-
Iye Amamvetsa Mavuto AthuNsanja ya Olonda—2008 | May 1
-
-
Lazaro yemwe anali mnzake wa Yesu atamwalira, Yesu anapita kwawo kwa Lazaroyo. N’zomveka kuti Mariya ndiponso Marita, omwe anali alongo ake a Lazaro, anali ndi chisoni kwambiri. Ndipo Yesu ankalikonda kwambiri banja limeneli. (Yohane 11:5) Ndiyeno kodi Yesu akanachita chiyani? Nkhaniyo imati: “Yesu atamuona [Mariya] akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mu mtima ndi kumva chisoni. Kenako anati: ‘Mwamuika kuti?’ Iwo anati kwa iye: ‘Ambuye tiyeni mukaone.’ Yesu anagwetsa misozi.” (Yohane 11:33-35) N’chifukwa chiyani Yesu analira? N’zoona kuti Lazaro, yemwe anali mnzake, anali atamwalira, komabe Yesu anali atatsala pang’ono kumuukitsa. (Yohane 11:41-44) Kodi pali chinthu chinanso chimene chinam’khudza mtima kwambiri Yesu?
Taonaninso mawu a m’Baibulo amene ali m’ndime yapitayi. Onani kuti Yesu ataona Mariya ndiponso anthu ena omwe anali naye akulira, iye “anadzuma” ndipo ‘anavutika mu mtima.’ Mawu a Chigiriki omwe anawagwiritsira ntchito palembali amasonyeza kukhudzidwa mtima kwambiri.a Zimene iye anaona zinamukhudza kwambiri. Umboni wa zimenezi ndi woti m’maso mwake munalengeza misozi. N’zoonekeratu kuti Yesu anakhudzidwa mtima ndi ululu umene anthu ena anali kumva. Kodi inuyo munayamba mwalirapo chifukwa choona munthu amene mumam’konda akulira?—Aroma 12:15.
-
-
Iye Amamvetsa Mavuto AthuNsanja ya Olonda—2008 | May 1
-
-
a Mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “anagwetsa misozi” nthawi zambiri amatanthauza “kusisima.” Koma mawu amene anawagwiritsira ntchito pofotokoza kulira kwa Mariya ndi anthu ena aja angatanthauze “kulira mofuula kapena kubuma.”
-