Kumasulira Baibulo—Mwa Mphamvu Yayani?
TANTHAUZO lina la mawu akuti “kumasulira” n’lakuti “kuzindikira mfundo malinga ndi chikhulupiriro cha munthuwe, kuganiza kwako, kapenanso mkhalidwe wako.” (Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary) Choncho, mmene munthu amamasulira nkhani iliyonse nthaŵi zambiri zimadalira ndi zimene munthuyo akudziŵa, maphunziro ake, kapena mmene anakulira.
Bwanji nanga za kumasulira Baibulo? Kodi tili ndi ufulu wofotokoza ndime za m’Baibulo malinga ndi “chikhulupiriro chathu, kuganiza kwathu, kapena mkhalidwe wathu”? Kaŵirikaŵiri, akatswiri a maphunziro a Baibulo ndi otembenuza ambiri amakana kuti sachita zimenezi, m’malomwake amati amatsogozedwa ndi Mulungu.
Chitsanzo chabwino ndi mawu am’tsinde a pa Yohane 1:1 m’Baibulo la A New Version of the Four Gospels, lofalitsidwa mu 1836 ndi John Lingard amene anagwiritsa ntchito dzina lopeka lakuti “A Catholic.” Iwo amati: “Anthu a m’zipembedzo zonse amapeza umboni wochirikiza maganizo awoawo m’malemba opatulika: komatu si Malemba amene amawauza, koma kuti anthuwo ndiwo amapereka matanthauzo a m’mutu mwawo pa mawu a m’Malemba.”
Ngakhale kuti mfundoyi n’njomveka, kodi cholinga cha wolembayo chinali chiyani? Ananena zimenezo kuchirikiza mmene anamasulira vesili kuti: “Pachiyambi panali ‘mawu;’ ndipo ‘mawuwo’ anali ndi Mulungu; ndipo ‘mawuwo’ anali Mulungu,” kumasulira kogwirizana kwambiri ndi chiphunzitso cha Utatu.
Kodi chinam’chititsa wolemba ameneyu kumasulira Yohane 1:1 mochirikiza chiphunzitso cha Utatu n’chiyani? Kodi ndi “Malemba amene anamuuza” kuti achite zimenezi? Zimenezo n’zosatheka popeza kuti chiphunzitso cha Utatu sichipezeka paliponse m’Baibulo. Pamfundoyi, taonani zimene The New Encyclopædia Britannica imanena. Imati: “Ngakhale liwu lakuti Utatu kapena chiphunzitso chake sizipezeka m’Chipangano Chatsopano.” Powonjezera, polofesa E. Washburn Hopkins wa pa Yunivesite ya Yale ananena kuti: “Yesu ndi Paulo mwachiwonekere sanali kuchidziŵa chiphunzitso cha Utatu; . . . sanachitchulepo.”
Nanga kodi tinganenenji za awo amene amalimbikira kumasulira Yohane 1:1 kapena mavesi ena m’Baibulo malinga ndi chiphunzitso cha Utatu? Malinga ndi ndemanga ya a Lingard, “si Malemba amene amawauza, komatu kuti anthuwo ndiwo amapereka matanthauzo a m’mutu mwawo pa mawu a m’Malemba.”
Bwino lake n’loti tili ndi Mawu a Mulungu otitsogolera pankhani imeneyi. ‘Mudziŵa ichi poyamba,’ anatero mtumwi Petro, “kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.”—2 Petro 1:20, 21.