Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 9/1 tsamba 13-18
  • Khalanibe m’Teokrase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalanibe m’Teokrase
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Teokrase Yeniyeni Nchiyani?
  • Gulu Lateokrase
  • Kaonedwe Kateokrase ka Ulamuliro wa Anthu
  • Ikani Ulemerero wa Mulungu Patsogolo
  • “Khalani Akutsanza a Mulungu”
  • Yehova Alamulira—Kupyolera mwa Teokrase
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Abusa ndi Nkhosa M’teokrase
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Gawo 10: Pomalizira Pake Papezeka Boma Langwiro!
    Galamukani!—1991
  • Kuŵeta Limodzi ndi Mlengi Wathu Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 9/1 tsamba 13-18

Khalanibe m’Teokrase

“Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.”​—YESAYA 33:22.

1. Kodi nchifukwa ninji boma ndi nkhani yaikulu kwa anthu ambiri?

NKHANI yonena za boma ndi nkhani yaikulu kwa aliyense. Boma labwino limadzetsa mtendere ndi chitukuko. Baibulo limati: “Mfumu akhazikitsa dziko ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW].” (Miyambo 29:4) Koma boma loipa limachititsa chisalungamo, chinyengo, ndi kupondereza ena. “Polamulira woipa anthu ausa moyo.” (Miyambo 29:2) M’mbiri yonse, anthu ayesa maboma amitundumitundu, ndipo, momvetsa chisoni, iwo “ausa” moyo chifukwa cha kuponderezedwa ndi olamulira awo. (Mlaliki 8:9) Kodi pali mtundu uliwonse wa boma umene udzakhutiritsadi anthu kosatha?

2. Kodi nchifukwa ninji “teokrase” ndi mawu abwino ofotokoza boma lakale la Israyeli?

2 Wolemba mbiri Josephus anatchula mtundu wapadera wa boma pamene analemba kuti: “Mitundu ina ya anthu yapatsa mphamvu zonse za ndale kwa mafumu, ina kwa timagulu ta anthu, komanso ina kwa anthu onse. Komabe, wotipatsa malamulo wathu [Mose], sanakopeke ndi mtundu uliwonse wandale zimenezi, koma malamulo ake anali a mtundu umene​—ngati tingaupangire dzina​—tingautche kuti ‘teokrase,’ kuika uchifumu wonse ndi mphamvu zonse m’manja mwa Mulungu.” (Against Apion, II, 164-5) Malinga nkunena kwa Concise Oxford Dictionary, liwulo teokrase limatanthauza “boma lolamuliridwa ndi Mulungu.” Ngakhale kuti liwulo mulibe m’Baibulo, ilo limafotokoza bwino boma la Israyeli wakale. Ngakhale kuti Aisrayeli anadzakhala ndi mfumu yooneka, wolamulira wawo weniweni anali Yehova. Mneneri wachiisrayeli Yesaya anati: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.”​—Yesaya 33:22.

Kodi Teokrase Yeniyeni Nchiyani?

3, 4. (a) Kodi teokrase yeniyeni nchiyani? (b) Posachedwapa, kodi teokrase idzadzetsa madalitso otani kwa mtundu wonse wa anthu?

3 Kuyambira pamene Josephus anapanga liwulo, zitaganya zambiri zanenedwa kukhala zateokrase. Zina zinaoneka kukhala za anthu osalolera, otengeka maganizo, ndiponso opondereza ena mwankhanza. Kodi izo zinalidi zateokrase? Osati malinga ndi mmene Josephus analigwiritsirira ntchito liwulo. Vuto nlakuti awonjezera matanthauzo ena ku liwu lakuti “teokrase.” Buku lotchedwa kuti World Book Encyclopedia limamasulira liwulo kukhala “boma limene dziko lake limalamuliridwa ndi wansembe kapena ansembe, ndipo m’limene ansembe ali ndi ulamuliro pankhani za ntchito ndi zachipembedzo.” Komabe, teokrase yeniyeni si boma lolamuliridwa ndi ansembe. Iyo kwenikweni ndi ulamuliro wa Mulungu, boma lolamuliridwa ndi Mlengi wa chilengedwe chonse, Yehova Mulungu.

4 Posachedwapa, dziko lonse lapansi lidzakhala mu ulamuliro wateokrase, ndipo limenelo lidzakhala dalitso lalikulu chotani nanga! ‘Mulungu yekha adzakhala nawo [mtundu wa anthu], ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.’ (Chivumbulutso 21:3, 4) Palibe ulamuliro wa ansembe, anthu opanda ungwiro umene ungadzetse chimwemwe choterocho. Ulamuliro wokha wa Mulungu ndiwo ungachite zimenezo. Chotero, Akristu oona samayesa kudzetsa teokrase m’njira yandale. Iwo amayembekeza kwa Mulungu moleza mtima kuti akhazikitse teokrase yolamulira dziko lonse lapansi panthaŵi yake ndiponso m’njira yake.​—Danieli 2:44.

5. Kodi nkuti kumene teokrase yeniyeni ikugwira ntchito lerolino, ndipo pakufunsidwa mafunso otani okhudza teokrase imeneyo?

5 Komabe, teokrase yeniyeni panopo ikugwira ntchito. Kuti? Pakati pa awo amene amagonjera ulamuliro wa Mulungu modzifunira ndi kugwirizana kuti achite chifuniro chake. Anthu okhulupirika ameneŵa asonkhanitsidwa monga “mtundu” wauzimu wa padziko lonse mu “dziko” lawo lauzimu. Iwo ndiwo otsalira a “Israyeli wa Mulungu” ndi anzawo achikristu oposa mamiliyoni asanu ndi theka. (Yesaya 66:8; Agalatiya 6:16) Ameneŵa amagonjera Yesu Kristu, Mfumu yakumwamba yoikidwa ndi Yehova Mulungu, “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17; Chivumbulutso 11:15) Kodi gulu limeneli nlateokrase motani? Kodi anthu ake amauona bwanji ulamuliro wa maboma a anthu? Ndipo ndi motani mmene anthu okhala ndi ulamuliro m’gulu lawo lauzimuli amasungira pulinsipulo lateokrase?

Gulu Lateokrase

6. Kodi gulu looneka la anthu lingalamuliridwe motani ndi Mulungu?

6 Kodi gulu la anthu lingalamuliridwe motani ndi Yehova, amene amakhala kumwamba kosaoneka? (Salmo 103:19) Nzotheka chifukwa chakuti awo amene ali m’gululo amatsatira uphungu wouziridwawo wakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika paluntha lako.” (Miyambo 2:6; 3:5) Iwo amalola Mulungu kuwalamulira pamene atsatira “chilamulo cha Kristu” ndi kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a m’Baibulo pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. (Agalatiya 6:2; 1 Akorinto 9:21; 2 Timoteo 3:16; onani Mateyu 5:22, 28, 39; 6:24, 33; 7:12, 21.) Kuti achite zimenezi iwo ayenera kukhala ophunzira Baibulo. (Salmo 1:1-3) Monga Abereya akalewo amene anali “mfulu,” iwo samatsatira anthu koma nthaŵi zonse amafunafuna umboni m’Baibulo wa zinthu zimene akuphunzira. (Machitidwe 17:10, 11; Salmo 119:33-36) Iwo amapemphera monga wamasalmo kuti: “Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.”​—Salmo 119:66.

7. Kodi ndondomeko ya uyang’aniro m’teokrase ndi yotani?

7 M’gulu lililonse, payenera kukhala ena audindo kapena opereka chitsogozo. Mboni za Yehova nazonso zili nawo, ndipo zimatsatira makonzedwe a ulamuliro ofotokozedwa ndi mtumwi Paulo kuti: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Mogwirizana ndi zimenezi, amuna oyeneretsedwa okha ndiwo amatumikira monga akulu m’mipingo. Ndiponso ngakhale kuti Yesu​—“mutu wa munthu yense”​—ali kumwamba, padziko lapansi padakali “otsala” a abale ake odzozedwa, amene akuyembekezera kukalamulira naye kumwamba. (Chivumbulutso 12:17; 20:6) Ameneŵa ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wopangidwa ndi anthu ambiri. Akristu amasonyeza kuti amagonjera Yesu, ndiponso mutu wa Yesu, Yehova, mwa kuvomereza uyang’aniro wa “kapolo” ameneyo. (Mateyu 24:45-47; 25:40) Mwa njira imeneyi, teokrase imakhala yadongosolo. “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.”​—1 Akorinto 14:33.

8. Kodi akulu achikristu amachirikiza motani pulinsipulo la teokrase?

8 Akulu achikristu amachirikiza pulinsipulo la teokrase chifukwa chakuti amazindikira kuti Yehova adzawaŵerengera mlandu wa mmene akuchitira udindo wawo wokhala ndi polekezera. (Ahebri 13:17) Ndipo popanga zosankha, iwo amadalira nzeru ya Mulungu, osati nzeru zawo. Akamatere, amatsatira chitsanzo cha Yesu. Iye anali munthu wanzeru woposa onse amene anakhalako. (Mateyu 12:42) Komabe, iye anauza Ayuda kuti: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu payekha, koma chimene aona Atate achichita.” (Yohane 5:19) Akulu alinso ndi maganizo ofanana ndi a Mfumu Davide. Iye anali ndi udindo waukulu muulamuliro wateokrase. Koma anafuna kutsatira njira ya Yehova, osati njira yake. Iye anapemphera kuti: “Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere panjira yachidikha.”​—Salmo 27:11.

9. Ponena za ziyembekezo zosiyana ndi mautumiki osiyana m’teokrase, kodi Akristu odzipatulira ali ndi lingaliro loyenerera lotani?

9 Ena akayikira ngati chili chilungamo kuti amuna okha oyeneretsedwa ndiwo amakhala ndi udindo mumpingo kapena kuti ena ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba pamene ena akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. (Salmo 37:29; Afilipi 3:20) Komabe, Akristu odzipatulira amadziŵa kuti makonzedwe ameneŵa ngofotokozedwa m’Mawu a Mulungu. Ndi makonzedwe ateokrase. Ngati ngokayikitsa, kaŵirikaŵiri ngokayikitsa kwa awo amene sazindikira mapulinsipulo a Baibulo. Ndipotu Akristu amadziŵa kuti kwa Yehova, amuna ndi akazi ngolingana ponena za chipulumutso. (Agalatiya 3:28) Kwa Akristu oona, kukhala olambira Mfumu yachilengedwe chonse ndiwo mwayi waukulu koposa, ndipo amasangalala kuchita chilichonse chimene Yehova awauza kuchita. (Salmo 31:23; 84:10; 1 Akorinto 12:12, 13, 18) Ndiponso, moyo wosatha, kaya ukhale wakumwamba kapena wapadziko lapansi la paradaiso, nchiyembekezo chosangalatsa kwambiri.

10. (a) Kodi Yonatani anasonyeza maganizo abwino otani? (b) Kodi Akristu amasonyeza motani maganizo ofanana ndi a Yonatani lerolino?

10 Choncho, Mboni za Yehova zimafanana ndi Yonatani, mwana woopa Mulungu wa Mfumu Sauli. Yonatani ayenera kuti akanakhala mfumu yabwino kwambiri. Komabe, chifukwa cha kusakhulupirika kwa Sauli, Yehova anasankha Davide kuti akhale mfumu yachiŵiri ya Israyeli. Kodi Yonatani anapsa nazo mtima? Iyayi. Iye anakhala bwenzi lapamtima la Davide kufikira pomteteza kwa Sauli. (1 Samueli 18:1; 20:1-42) Mofananamo, awo oyembekezera kudzakhala padziko lapansi sachitira nsanje oyembekezera kupita kumwamba. Ndiponso Akristu oona sachitira nsanje awo amene ali ndi udindo wateokrase mumpingo. M’malo mwake, ‘amawachitira ulemu woposatu mwa chikondi,’ pozindikira ntchito yawo yaikulu imene amachitira abale ndi alongo awo auzimu.​—1 Atesalonika 5:12, 13.

Kaonedwe Kateokrase ka Ulamuliro wa Anthu

11. Kodi Akristu ogonjera ulamuliro wateokrase amawaona motani olamulira aumunthu?

11 Ngati Mboni za Yehova zili mu ulamuliro wateokrase, ulamuliro wa Mulungu, kodi zimawaona motani olamulira a maiko? Yesu ananena kuti otsatira ake ‘sadzakhala a dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Komabe, Akristu amadziŵa za mangaŵa awo kwa “Kaisara,” maboma a anthu. Yesu ananena kuti iwo ayenera ‘kupatsa kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.’ (Mateyu 22:21) Malinga nkunena kwa Baibulo, maboma a anthu “aikidwa ndi Mulungu.” Yehova, Mwini ulamuliro wonse, amalola maboma kukhalapo, ndipo amafuna kuti mabomawo achitire anthu awo zabwino. Akamatero, amakhala “mtumiki wa Mulungu.” Akristu amagonjera boma la dziko limene akukhalamo “chifukwa cha chikumbumtima [chawo].” (Aroma 13:1-7) Komano ngati boma lifuna chinachake chosemphana ndi lamulo la Mulungu, Mkristu ‘adzamvera Mulungu koposa anthu.’​—Machitidwe 5:29.

12. Pamene Akristu akuzunzidwa ndi akuluakulu a boma, kodi iwo amatsatira chitsanzo chayani?

12 Bwanji pamene Akristu oona azunzidwa ndi akuluakulu aboma? Pamenepo iwo amatsatira chitsanzo cha Akristu oyambirira, amene anapirira ziyeso zazikulu. (Machitidwe 8:1; 13:50) Iwo anadziŵa kuti chikhulupiriro chawo chidzayesedwa popeza kuti Yesu anali atawauziratu. (Mateyu 5:10-12; Marko 4:17) Komabe, Akristu oyambirirawo sanabwezere owazunzawo; komanso chikhulupiriro chawo sichinafooke potsenderezedwa. M’malo mwake, iwo anatsatira chitsanzo ichi cha Yesu: “Pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zoŵaŵa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.” (1 Petro 2:21-23) Inde, mapulinsipulo achikristu analaka zitokoso za Satana.​—Aroma 12:21.

13. Kodi Mboni za Yehova zachita motani ndi zizunzo ndi zinenezo zofalitsidwa?

13 Ndi mmenenso zilili lerolino. M’zaka za zana lino, olamulira opondereza asautsa Mboni za Yehova moipitsitsa​—monga momwe Yesu ananeneratu. (Mateyu 24:9, 13) M’maiko ena, mabodza ndi maumboni onama akufalitsidwa ndi anthu amene akufuna kukakamiza olamulira kuti akhaulitse Akristu oona mtima ameneŵa. Komabe, mosasamala kanthu za “mbiri yoipa” imeneyi, Mboni zimadzitsimikizira zokha kuti ndi atumiki a Mulungu mwa khalidwe lawo labwino. (2 Akorinto 6:4, 8) Ngati nkotheka, zimatengera milandu yawo kwa anthu audindo ndi kumabwalo amilandu a m’dzikolo kuti zipereke umboni wakuti zilibe mlandu. Zimagwiritsira ntchito njira ina iliyonse imene zingathe kuti zichirikize uthenga wabwino poyera. (Afilipi 1:7) Koma zitachita zonse zimene zingathe kuchita mwalamulo, zimasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. (Salmo 5:8-12; Miyambo 20:22) Ngati zachitika, izo sizimaopa kuvutika chifukwa cha chilungamo monga momwe Akristu oyambirira anachitira.​—1 Petro 3:14-17; 4:12-14, 16.

Ikani Ulemerero wa Mulungu Patsogolo

14, 15. (a) Kodi chofunika koposa nchiyani kwa awo amene akuchirikiza pulinsipulo la teokrase? (b) Kodi ndi pachochitika chiti pamene Solomo anapereka chitsanzo chabwino cha kudzichepetsa pamalo ake auyang’aniro?

14 Pamene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera, chinthu choyamba chimene anatchula ndicho kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. (Mateyu 6:9) Mogwirizana ndi zimenezi, awo amene ali m’teokrase amafunafuna ulemerero wa Mulungu, osati ulemerero wawo. (Salmo 29:1, 2) Baibulo limasimba kuti m’zaka za zana loyamba, zimenezi zinakhumudwitsa ena amene anakana kutsatira Yesu chifukwa chakuti “anakonda ulemerero wa anthu,” anakonda kulandira ulemerero wa anthu. (Yohane 12:42, 43) Ndithudi, pamafunika kudzichepetsa kuti uike Yehova patsogolo m’malo mwa kufunika kwako.

15 Solomo anasonyeza mzimu wabwino pankhaniyi. Yerekezerani zimene ananena popatulira kachisi waulemereroyo amene anamanga ndi mawu a Nebukadinezara onena za chipambano chake m’zomangamanga. Monyada, Nebukadinezara anadzitama kuti: “Suyu Babulo wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa?” (Danieli 4:30) Mosiyana ndi zimenezo, Solomo modzichepetsa sanadzitame pazimene anakwaniritsa, ndipo anati: “Kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m’mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?” (2 Mbiri 6:14, 15, 18; Salmo 127:1) Solomo sanadzikweze. Iye anadziŵa kuti anali wongoimirira Yehova nalemba kuti: “Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.”​—Miyambo 11:2.

16. Mwa kusadzifunira ulemerero, kodi akulu asonyeza motani kuti ali dalitso lalikulu?

16 Akulu achikristu nawonso amakweza Yehova, osati kudzikweza iwo okha. Amatsatira uphungu wa Petro wakuti: “Wina akatumikira, achite ngati mumphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 4:11) Mtumwi Paulo anafotokoza “udindo wa woyang’anira” kukhala “ntchito yabwino” osati malo aulemu apamwamba. (1 Timoteo 3:1) Akulu amaikidwa kuti atumikire, osati kulamulira. Iwo ndi aphunzitsi ndi abusa a nkhosa za Mulungu. (Machitidwe 20:28; Yakobo 3:1) Akulu odzichepetsa ndiponso odzimana ndi dalitso lalikulu pampingo. (1 Petro 5:2, 3) “Muchitire ulemu oterewa,” ndipo tithokoze Yehova kuti wapereka akulu ambiri oyeneretsedwa kuti achirikize teokrase mu “masiku [ano] otsiriza.”​—Afilipi 2:29; 2 Timoteo 3:1.

“Khalani Akutsanza a Mulungu”

17. Kodi awo amene ali m’teokrase amatsanzira Mulungu m’njira zotani?

17 Mtumwi Paulo analimbikitsa kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Awo amene amagonjera teokrase amayesa kutsanzira Mulungu monga momwe anthu opanda ungwiro angathere. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za Yehova kuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:3, 4) Kuti atsanzire mikhalidwe imeneyi ya Mulungu, Akristu amafuna kukhala okhulupirika ndiponso ochita bwino chilungamo. (Mika 6:8; 1 Atesalonika 3:6; 1 Yohane 3:7) Iwo amapeŵa zinthu zambiri zimene zakhala zololeka m’dzikoli, monga khalidwe loipa, kusirira, ndi umbombo. (Aefeso 5:5) Chifukwa chakuti atumiki a Yehova amatsatira malamulo a Mulungu, osati a anthu, gulu lake nlateokrase, loyera, ndiponso labwino.

18. Kodi mkhalidwe waukulu koposa wa Mulungu ndi uti, ndipo kodi Akristu amausonyeza motani mkhalidwewu?

18 Mkhalidwe waukulu wa Yehova Mulungu ndiwo chikondi. “Mulungu ndiye chikondi,” anatero mtumwi Yohane. (1 Yohane 4:8) Popeza kuti teokrase ndiwo ulamuliro wa Mulungu, ndiye kuti ndi ulamuliro wachikondi. Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Gulu lateokrase lasonyeza chikondi chachikulu kwambiri m’masiku otsiriza ano ovuta. Pamene kunali nkhondo yopululutsa fuko ku Afirika, Mboni za Yehova zinasonyeza chikondi kwa onse, mosasamala kanthu za fuko lawo. Pankhondo ya ku Yugoslavia wakale, Mboni za Yehova zochokera kumalo osiyanasiyana zinathandizana, pamene kuli kwakuti magulu ena azipembedzo anachita nawo nkhondo imene anati njoyeretsa fuko. Mboni za Yehova zimayesetsa, iliyonse payokha, kutsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”​—Aefeso 4:31, 32.

19. Kodi awo amene akugonjera teokrase amalandira madalitso otani tsopano ndi mtsogolo momwe?

19 Awo amene amagonjera teokrase ali ndi madalitso aakulu. Ali pamtendere ndi Mulungu ndi Akristu anzawo. (Ahebri 12:14; Yakobo 3:17) Moyo wawo uli ndi chifuno. (Mlaliki 12:13) Iwo ngosungika mwauzimu ndipo ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika chamtsogolo. (Salmo 59:9) Ndithudi, iwo akuoneratu mmene zidzakhalira pamene mtundu wonse wa anthu udzakhala mu ulamuliro wateokrase. Pomwepo, Baibulo limatero, “sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Imeneyo idzakhala nthaŵi yaulemerero chotani nanga! Tiyeni tonse titsimikizire kuti tidzakhala ndi malo m’Paradaiso wamtsogolo ameneyo mwa kukhalabe m’teokrase tsopano.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi teokrase yeniyeni nchiyani ndipo tingaipeze kuti lerolino?

◻ Kodi anthu amagonjera motani ulamuliro wateokrase pamoyo wawo?

◻ Kodi onse amene ali m’teokrase choyamba amafunafuna ulemerero wa Mulungu osati wawo motani?

◻ Kodi ndi mikhalidwe ina iti ya Mulungu imene ochirikiza teokrase amatsanzira?

[Chithunzi patsamba 17]

Solomo anaika ulemerero wa Mulungu patsogolo m’malo moikapo ulemerero wake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena