Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
“Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—MATEYU 16:16.
1, 2. (a) Kodi ukulu wa munthu ungapimidwe motani? (b) Kodi ndi anthu ati m’mbiri amene atchedwa Aakulu, ndipo chifukwa ninji?
KODI muganiza kuti ndimunthu uti wamkulu woposa onse amene anakhalako? Kodi mumapima motani ukulu wa munthu? Mwa nzeru zake m’zankhondo? mwamaluso ake apamwamba koposa? nyonga yake yakuthupi?
2 Olamulira osiyanasiyana atchedwa Aakulu, monga Koresi Wamkulu, Alexander Wamkulu, ndi Charlemagne, amene anatchedwa “Wamkulu” ngakhale m’nthaŵi ya moyo wake. Mwakukhalapo kwawo kochititsa mantha, amuna onga ameneŵa anagwiritsira ntchito chisonkhezero chachikulu pa awo amene anawalamulira.
3. (a) Kodi mapendedwe akupimira ukulu wa munthu ngotani? (b) Malinga ndi mapendedwe oterowo, kodi ndani amene ali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako?
3 Mokondweretsa, wolemba mbiri H. G. Wells analongosola mapendedwe ake akupimira ukulu wa munthu. Zoposa zaka 50 zapitazo, iye analemba kuti: “Mapendedwe a wolemba mbiri a ukulu wa munthu ngakuti ‘Kodi iye anasiyanji kuti chikule? Kodi iye anachititsa anthu kulingalira ziganizo zatsopano mwamphamvu zimene zinalondola zochita zake?’ Mwa mapendedwe ameneŵa,” Wells akupanga chigamulo, “Yesu akuwaposa onse.” Ngakhale Napoléon Bonaparte ananena kuti: “Yesu Kristu wasonkhezera ndi kulamulira otsatira Ake popanda kukhalapo Kwake m’thupi.”
4. (a) Kodi ndimalingaliro otsutsana otani amene alipo ponena za Yesu? (b) Kodi wolemba mbiri amene sanali Mkristu anaika Yesu pamalo otani m’mbiri?
4 Komabe, ena atsutsa kuti Yesu saali munthu wa m’mbiri, koma ngwanthano. Kumbali ina yonkitsa, ambiri alambira Yesu monga Mulungu, akumanena kuti Mulungu anadza kudziko lapansi monga Yesu. Komabe, akuzika zigomezo zake kwakukulukulu paumboni wa m’mbiri wa kukhalapo kwa Yesu monga munthu, Wells analemba kuti: “Kuli kokondweretsa ndi kofunika kuwona kuti wolemba mbiri, wopanda kuipitsidwa maganizo ndi zaumulungu zirizonse, apeza kuti sangathe kusonyeza kupita patsogolo kwa anthu mowona mtima popanda kupereka malo ofunika koposa kwa mphunzitsi wosauka wochokera ku Nazareti. . . . Wolemba mbiri ngati ine, amene samadzitcha Mkristu, amapeza chithunzithunzi chosumikidwa mosatsutsika pamoyo ndi mkhalidwe wa munthu wofunika koposa ameneyu.”
Kodi Yesu Anakhalakodi?
5, 6. Kodi nchiyani chimene olemba mbiri H. G. Wells ndi Will Durant akunena ponena za mbiri ya Yesu?
5 Koma bwanji ngati munthu wina akuuzani kuti Yesu sanakhaleko konse, kuti kwenikweni, iye anali nthano chabe, yopekedwa ndi anthu ena a m’zaka za zana loyamba? Kodi mungayankhe motani chinenezocho? Pamene kuli kwakuti Wells akuvomereza kuti “sitidziŵa zambiri ponena za [Yesu] monga momwe tikafunikira kudziŵa,” iye akuti: “Mauthenga Abwino anayi . . . amavomereza ndi kutipatsa chithunzithunzi cha munthu wotsimikizirika kwambiri; ali ndi zenizeni zokhutiritsa. Kuyerekezera kuti iye sanakhaleko konse, kuti zolembedwa za moyo wake ndizo nthano zopeka, kuli kovuta kwambiri ndipo kumadzutsa mavuto owonjezereka kwa wolemba mbiri kuposa kuvomereza mbali zofunika za mbiri za Uthenga Wabwino monga zowona.”
6 Wolemba mbiri wolemekezedwa Will Durant anapereka chigomeko mwanjira yofananayo, akumalongosola kuti: “Kuti anthu wamba ochepekera [amene anadzitcha Akristu] mumbadwo umodzi kukhala anapeka munthu wamphamvu ndi wosonkhezera kwambiri chotero, wolemekezeka ndi wapamwamba ndi masomphenya osonkhezera kwambiri aubale waumunthu, kukakhala chozizwitsa chosatheka konse koposa cholembedwa chirichonse m’Mauthenga Abwino.”
7, 8. Kodi Yesu anayambukira mbiri ya anthu mokulira chotani?
7 Motero, mukalingalira ndi wokaikira woteroyo kuti: Kodi munthu wopeka—munthu amene sanakhalekodi—akanayambukira mbiri ya anthu kwakukulu chotero? Bukhu lamaumboni lakuti The Historians’ History of the World limati: “Zotulukapo za m’mbiri za ntchito za [Yesu] zinali zamphamvu, ngakhale m’kawonedwe kachikunja kenikeni, kuposa ntchito za munthu aliyense wa m’mbiri. Nyengo yatsopano, yotchuka ndi kutsungula kwakukulu kwa dziko, imayambira pa deti la kubadwa kwake.” Tangolingalirani zimenezo. Ngakhale makalenda ena a lerolino amazikidwa pachaka cholingaliridwa kukhala cha kubadwa kwa Yesu. “Madeti a kumbuyo kwa chakacho amalembedwa monga B.C., kapena before Christ (Kristu asanadze), imatero The World Book Encyclopedia. “Madeti akutsogolo kwa chakacho amalembedwa monga A.D., kapena anno Domini (m’chaka cha Ambuye wathu).”
8 Mwa ziphunzitso zake zamphamvu ndi njira imene anakhalira ndi moyo mogwirizana nazo, Yesu wayambukira miyoyo ya ziŵerengero zosaneneka za anthu pafupifupi kwa zaka zikwi ziŵiri. Monga momwe wolemba wina ananenera moyenerera kuti: “Magulu onse ankhondo amene anaguba, ndi magulu onse omenya nkhondo panyanja amene anapangidwa, ndi nyumba zonse zamalamulo zimene zinakhalako, mafumu onse amene analamulira, ataikidwa pamodzi sanayambukire moyo wa munthu padziko lapansi mwamphamvu chotero.” Koma, osuliza akuti: “Zonse zimene timadziŵa ponena za Yesu nzochokera m’Baibulo. Palibe zolembedwa zina za m’nthaŵi yake zonena za kukhalako kwake zimene ziripo.’ Eya, kodi zimenezi nzowona?
9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene olemba mbiri akale akudziko ndi olemba nkhani ananena ponena za Yesu? (b) Malinga ndi umboni wa olemba mbiri akale, kodi nchigamulo chotani chimene nazonse wodalirika akuchipereka?
9 Ngakhale kuti maumboni onena za Yesu Kristu operekedwa ndi olemba mbiri zadziko oyambirira ali ochepa, maumboni oterowo alipo. Cornelius Tacitus, wolemba mbiri wolemekezeka wa Roma wa m’zaka za zana loyamba, analemba kuti wolamulira wa Roma Nero ‘anaika liŵongo la kutentha Roma pa Akristu,’ ndiyeno Tacitus analongosola kuti: “Dzinalo [Akristu] lichokera kwa Kristu, amene bwanamkubwa Pontiyo Pilato anapha m’nthaŵi ya kulamulira kwa Tiberiyo.” Suetonius ndi Pliny Wamng’ono, olemba mbiri ena Achiroma apanthaŵiyo, nawonso anatchula za Kristu. M’kuwonjezera, Flavius Josephus, wolemba mbiri Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba, analemba m’bukhu lake Antiquities of the Jews ponena za imfa ya wophunzira Wachikristu Yakobo. Polongosola Josephus ananena kuti Yakobo anali “mbale wa Yesu, amene anatchedwa Kristu.”
10 Chotero The New Encyclopædia Britannica imati: “Zolembedwa zolekana zimenezi zimatsimikizira kuti m’nthaŵi zakale ngakhale otsutsa Chikristu sanakaikire Yesu kukhala munthu weniweni, kumene kunatsutsidwa kwa nthaŵi yoyamba ndipo pamaziko osakwanira chakumapeto kwa zaka za zana la 18, mkati mwa zaka za zana la 19, ndi kuchiyambiyambi kwa zaka za zana la 20.”
Kodi Yesu Anali Yani Kwenikweni?
11. (a) Kwakukulukulu, kodi ndimagwero okha ati odziŵitsa mbiri ya Yesu? (b) Kodi ndifunso lotani limene otsatira a Yesu anali nalo ponena za iye?
11 Kwakukulukulu, zodziŵika zonse lerolino ponena za Yesu zinalembedwa ndi otsatira ake a m’zaka za zana loyamba. Malipoti awo asungidwa m’Mauthenga Abwino—mabuku a Baibulo olembedwa ndi aŵiri a atumwi ake, Mateyu ndi Yohane, ndiponso aŵiri a ophunzira ake, Marko ndi Luka. Kodi zolembedwa za amuna ameneŵa zimavumbulanji ponena za umunthu wa Yesu? Kodi iye kwenikweni anali yani? Mabwenzi a Yesu a m’zaka za zana loyamba anasinkhasinkha za funso limenelo. Pamene anawona Yesu mozizwitsa akutontholetsa nyanja yoŵinduka ndi namondwe, mwakudzudzula, anadabwa mozizwa kuti: “Uyu ndani nanga?” Pambuyo pake pachochitika china, Yesu anafunsa atumwi ake kuti: “Mutani kuti Ine ndine yani?”—Marko 4:41; Mateyu 16:15.
12. Kodi timadziŵa motani kuti Yesu sindiye Mulungu?
12 Mutafunsidwa funsolo, kodi mungayankhe bwanji? Kodi Yesu anali yani kwenikweni? Ndithudi, ambiri m’Chikristu Chadziko akanena kuti anali Mulungu Wamphamvuyonse mumpangidwe waumunthu, Mulungu wovala thupi. Komabe, mabwenzi enieni a Yesu sanakhulupirire konse kuti iye anali Mulungu. Mtumwi Petro anamutcha “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Ndipo funafunani kulikonse, simudzaŵerenga konse kuti Yesu anadzinenera kukhala Mulungu. Mmalomwake, iye anauza Ayuda kuti anali “Mwana wa Mulungu,” osati Mulungu.—Yohane 10:36.
13. Kodi Yesu anali wosiyana motani ndi anthu ena onse?
13 Pamene Yesu anayenda modutsa nyanja yochita mafunde, ophunzira anachitanso chidwi ndi chenicheni chakuti iye anali munthu wosiyana ndi munthu aliyense. (Yohane 6:18-21) Anali munthu wapadera kwambiri. Izi ziri chifukwa chakuti poyambirira iye adakhalapo ndi moyo monga munthu wauzimu pamodzi ndi Mulungu kumwamba, inde, monga mngelo, wodziŵika m’Baibulo monga mngelo wamkulu. (1 Atesalonika 4:16; Yuda 9) Mulungu anamlenga iye Asanalenge zinthu zina zonse. (Akolose 1:15) Motero, kwanyengo yanthaŵi yosadziŵika, ngakhale chilengedwe chakuthupi chisanalengedwe, Yesu anali ndi mayanjano athithithi ndi Atate wake kumwamba, Yehova Mulungu, Mlengi Wamkulu.—Miyambo 8:22, 27-31; Mlaliki 12:1.
14. Kodi ndimotani mmene Yesu anadzakhalira munthu?
14 Ndiyeno, pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitapo, Mulungu anasamutsira moyo wa Mwana wake m’mimba ya mkazi wina. Mwakutero, anafikira kukhala mwana waumunthu wa Mulungu, wobadwa mwanjira yozoloŵereka kudzera mwa mkazi. (Agalatiya 4:4) Pamene Yesu anali kukula m’mimba ya amake, Mariya, ndipo pambuyo pake pamene anali kukula monga mnyamata, anali wodalira pa awo amene Mulungu adawasankha kukhala makolo ake apadziko lapansi. Potsirizira pake Yesu anafika paumwamuna, ndiyeno anapatsidwa chikumbukiro chonse cha mayanjano ake apapitapo ndi Mulungu kumwamba. Izi zinachitika pamene ‘miyamba inatsegukira iye’ pa ubatizo wake.—Mateyu 3:16; Yohane 8:23; 17:5.
15. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yesu anali munthu kotheratu pamene anali padziko lapansi?
15 Ndithudi, Yesu anali munthu wapadera. Komabe, iye anali mwamuna, wofanana ndi Adamu, mwamuna amene poyambirira Mulungu adamlenga ndi kumuika m’munda wa Edeni. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: ‘Munthu woyamba Adamu, anakhala wamoyo. Adamu wotsirizirayo anakhala mzimu wopatsa moyo.’ Yesu akutchedwa ‘Adamu wotsirizira’ chifukwa chakuti, mofanana ndi Adamu woyamba, Yesu anali munthu wangwiro. Koma pamene Yesu anafa, iye anaukitsidwa, ndipo anakagwirizananso ndi Atate wake kumwamba monga munthu wauzimu.—1 Akorinto 15:45.
Njira Yabwino Koposa Yophunzirira Ponena za Mulungu
16. (a) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kuyanjana ndi Yesu kukhala mwaŵi wapadera kwenikweni? (b) Kodi tinganenerenji kuti kuwona Yesu kunali kofanana ndi kuwona Mulungu?
16 Tangolingalirani kwa kamphindi za mwaŵi wodabwitsa umene ena anali nawo monga mabwenzi aumwini a Yesu pamene anali padziko lapansi! Tangoyerekezerani kumvetsera, kuwonerera, ndipo ngakhale kulankhula ndi kugwira ntchito ndi Munthu amene anatha mwinamwake zaka mabiliyoni ambirimbiri monga tsamwali wapafupi wa Yehova Mulungu kumwamba! Monga mwana wokhulupirika, Yesu anatsanzira Atate wake wakumwamba m’chirichonse chimene adachita. Kwenikweni, Yesu anatsanzira Atate kotheratu kotero kuti anatha kuuza atumwi ake kuphedwa kwake kutayandikira kuti: ‘Iye amene wandiwona ine wawona Atate.’ (Yohane 14:9, 10) Inde, mumkhalidwe uliwonse umene anayang’anizana nawo padziko lapansi, Yesu anachita monga momwe Atate wake, Mulungu Wamphamvuyonse, akanachitira ngati Iwo anali pano. Motero, pamene tiphunzira za moyo ndi uminisitala wa Yesu Kristu, kwenikweni, timaphunziradi mtundu wa munthu amene Mulungu ali.
17. Kodi mpambo wa Nsanja ya Olonda wakuti “Moyo ndi Uminisitala za Yesu” unali nchifuno chotani?
17 Chotero, mpambo wakuti “Moyo ndi Uminisitala za Yesu” umene unali m’makope otsatizana a Nsanja ya Olonda kuchokera mu September 1985 mpaka June 1991, sunangopereka chithunzi chabwino cha munthu Yesu komanso unaphunzitsa zambiri ponena za Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu. Pambuyo pa zigawo zake zoyamba ziŵiri, minisitala wina mpainiya analembera Watch Tower Society kuyamikira kuti: “Ndinjira yabwino kwambiri chotani nanga yoyandikirira kwambiri kwa Atate mwakudziŵa bwinopo Mwanayo!” Zimenezo nzowona chotani nanga! Chisamaliro chachifundo cha Atate kulinga kwa anthu ndi kukoma mtima kwake zikuwonekera m’moyo wa Mwanayo.
18. Kodi ndani anali Woyambitsa wa uthenga wa Ufumu, ndipo ndimotani mmene Yesu anavomerezera chimenechi?
18 Chikondi cha Yesu pa Atate wake, monga momwe chasonyezedwera mwakugonjera kwake kotheratu ku chifuniro cha Atate wake, chiridi chokondweretsa kuchiwona. ‘Sindichita kanthu kwa ine ndekha,’ Yesu anauza Ayuda amene anali kufuna kumupha, ‘koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.’ (Yohane 8:28) Chotero, pamenepa, Yesu sanali woyambitsa uthenga wa Ufumu umene analalikira. Anali Yehova Mulungu! Ndipo Yesu mobwerezabwereza anapereka thamo kwa Atate wake. “Sindinalankhula mwa Ine ndekha,” iye anatero, “koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. . . . Chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula.”—Yohane 12:49, 50.
19. (a) Kodi timadziŵa motani kuti Yesu anaphunzitsa m’njira imene Yehova amachitira? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako?
19 Komabe, Yesu sanangolankhula kapena kuphunzitsa zimene Atate anamuuza. Iye anachita zowonjezereka. Iye analankhula kapena kuphunzitsa m’njira imene Atate wake akanalankhula kapena kuphunzitsa nayo. Ndiponso, m’zochitika zake zonse ndi maunansi, iye anadzisungira ndi kuchita monga momwe Atate akanadzisungira ndi kuchitira pansi pamikhalidwe yofananayo. ‘Sakhoza Mwana kuchita kanthu payekha,’ Yesu anafotokoza, ‘koma chimene awona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwenso.’ (Yohane 5:19) M’njira iriyonse, Yesu anali chithunzi changwiro cha Atate wake, Yehova Mulungu. Chotero nkosadabwitsa kuti Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako! Choncho, nkofunikadi kuti timpende ndi chisamaliro chachikulu munthu wofunika koposa ameneyu!
Chikondi cha Mulungu Chiwonedwa mwa Yesu
20. Kodi ndimotani mmene mtumwi Yohane anadziŵira kuti ‘Mulungu ndiye chikondi’?
20 Kodi timaphunziranji mwakupenda mozama ndi mosamalitsa, moyo ndi uminisitala za Yesu? Eya, mtumwi Yohane anavomereza kuti ‘kulibe munthu anawona Mulungu.’ (Yohane 1:18) Komabe, Yohane analemba ndi chidaliro chotheratu pa 1 Yohane 4:8 kuti: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ Yohane anatha kunena zimenezi chifukwa chakuti anadziŵa za chikondi cha Mulungu kudzera mwazimene adawona mwa Yesu.
21. Kodi nchiyani chimene chinapangitsa Yesu kukhala munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako?
21 Mofanana ndi Atate, Yesu anali wachifundo, wokoma mtima, wodzichepetsa, ndi wofikirika. Ofooka ndi otsenderezedwa anatsitsimulidwa mwa iye, monga momwenso anachitira anthu amitundu yonse—amuna, akazi, ana, olemera, amphaŵi, amphamvu, ndiponso ochimwa. Ndithudi, chinali makamaka chitsanzo chachikondi chapadera cha Yesu, m’kutsanzira Atate wake, chimene chinampangitsa kukhala munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Ngakhale Napoléon Bonaparte akusimbidwa kukhala ananena kuti: “Alexander, Caesar, Charlemagne, ndi ineyo tinamanga maufumu, koma kodi ntchito zathu zinamangidwa pamaziko otani? Pamphamvu. Yesu Kristu yekha anamanga ufumu wake pachikondi, ndipo lerolino mamiliyoni a anthu akanamfera iye.”
22. Kodi ndimotani mmene ziphunzitso za Yesu zinaliri zosiyana kotheratu?
22 Ziphunzitso za Yesu zinali zosiyana kotheratu. “Musakanize munthu woipa,” Yesu anachenjeza, “koma amene adzakupanda iwe patsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.” “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” ‘Chitirani ena monga momwe mukafuna iwo kukuchitirani.’ (Mateyu 5:39, 44; 7:12) Ha, dziko likakhala losiyana chotani nanga ngati munthu aliyense anagwiritsira ntchito ziphunzitso zopambana zimenezi!
23. Kodi Yesu anachitanji kuti akhudze mitima ya anthu ndi kuwasonkhezera kuchita zabwino?
23 Mafanizo a Yesu, kapena zoweruzirapo, zinakhudza mitima, zikumasonkhezera anthu kuchita chabwino ndi kupeŵa choipa. Mungakumbukire fanizo lake lodziŵika bwino kwambiri la Msamariya wonyozeka amene anathandiza munthu wovulala wa fuko lina pamene amuna olambira a fuko la munthu mwiniyo sanatero. Kapena fanizo lonena za atate wokoma mtima, wokhululukira ndi mwana wake woloŵerera. Ndipo bwanji ponena za fanizo la mfumu imene inakhululukira kapolo ngongole ya madinari 60 miliyoni, komabe kapoloyo anatembenuka ndi kuponya kapolo mnzake m’ndende amene anali wosakhoza kulipira ngongole ya madinari 100 okha? Mwamafanizo okhweka, Yesu anapangitsa zochitika zadyera ndi zaumbombo kuwoneka zonyansa, ndipo zochitika zachikondi ndi zachifundo kukhala zokopa kwambiri!—Mateyu 18:23-35; Luka 10:30-37; 15:11-32.
24. Kodi nchifukwa ninji tinganene popanda chikaikiro kuti, Yesu ndiye munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako?
24 Komabe, chimene kwenikweni chinakopera anthu kwa Yesu ndi kuwasonkhezera kuchita zabwino chinali chakuti moyo wa iyemwini unayenderana ndendende ndi zimene adaphunzitsa. Anachita zimene analalikira. Anapirira moleza mtima zophophonya za ena. Pamene ophunzira ake anakangana ponena za amene adali wamkulu koposa, iye anawawongolera mokoma mtima mmalo mwakuwadzudzula mwaukali. Iye modzichepetsa anawathandiza m’zosoŵa zawo, ngakhale kusambitsa mapazi awo. (Marko 9:30-37; 10:35-45; Luka 22:24-27; Yohane 13:5) Potsirizira pake, iye mofunitsitsa anafa imfa yopweteka, osati kokha kaamba ka iwo, koma kaamba ka anthu onse! Popanda chikaikiro, Yesu anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Yesu anali munthu weniweni m’mbiri?
◻ Kodi tidziŵa bwanji kuti Yesu anali munthu, komabe ndimotani mmene analiri wosiyana ndi anthu ena onse?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuphunzira moyo wa Yesu kuli njira yabwino koposa yodziŵira Mulungu?
◻ Kodi tingadziŵenji ponena za chikondi cha Mulungu mwakuphunzira ponena za Yesu?
[Chithunzi patsamba 10]
Atumwi a Yesu anazizwa nafuna kudziŵa nati: “Uyu ndani nanga?”