Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 9/15 tsamba 3-4
  • Mungapeze Chuma Chamtengo Woposa wa Golide!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungapeze Chuma Chamtengo Woposa wa Golide!
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Santhula, Nuone”
  • Chowonadi Chasukulutsidwa
  • Alephera Kumgwira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Alephera Kumugwira Iye
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • ‘Yesetsani Kufunafuna Yehova Kuti Mupitirize Kukhala ndi Moyo’
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 9/15 tsamba 3-4

Mungapeze Chuma Chamtengo Woposa wa Golide!

CHOWONADI chopezeka m’Baibulo chingayerekezedwe ndi golide, siliva, kapena chuma china chobisika. Ngakhale kuti mungakhale musanafunefunepo golide kapena siliva weniweni, mwachidziŵikire mukuzindikira kuti kutero kukafunikira ntchito yakalavula gaga ndi kuumirira. Ndipo kaŵirikaŵiri wofunafunayo amakumana ndi zogwiritsa mwala.

Komabe, kugwiritsa mwala koteroko sikumatulukapo konse pamene mukufuna chuma chobisika m’Baibulo. Tamverani chitsimikizo cholimbikitsa ichi: ‘Ukaifuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.’ (Miyambo 2:4, 5) Koma muyenera kufunafuna.

“Santhula, Nuone”

“Santhula, nuone kuti m’Galileya sanauka mneneri.” Uwu unali uphungu umene Afarisi Achiyuda a m’zaka za zana loyamba anampatsa Nikodemo, yemwe analinso Mfarisi. “Santhula, nuone.” Uphungu wabwinodi. Chinali chotheka kusanthula ndi kupeza chowonadi​—chinachake chamtengo wapatali kuposa golide.

Komabe, pankhaniyi anthu amene anapereka uphungu wakuti “santhula, nuone” analephera kuchita mogwirizana ndi uphunguwo. Motani?

Akulu ansembe ndi Afarisi adatumiza anyamata kukamgwira Yesu Kristu. Pokhala atakondweretsedwa ndi kaphunzitsidwe kake, anyamatawo anabwerera osamgwira. Motero, Afarisiwo anawafunsa motere: “Kodi mwasokeretsedwa inunso?” Nikodemo analankhula nati: ‘Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?’ Mawu ameneŵa anadzutsa uphungu wakuti “santhula, nuone.”​—Yohane 7:32, 45-52.

Kodi ansembewo ndi Afarisi analephera motani? Iwo sanadziŵe kapena kuvomereza kuti ngakhale kuti Yesu analeredwera m’Galileya, iye anabadwira m’Betelehemu. Mneneri Mika analosera motere: ‘Mwa iwe [Betelehemu] mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m’Israyeli.’ (Mika 5:2) Chotero anthu otsogolera amenewo analephera kusanthula ndi kuwona ziyeneretso za Yesu monga mneneri, amene akakhala woweruza m’Israyeli. Ichi chinatsogolera ku zotulukapo zangozi, ndipo chikusonyeza mwafanizo mmene kuliri kofunika koposa kusanthula ndi kupeza chowonadi chonse pa nkhani iriyonse. Koma kodi chowonadi chimawonedwa motani nthaŵi zambiri?

Chowonadi Chasukulutsidwa

Wolemba wa m’zaka za zana la 19 anati: “Chowonadi chenicheni, mofanana ndi golide weniweni, chapezedwa kukhala chosayenerera kugaŵiridwa, chifukwa chakuti anthu apeza kuti nkokhweka kwambiri kusukulutsa chowonadi kuposa ndi kudziyenga.” Mawuwa adakali owona chotani nanga ponena za mbali yachipembedzo chakudziko! Yemwe ali kumbuyo kwa kusukulutsa chowonadi kumeneku ndi ‘atate wake wa bodza,’ Satana Mdyerekezi. (Yohane 8:44; Chibvumbulutso 12:9) Iye amagwiritsira ntchito chipembedzo chonyenga kusukulutsa ziphunzitso zowona pa mafunso ofunika koposa onga awa: Kodi Mulungu ndani? Kodi Yesu ali ndi unansi wotani kwa iye? Kodi dziko lapansi ndi anthu ali ndi mtsogolo motani?

Ansembe ndi Afarisi akanasanthula ndikupeza chowonadi. Iwo akadapeza chuma chamtengo wake kuposa golide. Inde, iwo akanapeza chowonadi chonse chonena za Yesu ‘mwakumumva iye ndi kuzindikira chimene ankachita,’ monga momwe Nikodemo analingalirira. Ngati iwo adakhala owona mtima m’kuchita ichi, mosakaikira Yesu akanafotokoza zinthuzo kwa iwo, monga momwe anafotokozera ophunzira ake. (Marko 4:34) Koma kodi n’kuti kumene tingapeze chowonadi chenicheni lerolino? Kunena zowona, kodi palidi chitsimikizo chakuti tingasanthule mwachipambano ndi kupeza chowonadi chonse?

[Chithunzi patsamba 4]

Atsogoleri achipembedzo akadapeza chowonadi chonse chonena za Yesu mwa ‘kumva iye’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena