Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/1 tsamba 22-27
  • Chaka Choliza Lipenga cha Yehova—Nthawi Yathu Yakusangalala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chaka Choliza Lipenga cha Yehova—Nthawi Yathu Yakusangalala
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ufulu Woyambirira Ulalikidwa
  • Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chiyamba
  • Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chifika Pachimake mu Zaka Chikwi
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Chaka cha Ufulu Komanso Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo M’tsogolo
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/1 tsamba 22-27

Chaka Choliza Lipenga cha Yehova​—Nthawi Yathu Yakusangalala

“Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu ndi kulalikira kwa onse okhala m’dzikomo kuti akhale aufulu. Muchiyese chaka Choliza lipenga . . . Muchiyese chopatulika . . . ndipo mudzakhala m’dzikomo okhazikika.”​—LEVITIKO 25:10-12, 18.

1. Kodi ndi malemba otani amene amaoneka pa Belu la Ufulu, ndipo kodi mau amenewa anatengedwa kuchokera kuti?

KULI KONSE kumene mumakhala, mwina mwake munamvapo za Belu lotchuka La ufulu, lokhazikitsidwa mu Philadelphia, Penn sylvania, U.S.A. The World Book Encyclopedia imanena kuti belu limeneli “linaimbidwa pa July 8, 1776, limodzi ndi mabelu ena a tchalitchi, kulengeza kudzitengera kwa Kule ngeza kwa Kudzikhalila Paokha. Zolembedwa zake, ‘Kulalikira Kwa Onse okhala m’dziko kuti akhale aufulu,’ ziri zochokera mu Baibulo (Levitiko 25:10).”

2. Kodi mumadzimva motani ponena za chiyembekezo cha ufulu, koma kodi ndi mavuto ati omwe angabwere ponena za iwo?

2 Ufulu ukupitirizabe kukhala wofunika mokulira, kodi siumatero? Mofananamo inu mungasangalale pa chiyembekezo cha ufulu weni weni​—kuchoka ku malingaliro onyenga, ku chitsendelezo kapena chidodometso cha ndale, ku zoturukapo zofooketsa za ukalamba ndi matenda, zomwe zimaturukapo mu imfa. Ngati ndi choncho, pali chifukwa choyenera kaamba ka inu kusangalala, ndipo padzakhala chifukwa chokulira posachedwapa. ‘Ndi motani m’mene ichi chingakhalire tero?’ mungafunse, popeza palibe boma liri lonse lomwe panthawi ino lapereka ufulu weni weni, ndipo angakhale asayansi kapena madokotala sangathe kuletsa ukalamba, matenda, ndipo kenaka imfa. Komabe, tikubwereza, pali maziko kaamba ka inu kusangalala chifukwa cha ufulu weni weni. Kuti mumvetsetse ndi motani, lingalirani mbiri zofunikira zoyambilira zomwe zingaphatikize inu​—tsopano ndi mtsogolo.

3. Kodi Chaka Choliza Lipenga chinali chiyani, ndipo nchiyani chomwe chinali kuchitika mkati mwa chaka chimenecho?

3 Ndime yogwidwa mau pamwambapo imagwiritsira ntchito liu lakuti “Chaka Choliza Lipenga.” Chaka Choliza Lipenga chinali nye ngo yakusunga Sabata kwa chaka chimodzi kaamba ka Aisrayeli. Icho chinatsatira nyengo ya zaka za Sabata zisanu ndi ziwiri za kulima zomwe zonse pamodzi zinakwanira zaka 49. Chaka cha makumi asanu, Chaka Choliza Lipenga, chinali pachimake pa nyengo ya kusunga Sabata kwa dzikolo komwe Yehova anapatsa anthu ake, kukwaniritsa lonjezo lomwe anapanga kwa kholo lawo Abrahamu, “Bwenzi la Yehova.” (Yakobo 2:23; Yesaya 41:8) Pa nthawi ya Chaka Choliza Lipenga, ufulu unali kulalikiridwa kuzungulira m’dziko lonse. Ichi chinatanthauza ufulu kwa Aisrayeli onse omwe anadzigulitsa iwo eni kutumikira chifukwa cha ngongole. Chinthu china cha Chaka Choliza Lipenga chinali chakuti dziko la cholowa lomwe linali litagulitsidwa (chifukwa cha kubwezera ndalama) linali kubwezeretsedwa.​—Levitiko 25:1-54.

4. Ndi liti pamene Chaka Choliza Lipenga chinali kulengezedwa, ndipo motani?

4 Ndi mayambidwe amenewo, inu mungaya mikire nchifukwa ninji Chaka Choliza Lipe nga chinali phwando la pa chaka la ufulu. Chinalengezedwa mwa kuimba lipenga pa Tsiku la Chitetezero.a Monga momwe Mose ana lembera pa Levitiko 25:9, 10: “Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m’mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m’dziko lanu lonse. Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m’dzikomo kuti akhale aufulu. Muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu ali yense ku zake zake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.” Mu 1473 B. C.E., Yoswa anatsogolera Aisrayeli kuwoloka Mtsinje wa Yordani kupita ku Dziko Lolonjezedwa, komwe amayenera kukumbukira Chaka Choliza Lipenga.

Ufulu Woyambirira Ulalikidwa

5. Ndi mbali ziti za ufulu ndi Chaka Choliza Lipenga zimene tidzalingalirapo?

5 Zokambitsiridwazi zingaoneke kukhala mbiri ya makedzana yokhala ndi choturukapo chochepa pa miyoyo yathu, makamaka ngati ife sitiri ochokera kufuko la chiYuda. Komabe, Yesu Kristu anatipatsa ife chifukwa chenicheni cha kuyembekezerera Chaka Choliza Lipenga chokulira. Chiri chimenecho chomwe chimakhazikitsa maziko eni eni kaamba ka kusangalala kwathu chifukwa cha kumasulidwa, kapena ufulu. Kuti tiyamikire nchifukwa ninji, tikafunikira kuona m’mene Yesu mu njira ziwiri anaperekera chimasulo mu zana loyamba. Kenaka tidzalingalira ndi motani m’mene izi zimagwirizanira ndi zimasuko ziwiri mu nthawi yamoyo, koma zimasuko pa muyezo wokulira ndi kutipatsa ife chifukwa chokulira chakusangalalira.

6, 7. (a) Yesaya 61:1-7 inaneneratu ponena za zochitika zosangalatsa ziti? (b) Ndi motani m’mene Yesu anasonyezera kuti ulosi wa Yesaya unali kukwaniritsidwa?

6 Angakhale sanali kulankhula mwachindunji ponena za Chaka Choliza Lipenga cha ntha wi yakale, kulosera kwa ulosi ponena za ku bwera kwa chimasuko kunapangidwa pa Yesa ya 61:1-7: “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire [mbiri yabwino, NW) kwa ofatsa. Iye wandivtumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalivkire kwa am’nsinga amasulidwe ndi kutsegu lidwa [maso ngakhale, NW] kwa a m’ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro . . . Adzakhala nacho chikondwerero chosatha.” Ndi motani ndipo ndi liti pamene ulosi umenewu udzapeza chikwaniritso?

7 Pambuyo pa chikondwerero cha Paskha mu chaka cha 30 C.E., Yesu Kristu anapita m’sunagoge pa tsiku la Sabata. Iye kumeneko anawerenga mbali ya ulosi wa Yesaya ndi kugwiritsira ntchito kwa iye mwini. Luka 4: 16-21 imati, kugwira mbali: “Iye adafunyulula bukhulo, napeza pomwe panalembedwa: ‘Mzimu wa Yehova uli pa Ine, chifukwa chache Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino, ananditumiza Ine kukalalikira am’nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyenso, Kutulutsa ndi ufulu ophwanyika, kulalikira chaka chosankhika cha Yehova’ . . . Ndipo anayamba kunena kwa iwo: ‘Lero lembo ili lakwaniritsidwa m’makutu anu.’ ”

8 (a) Ndi ufulu woyambirira uti umene Yesu anapereka? (b) Ndi motani m’mene ichi chachitidwira chitsanzo pa Yohane 9:1-34?

8 Mbiri yabwino yomwe Yesu analengeza inapereka chimasuko cha uzimu kaamba ka Ayuda omwe anailandira iyo. Maso awo kukhala atamasulidwa ku chimene kulambira kowona kunatanthauza kweni kweni ndi kufuna, iwo anamasulidwa ku ziphunzitso zonye nga zambiri. (Mateyu 5:21-48) Ufulu umene wu unali wa mtengo wapatali kuposa kuchilitsa kwa kuthupi kumene Yesu anakupanga. Chotero, ngakhale Yesu anatsegula maso a munthu wobadwa wakhungu, zotulukapo zo satha zinatuluka kwa munthuyu kaamba ka kuzindikira kwake Yesu monga m’neneri wo chokera kwa Mulungu. Ufulu watsopano wa munthu ameneyu unasiyana ndi mkhalidwe wa atsogoleri achipembedzo omwe anali akapolo ku miyambo yawo ndi zikhulupiliro zawo zabodza. (Yohane 9:1-34; Deuteronomo 18:18; Mateyu 15:1-20) Koma uwu unali chabe ufulu woyambilira. Ngakhale mu zana loyamba, Yesu anafunikira kuthandiza ndi chiwombolo cha mtundu wina chomwe chinalingana ndi Chaka Choliza Lipenga m’nthawi ya Israyeli wakale. Nchifukwa ninji chiri chanzeru kumaliza motero?

9. Angakhale ponena za awo omwe amasulidwa mwa uzimu, ndi mtundu uti wa ukapolo womwe udakalipobe?

9 Yesu anati kwa munthu yemwe anali wakhungu: “Kudzaweruza ndadza Ine ku dziko lino lapansi; kuti iwo osapenya apenye ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.” Kenaka iye anauza Afarisi: “Mukadakhala osaona, simukadakhala nalo chimo. Koma tsopano munena kuti, ‘Tipenya.’ Chimo lanu lakhala.” (Yohane 9:35-41) Inde, chimo lotsogoza ku imfa linali vuto lalikulu kweni kweni, monga momwe liliri tsopano. (Aroma 5:12)Ayuda, kuphatikizapo atumwi, omwe anapindula kuchokera ku chimasuko choyambilira, chimasuko chauzimu chomwe Yesu Kristu anapereka, anakhalabe anthu opanda ungwiro. Iwo anapitiriza be kukhala akapolo ku chimo lomwe li matsogoza ku imfa. Kodi Yesu akanatha kusintha chimenecho? Kodi iye akanatero? Ngati ndi choncho, ndi liti?

10. Yesu analonjeza kuti adzapereka ufulu woonjezereka wa mtundu wanji?

10 Poyambirira, Yesu ananena kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu, ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidza kumasulani.” Amvetseri ake Achiyuda anayankha kuti: “Tiri mbeu ya Abrahamu ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iri yo nse. Munena bwanji, ‘Mudzayesedwa aufulu?’ ” Yesu anayankha: “Indetu, indetu, ndine na kwa inu, aliyense wakuchita chimo ali ka polo wa chimolo. Koma kapolo sakhala m’nyu mba nthawi yonse; mwana ndiye akhala ntha wi yonse.” (Yohane 8:31-36) Chotero, cholowa cha kuthupi kuchokera kwa Abrahamu sichi kanatha kupulumutsa Ayuda kuchokera ku ukapolo ku uchimo. Yesu anapanga chilengezo cha mbiri chimenecho mogwirizana ndi ufulu kukokera chidwi ku china chake chomwe chinali kubwera ndipo chomwe chidzakhala chokulirapo kusiyana ndi zomwe Aisrayeli anakumana nazo mu Chaka Choliza Lipenga chiri chonse.

Chaka Choliza Lipenga cha Akristu Chiyamba

11. Nchifukwa ninji chikondwerero chathu cha Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chimalunjikitsidwa pa chaka cha 33 C.E.?

11 Ayuda sanaone kuti Chaka Choliza Lipe nga cha M’pangano la Chilamulo cha Mose linali chifaniziro cha Chaka Choliza Lipenga chokulirapo. (Akolose 2:17; Aefeso 2:14, 15) Chaka Choliza Lipenga chimenechi kaamba ka Akristu chimaphatikizamo “chowonadi” chomwe chingamasule anthu—chowonadi chimenecho chozikidwa pa Mwana, Yesu Kristu. (Yohane 1:17) Ndi liti pamene Chaka Choliza Lipenga chokulirapo chimenechi chomwe chingabweretse ufulu angakhale chimasuko ku chimo ndi zotsatirapo zake chinayamba kukumbukiridwa? Munali mungululu ya 33 C.E., pa tsiku la Pentekoste. Panali pambuyo pa masi ku khumi pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Yesu kukapereka kuyenera kwa nsembe yake kwa Yehova Mulungu.​—Ahebri 9:24-28.

12, 13. Ndi chiyani chomwe chinachitika pa mbuyo pa imfa ya Yesu chomwe mwamsanga chinabweretsa chokumana nacho chapadera kwa ophunzira ake?

12 Pambuyo pa Yesu, panalibe cholengedwa cha umunthu chomwe chinaukitsidwa kuchokera kwa akufa ndi kupitirizabe kukhala ndi moyo ku nthawi yosatha. (Aroma 6:9-11) Komabe, onse anagona mu imfa ndipo adzapitirizabe kugona mpaka nthawi yokhazikitsidwa kaamba ka chiukiriro cha banja la munthu. Mwa chiukiriro chake kudzera mu mphamvu ya Mulungu, Yesu Kristu anakhala chomwe Malemba ouzilidwa amamutchula iye, “chipatso choundukula cha iwo akugona.”​—1 Akorinto 15:20.

13 Masiku makumi asanu pambuyo pa kuukitsidwa kwake, panali chizindikiritso chakuti Yesu Kristu woukitsidwa anali atakwela ku mwamba ndipo analowa kukaoneka pamaso pa Yehova Mulungu limodzi ndi mtengo wa nse mbe yake ya munthu yangwiro ndipo anaipereka iyo m’malo mwa mtundu wa anthu. Ili linali tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. M’kumve ra ku malangizo ochokera kwa Yesu, chifupi fupi ophunzira 120 anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu. Kenaka Yesu anatsanulira mzi mu wake woyera pa ophunzira amenewa, m’kukwaniritsa Yoweli 2:28, 29. Malilime mo nga ngati amoto anatera pamwamba pa mitu yawo, ndipo anayamba kulankhula m’zinenero zomwe zinali zachilendo kwa iwo. (Machitidwe 2:16-21, 33) Ichi chinali chitsimikiziro chakuti Yesu Kristu woukitsidwa anali atakwela ku mwamba ndipo analowa pamaso pa Mulungu limodzi ndi mtengo wa nsembe yake ya mu nthu yangwiro yomwe anaipereka m’malo mwa mtundu wa anthu

14. (a) Kodi ndi mkhalidwe wotani umene una lipo ponena za ophunzira a Yesu m’chigwirizano ndi mapangano? (b) Chipangano chatsopano chinaphatikizapo dalitso liti lapadera?

14 Kodi nchiyani chomwe chinali chotuluka po kaamba ka ophunzira amenewa? Choyambirira, iwo anamasulidwa ku Chipangano cha Lamulo la Mose, lomwe Mulungu anali atapanga ndi mtundu wachibadwa wa Israye li, lomwe iye anali asanalichotse, kulikhomera ku mtengo wozunzirapo wa Yesu. (Akolose 2: 13, 14; Agalatiya 3:13) Lamulo limenelo lina lowedwa m’malo ndi lamulo latsopano lopangidwa, osati ndi mtundu wachibadwa wa Israye li, koma ndi “mtundu” watsopano wa Israyeli wa uzimu. (Ahebri 8:6-13; Agalatiya 6:16) Chipangano chatsopano chimenechi, chonenedweratu pa Yeremiya 31:31-34, Chinakonzedwa kudzera mwa Nkhoswe yokulirapo kuposa m’neneri Mose wakale. Kokha chifukwa cha chikondwerero mu ufulu, tiyenera kuzindikira kweni kweni chinthu chimodzi ponena za chipangano chatsopano. Mtumwi Paulo anachititsidwa chidwi ku ichi, akumalemba: “Ichi ndi chipangano ndidzapangana nawo atapita ma siku ajawo, ‘. . . Ndipo machimo awo ndi masayeruziko awo sindidzawakumbukilanso. Koma pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.”​—Ahebri 10:16-18.

15. (Nchifukwa ninji tinganene kuti pa Penteko ste wa 33 C.E. Chaka Choliza Lipenga chinayamba kaamba ka odzozedwa? (Aroma 6:6, 16-18)

15 Yesu anali kuloza ku ufulu umenewu ku choka ku chimo pamene iye anati: “Ngati Mwana akumasulani inu, mudzakhala aufulu.” (Yohane 8:36) Tangolingalirani—ufulu kuchokera ku chimo unakhala wothekera pa maziko a nsembe ya Kristu! Kuyambira pa tsiku la Pentekoste, Mulungu analalikira kwa okhulupirira angwiro ndipo kenaka anawatenga iwo monga ana ake a uzimu okhala ndi ziyembekezo za kulamulira limodzi ndi Kristu kumwamba. Paulo akulongosola: “Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo womachiti tsa mantha kachiwiri, koma inu munalandira mzimu wakulandiridwa monga ana, . . . pame nepa, ngati ife tiri ana, ife tirinso olowa nyu mba; indedi olowa nyumba a Mulungu, koma olowa nyumba ogwirizana limodzi ndi Kristu.” (Aroma 8:15-17) Mosakaikira, Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chinayamba kaamba ka Akristu odzozedwa nga iwo monga ana ake a uzimu okhala ndi

16. Kodi ndi madalitso oonjezereka ati limodzi ndi ziyembekezo zomwe zinaphatikizidwamo kaamba ka awo okumbukira Chaka Choliza Lipenga cha Akristu?

16 Chotero pa tsiku limenelo la Pentekoste mu chaka cha 33 C.E., mtundu watsopano wa Israyeli wauzimu unayamba kukhalako. Una pangidwa ndi anthu omwe machimo awo anali atakhululukidwa pa maziko a nsembe ya mwa zi wa Kristu. (Aroma 5:1, 2; Aefeso 1:7) Ndani wa ife amene angakane kuti mamembala oyambilira amenewo Aisrayeli wauzimu amene anatengedwa mu chipangano chatsopano ana kumana ndi chiombolo chochititsa chidwi mwakukhala atakhululukidwa machimo awo? Iwo anapangidwa ndi Mulungu kulowa “ ‘mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, ndi anthu a mwini wace, kote ro kuti mukalalikire zoposazo’ za iye amene anakuitanani muturuke mumdima mulo we m’kuunika kwache kodabwitsa.” (1 Petro 2:9) Zowona, matupi awo aumunthu anali opa nda ungwiro ndipo anayenera kufa m’kupita kwa nthawi. Koma, tsopano popeza Mulungu analengeza iwo kukhala olungama ndipo ana walandira monga ana ake auzimu, imfa yawo ya kuthupi inali kokha “kumasulidwa” komwe kunawalola iwo kaamba kakuukitsidwa kwa Kristu ku “ufumu wa kumwamba.”​—2 Timoteo 4:6, 18.

17, 18. Nchifukwa ninji ufulu wa Chaka Choliza Lipenga cha Akristu unali wa mtengo wapatali koposa ndi ufulu woyambirira umene Yesu ana lengeza?

17 itepi loyambilira la kumasula Ayuda okhulupirira kuchokera ku ziphunzitso ndi machitachita olakwika liri la mtengo wapatali. Komabe, taona kuti Yesu anapyola ufulu wauzimu umenewo. Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. kunka mtsogolo, iye anamasula anthu okhulupirira kuchokera ku “lamulo la chimo ndi la imfa.” (Aroma 8:1, 2) Chotero chinayamba Chaka Choliza Lipenga cha Akristu kaamba ka Akristu odzozedwa. Ichi moo nadi chinali chiwombolo cha mtengo wapata li, popeza chinaphatikizamo ziyembekezo za moyo wakumwamba monga olowa m’malo li modzi ndi Kristu.

18 Talingalira mbali ziwiri za ufulu wa Chikristu mu zana loyamba, ndi omwe mosakaikira anali maziko kaamba ka chisangalalo. Ndipo akhulupiriri a mu zana loyamba anasangalala. (Machitidwe 13:44-52; 16:34; 1 Akorinto 13:6; Afilipi 4:4) Icho kweni kweni chinalidi chowona m’chigwirizano ndi kugawanamo kwawo mu Chaka Choliza Lipenga cha Akristu, chomwe chinatsegula njira kaamba ka iwo yakulandira madalitso osatha a ku mwamba.​—1 Petro 1:3-6; 4:13, 14.

19. Ndi mafunso ati omwe atsala kaamba ka Akristu omwe sali odzozedwa ndi mzimu, ndipo ndi chiyani chomwe chimasonyeza kuti iwonso adzakhala ndi mbali mu ufulu wopereka mwa umulungu?

19 Ndi kuti, pomwepo, kumene Akristu owona ambiri lerolino amakhalapo mu chifanizo chimenechi, popeza iwo sanalalikidwe kukhala olungama kaamba ka moyo ndipo sanadzozedwe ndi mzimu woyera? Pali chifukwa chaMalemba choyenera kuyang’anidwa kaambaka kumasulidwa kokulira m’malo mwawo monga mbali ya Chaka Choliza Lipenga cha Akristu. Kumbukirani Machitidwe 3:20, 21: “Yesu, amene thambo la kumwamba, liyenera, kumulandira kufikira za kukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera [akale, NW].” (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:31.) Mu mzera wofananawo, Yohane, mtumwi wodzozedwa yemwe anali akusangalala ndi Chaka Choliza Lipenga cha Akristu, analemba ponena za Yesu Kristu: “lye ndiye chiombolo cha machimo athu, koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:2) Kodi chimenechi chikutanthauza kuti Akristu ambiri omvera lerolino omwe alibe chiyembekezo chopita kumwamba angagawanemo mu ufulu wa Chikristu? Kodi chimenecho chiri kokha mtsogolo, kapena kodi tiri ndi chifukwa lero lino chakusangalalira? Tingapeze chimene chomwakusanthula mbali za ufulu wa Chikristu ndi Chaka Choliza Lipenga chomwe chiri ndi tanthauzo lapadera kaamba ka alambiri owona lerolino.

Mawu a M’munsi]

a Tsiku la Chitetezero la chaka ndi chaka linachitidwa pa tsiku la 10 la Tishri, mwezi wa kalenda ya chiHebri, yofanana ndi nyengo yathu ya September mpaka October

Kodi Malingaliro Anu ndi Otani?

◻ Kodi ndi mapindu otani omwe analipo kaamba ka Chaka Choliza Lipenga mu Israyeli wakale?

◻ Ndi motanim’mene Yesu analalikira ufulu woyambilira, ndipo ndi chiyani chomwe chinaphatikizapo?

◻ Ndi liti pamene Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chinayamba, ndipo nchiyani chomwe chiri maziko kaamba ka yankho lanu?

◻ Nchifukwa ninji tiri ndi chifukwa chakuyang’ana kutsogolo kaamba ka ufulu wophatikiza mamiliyoni a Akristu omwe sali odzozedwa ndi mzimu?

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”(Miyambo 4:18) M’chigwirizano ndi prinsipulo limenelo, nkhaniyi limodzi ndi yotsatirapo ikupereka kalongosoledwe koongokera ndi kokulitsidwa ka Chaka Choliza Lipenga

Chithunzi patsamba 24

Yesu alalikira ufulu mu 30 C.E.

Chithunzi patsamba 27

Chaka Choliza Lipenga cha Akristu chiyamba mu 33 C.E.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena