa kuvundulidwa kwa madziwo anakhala wa umoyo kuchokera ku matenda aliwonse amene anakanthidwa nawo.”

Ngakhale kuli tero, unyinji wa maBaibulo amakono, kuphatikizapo New World Translation of the Holy Scriptures, amasiya ndime imeneyi. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti m’kuthekera kulikonse iyo sinali mu Uthenga Wabwino wa Yohane. Mawu a m’munsi mu The Jerusalem Bible amawona kuti “mboni zabwino koposa” zimasiya ndime imeneyi. “Mboni zabwino koposa” zotanthauzidwa zinali mamanusikripiti achikale a Chigriki, monga ngati Codex Sinaiticus ndi Vatican 1209 (zonse ziŵiri za mzana la 4 C.E.), ndi malembedwe oyambirira a Syriac ndi Latin. Pambuyo pa kutchula ‘kusoweka kwa versi 4 kuchokera ku malemba a munusikripiti abwino koposa,’ The Expositor’s Bible Commentary ikuwonjezera kuti: “Iyo mwachisawawa imalingaliridwa kukhala kutembenuza komwe kunalowetsedwamo kulongosola kuvundulidwa kwa pa kanthaŵi kwa madzi, kumene anthu anakulingalira kukhala magwero othekera a kuchiritsa.”

Chotero Baibulo silimanena kwenikweni kuti mngelo wochokera kwa Mulungu anapanga zoziwitsa pa thamanda la Betesda. Chabwino, kodi kuchiritsa kozizwitsa kunawoneka pamene madziwo anali ovundulidwa? Palibe wina aliyense lerolino amene anganene motsimikizirika. Mwinamwake mwa njira ina yake mwambo unakulitsidwa kuti anthu odwala kapena opunduka anachiritsidwa pamenepo. Ngati nkhani za kuchiritsidwa koyerekezeredwako zafalitsidwa, anthu osowa chochita oyembekezera kuchiritsidwa angayambe kusonkhana kumeneko. Tikudziŵa kuti ichi chachitika ku malo osiyanasiyana m’nthaŵi yathu, ngakhale pamene palibe umboni wolembedwa wa kuchiritsa kwa umulungu.

Ife sitiyenera, ngakhale ndi tero, kukhala okaikira ponena za kuchiritsa komwe Mwana wa Mulungu anachita pa thamanda la Betesda. Nkulekelanji, popeza popanda ngakhale kulowa m’madzimo, munthuyo anachiritsidwa pa nthaŵi yomweyo ndi Sing’anga Wamkuluyo. Kuthekera kwake kolembedwa kwa kuchita chimenechi kuyenera kutipatsa ife chifukwa cha kuyang’anira kutsogolo ku kuchiritsa komwe iye adzachita mkati mwa Zaka Chikwi zikudzazo. Iye adzachiritsa ndi kuthandiza anthu okhulupirika kubwerera ku unwgiro.​—Chivumbulutso 21:4,5; 22:1,2.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena