Mmene Choonadi Chimatimasulira
1 Panthaŵi ina, Yesu analankhula kwa Ayuda amene anamukhulupirira kuti: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:32) Panopa Yesu anali kulankhula za ufulu umene sungafanane ndi maufulu amene nzika zimakhala nawo. Umenewu ndi ufulu umene onse angakhale nawo—olemera kapena osauka, ophunzira kapena osaphunzira. Choonadi chimene Yesu anaphunzitsa chinali kudzamasula anthu ku uchimo ndi imfa. Yesu anafotokoza kuti, “yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.” (Yoh. 8:34) Motero tikulakalaka kuti anthu onse omvera ‘adzamasulidwe ku ukapolo wa chivundi ndi kuloŵa ufulu wa ulemelero wa ana a Mulungu’!—Aroma 8:21.
2 Choonadi chokhudza Yesu komanso ntchito yake yokwaniritsa cholinga cha Mulungu chimabweretsa ufuluwo. Chimaphatikizapo chidziŵitso chokhudza nsembe ya dipo limene anatiperekera. (Aroma 3:24) Ngakhale panopa tikakhulupirira choonadi cha m’Baibulo ndi kuchitsatira, timakhala aufulu ndithu pomasuka ku mantha, kutaya mtima, ndi makhalidwe onse oipa.
3 Sitiopa Kapena Kutaya Mtima: Sitiyenera kutaya mtima ndi mmene dzikoli lilili popeza tikudziŵa chifukwa chake kuipaku kulipo ndipo tikudziŵanso kuti posachedwapa kuipaku kudzachotsedwa padziko lapansi. (Sal. 37:10, 11; 2 Tim. 3:1; Chiv. 12:12) Kuwonjezera pamenepo, choonadi chimatimasula ku ziphunzitso zonyenga zokhudza mmene akufa alili. Timadziŵa kuti akufa sangativulaze, kuti sali kumoto, ndiponso kuti Mulungu satenga anthu mu imfa kuti akakhale nawo kumalo a mizimu.—Mlal. 9:5; Mac. 24:15.
4 Choonadi chimenechi chinalimbikitsa bambo ndi mayi wina pamene mwana wawo anamwalira pangozi. “Tili ndi chisoni chimene sichingathe mpaka titaona mwana wathu atauka kwa akufa,” anatero mayiyo. “Koma tikudziŵa kuti chisonicho n’chakanthaŵi chabe.”
5 Kumasuka ku Makhalidwe Oipa: Choonadi cha Baibulo chingasinthe kaganizidwe ka munthu ndi umunthu wake, ndipo munthuyo amapeŵa mavuto. (Aef. 4:20-24) Kukhala wokhulupirika ndi wakhama kungathandize kuchepetsa umphaŵi. (Miy. 13:4) Kusonyeza chikondi chodzimana kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi ena. (Akol. 3:13, 14) Kulemekeza umutu wachikristu kumachepetsa mavuto m’banja. (Aef. 5:33–6:1) Kupeŵa kuledzera, chiwerewere, fodya, ndi mankhwala osokoneza bongo kumapangitsa kuti thupi likhale labwino.—Miy. 7:21-23; 23:29, 30; 2 Akor. 7:1.
6 Kwa zaka nayini mnyamata wina sanathe kusiya mankhwala osokoneza bongo. Tsiku lina anakumana ndi wofalitsa akulalikira pamsewu. Analandira buku kwa wofalitsayo, ndipo anagwirizana kuti akamuchezere kunyumba kwake. Anayamba kuphunzira Baibulo. Patapita miyezi iŵiri m’nyamata ameneyu anasiya mankhwala osokoneza bongo, ndipo ataphunzira kwa miyezi eyiti anabatizidwa. Achimwene ake ndi mlamu wake ataona kuti iye wasintha, anayamba kuphunzira Baibulo.
7 Thandizani Ena Kupeza Ufulu: Anthu amene akhala akapolo a ziphunzitso zonyenga kwanthaŵi yaitali angavutike kumvetsa ufulu umene Mawu a Mulungu amapereka. Chotero mphunzitsi angafunike kuchita khama komanso kukonzekera bwino kuti awafike pa mtima. (2 Tim. 4:2, 5) Inotu si nthaŵi yobwerera m’mbuyo ndi ntchito yathu ‘yolalikira kwa a m’nsinga mamasulidwe.’ (Yes. 61:1) Ufulu wachikristu ndi wamtengo wapatali. Kupeza ufulu umenewu ndi kupeza moyo wosatha.—1 Tim. 4:16.